ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: العاديات
آية:
 

العاديات

وَٱلۡعَٰدِيَٰتِ ضَبۡحٗا
“Ndikulumbilira akavalo othamanga ali ndi phuma,
التفاسير العربية:
فَٱلۡمُورِيَٰتِ قَدۡحٗا
“Ndi otulutsa moto ku zikhotwa (pomenyetsa miyendo m’miyala),
التفاسير العربية:
فَٱلۡمُغِيرَٰتِ صُبۡحٗا
“Ndi othira nkhondo adani mmawa (dzuwa lisadatuluke),
التفاسير العربية:
فَأَثَرۡنَ بِهِۦ نَقۡعٗا
“Ndi kuulutsa fumbi lambiri (kwa adani) nthawi imeneyo,
التفاسير العربية:
فَوَسَطۡنَ بِهِۦ جَمۡعًا
“Ndikulowelera mkatikati mwa adani.
التفاسير العربية:

إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لِرَبِّهِۦ لَكَنُودٞ
“Ndithu munthu ali wokanira Mbuye wake, (sathokoza Allah pa zimene amdalitsa nazo).
Mgulu la otaika mwapatulidwa anthu olungama amene zochita zawo zili zolungama, omwe amalamulira kutsatira njira yolungama ndi kupilira. Anthu otere saataika, chifukwa chakuti nthawi yawo amaigwiritsira ntchito pa zinthu zabwino, zowathandiza padziko ndi pambuyo pa imfa. Kupilira kulipo mitundu inayi:-
(a) Kupilira pochita zinthu zabwino zomwe zili zovuta kwa munthu kuzipitiriza, monga kupemphera Swala zisanu.
(b) Kupilira posiya kuchita zoipa zimene zili zovuta kwa munthu kuti azileke.
(c) Kuwapilira anthu anzako; kupilira ndi zoipa zawo posawabwezera choipa chilichonse.
(d) Kupilira ndi mazunzo a padziko, monga njala, matenda, kusauka ndi zina zotero.
التفاسير العربية:
وَإِنَّهُۥ عَلَىٰ ذَٰلِكَ لَشَهِيدٞ
“Ndithudi iye pa zimenezi ndi mboni (yodzichitira yekha kupyolera mzochitachita zake).
التفاسير العربية:
وَإِنَّهُۥ لِحُبِّ ٱلۡخَيۡرِ لَشَدِيدٌ
“Ndipo ndithu iye ndiwokonda chuma kwambiri (ndiponso ngwamsulizo).
Kujeda kwa mtundu uliwonse ndi koipa. Anthu ambiri amaganiza kuti kujeda ndi chinthu chochepa, saona kuti ndi chinthu choipa, pomwe Qur’an ikuletsa kwatunthu mpaka mwakuti imamufanizira munthu wojeda ngati munthu yemwe amadya minofu ya mnzake wakufa. Mu Ayah imeneyi, Allah wanena kuti “Wayilun” lomwe tanthauzo lake ndi “Kuonongeka koopsa.” Choncho nkofunika kwa munthu aliyense kupewa khalidwe lojeda.
التفاسير العربية:
۞أَفَلَا يَعۡلَمُ إِذَا بُعۡثِرَ مَا فِي ٱلۡقُبُورِ
“Kodi sakudziwa zikadzatulutsidwa za m’manda,
التفاسير العربية:
وَحُصِّلَ مَا فِي ٱلصُّدُورِ
“Ndikudzasonkhanitsidwa ndi kuonekera poyera zomwe zidali m’mitima?
التفاسير العربية:
إِنَّ رَبَّهُم بِهِمۡ يَوۡمَئِذٖ لَّخَبِيرُۢ
“Ndithu tsiku limenelo Mbuye wawo adzawadziwa kwambiri (ndikuwalongosolera zonse zochita zawo).
Mmenemo ndi momwe alili munthu wa umbombo, kukoma kwa chuma kwa iye, ndikuchisonkhanitsa ndikumachiwerengera akakhala ndi danga; sikuti akufuna kudziwa kuchuluka kwake koma kungokondweretsedwa ndikuchiwerengako. Saganizira zimene zingamuthandize iye mwini kapena kuthandiza anzake.
Chuma ntchito yake ndikuti chimthandize mwini chumacho pa zinthu zabwino zosiyanasiyana pamodzi ndi anzake, osati kungochikhazika ndikumangochiwerengera mokhumbiza ena.
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: العاديات
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق