ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: الحجر
آية:
 

الحجر

الٓرۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ وَقُرۡءَانٖ مُّبِينٖ
“۞ Alif-Lâm-Râ. Izi ndi Aaya (ndime) za m’buku (lomwe lasonkhanitsa chilichonse chofunika,) ndi Qur’an yomveka bwino.
التفاسير العربية:
رُّبَمَا يَوَدُّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوۡ كَانُواْ مُسۡلِمِينَ
“Nthawi zambiri omwe sadakhulupirire (pamene adzakhala m’Moto) adzalakalaka kuti akadakhala okhulupirira (pamoyo wa pa dziko lapansi).
التفاسير العربية:
ذَرۡهُمۡ يَأۡكُلُواْ وَيَتَمَتَّعُواْ وَيُلۡهِهِمُ ٱلۡأَمَلُۖ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ
“Asiye azidya (chakudya monga momwe zidyera nyama) ndi kusangalala; ndipo chiyembekezo chiziwatangwanitsa ndi kuwanyenga; posachedwa adziwa (kuti zimene amaziyembekezerazo nzabodza).
التفاسير العربية:
وَمَآ أَهۡلَكۡنَا مِن قَرۡيَةٍ إِلَّا وَلَهَا كِتَابٞ مَّعۡلُومٞ
“Ndipo sitidaononge mudzi uliwonse (m’midzi yochita zoipa) koma udali ndi nthawi yake (youwonongera) yodziwika.
التفاسير العربية:
مَّا تَسۡبِقُ مِنۡ أُمَّةٍ أَجَلَهَا وَمَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ
“Ndipo palibe mtundu wa anthu umene ungaitsogolere nthawi yake (yofera) kapena kuichedwetsa (itakwana kale).
التفاسير العربية:
وَقَالُواْ يَـٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِي نُزِّلَ عَلَيۡهِ ٱلذِّكۡرُ إِنَّكَ لَمَجۡنُونٞ
“Ndipo (osakhulupirira) akunena (mwachipongwe) “E iwe amene wavumbulutsiridwa ulaliki! Ndithudi ndiwe wamisala.”
التفاسير العربية:
لَّوۡمَا تَأۡتِينَا بِٱلۡمَلَـٰٓئِكَةِ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّـٰدِقِينَ
““Bwanji iwe osatibweretsera angelo (kuti akuchitire umboni) ngati uli mmodzi waonena zoona?”
التفاسير العربية:
مَا نُنَزِّلُ ٱلۡمَلَـٰٓئِكَةَ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَمَا كَانُوٓاْ إِذٗا مُّنظَرِينَ
“(Allah akuwauza:) “Ife sititsitsa angelo pokhapokha kutatsimikizika (tikawatuma kukapereka chilango kwa anthu). Ndipo pamenepo sangapatsidwe nthawi.”
التفاسير العربية:
إِنَّا نَحۡنُ نَزَّلۡنَا ٱلذِّكۡرَ وَإِنَّا لَهُۥ لَحَٰفِظُونَ
“Ndithu Ife ndife omwe tavumbulutsa Qur’an, ndipo ndithudi, tiisunga.
Mneneri Muhammad (s.a.w) pamene adakwezedwa kumwamba adaona zisonyezo zikuluzikulu za Allah monga Munda wa mtendere, Moto, mtengo wotchedwa Sidratul- Muntaha, Angelo, Aneneri ndi zina zododometsa.
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ فِي شِيَعِ ٱلۡأَوَّلِينَ
“Ndithudi tidatuma (atumiki) patsogolo pako m’magulu (a anthu) akale, oyamba.
التفاسير العربية:
وَمَا يَأۡتِيهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
“Ndipo sadali kuwadzera mtumiki aliyense, koma ankamchitira chipongwe.
التفاسير العربية:
كَذَٰلِكَ نَسۡلُكُهُۥ فِي قُلُوبِ ٱلۡمُجۡرِمِينَ
“Momwemo tikuupititsa (mkhalidwe wachipongwewu) m’mitima mwa oipa.
التفاسير العربية:
لَا يُؤۡمِنُونَ بِهِۦ وَقَدۡ خَلَتۡ سُنَّةُ ٱلۡأَوَّلِينَ
“Koma saikhulupirira Qur’aniyi chikhalirecho mafanizo a anthu oyamba awadutsa (ndipo aona momwe tidawaonongera).
التفاسير العربية:
وَلَوۡ فَتَحۡنَا عَلَيۡهِم بَابٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ فَظَلُّواْ فِيهِ يَعۡرُجُونَ
“Ndipo tikadawatsekulira (awa osakhulupirira) khomo lakumwamba ndipo nkukhala akukwera m’menemo (ndi kutsika monga momwe amafunira kuti zimenezo zikhale chozizwitsa cha Mtumiki),
التفاسير العربية:
لَقَالُوٓاْ إِنَّمَا سُكِّرَتۡ أَبۡصَٰرُنَا بَلۡ نَحۡنُ قَوۡمٞ مَّسۡحُورُونَ
“Akadati: “Ndithu maso athu aledzera; (iyayi) koma ndife anthu olodzedwa (tikuona zomwe sindizo).”
M’ndimeyi Allah akulamula anthu Ake kuti apembedze Iye Yekha; asapembedze china chake cholengedwa monga miyala, mitengo, dzuwa, mwezi, nkhalango zowilira, mizimu ya anthu akufa ndi ziwanda. Koma chikhulupiliro chathu chikhale mwa Allah yekha. Tikafuna kudziteteza tidziteteze ndi Allah. Ndiponso Allah watilamula kuchitira zabwino makolo. Tisawanenere mawu amwano ndiponso tisawakalipire. Koma tiwanenere mau aulemu.
التفاسير العربية:

وَلَقَدۡ جَعَلۡنَا فِي ٱلسَّمَآءِ بُرُوجٗا وَزَيَّنَّـٰهَا لِلنَّـٰظِرِينَ
“Ndithudi, kumwamba tidaikako “Buruji” (njira momwe zikuyendamo nyenyezi) ndipo tidakukongoletsa kwa okuwona.
التفاسير العربية:
وَحَفِظۡنَٰهَا مِن كُلِّ شَيۡطَٰنٖ رَّجِيمٍ
“Ndipo tidakuteteza kwa satana aliyense wopirikitsidwa (kumwambako akafuna kukamvetsera zimene zikunenedwa kumeneko).
التفاسير العربية:
إِلَّا مَنِ ٱسۡتَرَقَ ٱلسَّمۡعَ فَأَتۡبَعَهُۥ شِهَابٞ مُّبِينٞ
“Kupatula amene amamvetsera mobera; ndipo pompo chinsakali chamoto choonekera chimamtsata.
التفاسير العربية:
وَٱلۡأَرۡضَ مَدَدۡنَٰهَا وَأَلۡقَيۡنَا فِيهَا رَوَٰسِيَ وَأَنۢبَتۡنَا فِيهَا مِن كُلِّ شَيۡءٖ مَّوۡزُونٖ
“Ndipo nthaka tidaiyala ndi kuikamo mapiri ndipo tameretsa mmera wa chinthu chilichonse m’menemo mwamlingo (wake).
التفاسير العربية:
وَجَعَلۡنَا لَكُمۡ فِيهَا مَعَٰيِشَ وَمَن لَّسۡتُمۡ لَهُۥ بِرَٰزِقِينَ
“Ndipo mmenemo takupangirani zinthu zoyendetsa moyo (wanu zakudya ndi zakumwa ndi zina zotere) ndiponso (tidakupatsani ana ndi ziweto) zomwe inu simungathe kuzidyetsa. (Ife ndife amene tikuzikonzera chakudya chawo, osati inu).
التفاسير العربية:
وَإِن مِّن شَيۡءٍ إِلَّا عِندَنَا خَزَآئِنُهُۥ وَمَا نُنَزِّلُهُۥٓ إِلَّا بِقَدَرٖ مَّعۡلُومٖ
“Ndipo palibe chinthu chilichonse koma gwero lake likuchokera kwa Ife; ndipo sitichitsitsa koma mwamlingo wodziwika (osati mwachisawawa).
التفاسير العربية:
وَأَرۡسَلۡنَا ٱلرِّيَٰحَ لَوَٰقِحَ فَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَسۡقَيۡنَٰكُمُوهُ وَمَآ أَنتُمۡ لَهُۥ بِخَٰزِنِينَ
“Ndipo timazitumiza mphepo zitasenza madzi, ndipo madziwo tikuwatsitsa kuchokera kumitamboyo; kenako tikukumwetsani madziwo (tikukumwetseraninso ziweto zanu, mitengo yanu ndi zina), ndipo inu si amene mukuwasunga (madziwo).
التفاسير العربية:
وَإِنَّا لَنَحۡنُ نُحۡيِۦ وَنُمِيتُ وَنَحۡنُ ٱلۡوَٰرِثُونَ
“Ndipo ndithudi, Ife ndife omwe timapereka moyo, ndi kupereka imfa. Ndiponso Ife ndi Amlowam’malo (a chinthu chilichonse chimene chikusiidwa chopanda mwini).
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ عَلِمۡنَا ٱلۡمُسۡتَقۡدِمِينَ مِنكُمۡ وَلَقَدۡ عَلِمۡنَا ٱلۡمُسۡتَـٔۡخِرِينَ
“Ndipo ndithu tikuwadziwa mwa inu amene atsogola (amene adafa kale), ndipo ndithu tikuwadziwanso amene atsalira (ali ndi moyobe ndi amene sanabadwe).
التفاسير العربية:
وَإِنَّ رَبَّكَ هُوَ يَحۡشُرُهُمۡۚ إِنَّهُۥ حَكِيمٌ عَلِيمٞ
“Ndipo ndithu palibe chikaiko, Mbuye wako ndi Yemwe adzawasonkhanitsa (pambuyo pa imfa kuti adzawaweruze). Iye ndi Wanzeru zakuya, Wodziwa chilichonse.
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِن صَلۡصَٰلٖ مِّنۡ حَمَإٖ مَّسۡنُونٖ
“Ndipo ndithu tidamlenga munthu ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera, osinthika mtundu;
التفاسير العربية:
وَٱلۡجَآنَّ خَلَقۡنَٰهُ مِن قَبۡلُ مِن نَّارِ ٱلسَّمُومِ
“Ndipo ziwanda tidazilenga kale ndi moto wamphepo yotentha kwambiri.
التفاسير العربية:
وَإِذۡ قَالَ رَبُّكَ لِلۡمَلَـٰٓئِكَةِ إِنِّي خَٰلِقُۢ بَشَرٗا مِّن صَلۡصَٰلٖ مِّنۡ حَمَإٖ مَّسۡنُونٖ
“Ndipo (kumbuka) pamene Mbuye wako adauza angelo (kuti): “Ndithu Ine ndilenga munthu ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera osinthika mtundu.”
التفاسير العربية:
فَإِذَا سَوَّيۡتُهُۥ وَنَفَخۡتُ فِيهِ مِن رُّوحِي فَقَعُواْ لَهُۥ سَٰجِدِينَ
““Choncho ndikamkwaniritsa ndikumuuzira mzimu wolengedwa ndi Ine, muweramireni momulemekeza.’’
التفاسير العربية:
فَسَجَدَ ٱلۡمَلَـٰٓئِكَةُ كُلُّهُمۡ أَجۡمَعُونَ
“Choncho angelo onse adamuweramira.
التفاسير العربية:
إِلَّآ إِبۡلِيسَ أَبَىٰٓ أَن يَكُونَ مَعَ ٱلسَّـٰجِدِينَ
“Kupatula Iblis; adakana kukhala mmodzi mwa owerama.
التفاسير العربية:

قَالَ يَـٰٓإِبۡلِيسُ مَا لَكَ أَلَّا تَكُونَ مَعَ ٱلسَّـٰجِدِينَ
“Allah adati: “E iwe Iblis! Chifukwa ninji sudakhale pamodzi ndi owerama?”
التفاسير العربية:
قَالَ لَمۡ أَكُن لِّأَسۡجُدَ لِبَشَرٍ خَلَقۡتَهُۥ مِن صَلۡصَٰلٖ مِّنۡ حَمَإٖ مَّسۡنُونٖ
“Adati: “Sindingamuweramire munthu yemwe mwam’lenga ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera osinthika mtundu.”
التفاسير العربية:
قَالَ فَٱخۡرُجۡ مِنۡهَا فَإِنَّكَ رَجِيمٞ
“(Allah) adati: “Choncho choka m’menemo; ndithu iwe ndiwe wopirikitsidwa (ku chifundo Changa).”
التفاسير العربية:
وَإِنَّ عَلَيۡكَ ٱللَّعۡنَةَ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلدِّينِ
““Ndipo ndithu matembelero ali pa iwe mpaka tsiku lamalipiro.”
التفاسير العربية:
قَالَ رَبِّ فَأَنظِرۡنِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ
“(Iblis) adati: “Mbuye wanga choncho ndipatseni nthawi mpaka tsiku limene adzaukitsidwe kwa akufa.”
التفاسير العربية:
قَالَ فَإِنَّكَ مِنَ ٱلۡمُنظَرِينَ
“(Allah) adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi mwa opatsidwa nthawi (danga).”
التفاسير العربية:
إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡوَقۡتِ ٱلۡمَعۡلُومِ
“Kufikira tsiku la nthawi yodziwika (ikadzafika nthawi imeneyo, udzafa).”
التفاسير العربية:
قَالَ رَبِّ بِمَآ أَغۡوَيۡتَنِي لَأُزَيِّنَنَّ لَهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَأُغۡوِيَنَّهُمۡ أَجۡمَعِينَ
“(Satana) adati: “Mbuye wanga! Pakuti mwanena kuti ndine wosokera, choncho ndikawakometsera za m’dziko (kufikira kuti akakulakwireni), ndithu ndikawasokeretsa onse.”
التفاسير العربية:
إِلَّا عِبَادَكَ مِنۡهُمُ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
““Kupatula akapolo anu oyeretsedwa, mwa iwo.”
التفاسير العربية:
قَالَ هَٰذَا صِرَٰطٌ عَلَيَّ مُسۡتَقِيمٌ
“(Allah) adati: “Iyi ndinjira yoongoka yobwerera kwa Ine (ndipo adzandidzera akadzafuna).”
التفاسير العربية:
إِنَّ عِبَادِي لَيۡسَ لَكَ عَلَيۡهِمۡ سُلۡطَٰنٌ إِلَّا مَنِ ٱتَّبَعَكَ مِنَ ٱلۡغَاوِينَ
“Ndithudi akapolo Anga pa iwo sudzakhala ndi mphamvu kupatula okutsata (mwachifuniro chawo) mwa opotoka.”
التفاسير العربية:
وَإِنَّ جَهَنَّمَ لَمَوۡعِدُهُمۡ أَجۡمَعِينَ
“Ndithu Jahannam ndiwo malo awo olonjezedwa kwa onse.
التفاسير العربية:
لَهَا سَبۡعَةُ أَبۡوَٰبٖ لِّكُلِّ بَابٖ مِّنۡهُمۡ جُزۡءٞ مَّقۡسُومٌ
“Ili ndi makomo asanu ndi awiri; khomo lililonse lili ndi gawo logawidwa mwa iwo.
التفاسير العربية:
إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّـٰتٖ وَعُيُونٍ
“Ndithudi owopa Allah adzakhala m’minda ndi akasupe (omwe adzakhala patsogolo pawo).
التفاسير العربية:
ٱدۡخُلُوهَا بِسَلَٰمٍ ءَامِنِينَ
“(Ndipo tidzawauza) “Lowani m’menemo mwamtendere, mosatekeseka.”
التفاسير العربية:
وَنَزَعۡنَا مَا فِي صُدُورِهِم مِّنۡ غِلٍّ إِخۡوَٰنًا عَلَىٰ سُرُرٖ مُّتَقَٰبِلِينَ
“Ndipo tidzawachotsera mfundo za chidani zomwe zidali m’mitima mwawo; (adzakhala) mwachibale, (mokondana,) atakhala pa mipando yachifumu atayang’anizana nkhope.
التفاسير العربية:
لَا يَمَسُّهُمۡ فِيهَا نَصَبٞ وَمَا هُم مِّنۡهَا بِمُخۡرَجِينَ
“Mmenemo masautso sakawakhudza, ndiponso sadzatulutsidwamo.
التفاسير العربية:
۞نَبِّئۡ عِبَادِيٓ أَنِّيٓ أَنَا ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ
“Auze akapolo anga kuti ndithu Ine ndine Wokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha.
التفاسير العربية:
وَأَنَّ عَذَابِي هُوَ ٱلۡعَذَابُ ٱلۡأَلِيمُ
“Ndipo ndithu chilango Changa ndi chilango chopweteka zedi.
التفاسير العربية:
وَنَبِّئۡهُمۡ عَن ضَيۡفِ إِبۡرَٰهِيمَ
“Ndipo auze nkhani ya alendo a (Mneneri) Ibrahim.
التفاسير العربية:

إِذۡ دَخَلُواْ عَلَيۡهِ فَقَالُواْ سَلَٰمٗا قَالَ إِنَّا مِنكُمۡ وَجِلُونَ
“Pamene adalowa kwa iye ndikunena: “Salaman (Mtendere!)” (Iyenso adawayankha: “Mtendere ukhalenso pa inu.” Ndipo Pamene adaona kuti akana chakudya) Adati: “Ndithu ife tikukuopani.”
التفاسير العربية:
قَالُواْ لَا تَوۡجَلۡ إِنَّا نُبَشِّرُكَ بِغُلَٰمٍ عَلِيمٖ
“Iwo adati: “Usaope! Ife tikukuuza nkhani yabwino ya (kuti ubala) mwana wanzeru kwambiri.”
التفاسير العربية:
قَالَ أَبَشَّرۡتُمُونِي عَلَىٰٓ أَن مَّسَّنِيَ ٱلۡكِبَرُ فَبِمَ تُبَشِّرُونَ
“Iye adati: “Ha! Mukundiuza nkhani iyi pomwe ukalamba wandifikira? Kodi nkhani yabwinoyi mukundiuza mnjira yotani?”
التفاسير العربية:
قَالُواْ بَشَّرۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ فَلَا تَكُن مِّنَ ٱلۡقَٰنِطِينَ
“Iwo adati: “Takuuza nkhani yabwinoyi mwachoonadi; choncho, usakhale mwa otaya mtima.”
التفاسير العربية:
قَالَ وَمَن يَقۡنَطُ مِن رَّحۡمَةِ رَبِّهِۦٓ إِلَّا ٱلضَّآلُّونَ
“Iye adati: “(Ine sinditaya mtima ndi chifundo cha Allah. Ndipo) palibe angataye mtima ndi chifundo cha Allah, koma wosokera basi (yemwe sazindikira ukulu wa Allah).”
التفاسير العربية:
قَالَ فَمَا خَطۡبُكُمۡ أَيُّهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ
“Iye adati: “Nanga cholinga chanu china nchiyani, E inu otumidwa?”
التفاسير العربية:
قَالُوٓاْ إِنَّآ أُرۡسِلۡنَآ إِلَىٰ قَوۡمٖ مُّجۡرِمِينَ
“Iwo adati: “Ife tatumidwanso kwa anthu aja oipa (kuti tikawaononge).”
التفاسير العربية:
إِلَّآ ءَالَ لُوطٍ إِنَّا لَمُنَجُّوهُمۡ أَجۡمَعِينَ
““Kupatula akubanja la Luti, ndithu ife tikawapulumutsa onse.”
التفاسير العربية:
إِلَّا ٱمۡرَأَتَهُۥ قَدَّرۡنَآ إِنَّهَا لَمِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ
““Koma mkazi wake (wa Luti), tamkonzera kukhala mmodzi wa otsalira pambuyo.”
التفاسير العربية:
فَلَمَّا جَآءَ ءَالَ لُوطٍ ٱلۡمُرۡسَلُونَ
“Ndipo pamene atumikiwo adawadzera anthu a Luti (ali mmaonokedwe amunthu)
التفاسير العربية:
قَالَ إِنَّكُمۡ قَوۡمٞ مُّنكَرُونَ
“(Luti) adati: “Ndithudi, inu ndi anthu osadziwika (sitikudziwani).”
التفاسير العربية:
قَالُواْ بَلۡ جِئۡنَٰكَ بِمَا كَانُواْ فِيهِ يَمۡتَرُونَ
“Iwo adati: “Inde, ife takudzera ndi zomwe (iwo) adali kuzikaikira, (zomwe ndi chilango chawo).”
التفاسير العربية:
وَأَتَيۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ وَإِنَّا لَصَٰدِقُونَ
““Ndipo tadza kwa iwe ndi (chinthu) choonadicho, ndithu ife ndi owona (pazimene tinenazi).”
التفاسير العربية:
فَأَسۡرِ بِأَهۡلِكَ بِقِطۡعٖ مِّنَ ٱلَّيۡلِ وَٱتَّبِعۡ أَدۡبَٰرَهُمۡ وَلَا يَلۡتَفِتۡ مِنكُمۡ أَحَدٞ وَٱمۡضُواْ حَيۡثُ تُؤۡمَرُونَ
““Choncho, choka ndi banja lako mkati mwa usiku; ndipo iwe udziwatsata pambuyo pawo; tsono aliyense wa inu asayang’ane kumbuyo (akamva mkokomo wachilango chochokera kumwamba, kuopa kuti angafe), ndipo yendani (mwachangu) kunka komwe mukulamulidwa.”
التفاسير العربية:
وَقَضَيۡنَآ إِلَيۡهِ ذَٰلِكَ ٱلۡأَمۡرَ أَنَّ دَابِرَ هَـٰٓؤُلَآءِ مَقۡطُوعٞ مُّصۡبِحِينَ
“Ndipo tidamudziwitsa iyeyo (Luti) lamulo lathu lakuti ndithu phata lawo anthu (ochimwawo) lidzadulidwa kum’banda kucha.
التفاسير العربية:
وَجَآءَ أَهۡلُ ٱلۡمَدِينَةِ يَسۡتَبۡشِرُونَ
“Ndipo adadza (kwa Luti) anthu a m’mudziwo akusangalala (poona kuti kwadza alendo okongola kuti achite nawo zadama).
Tanthauzo la ndime iyi nkuti mkono wako usakhale wofumbata posiya kugawira ena zomwe ulinazo; ndikutinso usatambasule popatsa mosakaza koma kuchita zapakatikati; osachita umbombo ndiponso osasakaza. Anthu aumbombo ndi osakaza chuma, ndi abale a satana.
التفاسير العربية:
قَالَ إِنَّ هَـٰٓؤُلَآءِ ضَيۡفِي فَلَا تَفۡضَحُونِ
“(Mneneri Luti) adati: “Ndithu awa ndialendo anga; choncho musandiyalutse (pochita nawo zadama).”
التفاسير العربية:
وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَلَا تُخۡزُونِ
““Muopeninso Allah, ndipo musandichititse manyazi (pamaso pawo).”
التفاسير العربية:
قَالُوٓاْ أَوَلَمۡ نَنۡهَكَ عَنِ ٱلۡعَٰلَمِينَ
“Iwo adati (kwa Mneneri Luti): “Kodi sitidakuletse kulandira anthu (achilendo)?”
التفاسير العربية:

قَالَ هَـٰٓؤُلَآءِ بَنَاتِيٓ إِن كُنتُمۡ فَٰعِلِينَ
“Iye adati: “Awa (akazi onsewa ali ngati) ana anga. Ngati inu ndinu ochita (chimene chalamulidwa, akwatireni; musachite zauve ndi alendowa).”
التفاسير العربية:
لَعَمۡرُكَ إِنَّهُمۡ لَفِي سَكۡرَتِهِمۡ يَعۡمَهُونَ
“Ndikulumbira moyo wako, ndithu iwo m’kuledzera kwawo (ndi zoipa) akungoyumbayumba.
التفاسير العربية:
فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّيۡحَةُ مُشۡرِقِينَ
“Choncho mkuwe wa chilango udawagwira pamene dzuwa linkatuluka.
التفاسير العربية:
فَجَعَلۡنَا عَٰلِيَهَا سَافِلَهَا وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهِمۡ حِجَارَةٗ مِّن سِجِّيلٍ
“Choncho (midziyo) tidaigadabula kumwamba kukhala pansi, (pansi kukhala kumwamba); ndipo tidawavumbwitsira mvula yamiyala (yotentha) ya moto.
التفاسير العربية:
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّلۡمُتَوَسِّمِينَ
“Ndithudi, (m’nkhani iyi) muli malingaliro (aakulu) kwa anthu olingalira zinthu.
التفاسير العربية:
وَإِنَّهَا لَبِسَبِيلٖ مُّقِيمٍ
“Ndipo (midzi) iyi (yomwe tidaiwononga chotereyi), ili chikhalire m’njira moyenda anthu (ndipo iwo akuona zizindikiro zake).
التفاسير العربية:
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ
“Ndithudi, mzimenezi muli phunziro (lalikulu) kwa okhulupirira.
التفاسير العربية:
وَإِن كَانَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡأَيۡكَةِ لَظَٰلِمِينَ
“Ndipo ndithu anthu a m’nkhalango (anthu a Mneneri Shuaib) adali ochita zoipa kwabasi.
التفاسير العربية:
فَٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡ وَإِنَّهُمَا لَبِإِمَامٖ مُّبِينٖ
“Choncho, tidawalanga. Ndipo (maiko) awiriwa ali m’njira zoonekera, (momwe Aquraish amadutsa pa maulendo awo).
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ كَذَّبَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡحِجۡرِ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
“Ndipo ndithu okhala m’chigwa cha Hijr (Asamuda), Adatsutsa atumiki.
التفاسير العربية:
وَءَاتَيۡنَٰهُمۡ ءَايَٰتِنَا فَكَانُواْ عَنۡهَا مُعۡرِضِينَ
“Tidawapatsa zisonyezo zathu, koma sadazilabadire.
التفاسير العربية:
وَكَانُواْ يَنۡحِتُونَ مِنَ ٱلۡجِبَالِ بُيُوتًا ءَامِنِينَ
“Iwo adali kujoba nyumba m’mapiri mwamtendere (ankaboola mapiri kuwasandutsa nyumba zawo).
التفاسير العربية:
فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّيۡحَةُ مُصۡبِحِينَ
“Choncho, chiphokoso cha chilango chidawapeza m’mawa.
التفاسير العربية:
فَمَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
“Sichidawathandize (chuma) chomwe ankachipeza (ngakhalenso zimene ankazichita).
التفاسير العربية:
وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَآ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۗ وَإِنَّ ٱلسَّاعَةَ لَأٓتِيَةٞۖ فَٱصۡفَحِ ٱلصَّفۡحَ ٱلۡجَمِيلَ
“Sitidalenge thambo ndi nthaka ndi (zonse) zapakati pake koma (kulimbikitsa) choonadi. Ndipo palibe chikaiko, Qiyâma idza. Choncho mkhululukire kukhululuka kwabwino (aliyense wokuchitira zoipa).
التفاسير العربية:
إِنَّ رَبَّكَ هُوَ ٱلۡخَلَّـٰقُ ٱلۡعَلِيمُ
“Ndithudi, Mbuye wako, Iye ndi Mlengi wa zonse, Wodziwa kwambiri.
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَٰكَ سَبۡعٗا مِّنَ ٱلۡمَثَانِي وَٱلۡقُرۡءَانَ ٱلۡعَظِيمَ
“Ndipo ndithu takupatsa (Ayah izi) zisanu ndi ziwiri zomawerenga kawirikawiri, (Sûrat Al-Fatihah), ndi Qur’an yolemekezeka.
التفاسير العربية:
لَا تَمُدَّنَّ عَيۡنَيۡكَ إِلَىٰ مَا مَتَّعۡنَا بِهِۦٓ أَزۡوَٰجٗا مِّنۡهُمۡ وَلَا تَحۡزَنۡ عَلَيۡهِمۡ وَٱخۡفِضۡ جَنَاحَكَ لِلۡمُؤۡمِنِينَ
“Usatong’olere maso ako (kuyang’ana) zimene tawasangalatsa nazo mitundumitundu ya mwa iwo (monga chuma cha anthu osakhulupirira). Usawadandaulirenso iwo ndipo tsitsa phiko lako kwa okhululupirira, (uwafungatire).
التفاسير العربية:
وَقُلۡ إِنِّيٓ أَنَا ٱلنَّذِيرُ ٱلۡمُبِينُ
“Ndipo nena: “Ndithu ine ndine mchenjezi woonekera (sindikubisa chilichonse kuopera kuti chingakutsikireni chilango).”
التفاسير العربية:
كَمَآ أَنزَلۡنَا عَلَى ٱلۡمُقۡتَسِمِينَ
“Monga momwe tidatsitsira (chilango) kwa amene adadzigawa m’magulu.
التفاسير العربية:

ٱلَّذِينَ جَعَلُواْ ٱلۡقُرۡءَانَ عِضِينَ
“Omwe aichita Qur’an kukhala magawomagawo; (zina nkuzikhulupirira, zina nkuzitsutsa).
التفاسير العربية:
فَوَرَبِّكَ لَنَسۡـَٔلَنَّهُمۡ أَجۡمَعِينَ
“(Allah akudzilumbilira kuti:) Pali Mbuye wako, tidzawafunsa onse (tsiku la Qiyâma).
التفاسير العربية:
عَمَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
“Pazimene ankachita (padziko lapansi).
التفاسير العربية:
فَٱصۡدَعۡ بِمَا تُؤۡمَرُ وَأَعۡرِضۡ عَنِ ٱلۡمُشۡرِكِينَ
“Choncho, lengeza zimene ukulamulidwa, ndipo uwapewe opembedza mafano, (usaope chilichonse kwa iwo).
التفاسير العربية:
إِنَّا كَفَيۡنَٰكَ ٱلۡمُسۡتَهۡزِءِينَ
“Ndithu Ife tikukwanira kukuteteza ku (zoipa za) achipongwe.
التفاسير العربية:
ٱلَّذِينَ يَجۡعَلُونَ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَۚ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ
“Omwe akupanga milungu ina ndi kuiphatikiza ndi Allah, posachedwapa adziwa (zotsatira zake).
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ نَعۡلَمُ أَنَّكَ يَضِيقُ صَدۡرُكَ بِمَا يَقُولُونَ
“Ndithu Ife tikudziwa kuti chifuwa chako chikubanika ndi zimene akunenazo.
التفاسير العربية:
فَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ وَكُن مِّنَ ٱلسَّـٰجِدِينَ
“(Koma pirira), lemekeza Mbuye wako pamodzi ndi kumtamanda (ndi rnbiri Zake zabwino) ndipo khala mwa olambira (Allah.)
التفاسير العربية:
وَٱعۡبُدۡ رَبَّكَ حَتَّىٰ يَأۡتِيَكَ ٱلۡيَقِينُ
“Ndipo mpembedze Mbuye wako mpaka chikufike chitsimikizo (imfa).
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: الحجر
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق