ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني آية: (10) سورة: الكهف
إِذۡ أَوَى ٱلۡفِتۡيَةُ إِلَى ٱلۡكَهۡفِ فَقَالُواْ رَبَّنَآ ءَاتِنَا مِن لَّدُنكَ رَحۡمَةٗ وَهَيِّئۡ لَنَا مِنۡ أَمۡرِنَا رَشَدٗا
Pamene anyamata adathawira kuphanga nati: “Mbuye wathu! Tipatseni chifundo chochokera kwa Inu, ndipo tikonzereni chiongoko m’zochita zathu.”[256]
[256] Nkhani ya eni phanga monga momwe adaifotokozera omasulira Qur’an, idali motere:-
Mfumu yomwe idapondereza anthu inkatchedwa Dikiyanusu idali mu m’zinda wina kudziko la Roma umene unkatchedwa Tartusi, Mneneri Isa (Yesu) atapita kale. Mfumuyi idali kuitana anthu kuti azipembedza mafano. Ndipo imapha aliyense wokhulupilira mwa Allah amene sadali kuvomereza uthenga wake wopotokawo kufikira chisokonezo ndi masautso zidawakulira anthu okhulupilira Allah. Anyamata omwe adali okhulupilira Allah ataona zimenezo, anadandaula kwambiri. Ndipo nkhani ya anyamata idamufika mfumu yopondereza anthuyo ndipo adatumiza mithenga kuti akawatenge anyamatawo. Anyamatawo pamene adaimilira pamaso pa mfumu, iyo idawaopseza kuti iwapha ngati akana kupembedza mafano ndi kukana kupereka nsembe. Koma iwo adatsutsana nayo naonetsera poyera chikhulupiliro chawo mwa Allah. Adati: ‘‘Mbuye wathu ndi Mbuye wathambo ndi nthaka. Sitingapembedze mulungu wina kusiya Iye.”
Mfumu idati kwa iwo: “ Inu ndinu anyamata amisinkhu yochepa, choncho ndikukupatsani mwayi mpaka mawa kuti mukaganize bwino.” Tero iwo adathawa usiku namdutsa m’busa yemwe adali ndi galu. M’busayo pamodzi ndi galu wake adawatsatira, ndipo pamene kudacha adabisala m’phanga lalikulu la m’phiri. Mfumu pamodzi ndi ankhondo ake, adawatsatira mpaka kukafika ku phangalo. Koma anthu ake adaopa kulowa m’phangamo ndipo mfumu idati: “Atsekereni khomo laphangali kuti afere komweko ndi njala ndi ludzu. Ndipo Allah adawagoneka tulo anyamata a kuphanga aja; adakhala ali mtulo chigonere osadziwa kanthu mpaka padapita zaka zikwi zitatu (300) ndi zaka zisanu ndi zinayi (9). Kenako Allah adawaukitsa. Ndipo iwo amaganiza kuti akhala kuphangako tsiku limodzi, kapena theka la tsiku. Ndipo adayamba kumva njala namtuma m’modzi wawo kuti akawagulire chakudya. Koma adamulangiza akadzibise ndiponso akachenjere kuti anthu asamuzindikire. Choncho iye adapita mpaka kukafika m’mudzimo. Kuja anapeza zizindikiro za mudziwo zasintha.
Palibe aliyense mwa nzika zam’mudzimo amene adamdziwa. Yekha adadzinong’oneza: “Mwinatu ine ndasokera njira yakumudzi kwathu kuja.” Komabe adagula chakudya. Ndipo pamene adapereka ndalama kwa wogulitsa adayamba kuitembenuzatembenuza ndalama ija m’manja mwake. Adati: “Mwaipeza kuti ndalama iyi?” Choncho anthu adasonkhana nayang’ana ndalama ija modabwa nati: “Kodi mnyamata iwe ndiwe yani, kapenatu mwatulukira chuma chomwe chidabisidwa m’nthaka ndi anthu akale?” Iye adati kwa iwo “lyayi. Ndikulumbira Allah, sindidapeze chuma chokwiliridwa m’nthaka. Iyi ndi ndalama yomwe mtundu wanga umagwiritsa ntchito.” Iwo adati kwa iye: “Ndalamayi njakale kwambiri, m’nyengo ya mfumu Dikiyanusu.” Iye adati modabwa: “Adatani Dikiyanusiyo?” Iwo adati, “Adafa kalekale!” Iye adati:” Ndikulumbira Allah, sangandikhulupirire aliyense zimene nditi ndikuuzeni. Ife tidali anyamata. Ndipo mfumuyo idatikakamiza kupembedza mafano. Choncho tidaithawa usiku wadzulo nkupita kukabisala kuphanga. Tere lero anzanga andituma kuti ndikagule chakudya. Choncho tiyeni pamodzi kuphangalo kuti nkakuonetseni anzangawo. Iwo adadodoma ndi zonena zakezo nadziwitsa mfumu ya nthawi imeneyo nkhani za munthuyu. Mfumuyo idali yokhulupilira Allah. Ndipo iyo itamva nkhaniyi, idapita pamodzi ndi ankhondo ake ndi nzika za m’mudziwo. Atafika kuja pafupi ndi phangalo, anthu akuphangalo adamva phokoso ndi migugu yamahatchi ndipo adaganiza kuti adali ankhondo a Dikiyanusu. Choncho onse adaimilira kupemphera. Ndipo mfumu idalowa nkuwapeza akupemphera. Pamene adamaliza kupemphera mfumu idagwirana nawo chanza niiwauza kuti iyo imakhulupilira Allah, ndikuti Dikiyanusu adamwalira kalekale. Kenako mfumuyo idamvera nkhani yawo niidziwa kuti, Allah wawaukitsa kuti chikhale chisonyezo kwa anthu kuti Allah adzawaukitsa anthu akufa. Kenako Allah adawagonekanso natenga mizimu yawo iwo ali mtulo chomwecho. Ndipo anthu adayamba kunena: “Timange Msikiti pomwe pali iwowapa wopembedzamo Allah.”
التفاسير العربية:
 
ترجمة معاني آية: (10) سورة: الكهف
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق