“Iye ndi Yemwe wakuvumbulutsira buku (ili la Qur’an), lomwe mkati mwake muli ndime zomveka zomwe ndimaziko a bukuli. Ndipo zilipo zina zokuluwika. Koma amene m’mitima mwawo muli kusokera, akutsata zomwe zili zokuluwika ndi cholinga chofuna kusokoneza anthu, ndi kufuna kudziwa tanthauzo lake lenileni. Palibe amene akudziwa tanthauzo lake lenileni koma Allah basi. Koma amene azama pa maphunziro, amanena: “Tawakhulupirira (ma Ayah amenewa). Onse ngochokera kwa Mbuye wathu.” Ndipo palibe angakumbukire koma eni nzeru basi.
“(Khalidwe la awa osakhulupiira, amumbadwo wako iwe mneneri Muhammad {s.a.w}, liri) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi amene adalipo pambuyo pawo. (Iwo) adatsutsa zisonyezo Zathu. Choncho, Allah adawakhaulitsa chifukwa cha machimo awo. Ndipo Allah Ngolanga mwaukali.
“Auze amene sadakhulupirire: “Posachedwapa mugonjetsedwa ndi kusonkhanitsidwa ndi kuponyedwa ku Moto. Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!”
Apa akunena zina mwa zozizwitsa zomwe mneneri Isa (Yesu) anadza nazo, ndipo zina mwa izo ndikuumba ndi dongo chifanizo cha mbalame. Kenako nkuchiuzira chikhaladi mbalame yamoyo mwa chilolezo cha Allah.
““Ndithudi, padapezeka chisonyezo chachikulu kwa inu m’magulu awiri omwe adakumana (tsiku la nkhondo ya Badri), pomwe gulu limodzi limamenya (nkhondo) pa njira ya Allah, pamene linalo lokanira, (ndipo gululo) linkawaona (Asilamu) kukhala ochuluka kawiri kuposa ilo, poona ndi maso awo. Ndipo Allah amamlimbikitsira mphamvu ndi chipulumutso chake amene wamfuna. Ndithudi, m’zimenezo muli malingaliro (akulu) kwa eni kupenyetsetsa mwanzeru.”
“Kwakometsedwa kwa anthu kukonda zilakolako (za moyo wawo) monga akazi, ana, milumilu ya chuma cha golide ndi siliva, ndi mahachi oyang’aniridwa bwino, ziweto ndi mbewu. Izo ndi zosangalatsa za moyo wa dziko lapansi (zomwe sizili kanthu). Koma kwa Allah ndiko kuli mabwelero abwino.
“Allah (Mwini) akuikira umboni kuti: “Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye basi.” Ndipo akuikiranso umboni (zomwezi) angelo ndi eni nzeru (kuti Iye) Ngokhazikitsa chilungamo. Palibe wina wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
“Ndithudi, chipembedzo (choona) kwa Allah ndi Chisilamu. Ndipo amene adapatsidwa buku (Ayuda ndi Akhrisitu) sadatsutsane koma pambuyo powabwerera kuzindikira. (Adatsutsana) chifukwa cha dumbo lomwe lidali pakati pawo. Ndipo amene akukana zisonyezo za Allah, (Allah akamulanga pa tsiku la chiweruziro). Ndithu Allah Ngwachangu powerengera.
“Kodi sukuwaona omwe apatsidwa gawo la buku (la Allah)? Akuitanidwa ku buku la Allah kuti liwaweruze pakati pawo; kenako gulu lina la iwo likutembenukira kumbali iwo ali onyoza.
(Ndime 59-62) Ndime izi zidavumbulutsidwa pamene nthumwi za Chikhirisitu zidadza kwa Mtumiki (s.a.w) kuchokera ku Najirani. Iwowo adakangana ndi Mtumiki wa Allah pa nkhani ya Isa (Yesu). Iwo adati kwa Mtumiki wa Allah: “Bwanji iwe ukutukwana Mneneri wathu?” Iye adati: “Kodi ndikutukwana chotani?” Iwo adati: “Iwe ukuti iyeyo ndikapolo wa Allah.” Iye adati: “Inde. Iyeyo ndi kapolo wa Allah ndiponso mawu ake omwe adawaponya mwa namwali.’ Zitatero iwo adapsa mtima ndipo anakwiya nati: “Kodi iwe udamuonapo munthu wobadwa popanda tate? Ngati ukunenadi zoona tationetsa munthu wotere.” Apa mpomwe Allah adavumbulutsa ndime yakuti “Ndithudi, fanizo la Isa (Yesu) kwa Allah lili ngati fanizo la Adam”. Kenako anawaitanira ku Chisilamu. Iwo adati: “Tidalowa kale m’Chisilamu iwe usanadze.” Mtumiki (s.a.w) adati: “Mwanama. Pali zinthu zitatu zikukuletsani kulowa m’Chisilamu:
(a) Kunena kwanu mawu oti Allah wadzipangira mwana.
(b) Kudya kwanu nyama ya nkhumba.
(c) Kulambira kwanu mtanda.”
Pamene adapitiriza kumtsutsa mneneri Muhammad (s.a.w) adawapempha kuti atembelerane ponena kuti: “E Ambuye Mulungu! Mtembelereni ndi kumlanga amene akunena zabodza mwa ife pa nkhani ya Isa (Yesu)! Pompo Mtumiki (s.a.w) adasonkhanitsa anthu ake. Koma iwo atakhala upo adagwirizana kuti asalole kuopa kuti chilango chingawatsikire. Potero zidadziwika kwa anthu kuti iwo ngabodza.
“Asilamu asapale ubwenzi osakhulupirira kusiya Asilamu anzawo. Amene achite zimenezo, sadzakhala ndi chilichonse pachipembedzo cha Allah, kupatula (kupalana nawo ubwenzi mwachiphamaso) chifukwa cha kudzitchinjiriza kwa iwo. Ndipo Allah Iye Mwini akukuchenjezani (za chilango Chake). Ndipo kobwerera ndi kwa Allah (basi).
“Ana ena kuchokera mwa ena pakati pawo. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa.
Apa akunenetsa kuti nyumba yoyamba kukhazikitsidwa kwa anthu kuti ikhale yochitira mapemphero ndi Al-Kaaba, osati Baiti Muqaddas monga momwe Ayuda amakhulupilira.
“Mwadzidzidzi, mngelo adamuitana uku iye ataimilira akupemphera mchipinda cha m’kachisi: “Allah akukuuza nkhani yabwino (yakuti ubereka mwana; dzina lake) Yahya yemwe adzakhala wotsimikizira (mneneri yemwe adzabadwa) ndi liwu lochokera kwa Allah, (yemwe ndi mneneri Isa (Yesu) amene adzakhalanso wolemekezeka ndi wolungama ndi mneneri wa mwa anthu abwino.”
“(Kumbukira) pamene angelo adati: “E iwe Mariya! Ndithu Allah akukuuza nkhani yabwino (kuti ubereka mwana popanda mwamuna koma kupyolera mu) liwu lochokera kwa Iye (Allah, lakuti: “Bereka,” ndipo nkubereka popanda kupezana ndi mwamuna). Dzina lake ndi Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, adzakhala wolemekezeka pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro; ndiponso ndi mmodzi wa oyandikitsidwa kwa Allah.
“Koma pamene Isa (Yesu) adazindikira mwa iwo kusakhulupirira adati: “Ndani akhale athandizi anga kwa Allah (popitiriza kufalitsa Chipembedzo Chake)?” Ophunzira ake adati: “Ife ndife athandizi a Allah (pofalitsa Chipembedzo Chake). Takhulupirira Allah; ndipo ikira umboni kuti ife ndithu ndi odzipereka kwa Allah (Asilamu).”
“Ndipo (Ayuda) adakonza chiwembu (chofuna kupha Isa (Yesu), koma Allah adachiwononga chiwembu chawocho. Allah Ngokhoza bwino zedi poononga ziwembu za anthu a chiwembu.
“(Kumbukirani) pamene Allah adati: “Iwe Isa (Yesu)! Ine ndikukwaniritsira nyengo yako yokhala ndi moyo (Ayuda sachita kanthu kwa iwe). Ndipo ndikunyamulira kwa Ine ndiponso ndikuyeretsa kwa anthu osakhulupirira (omwe ndi adani ako). Ndipo amene akutsata (iwe) ndiwasankha kukhala apamwamba pa amene sadakhulupirire kufikira tsiku lachimaliziro. Kenako kobwerera kwanu nkwa Ine, ndipo ndidzaweruza pakati panu pa zomwe mudali kusiyana.
“Tsopano amene akutsutsana nawe (iwe Mtumiki s.a.w) pa ichi pambuyo pokudzera kuzindikira, auze: “Bwerani tiitane ana athu ndi ana anu, akazi athu ndi akazi anu, ife ndi inu; kenako modzichepetsa tipemphe tembelero la Allah kuti likhale pa amene ali abodza (mwa ife).”
“Nena: “Inu eni buku (la Allah, Ayuda ndi Akhrisitu!) Idzani ku liwu lolingana pakati pathu ndi inu (lakuti) tisapembedze aliyense koma Allah (Mmodzi Yekha), ndiponso tisamphatikize ndi chilichonse ndipo ena mwa ife asawasandutse anzawo kukhala milungu m’malo mwa Allah.” Ngati atembenuka ndi kunyoza, nenani: “Ikirani umboni kuti ife ndife Asilamu (ogonjera malamulo a Allah).”
“Ndithu anthu omwe ali oyenera kudzilumikiza ndi Ibrahim ndi amene adamutsata (m’nyengo yake) ndi Mtumiki uyu (Muhammad {s.a.w}) ndi amene amkhulupirira (Mtumikiyu). Ndipo Allah ndi Mtetezi wa okhulupirira.
“Ndipo musakhulupirire aliyense kupatula yekhayo yemwe watsata chipembedzo chanu. (Allah adauza Mtumiki {s.a.w}), nena: “Ndithudi, chiongoko chenicheni ndi chiongoko cha Allah basi.” (Amene adapatsidwa buku Adanena kwa anzawo: “Musakhulupirire) kuti angapatsidwe aliyense zofanana ndi zomwe mwapatsidwa inu (Ayuda ndi Akhrisitu), kapena kuti angakutsutseni kwa Mbuye wanu.” (Allah adati kwa mtumiki{s.a.w}), nena: “Ndithu zabwino zonse zili m’manja mwa Allah; amazipereka kwa yemwe wamfuna. Allah ndi Mataya, Ngodziwa.”
“Ndipo mwa iwo muli anthu ena oti ukawasungitsa milumilu ya chuma, akubwezera. Ndipo mwa iwo muli ena oti ukawasungitsa “dinar” (ndalama imodzi) sangakubwezere pokhapokha upitirize kwa iye kuimilira (kulonjelera). Izi nchifukwa chakuti amanena: “Palibe njira pa ife (yotidzudzulira) chifukwa chozibera mbulizi.” Koma akumnamizira Allah uku iwo akudziwa.
“Ndipo ndithu mwa iwo muli gulu lomwe likukhotetsa malirime awo (powerenga) buku kuti muwaganizire (mawu awowo) kuti ndi a m’buku la Allah); pomwe si a m’buku (la Allah). Ndipo akunena: “Izi zachokera kwa Allah.” Pomwe zimenezo sizinachokere kwa Allah; ndipo akumnamizira Allah uku akudziwa.
“Sikoyenera kwa munthu yemwe Allah wampatsa buku ndi chiweruzo ndi uneneri, kenako nanena kwa anthu: “Khalani opembedza ine, mmalo mwa Allah.” Koma (awauze): “Khalani opembedza Allah, anzeru, aluntha chifukwa choti mukuphunzitsa buku ndi chifukwanso cha zomwe mukaphunzira.”
“Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adatenga lonjezo kwa aneneri, (n’kuwauza): “Ndikakupatsani buku ndi nzeru, nakudzerani Mtumiki wotsimikizira zomwe zili pamodzi ndi inu, mudzamkhulupirire ndi kumthangata.” (Allah) adatinso: “Kodi mwavomereza ndi kulandira pa zimenezi pangano langali?” (Iwo) adati: “Tavomereza.” (Iye) adati: “Tsono chitirani umboni, ine ndili pamodzi nanu mwa oikira umboni.”
“Kodi akufuna chipembedzo chomwe si cha Allah pomwe chinthu chilichonse chili kumwamba ndi pansi chikugonjera Iye, mofuna kapena mosafuna? Ndipo onse adzabwezedwa kwa Iye.
“Nena: “Takhulupirira Allah ndi zomwe zavumbulutsidwa pa ife, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa Ibrahim, ndi Ismail, Ishâq ndi Yaqub ndi zidzukulu (zake), ndi zimene adapatsidwa Mûsa ndi Isa (Yesu), ndi aneneri (ena) zochokera kwa Mbuye wawo. Sitisiyanitsa aliyense pakati pawo, ndipo ife kwa Iye ndi Asilamu (odzipereka kwathunthu).”
“Ndithudi amene sadakhulupirire, nkumwalira pamene ali osakhulupirira, sikudzalandiridwa kwa aliyense wa iwo ngakhale atapereka dipo la golide lodzadza dziko lonse. Iwo ndi omwe adzalandire chilango chopweteka, ndipo sadzakhala ndi athandizi.
“Zakudya zonse zidali zololedwa kwa ana a Israyeli kupatula chimene adadziretsa Israyeli mwini wake Taurat isadavumbulutsidwe. Nena: “Bwerani ndi Tauratiyo ndipo iwerengeni ngati mukunena zoona.”
Apa akunena nkhani ya nkhondo yachiwiri yaikulu kwabasi pambiri ya Chisilamu, nkhondo ya Uhudi. Nkhondo imeneyi Asilamu adakumana ndi masautso akulu chifukwa cha Asilamu ena amene adaswa lamulo la Mtumiki (s.a.w). Ndiponso chifukwa cha anthu ena omwe adalowa Chisilamu mwachiphamaso, (achiphamaso) omwe adapita ku nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w) koma adakathawa kunkhondoko. Ndipo adali ochuluka gawo limodzi mwa magawo atatu a Asilamu (1/3). Pothawapo adathawa ochuluka kuposa nambala yatchulidwayi. Koma ena mwa iwo adabwerera nkudzalumikizananso ndi gulu la nkhondo la Mtumiki (s.a.w).
“Ndithudi, nyumba yoyamba yomwe idakhazikitsidwa chifukwa cha anthu (kuti azipempheramo) ndiyomwe ili pa Bakka (ku Makka); yodalitsidwa ndiponso ndichiongolo kwa anthu onse.
M’ndime iyi akunena kuti Asilamu pankhondo zawo zolimbana ndi anthu osakhulupilira Allah, adali kuthandizidwa ndi magulumagulu a Angelo. Angelowo amadza monga anthu ndipo amamenya nkhondo ndi mphamvu zaumunthu, osati zaungelo. Akadamenya nkhondoyo ndimphamvu yaungelo ndiye kuti mngelo mmodzi yekha akadawamaliza osakhulupilira onse psiti.
“Kodi mukukanira bwanji pomwe ndime za Allah zikuwerengedwa kwa inu, pomwenso Mtumiki Wake ali pamodzi nanu? Ndipo amene agwiritse mwa Allah (bwinobwino), ndithudi iye wawongoleredwa kunjira yoongoka.
“Ndipo gwiritsani chingwe (chipembedzo) cha Allah nonsenu, ndipo musagawikane. Kumbukirani mtendere wa Allah womwe uli pa inu; pamene mudali odana ndipo Iye adalunzanitsa pakati pa mitima yanu, tero mwa mtendere Wake mudakhala abale; ndipo mudali m’mphepete mwa dzenje la moto (wa Jahanama), ndipo Iye adakupulumutsanimo. Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani ma Ayah Ake (ndime Zake) kuti muongoke.
Kuipa kwina kwa malonda a katapira (Riba) ndiko kuti amangoonjezeraonjezera mpaka kuchimaliza chuma chamnzakeyo momchenjelera. Ndipo nchifukwa chake m’ndime yachiwiriyi ya 131 akunenetsa kuti ngati sasiya mchitidwe wa katapira (Riba) ndi kubweza kwa eni zomwe adalandazo, moto wa Jahanama ukuwadikira.
“Inu (Asilamu) ndinu gulu labwino limene lasankhidwa kwa anthu. Mukulamula (kuchita) zabwino ndi kuletsa zoipa, ndipo mukukhulupirira mwa Allah. Ndipo aja adapatsidwa buku akadakhulupirira monga momwe (adawalamulira) kukadakhala kwabwino kwa iwo. (Koma) mwa iwo alipo okhulupirira pomwe ambiri mwa iwo ngopandukira (chilamulo cha Allah).
Ndime iyi ikulimbikitsa anthu kuti akangaze kuchita zinthu zowapezetsa chikondi cha Allah.
“Amakhulupirira Allah ndi lsiku lomaliza; ndipo amalamulira (kuchita) zabwino ndikuletsa zoipa; ndipo amachita changu pa zinthu zabwino. Ndipo iwo ndi omwe ali mwa anthu abwino.
“Ndithudi, amene sakhulupirira, chuma chawo ngakhale ana awo, sizidzawathandiza chilichonse kwa Allah. Ndipo iwo ndi anthu a ku Moto basi; adzakhala mmenemo nthawi yaitali.
“Fanizo la chimene akupereka mwaulere pa moyo uwu wa dziko lapansi, chili ngati mphepo yomwe mkati mwake muli chisanu chaukali, chagwera pa munda wa anthu omwe adadzichitira okha zoipa, n’kuuonongeratu. Si Allah amene adawachitira zoipa, koma iwo okha adadzichitira zoipa.
M’ndime iyi Allah akukumbutsa Asilamu zinthu zosowetsa mtendere zomwe zidawapeza m’masiku a Uhudi powauza kuti monga iwo adavutitsidwa ndi adani awo, nawonso adaniwo adavutitsidwa. Umo ndi momwe zinthu zimachitikira mosinthasintha. Nthawi zina zigwera awa, kenako zigwera ena, malinga ndi zochita zawo. Allah sakondera.
“Ngati chabwino chikakufikirani, amaipidwa nacho; koma choipa chikakugwerani amachikondwelera. Koma ngati inu mupirira ndi kuopa Allah, ndale zawo sizingakuvutitseni chilichonse. Ndithu Allah akudziwa bwino zonse zimene iwo akuchita.
Apa akunena mwatsatanetsatane kuti Mneneri Muhammad (s.a.w) ndi mtumiki basi yemwe ndimunthu monga alili anthu ena onse. Adafa monga momwe ena adafera. Koma ngakhale iye wafa anthu ena atsanzire chikhalidwe chake ndi zophunzitsa zake zomwe amaphunzitsa. Asabwelere m’mbuyo kusiya Chipembedzo poona kuti iye wafa.
“(Kumbukira) pamene magulu awiri mwa inu anafunitsitsa kuti athawe (chifukwa cha mantha monga momwe adathawira achinyengo). Koma Allah adali Mtetezi wa magulu awiriwo. (Choncho adawasunga kuti asathawe). Ndipo okhulupirira ayadzamire kwa Allah Yekha basi.
“Allah adakupulumutsani pa (nkhondo) ya Badri pomwe inu munali ofooka (chifukwa chakuchepa ndi kusakhala ndi zida zokwanira). Choncho opani Allah kuti mumthokoze (nthawi zonse pa zomwe akukuchitirani).
“Ndipo Allah sadachite izi (potumiza angelo) koma kuti ukhale uthenga wabwino kwa inu ndi kuti pakutero mitima yanu ikhazikike ndi zimenezo. Ndipo chithandizo sichichokera (kwa wina aliyense) koma kwa Allah basi, Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.
Apa Allah akukumbutsa Asilamu za chisomo chomwe adawapatsa pakuwapatsa Mtumiki, pomwe Mtumikiyo asanawadzere iwo adali anthu osokera. Koma kupyolera mwa Mtumikiyo akhala olungama.
“Kodi mukuganiza kuti mukalowa ku Munda wamtendere pomwe Allah asadawaonetsere poyera amene amenyera chipembedzo cha Allah mwa inu ndi kuwaonetseranso poyera opirira (pa nkhondo ya Allah)?
“Tiponya mantha m’mitima mwa amene sadakhulupirire chifukwa chakumphatikiza Allah (ndi mafano) omwe Allah sadatsitsire umboni (wosonyeza umulungu wawo) ndipo malo awo adzakhala ku Moto. Taonani kuipitsitsa malo a anthu ochita zoipa.
“Ndithudi, Allah adakutsimikizirani lonjezo lake (lakuti muwagonjetsa adani). Choncho mudali kuwapha mwachilolezo Chake kufikira pamene mudafooka ndikuyamba kukangana za lamulolo, tero mudalinyozera pambuyo pokuonetsani zimene mumazikonda; (pamenepo mpomwe adasiya kukuthangatani). Alipo ena mwa inu amene akukonda dziko lapansi (zamdziko), ndipo alipo ena mwa inu amene akukonda tsiku lachimaliziro. Kenako (Allah) adakuchotsani pa iwo (adakusiitsani kuwamenya osakhulupirirawo) kuti akuyeseni mayeso. Koma Iye tsopano wakukhululukirani. Ndipo Allah ndi mwini kuchita zabwino pa okhulupirira.
“Kenako pambuyo pa kudandaula, adakutsitsirani mpumulo - tulo tomwe tidaphimba gulu lina mwa inu. Padali gulu lina lomwe maganizo awo adawatangwanitsa namuganizira Allah ndizoganizira zopanda choonadi, zoganizira zaumbuli; ankati: “Ha! Kodi tili ndi chiyani ife pa chinthu ichi?” Nena: “Zinthu zonse nza Allah.” Akubisa m’mitima mwawo zomwe sakuzionetsa kwa iwe. Akunena: “Tidakakhala ndi chilichonse pa chinthu ichi, sitikadaphedwa apa.” Nena: “Ngakhale mukadakhala m’nyumba zanu, ndithudi kwa iwo amene imfa idalembedwa (kuti amwalire) akadapita kumalo omwalilirawo, koma Allah (adachita izi) kuti awonetse poyera zomwe zili m’zifuwa zanu. Ndikuyeretsa zomwe zili m’mitima mwanu. Ndipo Allah Ngodziwa za mzifuwa.”
Apa anthu akuwauza kuti achite zinthu molimbika zokawalowetsa ku Munda wa mtendere ndi kupewa kuchita zinthu zokawalowetsa ku Moto. Chifukwa anthu akaponyedwa ku Moto kupyolera m’zochita zawo zoipa.
“Ndithudi, mwa inu amene adabwerera m’mbuyo (kuthawa) tsiku lomwe magulu awiri a nkhondo adakumana (pa nkhondo ya Uhudi; gulu la osakhulupirira ndi gulu lankhondo la Asilamu), satana ndiyemwe adawaterezetsa chifukwa cha zina (zolakwa) zomwe adachita; ndipo Allah (tsopano) wawakhululukira. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngoleza koposa.
“E inu amene mwakhulupirira! Musakhale ngati amene sadakhulupirire, nanena za anzawo pamene akuyenda pa dziko kapena pomwe akumenyana nkhondo (ndikufera konko): “Akadakhala ndi ife sakadafa, ndiponso sakadaphedwa.” Allah (adawathira maganizo amenewa) kuti azipange zimenezo kukhala zodandaulitsa m’mitima mwawo. Komatu Allah ndi amene amapereka moyo ndi imfa. Ndipo Allah akuona zonse zomwe mukuchita.
Ndime iyi ikulimbikitsa za kuopa Allah ndi kumulemekeza potsatira malamulo ake ndi kupewa zomwe Iye waletsa. Iye ndi amene adakulenga. Ndiyemwenso adalenga zonse zimene iwe adakulengera. Ngakhale iwe amene utafuna chithandizo kwa anzako umampempha ponena kuti: ‘‘Ndikukupempha m’dzina la Allah kuti undichitire chakuti.” Izi umachita poona kuti iye adzalemekeza dzina la Allah, ndipo adzakwaniritsa chomwe ukufunacho. Koma nanga bwanji ukuchita zimene Allah waletsa? Bwanji sukulemekeza lamulo lake pomwe iwe ukufuna kuti anthu achite zomwe sukuchita. Apa akutiuzanso kuti Allah akuona chilichonse chimene anthu ake akuchita, ngakhale chikhale chochepa chotani.
“Ndipo ngati mwaphedwa pa njira ya Allah, kapena kufa, (palibe chotaika kwa inu) pakuti chikhululuko ndi chisoni zochokera kwa Allah nzabwino kuposa zomwe akuzisonkhanitsa (pa moyo wa pa dziko lapansi).
“Kodi amene akutsata chokondweretsa Allah angalingane ndi yemwe wabwerera ndi mkwiyo wochokera kwa Allah, ndipo Jahannam nkukhala malo ake? Taonani kuipa kumalo obwerera!
“Ndithudi, Allah adawachitira ubwino waukulu okhulupirira powatumizira Mtumiki wochokera mwa iwo yemwe akuwawerengera ma Ayah ake (ndime zake) ndikuwayeretsa ndikuwaphunzitsa buku ndi (mawu a) nzeru. Ndithudi, kale adali mkusokera koonekera.
Maulama onse a malamulo a Chisilamu adamvana kuti ndime iyi yaika malire amitala yomwe munthu akhoza kukwatira. Ndipo ikuletsa kukwatira akazi opyola anayi pa nthawi imodzi.
“Omwenso adauzidwa ndi anthu (olembedwa ganyu ndi Akafiri aku Makka) kuti: “Anthu Akusonkhanirani. Choncho aopeni.” Koma (zonenazo) zidawaonjezera chikhulupiliro (Asilamu). Ndipo adati: “Allah akutikwanira, ndipo Iye ndi Mtetezi wabwino koposa.”
“Choncho adabwerera ndi chisomo ndi ubwino zochokera kwa Allah. Sichidawakhudze choipa chilichonse; adatsatira zokondweretsa Allah. Ndipo Allah ndimwini ubwino waukulu.
“Ndithudi, amene asinthanitsa kusakhulupirira ndi chikhulupiliro, sangathe kumvutitsa Allah ndi chilichonse. Ndipo pa iwo padzakhala chilango chopweteka.
“Nkosatheka kwa Allah kusiya okhulupirira momwe mulilimu, mpaka atalekanitsa (pakati pawo) oipa ndi abwino. Ndipo nkosatheka kwa Allah kukudziwitsani zinthu zamseri, koma Allah amasankha mwa atumiki ake amene wamfuna (nkumdziwitsa zina mwa zimenezo). Choncho khulupirirani Allah ndi atumiki ake. Ndipo ngati mukhulupirira ndi kuopa (Allah), pa inu padzakhala malipiro aakulu.
Ayang’aniri a ana amasiye, monga momwe awauzira kuti asawachenjelere ana amasiye koma kuti awapatse chuma chawo mokwanira, apa akuwauzanso kuti apitirize kuyang’anira chuma cha ana amasiyewo. Asawapatse pomwe sali ozindikira zinthu, ali ofooka m’maganizo pomwe sakuzindikira kufunika kwa chuma kuopa kuti angasakaze chumacho. Tero asawapatse ngakhale misinkhu yawo ili yaikulu. Koma apitirize kuwasungira chumacho ndi kumawauza mawu abwino ponena kuti: “Mpaka pano ndikuona kuti mwanokha simungathe kuchiyendetsa bwino chuma chanu. Tero ndiloleni ndikusungirenibe mpaka nthawi yochepa kutsogoloku. Ndikadzaona kuti nzeru zakhazikika apo mpomwe ndidzakupatsani chumachi.”
“Ndipo asaganize amene akuchitira umbombo zimene Allah wawapatsa kuchokera m’zabwino Zake kuti kutero ndibwino kwa iwo, koma kutero nkoipa kwa iwo. Adzanjatidwa magoli pa zomwe adazichitira umbombo pa tsiku lachimaliziro. Ndipo um’lowam’malo wa zakumwamba ndi pansi ngwa Allah. Ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita.
184.Ndipo ngati akutsutsa iwe (Mtumiki Muhammad (s.a.w}, sichachilendo) adatsutsidwanso atumiki patsogolo pako omwe adadza ndi zisonyezo zoonekera ndi mabuku anzeru, ndi mabukunso ounika.
“Munthu aliyense adzalawa imfa. Ndithudi, mudzalipidwa malipiro anu mokwanira tsiku lachimaliziro. Ndipo amene adzatalikitsidwe ndi Moto nalowetsedwa ku Munda wamtendere, ndiye kuti wapambana, (kupambana kwakukulu), ndipo moyo wapadziko lapansi sulikanthu koma ndichisangalalo chonyenga basi.
Apa akufotokoza mmene anthu ena angawagawireko chuma chamasiye.
a) Ngati atafa mkazi nkusiya mwamuna wake yekha popanda kusiya ana kapena adzukulu, mwamunayo alandire gawo limodzi mwa magawo awiri (1/2) a chuma chomwe wasiya mkazi wakecho.
b) Akafa mkazi nkusiya mwamuna ndi nnwana wake kapena mdzukulu wake apa ndiye kuti mwamunayo adzalandira (1/4) gawo limodzi mwa magawo anayi achumacho.
c) Akafa mwamuna nkusiya mkazi wake popanda mwana kapena mdzukulu wake ndiye kuti mkaziyo adzalandira (1/4) gawo limodzi mwamagawo anayi achuma cha mwamuna wakecho. Ndipo chotsalacho achipereke kwa ena ofunika kuwagawira.
d) Akafa mwamuna nkusiya mkazi wake ndi mwana wake kapena mdzukulu wake, apa mkazi alandire (1/8) gawo limodzi mwa magawo asanu ndi atatu a chuma cha mwamunayo.
e) Akamwalira munthu popanda kusiya ana kapena zidzukulu ndi makolo, koma nkusiya m’bale mmodzi wamwamuna kapena wamkazi wakumbali ya mayi, apa ndiye kuti m’baleyo adzalandira (1/6) gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi a chumacho. Ndipo chotsalacho adzawagawira ena oyenera kuwagawira ngati alipo. Koma ngati palibe ndiye kuti m’baleyo adzatenganso chotsalacho.
f) Akamwalira munthu popanda kusiya ana kapena adzukulu ndi makolo, koma wasiya abale akumbali yamayi, amuna kapena akazi, apa ndiye kuti abalewa adzalandira (1/3) gawo limodzi mwa magawo atatu achuma cha womwalirayo. Ndipo adzagawana pakati pawo mofanana amuna ndi akazi omwe.
“Ndithu mudzayesedwa m’chuma chanu ndi miyoyo yanu; ndipo mudzamva masautso ambiri kuchokera kwa omwe adapatsidwa mabuku kale ndiponso kuchokera kwa omwe akuphatikiza Allah ndi zinthu zina (Arab), koma ngati mupirira ndi kudzisunga ku zomwe mwaletsedwa ndi Allah, (ndiye kuti mwachita chinthu chabwino kwambiri) pakuti zinthu izi (ndi zinthu zazikulu) zofunika munthu kuikirapo mtima.
“Omwe amakumbukira Allah, ali chiimire, ali chikhalire, ndi ali chigonere chamnthiti mwawo; namalingalira kalengedwe ka thambo ndi nthaka (mmene Allah adazilengera, uku akuti): “E Mbuye wathu! simunalenge izi mwachabe. Ulemelero Ngwanu. Tichinjirizeni ku chilango cha Moto.”
“Ndithudi mwa amene adapatsidwa buku, alipo amene akukhulupirira Allah ndi zimene zavumbulutsidwa kwa inu, ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa iwo, uku akudzichepetsa kwa Allah; sagulitsa ndime za Allah ndi mtengo wochepa (wa pa dziko lapansi). Iwo adzalandira malipiro awo kwa Mbuye wawo. Ndithudi, Allah Ngwachangu pakuwerengera.
بوابة إلكترونية لنشر ترجمات مجانية وموثوقة ومتطورة لمعاني وتفاسير القرآن الكريم بلغات العالم، تم تجهيزها بإشراف ورعاية وتطوير جهات متخصصة ومترجمين ثقات، يتاح الوصول إليها وأخذ نسخ منها وإعادة نشرها لعموم الجهات والأفراد بكل يسر وسهولة، من خلال جميع وسائل النشر والتواصل الإلكتروني.
أهداف الموسوعة:
إيجاد مرجعية إلكترونية مجانية موثوقة لترجمات معاني القرآن الكريم وفق منهج أهل السنة والجماعة لتكون بديلاً عن المرجعيات الإلكترونية غير الموثوقة الشائعة في الفضاء الإلكتروني.
توفير صيغ إلكترونية متنوعة للترجمات تتناسب مع تطور الأجهزة الذكية والتطبيقات والأنظمة الإلكترونية.
تعميم النفع بالترجمات الموثوقة وإتاحتها مجاناً، وتسهيل الوصول إليها من خلال محركات البحث ومصاد