ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: الطور
آية:
 

الطور

وَٱلطُّورِ
“Ndikulumbilira phiri la Turi (ku Sinai pamene Mûsa adalankhulana ndi Allah).
التفاسير العربية:
وَكِتَٰبٖ مَّسۡطُورٖ
“Ndi buku lolembedwa.
التفاسير العربية:
فِي رَقّٖ مَّنشُورٖ
“M’mipukutu yazikopa zotambasuka (zosavuta kuwerenga).
التفاسير العربية:
وَٱلۡبَيۡتِ ٱلۡمَعۡمُورِ
“Ndi nyumba yopitako kawirikawiri (pochitamo mapemphero).
التفاسير العربية:
وَٱلسَّقۡفِ ٱلۡمَرۡفُوعِ
“Ndi thambo limene latukulidwa (popanda mzati).
التفاسير العربية:
وَٱلۡبَحۡرِ ٱلۡمَسۡجُورِ
“Ndi nyanja yodzadza ndi madzi.
التفاسير العربية:
إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ لَوَٰقِعٞ
“Ndithu chilango cha Mbuye wako (chimene wawalonjeza nacho osakhulupirira) chiwapeza (popanda chipeneko).
التفاسير العربية:
مَّا لَهُۥ مِن دَافِعٖ
“Palibe wochichotsa (pa iwo).
التفاسير العربية:
يَوۡمَ تَمُورُ ٱلسَّمَآءُ مَوۡرٗا
“Pa tsikulo thambo lidzagwedezeka; kugwedezeka kwamphamvu.
التفاسير العربية:
وَتَسِيرُ ٱلۡجِبَالُ سَيۡرٗا
“Ndipo mapiri adzayenda mwamphavu (kuchoka m’malo mwake).
التفاسير العربية:
فَوَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ
“Kuonongeka koopsa pa tsiku limenelo kuzakhala pa otsutsa choonadi.
التفاسير العربية:
ٱلَّذِينَ هُمۡ فِي خَوۡضٖ يَلۡعَبُونَ
“Iwo amene akungosewera mzinthu zopanda pake.
التفاسير العربية:
يَوۡمَ يُدَعُّونَ إِلَىٰ نَارِ جَهَنَّمَ دَعًّا
“Tsiku limene adzakankhidwira mwamphamvu ku Jahannam (ku Moto Woopsa).
التفاسير العربية:
هَٰذِهِ ٱلنَّارُ ٱلَّتِي كُنتُم بِهَا تُكَذِّبُونَ
“(Kudzanenedwa kwa iwo): “Uwu ndi Moto uja umene mudali kuutsutsa (pa dziko lapansi)
التفاسير العربية:

أَفَسِحۡرٌ هَٰذَآ أَمۡ أَنتُمۡ لَا تُبۡصِرُونَ
“Kodi awa ndi matsenga kapena inu simukuona?
التفاسير العربية:
ٱصۡلَوۡهَا فَٱصۡبِرُوٓاْ أَوۡ لَا تَصۡبِرُواْ سَوَآءٌ عَلَيۡكُمۡۖ إِنَّمَا تُجۡزَوۡنَ مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
“Lowanimo, (mulawe kupsereza kwake) pirirani (ndi mavuto ake) kapena musapirire, ndichimodzimodzi kwa inu. Ndithu mulipidwa pazimene munkachita.”
التفاسير العربية:
إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّـٰتٖ وَنَعِيمٖ
“Ndithu oopa Allah adzakhala m’Minda yamtendere ndi chisangalalo chachikulu.
التفاسير العربية:
فَٰكِهِينَ بِمَآ ءَاتَىٰهُمۡ رَبُّهُمۡ وَوَقَىٰهُمۡ رَبُّهُمۡ عَذَابَ ٱلۡجَحِيمِ
“Uku akukondwelera pazimene wawapatsa Mbuye wawo ndipo Mbuye wawo azawatchinjiriza ku chilango cha Jahena.
التفاسير العربية:
كُلُواْ وَٱشۡرَبُواْ هَنِيٓـَٔۢا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
“(Kudzanenedwa kwa iwo): “Idyani (chakudya chamtendere); ndipo imwani mosangalala kukhala malipiro pazimene munkachita (pa dziko lapansi).”
التفاسير العربية:
مُتَّكِـِٔينَ عَلَىٰ سُرُرٖ مَّصۡفُوفَةٖۖ وَزَوَّجۡنَٰهُم بِحُورٍ عِينٖ
“Uku atakhala moyadzamira pa makama ondandika bwino ndi kuyalidwa bwino; ndipo tidzawakwatitsa akazi ophanuka maso mokongola.
التفاسير العربية:
وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَٱتَّبَعَتۡهُمۡ ذُرِّيَّتُهُم بِإِيمَٰنٍ أَلۡحَقۡنَا بِهِمۡ ذُرِّيَّتَهُمۡ وَمَآ أَلَتۡنَٰهُم مِّنۡ عَمَلِهِم مِّن شَيۡءٖۚ كُلُّ ٱمۡرِيِٕۭ بِمَا كَسَبَ رَهِينٞ
“Ndipo amene akhulupirira ndipo ana awo nkuwatsatira pa chikhulupiliro tidzawakumanitsa iwo ndi ana awowo ndipo sitikawachepetsera kalikonse m’mphoto za ntchito zawo; munthu aliyense adzakoledwa ndi zochita zake;
التفاسير العربية:
وَأَمۡدَدۡنَٰهُم بِفَٰكِهَةٖ وَلَحۡمٖ مِّمَّا يَشۡتَهُونَ
“Ndipo tidzawaonjezera zipatso ndi nyama imene adzakhala akuilakalaka.
التفاسير العربية:
يَتَنَٰزَعُونَ فِيهَا كَأۡسٗا لَّا لَغۡوٞ فِيهَا وَلَا تَأۡثِيمٞ
“Azikalandirana m’menemo (mwachikondi wina ndi mnzake) chikho chodzaza ndi zakumwa; sipakakhala kwa iwo zolankhula zachabe ngakhale zochita zamachimo.
التفاسير العربية:
۞وَيَطُوفُ عَلَيۡهِمۡ غِلۡمَانٞ لَّهُمۡ كَأَنَّهُمۡ لُؤۡلُؤٞ مَّكۡنُونٞ
“Ndipo azikawazungulira anyamata owatumikira onga ngale yosungidwa m’chigoba chake (kukongola kwawo).
التفاسير العربية:
وَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖ يَتَسَآءَلُونَ
“Azidzatembenukirana wina ndi mnzake uku akufunsana (za kukula kwa mtendere umene adzakhala nawo ndi kuti adaupeza chotani).
التفاسير العربية:
قَالُوٓاْ إِنَّا كُنَّا قَبۡلُ فِيٓ أَهۡلِنَا مُشۡفِقِينَ
“Adzanena: “Ife tidali oopa chilango cha Allah pakati pa maanja athu (tisadalandire mtenderewu).
التفاسير العربية:
فَمَنَّ ٱللَّهُ عَلَيۡنَا وَوَقَىٰنَا عَذَابَ ٱلسَّمُومِ
“Ndipo Allah watidalitsa ndipo watitchinjiriza ku chilango cha Moto.
التفاسير العربية:
إِنَّا كُنَّا مِن قَبۡلُ نَدۡعُوهُۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡبَرُّ ٱلرَّحِيمُ
“Ndithu ife timampembedza (kalero pa dziko lapansi) ndithu Iye Yekha Ngwabwino, Ngwachifundo.”
التفاسير العربية:
فَذَكِّرۡ فَمَآ أَنتَ بِنِعۡمَتِ رَبِّكَ بِكَاهِنٖ وَلَا مَجۡنُونٍ
“Choncho kumbutsa, iwe suli mlosi kapena wamisala pamtendere wa Mbuye wako.
التفاسير العربية:
أَمۡ يَقُولُونَ شَاعِرٞ نَّتَرَبَّصُ بِهِۦ رَيۡبَ ٱلۡمَنُونِ
“Kapena akunena kuti ndiwe mlakatuli, tikumuyembekezera imfa impeze.
التفاسير العربية:
قُلۡ تَرَبَّصُواْ فَإِنِّي مَعَكُم مِّنَ ٱلۡمُتَرَبِّصِينَ
“Nena: “Yembekezerani! Ndithu ine ndili nanu mwa mmodzi woyembekezera.”
التفاسير العربية:

أَمۡ تَأۡمُرُهُمۡ أَحۡلَٰمُهُم بِهَٰذَآۚ أَمۡ هُمۡ قَوۡمٞ طَاغُونَ
“Kapena nzeru zawo ndizo zikuwauza izi kapena iwo ndi anthu opyola malire.
التفاسير العربية:
أَمۡ يَقُولُونَ تَقَوَّلَهُۥۚ بَل لَّا يُؤۡمِنُونَ
“Kodi akunena kuti: “Wadzipekera (Mtumiki {s.a.w} Qur’an)?” Iyayi, koma iwo sakukhulupirira.
التفاسير العربية:
فَلۡيَأۡتُواْ بِحَدِيثٖ مِّثۡلِهِۦٓ إِن كَانُواْ صَٰدِقِينَ
“Tero abwere ndi nkhani yofanana ndi iyo (Qur’an) ngati ali owona m’kuyankhula kwawo (koti Mtumiki{s.a.w} wapeka Qur’an.)
التفاسير العربية:
أَمۡ خُلِقُواْ مِنۡ غَيۡرِ شَيۡءٍ أَمۡ هُمُ ٱلۡخَٰلِقُونَ
“Kapena adalengedwa popanda Mlengi kapena iwo adadzilenga okha (nchifukwa sakuvomereza za Mlengi Wopembedzedwayo?)
التفاسير العربية:
أَمۡ خَلَقُواْ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَۚ بَل لَّا يُوقِنُونَ
“Kapena ndiwo adalenga thambo ndi nthaka? Koma satsimikiza (zoyenera kumchitira Mlengi).
التفاسير العربية:
أَمۡ عِندَهُمۡ خَزَآئِنُ رَبِّكَ أَمۡ هُمُ ٱلۡمُصَۜيۡطِرُونَ
“Kapena nkhokwe (za zabwino) za Mbuye wako zili ndi iwo (kotero kuti akuzigwiritsa ntchito mmene angafunire?) Kapena iwo ngopambana?
التفاسير العربية:
أَمۡ لَهُمۡ سُلَّمٞ يَسۡتَمِعُونَ فِيهِۖ فَلۡيَأۡتِ مُسۡتَمِعُهُم بِسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٍ
“Nanga kapena ali nawo makwelero (amene akukwelera kumwamba) kotero kuti akumvetsera zimene Allah akulamula? Choncho, omvetsera awo abwere nawo umboni owonekera (osonyeza kuona kwawo pa zimene akunenazi).
التفاسير العربية:
أَمۡ لَهُ ٱلۡبَنَٰتُ وَلَكُمُ ٱلۡبَنُونَ
“Kapena Iye (Allah) ndiye ali ndi ana akazi ndipo inu muli ndi ana amuna?
التفاسير العربية:
أَمۡ تَسۡـَٔلُهُمۡ أَجۡرٗا فَهُم مِّن مَّغۡرَمٖ مُّثۡقَلُونَ
“Kapena ukuwapempha malipiro alionse (pofikitsa uthenga); kotero kuti iwo akulemedwa ndi kulipira (uthengawu)?
التفاسير العربية:
أَمۡ عِندَهُمُ ٱلۡغَيۡبُ فَهُمۡ يَكۡتُبُونَ
“Kapena iwo amadziwa zamseri kotero kuti iwo akumalemba (zimene afuna)?
التفاسير العربية:
أَمۡ يُرِيدُونَ كَيۡدٗاۖ فَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ هُمُ ٱلۡمَكِيدُونَ
“Kapena akufuna kukuchitira chiwembu (ndikuononga uthenga wako?) Koma amene sadakhulupirire ndiwo omwe chiwabwelere chiwembu (chawo.)
التفاسير العربية:
أَمۡ لَهُمۡ إِلَٰهٌ غَيۡرُ ٱللَّهِۚ سُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ عَمَّا يُشۡرِكُونَ
“Kodi ali naye wompembedza, osati Allah (amene angawateteze ku chilango cha Allah)? Allah wapatukana ndi zimene akumuphatikiza nazo.
التفاسير العربية:
وَإِن يَرَوۡاْ كِسۡفٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ سَاقِطٗا يَقُولُواْ سَحَابٞ مَّرۡكُومٞ
“Koma akaona gawo lathambo likugwa (kuti liwalange) akunena (mwamakani ndi kunyada): “Uwu ndi mtambo umene wasonkhanitsa madzi a mvula.”
التفاسير العربية:
فَذَرۡهُمۡ حَتَّىٰ يُلَٰقُواْ يَوۡمَهُمُ ٱلَّذِي فِيهِ يُصۡعَقُونَ
“Choncho asiye; (usalabadire za iwo) mpaka pomwe adzakumana ndi tsiku lawo limene adzaonongedwa.
التفاسير العربية:
يَوۡمَ لَا يُغۡنِي عَنۡهُمۡ كَيۡدُهُمۡ شَيۡـٔٗا وَلَا هُمۡ يُنصَرُونَ
“Tsiku lomwe chiwembu chawo sichidzawathandiza chilichonse; ndipo iwo sadzapulumutsidwa.
التفاسير العربية:
وَإِنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ عَذَابٗا دُونَ ذَٰلِكَ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
“Ndipo ndithu amene achita zosalungama ali nacho chilango china chosakhala chimenecho (chisanawapeze chilango cha ku Âkhira)! Koma ambiri a iwo sadziwa (zimenezi).
التفاسير العربية:
وَٱصۡبِرۡ لِحُكۡمِ رَبِّكَ فَإِنَّكَ بِأَعۡيُنِنَاۖ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ حِينَ تَقُومُ
“Ndipo pirira ndi lamulo la Mbuye wako ndithu iwe ndiwe wosungidwa ndi kuyang’aniridwa ndi Ife; ndipo lemekeza ndi kumuyamika Mbuye ako pamene ukuimilira (kupemphera).
التفاسير العربية:
وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَسَبِّحۡهُ وَإِدۡبَٰرَ ٱلنُّجُومِ
“Ndipo m’gawo la usiku mlemekeze Iye ndi nthawi yolowa nyenyezi.
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: الطور
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق