ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني آية: (7) سورة: المنافقون
هُمُ ٱلَّذِينَ يَقُولُونَ لَا تُنفِقُواْ عَلَىٰ مَنۡ عِندَ رَسُولِ ٱللَّهِ حَتَّىٰ يَنفَضُّواْۗ وَلِلَّهِ خَزَآئِنُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلَٰكِنَّ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ لَا يَفۡقَهُونَ
Amenewa ndiwo omwe akunena kwa Answari; (Asilamu aku Madina, kuti): “Musawapatse chuma (chanu) amene ali ndi Mtumiki wa Allah kuti abalalikane.” Pomwe nkhokwe zonse (zachuma) za kumwamba ndi dziko lapansi zili m’manja mwa Allah (ndipo amachipereka kwa amene wamfuna); koma achiphamaso sakuzindikira (zimenezo).[364]
[364] (Ndime 7-8) Chifukwa chomwe ndime izi zidavumbulutsidwira ndi kuti tsiku lina Mtumiki (s.a.w) pomwe adali ndi gulu lake la nkhondo, munthu wina wa m’madera am’midzi adakangana ndi Msilamu wa mu mzinda wa Madina chifukwa cha madzi. Ndipo Mwarabu wa kumudzi uja adamenya Msilamu wa m’Madina ndi thabwa. Poona izi Msilamu wa ku Madina adapita kukasuma kwa mwana wa Ubayye amene adali munafiki (wachinyengo). Mwana wa Ubayyeyo adamuuza wosumayo kuti: “Musamawapatse chakudya omwe ali ndi Muhammad kuti abalalikane, athawe njala ndi kumsiya yekha Muhammad (s.a.w).” Adatinso: “Tikabwerera ku mzinda wa Madina, wolemekezeka adzatulutsa wonyozeka.” Apa amatanthauza kuti wolemekezeka ndiye iye, ndipo wonyozeka ndi Mtumiki Muhammad (s.a.w). Ndipo Allah adamuyankha ponena kuti: “Kulemekezeka ndi kwa Allah ndi Mthenga wake ndi okhulupilira; koma anthu achiphamaso sakudziwa zimenezi.”
التفاسير العربية:
 
ترجمة معاني آية: (7) سورة: المنافقون
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق