ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: التغابن
آية:
 

التغابن

يُسَبِّحُ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۖ لَهُ ٱلۡمُلۡكُ وَلَهُ ٱلۡحَمۡدُۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٌ
“Zonse zakumwamba ndi zam’dziko lapansi zikulemekeza Allah (ndi kumyeretsa ku zinthu zosayenerana ndi ulemelero Wake; ufumu Ngwake ndipo kutamandidwa kwabwino Nkwake. Ndipo Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse.
التفاسير العربية:
هُوَ ٱلَّذِي خَلَقَكُمۡ فَمِنكُمۡ كَافِرٞ وَمِنكُم مُّؤۡمِنٞۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٌ
“Iye ndiamene adakulengani (nonsenu popanda kuchokera ku chilichonse) choncho mwa inu alipo wosakhulupirira ndiponso mwa inu alipo wokhulupirira. Ndipo Allah Ngopenya zonse zimene mukuchita (ndipo adzakulipirani nazo).
التفاسير العربية:
خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّ وَصَوَّرَكُمۡ فَأَحۡسَنَ صُوَرَكُمۡۖ وَإِلَيۡهِ ٱلۡمَصِيرُ
“Adalenga thambo ndi nthaka mwachoonadi ndipo adakujambulani majambulidwe abwino; ndipo kobwerera nkwa Iye (pa tsiku lachiweruziro).
التفاسير العربية:
يَعۡلَمُ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَيَعۡلَمُ مَا تُسِرُّونَ وَمَا تُعۡلِنُونَۚ وَٱللَّهُ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ
“(Allah) akudziwa za kumwamba ndi za m’dziko lapansi, ndiponso akudziwa zimene mukuzibisa ndi zimene mukuzilengeza (zochita ndi zoyankhula); Allah Ngodziwa za m’zifuwa.
التفاسير العربية:
أَلَمۡ يَأۡتِكُمۡ نَبَؤُاْ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن قَبۡلُ فَذَاقُواْ وَبَالَ أَمۡرِهِمۡ وَلَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ
“Kodi siidakufikeni nkhani ya omwe sadakhulupirire kale? Adalawa (zowawa) za zoipa za zinthu zawo (pa dziko lapansi). Ndipo chilango chowawa chidzakhala pa iwo (tsiku lachimaliziro).
التفاسير العربية:
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُۥ كَانَت تَّأۡتِيهِمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَقَالُوٓاْ أَبَشَرٞ يَهۡدُونَنَا فَكَفَرُواْ وَتَوَلَّواْۖ وَّٱسۡتَغۡنَى ٱللَّهُۚ وَٱللَّهُ غَنِيٌّ حَمِيدٞ
“Zimenezo nchifukwa chakuti atumiki awo amawadzera ndi zozizwitsa koma iwo amanena (mwachipongwe): “Ha! Anthu anzathu (onga ife) angationgole?” Choncho sadakhulupirire (utumiki wawo) ndipo adanyoza (choonadi) potero Allah adawasiya (ndi kupanda chikhulupiliro kwawo) ndipo Allah Ngokwanira ndiponso Ngoyamikidwa.
التفاسير العربية:
زَعَمَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَن لَّن يُبۡعَثُواْۚ قُلۡ بَلَىٰ وَرَبِّي لَتُبۡعَثُنَّ ثُمَّ لَتُنَبَّؤُنَّ بِمَا عَمِلۡتُمۡۚ وَذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرٞ
“Amene sadakhulupirire akumazinamiza kuti sadzaukitsidwa ku imfa. Nena (kwa iwo iwe Mtumiki{s.a.w}): “Sizili choncho pali Mbuye wanga, ndithu mudzaukitsidwa ku imfa, ndipo mudzauzidwa zimene mumachita (pa dziko lapansi). Zimenezo kwa Allah nzosavuta (kuzichita).”
التفاسير العربية:
فَـَٔامِنُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَٱلنُّورِ ٱلَّذِيٓ أَنزَلۡنَاۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرٞ
“Khulupirirani Allah ndi Mtumiki Wake, ndi dangalira limene talivumbulutsa (Qur’an). Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri zimene mukuchita.
التفاسير العربية:
يَوۡمَ يَجۡمَعُكُمۡ لِيَوۡمِ ٱلۡجَمۡعِۖ ذَٰلِكَ يَوۡمُ ٱلتَّغَابُنِۗ وَمَن يُؤۡمِنۢ بِٱللَّهِ وَيَعۡمَلۡ صَٰلِحٗا يُكَفِّرۡ عَنۡهُ سَيِّـَٔاتِهِۦ وَيُدۡخِلۡهُ جَنَّـٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدٗاۚ ذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
“(Kumbukirani) tsiku limene adzakusonkhanitsani chifukwa cha tsiku lakusonkhana (zolengedwa zonse), limenelo ndi tsiku lolephera; ndipo amene akhulupirira mwa Allah ndi kuchita zabwino, amfafanizira zoipa zake, ndipo akamulowetsa m’minda momwe pansi pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo muyaya; kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.
Allah, apa, akuwauza kuti asiye kuganizira zinthu zopanda pake. Kodi sadadziwebe mpaka pano kuti Muhammad ndi Mneneri wa Allah, ndikuti Allah ndi Mmodzi yekha? Ndikutinso kuli tsiku lachimaliziro; pamene munthu aliyense adzalipidwa pa zimene adachita? Basi tsiku lachimaliziro likadzawafikira adzadziwa kuti zimene adali kuwauza Mneneri nzoona.
التفاسير العربية:

وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَآ أُوْلَـٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِ خَٰلِدِينَ فِيهَاۖ وَبِئۡسَ ٱلۡمَصِيرُ
“Koma amene sadakhulupirire natsutsa zozizwitsa Zathu (zimene zidaperekedwa kwa Aneneri Athu;) iwowo ndi anthu a ku Moto; adzakhala mmenemo nthawi yaitali, amenewo ndiwo mabwelero oipa.
التفاسير العربية:
مَآ أَصَابَ مِن مُّصِيبَةٍ إِلَّا بِإِذۡنِ ٱللَّهِۗ وَمَن يُؤۡمِنۢ بِٱللَّهِ يَهۡدِ قَلۡبَهُۥۚ وَٱللَّهُ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ
“Palibe vuto lililonse lingapezeke pokhapokha Allah atafuna; ndipo amene akhulupirira Allah, (Allah) aongola mtima wake (kuti ukhale wokhutira ndi chiweruzo cha Allah). Ndipo Allah Ngodziwa chinthu chilichonse.
التفاسير العربية:
وَأَطِيعُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُواْ ٱلرَّسُولَۚ فَإِن تَوَلَّيۡتُمۡ فَإِنَّمَا عَلَىٰ رَسُولِنَا ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ
“Choncho mverani Allah ndipo mverani Mtumiki, ngati munyozera (ndi zanu), ndithu udindo wa Mtumiki Wathu ndikufikitsa uthenga omveka.
التفاسير العربية:
ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۚ وَعَلَى ٱللَّهِ فَلۡيَتَوَكَّلِ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ
“Allah, palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ndipo kwa Allah Yekha, okhulupirira atsamire.
التفاسير العربية:
يَـٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِنَّ مِنۡ أَزۡوَٰجِكُمۡ وَأَوۡلَٰدِكُمۡ عَدُوّٗا لَّكُمۡ فَٱحۡذَرُوهُمۡۚ وَإِن تَعۡفُواْ وَتَصۡفَحُواْ وَتَغۡفِرُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٌ
“E inu amene mwakhulupirira! Ndithu ena mwa akazi anu ndi ana anu ndiadani anu (chifukwa chakuti amakuchotsani kumbali yomvera Allah pofuna kuti mukwaniritse zofuna zawo). Chenjerani nawo. Ngati muwakhululukira ndi kunyalanyaza ndi kubisa zolakwa zawo ndibwino kwambiri, ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.
Kuyambira Ayah iyi, kudzafika Ayah 16, Allah akusonyeza anthu Ake madalitso ambiri omwe wawadalitsa nawo kuti azindikire kuti Mwini kupereka madalitso amenewa m’dziko sangawasiye anthu Ake m’kusokera popanda kuwatumizira munthu wowaongolera ku njira yabwino, ndikuwadziwitsa zamtendere wapadziko ndi tsiku lachimaliziro. Ndikuti Allah amene adapanga zonsezi palibe chimene angachilephere. Ndipo tanthauzo la choyala, apa, ndi pamalo poti nkutheka munthu kuchita chimene akufuna pa moyo wake. Tanthauzo lake sikuti dothi lakhala ngati mkeka wa pabedi ayi.
التفاسير العربية:
إِنَّمَآ أَمۡوَٰلُكُمۡ وَأَوۡلَٰدُكُمۡ فِتۡنَةٞۚ وَٱللَّهُ عِندَهُۥٓ أَجۡرٌ عَظِيمٞ
“Ndithu chuma chanu ndi ana anu ndimayesero (kwa inu); koma kwa Allah kuli malipiro akulu (kwa yemwe wasankha kumvera Allah).
التفاسير العربية:
فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ مَا ٱسۡتَطَعۡتُمۡ وَٱسۡمَعُواْ وَأَطِيعُواْ وَأَنفِقُواْ خَيۡرٗا لِّأَنفُسِكُمۡۗ وَمَن يُوقَ شُحَّ نَفۡسِهِۦ فَأُوْلَـٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ
“Choncho muopeni Allah mmene mungathere, mverani (zophunzitsa Zake) ndipo tsatirani (malamulo Ake) komanso perekani zimene wakupatsani zikhala zabwino kwa inu. Dzichitireni nokha zabwino. Ndipo amene watchinjirizidwa ku umbombo wa mtima wake, iwowo ndiwo opambana.
التفاسير العربية:
إِن تُقۡرِضُواْ ٱللَّهَ قَرۡضًا حَسَنٗا يُضَٰعِفۡهُ لَكُمۡ وَيَغۡفِرۡ لَكُمۡۚ وَٱللَّهُ شَكُورٌ حَلِيمٌ
“Ngati mungamkongoze Allah ngongole yabwino aiwonjezera kwa inu (malipiro ake) ndipo akukhululukirani (zolakwa zanu.) Ndipo Allah Ngolandira kuthokoza, Ngoleza.
التفاسير العربية:
عَٰلِمُ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
“Ngodziwa zobisika ndi zoonekera, Ngwamphamvu zopambana, Ngwanzeru zakuya.
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: التغابن
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق