ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: النازعات
آية:
 

النازعات

وَٱلنَّـٰزِعَٰتِ غَرۡقٗا
“Ndikulumbilira (angelo) amene amazula mwamphamvu (mizimu ya osakhulupirira).
Surah zambiri zimene zidavumbulutsidwa ku Makka zimanena zododometsa za tsiku lachimaliziro.
التفاسير العربية:
وَٱلنَّـٰشِطَٰتِ نَشۡطٗا
“Ndikulumbiliranso (angelo) amene amachotsa moleza (mizimu ya okhulupirira).
التفاسير العربية:
وَٱلسَّـٰبِحَٰتِ سَبۡحٗا
“Ndi omwe amasambira (nayo mizimuyo) mu mlengalenga (ponka nayo ku malo ake oyembekezera).
التفاسير العربية:
فَٱلسَّـٰبِقَٰتِ سَبۡقٗا
“Ndi iwo amene akupikisana pokwaniritsa malamulo a Allah.
التفاسير العربية:
فَٱلۡمُدَبِّرَٰتِ أَمۡرٗا
“Ndi iwo (angelo) amene akulongosola malamulo (Ake). (Ndithudi inu anthu mudzauka kwa akufa).
التفاسير العربية:
يَوۡمَ تَرۡجُفُ ٱلرَّاجِفَةُ
“Patsiku lomwe (lipenga loyamba lidzaimbidwa), dziko lapansi ndi mapiri ake zidzagwedezeka (ndipo aliyense adzafa).
التفاسير العربية:
تَتۡبَعُهَا ٱلرَّادِفَةُ
“Ndipo kudzatsatira kuyimba kwa lipenga lachiwiri (kumene kudzaukitsa akufa onse).
التفاسير العربية:
قُلُوبٞ يَوۡمَئِذٖ وَاجِفَةٌ
“Tsiku limenelo mitima idzanjenjemera ndi kuopa.
التفاسير العربية:
أَبۡصَٰرُهَا خَٰشِعَةٞ
“Maso a eni mitimayo adzakhala ozyolika (chifukwa chamadandaulo);
التفاسير العربية:
يَقُولُونَ أَءِنَّا لَمَرۡدُودُونَ فِي ٱلۡحَافِرَةِ
“(Osakhulupirira) akunena: “Kodi nzoona tidzabwezedwa pambuyo pa imfa monga tidalili kale?”
التفاسير العربية:
أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمٗا نَّخِرَةٗ
““Pomwe ife titakhala mafupa ofumbwa (tingabwezedwe ndi kuukitsidwa mwa tsopano)?”
التفاسير العربية:
قَالُواْ تِلۡكَ إِذٗا كَرَّةٌ خَاسِرَةٞ
“Adanena (mokanira ndi mwachipongwe): “Choncho kubwerera kumeneko ngati kudzakhalepodi kudzakhala kotaika (ndi kopanda phindu kwa ife. Pomwe ife sindife oyenera kutaika).”
التفاسير العربية:
فَإِنَّمَا هِيَ زَجۡرَةٞ وَٰحِدَةٞ
“(Musaganize kubwererako nchinthu chovuta). Ndithundithu Kiyamayo ndi nkuwo umodzi.
التفاسير العربية:
فَإِذَا هُم بِٱلسَّاهِرَةِ
“Mwadzidzidzi (zolengedwa zonse) zidzangoona zili pa dziko latsopano (zili zamoyo).
التفاسير العربية:
هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ مُوسَىٰٓ
“Kodi yakufika (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Mûsa?
Tsiku limenelo mapiri adzakhala osalimba ngati thonje limene likungouluka ndi mphepo.
التفاسير العربية:
إِذۡ نَادَىٰهُ رَبُّهُۥ بِٱلۡوَادِ ٱلۡمُقَدَّسِ طُوًى
“Pamene Mbuye wake adamuitana pa chigwa choyera (chotchedwa) Tuwaa.
التفاسير العربية:

ٱذۡهَبۡ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ
“(Adamuuza kuti) pita kwa Farawo ndithu iye wapyola malire, (mkudzitukumula kwake ndikupondereza anthu).
التفاسير العربية:
فَقُلۡ هَل لَّكَ إِلَىٰٓ أَن تَزَكَّىٰ
“Choncho ukamuuze kuti: “Kodi ukufuna kudziyeretsa?”
التفاسير العربية:
وَأَهۡدِيَكَ إِلَىٰ رَبِّكَ فَتَخۡشَىٰ
““Ndikuti ndikuongolere kwa Mbuye wako kuti uzimuopa?”
التفاسير العربية:
فَأَرَىٰهُ ٱلۡأٓيَةَ ٱلۡكُبۡرَىٰ
“(Basi Mûsa) adamuonetsa (Farawo) chozizwitsa chachikulu.
التفاسير العربية:
فَكَذَّبَ وَعَصَىٰ
“Koma (Farawo) adatsutsa (Mûsa pazimene adadza nazo zija) ndi kunyoza.
التفاسير العربية:
ثُمَّ أَدۡبَرَ يَسۡعَىٰ
“Kenaka adabwerera uku akulimbika kutsutsana naye (Allah),
التفاسير العربية:
فَحَشَرَ فَنَادَىٰ
“Adawasonkhanitsa (afiti) uku akuitana anthu;
التفاسير العربية:
فَقَالَ أَنَا۠ رَبُّكُمُ ٱلۡأَعۡلَىٰ
“Nanena: “Ine ndine mbuye wanu wapamwambamwamba!”
التفاسير العربية:
فَأَخَذَهُ ٱللَّهُ نَكَالَ ٱلۡأٓخِرَةِ وَٱلۡأُولَىٰٓ
“Pamenepo Allah adamulanga chifukwa cha mawu ake omaliza ndi oyamba.
التفاسير العربية:
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَعِبۡرَةٗ لِّمَن يَخۡشَىٰٓ
“Ndithu pa zimenezi pali phunziro (lalikulu) kwa yemwe akuopa Allah.
التفاسير العربية:
ءَأَنتُمۡ أَشَدُّ خَلۡقًا أَمِ ٱلسَّمَآءُۚ بَنَىٰهَا
“Kodi kulengedwa kwanu, (inu osakhulupirira kuti muuke) nkovuta kapena thambo limene adalimanga (posonkhanitsa mbali zake zosiyanasiyana ndikukhala chinthu chimodzi)?
Ngamira za bere ndi chuma cha mtengo wapatali kwa Aarabu. Akuuzidwa apa kuti tsiku limenelo adzazisiya osazilabadira konse.
التفاسير العربية:
رَفَعَ سَمۡكَهَا فَسَوَّىٰهَا
“Adatukula nsinkhu wake ndikulikonza bwino (popanda pena pong’ambika kapena posiyana ndi pena).
التفاسير العربية:
وَأَغۡطَشَ لَيۡلَهَا وَأَخۡرَجَ ضُحَىٰهَا
“Ndipo amauvindikira usiku wake ndi mdima ndipo amatulutsa kuwala wake.
التفاسير العربية:
وَٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ ذَٰلِكَ دَحَىٰهَآ
“Ndipo pambuyo pazimenezo, nthaka adaiyala (kuti ikhale yoyenera kuikhala).
التفاسير العربية:
أَخۡرَجَ مِنۡهَا مَآءَهَا وَمَرۡعَىٰهَا
“Adatulutsa m’menemo madzi ake (potulutsa akasupe) ndikumeretsa msipu wake;
التفاسير العربية:
وَٱلۡجِبَالَ أَرۡسَىٰهَا
“Ndipo mapiri adawakhazikitsa (ndikuwalimbika);
التفاسير العربية:
مَتَٰعٗا لَّكُمۡ وَلِأَنۡعَٰمِكُمۡ
“(Adachita zonsezi) chifukwa chokusangalatsani inu ndi ziweto zanu.
Mwa zina zododometsa pa tsiku limenelo ndi nyama za mtchire kusonkhanitsidwa pamodzi popanda kumenyana kapena kudyana.
التفاسير العربية:
فَإِذَا جَآءَتِ ٱلطَّآمَّةُ ٱلۡكُبۡرَىٰ
“Choncho likadzafika tsoka lalikulu (tsiku la Qiyâma).
التفاسير العربية:
يَوۡمَ يَتَذَكَّرُ ٱلۡإِنسَٰنُ مَا سَعَىٰ
“Tsiku limenelo munthu adzakumbukira zimene adachita, (zabwino ndi zoipa).
التفاسير العربية:
وَبُرِّزَتِ ٱلۡجَحِيمُ لِمَن يَرَىٰ
“Ndipo Moto waukali udzawonetsedwa kwa yense openya.
التفاسير العربية:
فَأَمَّا مَن طَغَىٰ
“Tsono amene adapyola malire (pochita machimo),
التفاسير العربية:
وَءَاثَرَ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا
“Ndikudzisankhira (yekha) moyo wa pa dziko lapansi,
التفاسير العربية:
فَإِنَّ ٱلۡجَحِيمَ هِيَ ٱلۡمَأۡوَىٰ
“Ndithu Jahannam ndiwo malo ake.
التفاسير العربية:
وَأَمَّا مَنۡ خَافَ مَقَامَ رَبِّهِۦ وَنَهَى ٱلنَّفۡسَ عَنِ ٱلۡهَوَىٰ
“Tsono amene akuopa kuti adzaimilira pamaso pa Mbuye wake, nauletsa mtima wake ku zilakolako zoipa,
التفاسير العربية:
فَإِنَّ ٱلۡجَنَّةَ هِيَ ٱلۡمَأۡوَىٰ
“Ndithu Munda wamtendere ndiwo adzakhale malo ake.
التفاسير العربية:
يَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلسَّاعَةِ أَيَّانَ مُرۡسَىٰهَا
“Akukufunsa (iwe Mtumiki) (s.a.w) za nthawi (ya tsiku lachimaliziro kuti): “Idzakhala liti?”
التفاسير العربية:
فِيمَ أَنتَ مِن ذِكۡرَىٰهَآ
“Uli ndi mphamvu yanji iwe yofotokozera za tsikulo? (Iwe ulibe kuzindikira za nthawiyo kotero kuti ungaitchule kwa iwo).
التفاسير العربية:
إِلَىٰ رَبِّكَ مُنتَهَىٰهَآ
“Kwa Mbuye wako ndiko kuli mathero ake.
التفاسير العربية:
إِنَّمَآ أَنتَ مُنذِرُ مَن يَخۡشَىٰهَا
“Iwe (ntchito yako) ndikuwachenjeza amene akuiopa; (osati kulengeza zanthawi yake).
التفاسير العربية:
كَأَنَّهُمۡ يَوۡمَ يَرَوۡنَهَا لَمۡ يَلۡبَثُوٓاْ إِلَّا عَشِيَّةً أَوۡ ضُحَىٰهَا
“Tsiku limene adzaiona adzakhala ngati sadakhale (pa dziko nthawi yayitali), koma ngati madzulo amodzi kapena masana ake (nthawi ya m’mawa).
(Ndime 8-9) Ma Ayah awiriwa akufotokoza momwe Aarabu adalili Usilamu usadabwere. Munthu ankati akapatsidwa mphatso ya mwana wa mkazi adali kukhumudwa ndi kudandaula kwambiri. Ankanena kuti asungwana ngopanda phindu ndipo kuti kudali kuononga zinthu pakumulera, kumudyetsa, ndi kumuveka. Ndipo akadzakhala wachiwerewere adzakhala manyazi aakulu kwa makolo ake. Pamene chidadza chisilamu chidathetsa mkhalidwewu. Ndipo apa Allah akutisonyeza kuti patsiku limenelo, la chiweruziro, mwana uja adaikidwa wa moyo, adzafunsidwa kuti adaphedwa ndi tchimo lanji. Iye adzayankha kuti sadachite tchimo lililonse koma adaphedwa mopanda chilungamo.
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: النازعات
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق