Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - الترجمة الشيشيوا * - Übersetzungen


Übersetzung der Bedeutungen Surah / Kapitel: At-Tahrîm   Vers:

At-Tahrîm

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ لِمَ تُحَرِّمُ مَآ أَحَلَّ ٱللَّهُ لَكَۖ تَبۡتَغِي مَرۡضَاتَ أَزۡوَٰجِكَۚ وَٱللَّهُ غَفُورٞ رَّحِيمٞ
E iwe Mneneri (s.a.w)! Nchifukwa ninji ukudziletsa chimene Allah wakuloleza kuchita? Ukufuna kukondweretsa akazi ako (nchifukwa Chake wachita izi?) Koma Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قَدۡ فَرَضَ ٱللَّهُ لَكُمۡ تَحِلَّةَ أَيۡمَٰنِكُمۡۚ وَٱللَّهُ مَوۡلَىٰكُمۡۖ وَهُوَ ٱلۡعَلِيمُ ٱلۡحَكِيمُ
Ndithu Allah wakhazikitsa kamasulidwe kakulumbira kwanu, ndipo Allah ndiye Mtetezi wanu, Iye Ngodziwa kwambiri ndiponso Ngwanzeru zakuya (pa malamulo amene wawakhazikitsa kwa inu).[368]
[368] Mkazi ndimkazi basi. Mtumiki adanena m’Mahadisi kuti sipadapezeke mkazi amene ali wokwanira pa chinthu chilichonse kuyambira pamene dziko lidayamba mpaka kutha kwake kupatula akazi anayi basi. Iwowa ndi awa: Mayi Fatuma, Mayi Khadija, Mayi Mariya ndi mayi Asiya (mkazi wa Farawo). Kusakwanira kwa akazi pa chilichonse kumapezekanso ngakhale mwa akazi a Mtumiki, amamsautsa Mtumiki pomuchitira nsanje ngakhale kuti iwo amapemphera kwambiri, kawirikawiri makamaka amayi awiri awa Mayi Aisha ndi Mayi Hafsa monga momwe zilili m’ndime 4 ya sura iyi. Allah wawakalipira kwambiri m’ndime 5 ya sura yomweyi ndi m’ndime 28 ya surat Ahzab. Koma adalapa mwachangu ndipo Allah adawayanja monga zilili m’ndime 52 ya Sûrat Ahzab.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَإِذۡ أَسَرَّ ٱلنَّبِيُّ إِلَىٰ بَعۡضِ أَزۡوَٰجِهِۦ حَدِيثٗا فَلَمَّا نَبَّأَتۡ بِهِۦ وَأَظۡهَرَهُ ٱللَّهُ عَلَيۡهِ عَرَّفَ بَعۡضَهُۥ وَأَعۡرَضَ عَنۢ بَعۡضٖۖ فَلَمَّا نَبَّأَهَا بِهِۦ قَالَتۡ مَنۡ أَنۢبَأَكَ هَٰذَاۖ قَالَ نَبَّأَنِيَ ٱلۡعَلِيمُ ٱلۡخَبِيرُ
Ndipo kumbuka pamene Mneneri (s.a.w) adauza wina mwa akazi ake nkhani mwachinsinsi, choncho (mkaziyo) pamene adaiulula, Allah adamdziwitsa (Mtumiki) za kuululidwa kwa nkhaniyo, (ndipo Mtumiki) adaifotokoza mbali ina ya nkhaniyo, koma mbali ina adaisiya. Pamene adamfotokozera (mkazi wake) zankhaniyo adati: “Ndani wakuuza zimenezi?” (Mtumiki {s.a.w}) adati: “Wandiuza Wodziwa kwambiri ndiponso Wodziwa zazing’ono ndi zazikulu (Amene sichibisika kwa Iye chobisika chilichonse.)
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
إِن تَتُوبَآ إِلَى ٱللَّهِ فَقَدۡ صَغَتۡ قُلُوبُكُمَاۖ وَإِن تَظَٰهَرَا عَلَيۡهِ فَإِنَّ ٱللَّهَ هُوَ مَوۡلَىٰهُ وَجِبۡرِيلُ وَصَٰلِحُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَۖ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ بَعۡدَ ذَٰلِكَ ظَهِيرٌ
Ngati awirinu mulapa kwa Allah pazimene mwachita (chitani changu kulapa) chifukwa chakuti mitima yanu yapotoka pang’ono (chifukwa cha nsanje pa zimene Mneneri akufuna zosunga chinsinsi Chake); koma ngati awirinu muthandizana pazimene zingamvutitse, ndithu Allah ndiye Mtetezi wake ndi Jibril (Gabriele) ndiponso okhulupirira abwino; naonso angelo, kuonjezera apa ndiathandizi (ake).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
عَسَىٰ رَبُّهُۥٓ إِن طَلَّقَكُنَّ أَن يُبۡدِلَهُۥٓ أَزۡوَٰجًا خَيۡرٗا مِّنكُنَّ مُسۡلِمَٰتٖ مُّؤۡمِنَٰتٖ قَٰنِتَٰتٖ تَٰٓئِبَٰتٍ عَٰبِدَٰتٖ سَٰٓئِحَٰتٖ ثَيِّبَٰتٖ وَأَبۡكَارٗا
Ngati (Mtumiki) akakusudzulani, ndithu Mbuye wake, ampatsa akazi ena mmalo mwa inu, abwino kuposa inu: ogonjera (Allah), okhulupirira (ndi mitima yawo), omvera, olapa, odzichepetsa (pamaso pa Allah) ochita mapemphero (kwambiri), oyenda (pa chikhulupiliro cha Allah kapena ochulukitsa kusala) amene adakwatiwapo kale ndi osakwatiwapo.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ قُوٓاْ أَنفُسَكُمۡ وَأَهۡلِيكُمۡ نَارٗا وَقُودُهَا ٱلنَّاسُ وَٱلۡحِجَارَةُ عَلَيۡهَا مَلَٰٓئِكَةٌ غِلَاظٞ شِدَادٞ لَّا يَعۡصُونَ ٱللَّهَ مَآ أَمَرَهُمۡ وَيَفۡعَلُونَ مَا يُؤۡمَرُونَ
E inu amene mwakhulupirira! Dzitchinjirizeni inu ndi mawanja anu ku Moto umene nkhuni zake ndi anthu ndi miyala; oyang’anira ake ndi angelo ouma mtima, amphamvu, sanyoza Allah pa zimene Wawalamula, ndipo amachita (zokhazo) zimene alamulidwa.[369]
[369] Akuluakulu ndiponso aliyense amene ali ndi udindo akuwalamula kuwakonza amene ali pansi pawo powaphunzitsa chipembedzo ndi chikhalidwe chimene Allah akuchifuna kuti awatchinjirize ku chionongeko. Ngati satero ndiye kuti chilango chikafika chidzakhala cha onse.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَا تَعۡتَذِرُواْ ٱلۡيَوۡمَۖ إِنَّمَا تُجۡزَوۡنَ مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
(Adzawauza osakhulupirira pa tsiku la chiweruziro) E inu amene simdakhulupirire! Musadandaule lero, ndithu mukulipidwa pa zimene mumachita (padziko lapansi).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ تُوبُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ تَوۡبَةٗ نَّصُوحًا عَسَىٰ رَبُّكُمۡ أَن يُكَفِّرَ عَنكُمۡ سَيِّـَٔاتِكُمۡ وَيُدۡخِلَكُمۡ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ يَوۡمَ لَا يُخۡزِي ٱللَّهُ ٱلنَّبِيَّ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥۖ نُورُهُمۡ يَسۡعَىٰ بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَبِأَيۡمَٰنِهِمۡ يَقُولُونَ رَبَّنَآ أَتۡمِمۡ لَنَا نُورَنَا وَٱغۡفِرۡ لَنَآۖ إِنَّكَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
E inu amene mwakhulupirira! Lapani kwa Allah; kulapa koona; ndithu Mbuye wanu akufafanizirani zoipa zanu ndi kukakulowetsani m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake, tsiku limene Allah sadzayalutsa mneneli ndi amene adakhulupirira pamodzi naye. Dangalira lawo lidzayenda chapatsogolo pawo ndi mbali yakumanja kwawo, uku akunena: “Mbuye wathu! Tikwanitsireni dangalira lathu (mpaka likatifikitse ku Munda wamtendere), ndiponso tikhululukireni ndithu Inu ndi Wokhoza chilichonse.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ جَٰهِدِ ٱلۡكُفَّارَ وَٱلۡمُنَٰفِقِينَ وَٱغۡلُظۡ عَلَيۡهِمۡۚ وَمَأۡوَىٰهُمۡ جَهَنَّمُۖ وَبِئۡسَ ٱلۡمَصِيرُ
E iwe Mneneri! Limbana ndi akafiri (osakhulupirira) ndi Amunafikina (Achiphamaso), aumire mtima. Ndipo malo awo ndi ku Jahannam, taonani kuipa kobwerera (kwawo)!
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
ضَرَبَ ٱللَّهُ مَثَلٗا لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ ٱمۡرَأَتَ نُوحٖ وَٱمۡرَأَتَ لُوطٖۖ كَانَتَا تَحۡتَ عَبۡدَيۡنِ مِنۡ عِبَادِنَا صَٰلِحَيۡنِ فَخَانَتَاهُمَا فَلَمۡ يُغۡنِيَا عَنۡهُمَا مِنَ ٱللَّهِ شَيۡـٔٗا وَقِيلَ ٱدۡخُلَا ٱلنَّارَ مَعَ ٱلدَّٰخِلِينَ
Allah wapereka fanizo la osakhulupirira monga mkazi wa Nuh ndi mkazi wa Luti. Awiriwa adali pansi pa akapolo Athu awiri abwino, koma adali osakhulupirika kwa amuna awo, (ndipo amuna awo) sadawateteze kalikonse ku chilango cha Allah, ndipo kudanenedwa kwa iwo “Lowani ku Moto pamodzi (ndi ena) olowa.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَضَرَبَ ٱللَّهُ مَثَلٗا لِّلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱمۡرَأَتَ فِرۡعَوۡنَ إِذۡ قَالَتۡ رَبِّ ٱبۡنِ لِي عِندَكَ بَيۡتٗا فِي ٱلۡجَنَّةِ وَنَجِّنِي مِن فِرۡعَوۡنَ وَعَمَلِهِۦ وَنَجِّنِي مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ
Ndiponso Allah wapereka fanizo la amene akhulupirira monga mkazi wa Firiauna (Farawo) pamene adanena: “Mbuye wanga! Ndimangireni kwa inu Nyumba mu Jannah, ndipo ndipulumutseni kwa Firiauna ndi zochita zake, ndiponso ndipulumutseni kwa anthu oipa (ndi amtopola.)”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَمَرۡيَمَ ٱبۡنَتَ عِمۡرَٰنَ ٱلَّتِيٓ أَحۡصَنَتۡ فَرۡجَهَا فَنَفَخۡنَا فِيهِ مِن رُّوحِنَا وَصَدَّقَتۡ بِكَلِمَٰتِ رَبِّهَا وَكُتُبِهِۦ وَكَانَتۡ مِنَ ٱلۡقَٰنِتِينَ
Ndi (fanizo lina la wokhulupirira monga) Mariya mwana wa Imran amene adasunga umaliseche wake; ndipo tidauzira mmenemo Mzimu Wathu ndipo adavomereza mawu a Mbuye wake (omwe adali zolamula Zake ndi zoletsa Zake) ndi mabuku Ake (amene adavumbulutsidwa kwa Aneneri Ake); ndipo adali mmodzi wa opitiriza kudzichepetsa (ndi kumvera Allah).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
 
Übersetzung der Bedeutungen Surah / Kapitel: At-Tahrîm
Suren/ Kapiteln Liste Nummer der Seite
 
Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - الترجمة الشيشيوا - Übersetzungen

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

Schließen