Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation * - Translations’ Index


Translation of the meanings Surah: Al-Hujurāt   Ayah:

Al-Hujurāt

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تُقَدِّمُواْ بَيۡنَ يَدَيِ ٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦۖ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٞ
E inu amene mwakhulupirira! Musamatsogoze (kulamula chinthu chapachipembedzo kapena cham’dziko) patsogolo pa (mawu a) Allah ndi Mthenga Wake. Ndipo muopeni Allah, ndithu Allah Ngwakumva, Ngodziwa.
Arabic explanations of the Qur’an:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَرۡفَعُوٓاْ أَصۡوَٰتَكُمۡ فَوۡقَ صَوۡتِ ٱلنَّبِيِّ وَلَا تَجۡهَرُواْ لَهُۥ بِٱلۡقَوۡلِ كَجَهۡرِ بَعۡضِكُمۡ لِبَعۡضٍ أَن تَحۡبَطَ أَعۡمَٰلُكُمۡ وَأَنتُمۡ لَا تَشۡعُرُونَ
E inu amene mwakhulupirira! Musamakweze mawu anu pamwamba pa mawu a Mneneri; musakweze mawu pokamba naye monga momwe mumayankhulira nokhanokha, kuopa kuti zochita zanu zingaonongeke (ndi kukhala zopanda mphoto) pomwe inu simukuzindikira.
Arabic explanations of the Qur’an:
إِنَّ ٱلَّذِينَ يَغُضُّونَ أَصۡوَٰتَهُمۡ عِندَ رَسُولِ ٱللَّهِ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ ٱمۡتَحَنَ ٱللَّهُ قُلُوبَهُمۡ لِلتَّقۡوَىٰۚ لَهُم مَّغۡفِرَةٞ وَأَجۡرٌ عَظِيمٌ
Ndithu amene akutsitsa mawu awo pamaso pa mtumiki wa Allah, iwo ndiamene Allah wawayeretsa mitima yawo pomuopa Iye; chikhululuko ndi malipiro akulu zidzakhala pa iwo.
Arabic explanations of the Qur’an:
إِنَّ ٱلَّذِينَ يُنَادُونَكَ مِن وَرَآءِ ٱلۡحُجُرَٰتِ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡقِلُونَ
Ndithu amene akukuitana (uku ali) kuseri kwa zipinda (za nyumba), ambiri a iwo sazindikira.
Arabic explanations of the Qur’an:
وَلَوۡ أَنَّهُمۡ صَبَرُواْ حَتَّىٰ تَخۡرُجَ إِلَيۡهِمۡ لَكَانَ خَيۡرٗا لَّهُمۡۚ وَٱللَّهُ غَفُورٞ رَّحِيمٞ
Ndipo iwo akadapirira ndi kuyembekeza (kuti) mpaka utuluke ndi kudza kwa iwo, zikadakhala zabwino kwa iwo; koma Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha.
Arabic explanations of the Qur’an:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِن جَآءَكُمۡ فَاسِقُۢ بِنَبَإٖ فَتَبَيَّنُوٓاْ أَن تُصِيبُواْ قَوۡمَۢا بِجَهَٰلَةٖ فَتُصۡبِحُواْ عَلَىٰ مَا فَعَلۡتُمۡ نَٰدِمِينَ
E inu amene mwakhulupirira! Ngati atakudzerani munthu wosakhulupirika ndi nkhani (iliyonse, musamuvomereze); ifufuzeni (kaye) kuopa kuti mungachitire anthu (mtopola) mwa umbuli, ndikuti mungazanong’oneze bondo pa zomwe mwachita.
Arabic explanations of the Qur’an:
وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ فِيكُمۡ رَسُولَ ٱللَّهِۚ لَوۡ يُطِيعُكُمۡ فِي كَثِيرٖ مِّنَ ٱلۡأَمۡرِ لَعَنِتُّمۡ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ حَبَّبَ إِلَيۡكُمُ ٱلۡإِيمَٰنَ وَزَيَّنَهُۥ فِي قُلُوبِكُمۡ وَكَرَّهَ إِلَيۡكُمُ ٱلۡكُفۡرَ وَٱلۡفُسُوقَ وَٱلۡعِصۡيَانَۚ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلرَّٰشِدُونَ
Ndipo dziwani kuti ndithu mwa inu muli Mtumiki wa Allah, (mumvereni iye zimene akukuuzani) kukadakhala kuti iye akukumverani pa zinthu zambiri (zimene mukumuuza), mukadavutika. Koma Allah wachichita chikhulupiliro kukhala chokondeka kwa inu ndipo wachikometsa m’mitima mwanu ndipo wakuchitani kuti mukude kusakhulupirira ndi ufasiki (kutuluka m’malamulo a Allah) ndi kunyoza (Allah.) Iwowo ndiwo oongoka.
Arabic explanations of the Qur’an:
فَضۡلٗا مِّنَ ٱللَّهِ وَنِعۡمَةٗۚ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٞ
(Chifukwa cha) ubwino wochokera kwa Allah ndi mtendere (Wake, mwapeza zimenezi); ndipo Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya.
Arabic explanations of the Qur’an:
وَإِن طَآئِفَتَانِ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٱقۡتَتَلُواْ فَأَصۡلِحُواْ بَيۡنَهُمَاۖ فَإِنۢ بَغَتۡ إِحۡدَىٰهُمَا عَلَى ٱلۡأُخۡرَىٰ فَقَٰتِلُواْ ٱلَّتِي تَبۡغِي حَتَّىٰ تَفِيٓءَ إِلَىٰٓ أَمۡرِ ٱللَّهِۚ فَإِن فَآءَتۡ فَأَصۡلِحُواْ بَيۡنَهُمَا بِٱلۡعَدۡلِ وَأَقۡسِطُوٓاْۖ إِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلۡمُقۡسِطِينَ
Ndipo ngati magulu awiri aokhulupirira atamenyana ayanjanitseni pakati pawo. Ngati gulu limodzi mwa magulu awiriwo likuchitira mtopola linalo, limenyeni limene likuchita mtopola mpaka libwelere ku lamulo la Allah; ngati litabwerera, ayanjanitseni pakati pawo mwachilungamo, ndipo chitani chilungamo; ndithu Allah amakonda ochita chilungamo.
Arabic explanations of the Qur’an:
إِنَّمَا ٱلۡمُؤۡمِنُونَ إِخۡوَةٞ فَأَصۡلِحُواْ بَيۡنَ أَخَوَيۡكُمۡۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ
Ndithu okhulupirira onse ndi pachibale choncho yanjanitsani pakati pa abale anu; (musanyozere lamulo la kuyanjanitsa) ndipo muopeni Allah kuti akuchitireni chifundo.
Arabic explanations of the Qur’an:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا يَسۡخَرۡ قَوۡمٞ مِّن قَوۡمٍ عَسَىٰٓ أَن يَكُونُواْ خَيۡرٗا مِّنۡهُمۡ وَلَا نِسَآءٞ مِّن نِّسَآءٍ عَسَىٰٓ أَن يَكُنَّ خَيۡرٗا مِّنۡهُنَّۖ وَلَا تَلۡمِزُوٓاْ أَنفُسَكُمۡ وَلَا تَنَابَزُواْ بِٱلۡأَلۡقَٰبِۖ بِئۡسَ ٱلِٱسۡمُ ٱلۡفُسُوقُ بَعۡدَ ٱلۡإِيمَٰنِۚ وَمَن لَّمۡ يَتُبۡ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ
E inu amene mwakhulupirira! Amuna asanyoze amuna anzawo; mwina (onyozedwa) nkukhala abwino (kwa Allah) kuposa iwo (onyoza). Nawonso akazi asanyoze akazi anzawo; mwina onyozedwa nkukhala abwino (kwa Allah) kuposa iwo (onyoza). Ndipo musatukwanizane pokumbana mitundu kapena kuitanana ndi maina oipa. Taonani kuipa kumuyitanira munthu ndi dzina loti fasiki (wotuluka m’malamulo a Allah) atakhulupirira kale; ndipo amene salapa (ku zimenezi), iwo ndiwo (ochimwa) odzichitira okha chinyengo.
Arabic explanations of the Qur’an:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱجۡتَنِبُواْ كَثِيرٗا مِّنَ ٱلظَّنِّ إِنَّ بَعۡضَ ٱلظَّنِّ إِثۡمٞۖ وَلَا تَجَسَّسُواْ وَلَا يَغۡتَب بَّعۡضُكُم بَعۡضًاۚ أَيُحِبُّ أَحَدُكُمۡ أَن يَأۡكُلَ لَحۡمَ أَخِيهِ مَيۡتٗا فَكَرِهۡتُمُوهُۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَۚ إِنَّ ٱللَّهَ تَوَّابٞ رَّحِيمٞ
E inu amene mwakhulupirira! Dzitalikitseni kuwaganizira kwambiri zoipa (anthu abwino). Ndithu kuganizira (anthu) maganizo (oipa) nditchimo. Ndipo musafufuzefufuze (nkhani za anthu) ndiponso musajedane pakati panu. Kodi mmodzi wa inu angakonde kudya minofu ya m’bale wake wakufa? Simungakonde zimenezo ndipo muopeni Allah. Ndithu Allah Ngolandira kulapa, Ngwachisoni chosatha.
Arabic explanations of the Qur’an:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِنَّا خَلَقۡنَٰكُم مِّن ذَكَرٖ وَأُنثَىٰ وَجَعَلۡنَٰكُمۡ شُعُوبٗا وَقَبَآئِلَ لِتَعَارَفُوٓاْۚ إِنَّ أَكۡرَمَكُمۡ عِندَ ٱللَّهِ أَتۡقَىٰكُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمٌ خَبِيرٞ
E inu anthu! Tidakulengani (nonse) kuchokera kwa mwamuna (m’modzi; Adam) ndi mkazi (m’modzi; Hawa), ndipo tidakuchitani kukhala a mitundu ndi mafuko (osiyanasiyana) kuti m’dziwane (basi). Ndithu wolemekezeka kwambiri mwa inu kwa Allah, ndi yemwe ali woopa. Ndithu Allah Ngodziwa, ndipo Ngodziwa kwambiri nkhani zonse.
Arabic explanations of the Qur’an:
۞ قَالَتِ ٱلۡأَعۡرَابُ ءَامَنَّاۖ قُل لَّمۡ تُؤۡمِنُواْ وَلَٰكِن قُولُوٓاْ أَسۡلَمۡنَا وَلَمَّا يَدۡخُلِ ٱلۡإِيمَٰنُ فِي قُلُوبِكُمۡۖ وَإِن تُطِيعُواْ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ لَا يَلِتۡكُم مِّنۡ أَعۡمَٰلِكُمۡ شَيۡـًٔاۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٌ
Arabu akumidzi adanena (kuti): “Takhulupirira.” Nena, Simudakhulupirire (kwenikweni); koma nenani (kuti): “Tagonjera (Allah).” Ndipo mpaka pano chikhulupiliro sichidalowe m’mitima mwanu (ndi kukhazikika bwinobwino). Koma ngati mumvera Allah ndi Mtumiki Wake, sakuchepetserani chilichonse m’zochita zanu. Ndithu Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachifundo chambiri.
Arabic explanations of the Qur’an:
إِنَّمَا ٱلۡمُؤۡمِنُونَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ ثُمَّ لَمۡ يَرۡتَابُواْ وَجَٰهَدُواْ بِأَمۡوَٰلِهِمۡ وَأَنفُسِهِمۡ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِۚ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلصَّٰدِقُونَ
Ndithu amene ali okhulupirira (moona) ndiomwe akhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake, ndipo kenako nkukhala osakaika, nkuchita nkhondo panjira ya Allah, ndi chuma chawo, ndi matupi awo, iwowo ndiwo owona (pa chikhulupiliro chawo).
Arabic explanations of the Qur’an:
قُلۡ أَتُعَلِّمُونَ ٱللَّهَ بِدِينِكُمۡ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ وَٱللَّهُ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ
Nena: “Kodi mukumdziwitsa Allah za chipembedzo chanu? Koma chikhalirecho Allah akudziwa zonse za kumwamba ndi za m’dziko lapansi. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse.
Arabic explanations of the Qur’an:
يَمُنُّونَ عَلَيۡكَ أَنۡ أَسۡلَمُواْۖ قُل لَّا تَمُنُّواْ عَلَيَّ إِسۡلَٰمَكُمۖ بَلِ ٱللَّهُ يَمُنُّ عَلَيۡكُمۡ أَنۡ هَدَىٰكُمۡ لِلۡإِيمَٰنِ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Akukukumba iwe chifukwa cha kulowa kwawo m’Chisilamu (ngati kuti akuchitira ufulu). Nena: “Kulowa kwanu m’Chisilamu musakuyese kuti mwandichitira ine ubwino, koma Allah ndiAmene wakuchitirani ubwino pokuongolerani ku chikhulupiliro, ngati muli owona.”
Arabic explanations of the Qur’an:
إِنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ غَيۡبَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَٱللَّهُ بَصِيرُۢ بِمَا تَعۡمَلُونَ
Ndithu Allah akudziwa zobisika za kumwamba ndi za mnthaka. Ndipo Allah akuona zimene mukuchita.
Arabic explanations of the Qur’an:
 
Translation of the meanings Surah: Al-Hujurāt
Surahs’ Index Page Number
 
Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Translations’ Index

Translation of the Quran meanings into Chewa by Khaled Ibrahim Betala (ed. 2020)

close