Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa * - Índice de traducciones


Traducción de significados Capítulo: Sura Maryam   Versículo:

Sura Maryam

كٓهيعٓصٓ
Kâf-Hâ-Yâ- ‘Aîn-Sâd.
Las Exégesis Árabes:
ذِكۡرُ رَحۡمَتِ رَبِّكَ عَبۡدَهُۥ زَكَرِيَّآ
Ichi (ndi) chikumbutso cha chifundo cha Mbuye wako pa kapolo Wake Zakariya.
Las Exégesis Árabes:
إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥ نِدَآءً خَفِيّٗا
Pamene adaitana Mbuye wake, kuitana kwa chinsinsi.
Las Exégesis Árabes:
قَالَ رَبِّ إِنِّي وَهَنَ ٱلۡعَظۡمُ مِنِّي وَٱشۡتَعَلَ ٱلرَّأۡسُ شَيۡبٗا وَلَمۡ أَكُنۢ بِدُعَآئِكَ رَبِّ شَقِيّٗا
Adati: “E Mbuye wanga! Ndithu mafupa anga afooka, ndipo mutu wanga wayaka (ukung’anima) ndi imvi; sindidali watsoka pokupemphani Mbuye wanga (koma nthawi iliyonse ndikakupemphani mumandivomereza)[264]
[264] Apa tanthauzo lake nkuti: “E Mbuye wanga! Palibe pamene mudalitaya pachabe pempho langa koma mudandizoloweza kuti ndikakupemphani mumandipatsa zomwe ndapempha. Choncho yankhaninso pempho langali.”
Las Exégesis Árabes:
وَإِنِّي خِفۡتُ ٱلۡمَوَٰلِيَ مِن وَرَآءِي وَكَانَتِ ٱمۡرَأَتِي عَاقِرٗا فَهَبۡ لِي مِن لَّدُنكَ وَلِيّٗا
“Ndipo ndithu ine ndikuopera abale anga (kuononga chipembedzo) pambuyo panga; ndipo mkazi wanga ndi chumba; choncho ndipatseni (mwana) mlowammalo wanga wochokera kwa Inu.”
Las Exégesis Árabes:
يَرِثُنِي وَيَرِثُ مِنۡ ءَالِ يَعۡقُوبَۖ وَٱجۡعَلۡهُ رَبِّ رَضِيّٗا
“Adzandilowe chokolo (pa nzeru za utsogoleri ndi uneneri) ndikulowanso ufumu wa banja la Ya’qub; ndipo Mbuye wanga nchiteni kukhala woyanjidwa (ndi Inu)”
Las Exégesis Árabes:
يَٰزَكَرِيَّآ إِنَّا نُبَشِّرُكَ بِغُلَٰمٍ ٱسۡمُهُۥ يَحۡيَىٰ لَمۡ نَجۡعَل لَّهُۥ مِن قَبۡلُ سَمِيّٗا
(Adauzidwa): “E iwe Zakariya! Ife tikukuuza nkhani yabwino yakuti ubereka mwana dzina lake Yahya palibe patsogolo pake amene tidamutcha dzina longa lake.”
Las Exégesis Árabes:
قَالَ رَبِّ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَٰمٞ وَكَانَتِ ٱمۡرَأَتِي عَاقِرٗا وَقَدۡ بَلَغۡتُ مِنَ ٱلۡكِبَرِ عِتِيّٗا
(Zakariya) adati: “Mbuye wanga! Ndingapeze bwanji mwana pomwe mkazi wanga ndi nkhalamba yosabereka ndipo ine ndafikanso pa ukulu wopyola muyeso?”
Las Exégesis Árabes:
قَالَ كَذَٰلِكَ قَالَ رَبُّكَ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٞ وَقَدۡ خَلَقۡتُكَ مِن قَبۡلُ وَلَمۡ تَكُ شَيۡـٔٗا
Adati: “Ndimomwemo. Mbuye wako wanena (kuti): ‘Izi nzofewa kwa Ine; ndithu ndidakulenga kale pomwe iwe sudali kanthu.”
Las Exégesis Árabes:
قَالَ رَبِّ ٱجۡعَل لِّيٓ ءَايَةٗۖ قَالَ ءَايَتُكَ أَلَّا تُكَلِّمَ ٱلنَّاسَ ثَلَٰثَ لَيَالٖ سَوِيّٗا
Adati: “Mbuye wanga ndipatseni chizindikiro (chodziwitsa kuti mkazi wanga ali ndi pakati).” Adati: “Chizindikiro chako ndikuti sudzatha kuyankhula ndi anthu mpaka masiku atatu pomwe iwe uli bwinobwino.”
Las Exégesis Árabes:
فَخَرَجَ عَلَىٰ قَوۡمِهِۦ مِنَ ٱلۡمِحۡرَابِ فَأَوۡحَىٰٓ إِلَيۡهِمۡ أَن سَبِّحُواْ بُكۡرَةٗ وَعَشِيّٗا
Ndipo adatuluka kuchipinda chopemphelera ndikuonekera kwa anthu ake, ndipo adawalozera (pomwe sadathe kuyankhula) kuti: “Lemekezani Allah m’mawa ndi madzulo.”
Las Exégesis Árabes:
يَٰيَحۡيَىٰ خُذِ ٱلۡكِتَٰبَ بِقُوَّةٖۖ وَءَاتَيۡنَٰهُ ٱلۡحُكۡمَ صَبِيّٗا
“E iwe Yahya! Gwira buku ili mwamphamvu (ndi mwachidwi).” Ndipo tidampatsa nzeru ali mwana.
Las Exégesis Árabes:
وَحَنَانٗا مِّن لَّدُنَّا وَزَكَوٰةٗۖ وَكَانَ تَقِيّٗا
Ndi chisoni chochokera kwa Ife ndi kumuyeretsa (mwanayo), ndipo adali woopa (Allah).
Las Exégesis Árabes:
وَبَرَّۢا بِوَٰلِدَيۡهِ وَلَمۡ يَكُن جَبَّارًا عَصِيّٗا
Komanso wochitira zabwino makolo ake ndipo sadali wodzitukumula (kwa anthu) kapena kunyoza (Allah).
Las Exégesis Árabes:
وَسَلَٰمٌ عَلَيۡهِ يَوۡمَ وُلِدَ وَيَوۡمَ يَمُوتُ وَيَوۡمَ يُبۡعَثُ حَيّٗا
Ndipo mtendere wa Allah udali pa iye kuyambira tsiku lomwe adabadwa ndi tsiku lomwe adamwalira, ndi tsiku limene adzaukitsidwa ku imfa kukhala wamoyo.
Las Exégesis Árabes:
وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَرۡيَمَ إِذِ ٱنتَبَذَتۡ مِنۡ أَهۡلِهَا مَكَانٗا شَرۡقِيّٗا
Ndipo mtchule Mariya m’buku ili pamene adadzipatula ku anthu a kubanja lake (ndikunka) kumalo ambali ya kummawa.[265]
[265] M’sura iyi muli nkhani zododometsa. Yoyamba njakubadwa kwa Yahya (Yohane) yemwe adabadwa kuchokera kwa nkhalamba ziwiri zotheratu; pomwe mwamuna adali ndi zaka 120 ndipo mkazi adali ndi zaka 98. Choncho kubadwa kwa Yahya kudali kododometsa. Koma kubadwa kwa Isa (Yesu) ndikumene kudali kododometsa zedi poti iye anabadwa kwa namwali wosakwatiwa. Tero iye anamubereka popanda mwamuna. Zonsezi Allah adafuna kuwadziwitsa anthu ndi kuwatsimikizira kuti Iye ali ndi mphamvu zolengera munthu popanda mwamuna.
Las Exégesis Árabes:
فَٱتَّخَذَتۡ مِن دُونِهِمۡ حِجَابٗا فَأَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡهَا رُوحَنَا فَتَمَثَّلَ لَهَا بَشَرٗا سَوِيّٗا
Ndipo adadzitsekereza kwa iwo (kuti athe kutumikira Allah mokwanira), choncho tidatuma Mzimu Wathu (Mngelo Gabriel) kwa iye ndipo adadzifanizira kwa iye monga munthu weniweni.
Las Exégesis Árabes:
قَالَتۡ إِنِّيٓ أَعُوذُ بِٱلرَّحۡمَٰنِ مِنكَ إِن كُنتَ تَقِيّٗا
(Mariya) adati: “Ndithu ndikudzichinjiriza ndi (Allah) Mwini chifundo chambiri, kwa iwe ngati umaopa (Allah).”
Las Exégesis Árabes:
قَالَ إِنَّمَآ أَنَا۠ رَسُولُ رَبِّكِ لِأَهَبَ لَكِ غُلَٰمٗا زَكِيّٗا
(Mngelo) adati: “Ndithu ine ndine Mtumiki wa mbuye wako, (ndadza) kuti ndikupatse mwana woyera.”
Las Exégesis Árabes:
قَالَتۡ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَٰمٞ وَلَمۡ يَمۡسَسۡنِي بَشَرٞ وَلَمۡ أَكُ بَغِيّٗا
Adati: “Ndingakhale bwanji ndi mwana pomwe sadandikhudze mwamuna (aliyense), ndipo ine sindili (mkazi) wachiwerewere?”
Las Exégesis Árabes:
قَالَ كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٞۖ وَلِنَجۡعَلَهُۥٓ ءَايَةٗ لِّلنَّاسِ وَرَحۡمَةٗ مِّنَّاۚ وَكَانَ أَمۡرٗا مَّقۡضِيّٗا
(Mngelo) adati: “Ndimomwemo.” Mbuye Wako akuti: “Zimenezi kwa Ine nzosavuta. Ndipo timchita kukhala chozizwitsa kwa anthu ndi chifundo chochokera kwa Ife. (Nchifukwa chake tachita izi;) ndipo ichi ndi chinthu chimene chidalamulidwa kale. (Chichitika monga momwe Allah adafunira).”
Las Exégesis Árabes:
۞ فَحَمَلَتۡهُ فَٱنتَبَذَتۡ بِهِۦ مَكَانٗا قَصِيّٗا
Choncho adatenga pakati pake, ndipo adachoka ndi pakatipo kunka kumalo akutali.[266]
[266] Izi zidachitika pamene Gabriele adauzira m’thumba la chovala cha Mariya. Ndipo mpweya udafika mpaka m’mimba mwake. Choncho atakhala ndi pakati anadzipatula kwa anthu kunka kutali ali ndi pakati pa mwana wakeyo kuti anthu angamdzudzule pokhala ndi mimba yosadziwika mwamuna wake.
Las Exégesis Árabes:
فَأَجَآءَهَا ٱلۡمَخَاضُ إِلَىٰ جِذۡعِ ٱلنَّخۡلَةِ قَالَتۡ يَٰلَيۡتَنِي مِتُّ قَبۡلَ هَٰذَا وَكُنتُ نَسۡيٗا مَّنسِيّٗا
Ndipo matenda auchembere (atakwana), adampititsa ku thunthu la mtengo wa kanjedza (wouma kuti awutsamire pomubala mwanayo) adati: “Kalanga ine! Ndiponi ndikadafa izi zisanachitike ndikadakhala nditaiwalidwa ndithu.”
Las Exégesis Árabes:
فَنَادَىٰهَا مِن تَحۡتِهَآ أَلَّا تَحۡزَنِي قَدۡ جَعَلَ رَبُّكِ تَحۡتَكِ سَرِيّٗا
Kenaka (Mngelo) adamuitana kuchokera chapansi pake (kumuuza kuti): “Usadandaule. Ndithu Mbuye wako wakupangira kamtsinje pansi pako.”
Las Exégesis Árabes:
وَهُزِّيٓ إِلَيۡكِ بِجِذۡعِ ٱلنَّخۡلَةِ تُسَٰقِطۡ عَلَيۡكِ رُطَبٗا جَنِيّٗا
Ndipo ligwedezere kumbali yako thunthu la mtengo wakanjedza (woumawo), zipatso zabwino zakupsa zikugwera.”[267]
[267] Omasulira adati: Adamulamula kuti agwedeze thunthu lamtengo wouma kuti aone chizizwa chachiwiri mtengo wouma pokhala wauwisi ndikubereka zipatso nthawi yomweyo zakupsa. Adamuonetsanso kasupe wamadzi okoma yemwe anafwamphuka uku iye akuona. Ndipo iye adali kudya zipatsozo nkumamwera madziwo. Uku kudali kumulimbikitsa mtima kuti asade nkhawa pokhala ndi mwana wopanda tate wake koma zonsezi wazichita ndi Allah.
Las Exégesis Árabes:
فَكُلِي وَٱشۡرَبِي وَقَرِّي عَيۡنٗاۖ فَإِمَّا تَرَيِنَّ مِنَ ٱلۡبَشَرِ أَحَدٗا فَقُولِيٓ إِنِّي نَذَرۡتُ لِلرَّحۡمَٰنِ صَوۡمٗا فَلَنۡ أُكَلِّمَ ٱلۡيَوۡمَ إِنسِيّٗا
Choncho udye ndi kumwa ndikutonthoza diso lako, (khala ndi mpumulo wabwino). Ndipo ukaona munthu aliyense (akafunsa za mwanayo), nena: “Ndithu ine ndalonjeza kwa (Allah) Mwini chifundo chambiri kusala kuti lero sindiyankhula ndi munthu aliyense.”
Las Exégesis Árabes:
فَأَتَتۡ بِهِۦ قَوۡمَهَا تَحۡمِلُهُۥۖ قَالُواْ يَٰمَرۡيَمُ لَقَدۡ جِئۡتِ شَيۡـٔٗا فَرِيّٗا
Ndipo adadza naye (mwanayo) kwa anthu ake atamnyamula. (Anthu) adati: “E iwe Mariya! Ndithu wabwera ndi chinthu chachikulu; (chododometsa).”
Las Exégesis Árabes:
يَٰٓأُخۡتَ هَٰرُونَ مَا كَانَ أَبُوكِ ٱمۡرَأَ سَوۡءٖ وَمَا كَانَتۡ أُمُّكِ بَغِيّٗا
“E iwe mlongo wa Harun! Bambo wako sadali munthu woipa, ngakhalenso mayi wako sadali wachiwerewere.”[268]
[268] Katada adaati: Haaruna adali munthu wolungama kwambiri mu mtundu wa ana alsraeli. Adali wotchuka kwambiri pazakulungama. Choncho ana a Israeli adaili kufanizira Mariya ndi Haaruna chifukwa cha kulungama kwake; sikuti Mariya adali mlongo wake weniweni wa Haaruna yemwe adali m’bale wa Musa. Pakati pa Mariya ndi Haaruna padapita zaka chikwi chimodzi.
Las Exégesis Árabes:
فَأَشَارَتۡ إِلَيۡهِۖ قَالُواْ كَيۡفَ نُكَلِّمُ مَن كَانَ فِي ٱلۡمَهۡدِ صَبِيّٗا
(Mariya sadawayankhe) koma adaloza kwa iye (mwanayo kuti ayankhule naye). Ndipo iwo adati: “Timuyankhula chotani mwana yemwe ali m’chikuta?”
Las Exégesis Árabes:
قَالَ إِنِّي عَبۡدُ ٱللَّهِ ءَاتَىٰنِيَ ٱلۡكِتَٰبَ وَجَعَلَنِي نَبِيّٗا
(Mwanayo) adanena: “Ine ndine kapolo wa Allah. Wandipatsa buku ndikundichita kukhala Mneneri.”
Las Exégesis Árabes:
وَجَعَلَنِي مُبَارَكًا أَيۡنَ مَا كُنتُ وَأَوۡصَٰنِي بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱلزَّكَوٰةِ مَا دُمۡتُ حَيّٗا
“Ndipo wandichita kukhala wodala paliponse pomwe ndili, ndipo wandilamula kuswali ndi kupereka Zakaat pomwe ndili moyo.”
Las Exégesis Árabes:
وَبَرَّۢا بِوَٰلِدَتِي وَلَمۡ يَجۡعَلۡنِي جَبَّارٗا شَقِيّٗا
“Ndipo wandilangiza kuchitira mayi wanga zabwino, ndipo sadandichite kukhala wodzikuza, watsoka (woipa).”
Las Exégesis Árabes:
وَٱلسَّلَٰمُ عَلَيَّ يَوۡمَ وُلِدتُّ وَيَوۡمَ أَمُوتُ وَيَوۡمَ أُبۡعَثُ حَيّٗا
“Ndipo mtendere uli pa ine kuyambira tsiku lomwe ndidabadwa ndi tsiku limene ndidzamwalira, ndi tsiku limene ndidzaukitsidwa (kwa akufa tsiku la chiweruziro) ndikukhala ndi moyo.”
Las Exégesis Árabes:
ذَٰلِكَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَۖ قَوۡلَ ٱلۡحَقِّ ٱلَّذِي فِيهِ يَمۡتَرُونَ
Uyu ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya; (awa ndi) mau owona omwe (Akhrisitu) akuwakaikira.
Las Exégesis Árabes:
مَا كَانَ لِلَّهِ أَن يَتَّخِذَ مِن وَلَدٖۖ سُبۡحَٰنَهُۥٓۚ إِذَا قَضَىٰٓ أَمۡرٗا فَإِنَّمَا يَقُولُ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ
Sikoyenera kwa Allah kudzipangira mwana. Iye (Allah) wapatukana ndi zimenezi. Akafuna chinthu, amangonena kwa chinthucho: “Chitika,” ndipo icho chimachitikadi.
Las Exégesis Árabes:
وَإِنَّ ٱللَّهَ رَبِّي وَرَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُوهُۚ هَٰذَا صِرَٰطٞ مُّسۡتَقِيمٞ
(Isa (Yesu) adati:) “Ndipo ndithu Allah ndi Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu. Choncho mpembedzeni; iyi ndinjira yolunjika (yokufikitsani ku mtendere.)[269]
[269] Umu ndimomwe Isa (Yesu) adanenera za ukapolo wake kwa Allah. Iye sadali Mulungu kapena mwana wa Mulungu, kapena mmodzi wa atatu monga momwe Akhrisitu amanenera. Koma iye adali kapolo wa Allah ndiponso Mtumiki Wake. Allah adamulenga mwa mayi popanda bambo kuti akhale chisonyezo chosonyeza mphamvu za Allah zoposa.
Las Exégesis Árabes:
فَٱخۡتَلَفَ ٱلۡأَحۡزَابُ مِنۢ بَيۡنِهِمۡۖ فَوَيۡلٞ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن مَّشۡهَدِ يَوۡمٍ عَظِيمٍ
Koma magulu (a Akhrisitu ndi Ayuda) adapatukana pakati pawo; (ena adamuyesa Isa (Yesu) kuti ndimwana wa Mulungu, ndipo ena adamuyesa Mulungu weniweni, pomwe Ayuda ankati ndi mwana wobadwa m’njira ya chiwerewere), choncho chilango chaukali chidzatsimikizika pa amene sadakhulupirire pokaonekera tsiku lalikululo (kwa Allah).
Las Exégesis Árabes:
أَسۡمِعۡ بِهِمۡ وَأَبۡصِرۡ يَوۡمَ يَأۡتُونَنَا لَٰكِنِ ٱلظَّٰلِمُونَ ٱلۡيَوۡمَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
Taona kumvetsetsa kwawo ndi kupenyetsetsa kwawo tsiku lodzatidzera, (kudzanenedwa kuti:) “Koma osalungama lero ali m’kusokera koonekera.”
Las Exégesis Árabes:
وَأَنذِرۡهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡحَسۡرَةِ إِذۡ قُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ وَهُمۡ فِي غَفۡلَةٖ وَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Ndipo achenjeze (anthu) za tsiku la madandaulo, pamene chiweruzo chidzagamulidwa, (abwino kulowa ku munda wamtendere, oipa kulowa ku Moto); koma iwo (pano pa dziko lapansi) ali m’kusalabadira ndipo sakhulupirira.[270]
[270] Tsiku la Qiyâma (chimaliziro), anthu oipa adzadandaula kwambiri. Tsiku limenelo kwa iwo lidzakhala tsiku lamadandaulo okhaokha, osatinso chinachake. M’buku la swahihi la Musilim muli hadisi ya Abi Saidi Khuduriyi (r.a). Iye adati: Ndithu Mtumiki (s.a.w) adati: “Pamene anthu olungama adzalowa ku munda wa mtendere ndipo anthu oipa ku Moto, imfa idzadza tsiku la chimalizirolo. Idzaoneka ngati nkhosa yabwino. Ndipo idzaikidwa pakati pa Munda wa mtendere ndi Moto. Tsono kudzanenedwa: “E inu eni munda wa mtendere! Kodi ichi mukuchidziwa?” Onse adzatukula makosi kuyang’ana nkuzati: “Inde iyo ndi imfa.” Kenako kudzanenedwa: “E inu anthu a ku Moto! Kodi ichi mukuchidziwa?” Onse adzatukula makosi awo kuyang’ana nkuzati: “Inde iyo ndi imfa.” Ndipo kudzalamulidwa kuti izingidwe. Kenako kudzanenedwa: “E inu eni munda wa mtendere! Khalani muyaya m’menemo, palibe imfanso. Ndiponso inu eni Moto khalani muyaya mmenemo palibe imfanso.” Kenako Mtumiki (s.a.w) adawerenga Ayah (ndime) yakuti: “Achenjeze za tsiku lamadandaulo aakulu....”
Las Exégesis Árabes:
إِنَّا نَحۡنُ نَرِثُ ٱلۡأَرۡضَ وَمَنۡ عَلَيۡهَا وَإِلَيۡنَا يُرۡجَعُونَ
Ndithu Ife Tidzaitenga nthaka ndi amene ali pamenepo; (zonse zidzakhala za Ife) ndipo kwa Ife adzabwerera.
Las Exégesis Árabes:
وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِبۡرَٰهِيمَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صِدِّيقٗا نَّبِيًّا
Ndipo mtchule m’buku ili, Ibrahim. Ndithu iye adali wonena zoona zokhazokha, Mneneri.
Las Exégesis Árabes:
إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ يَٰٓأَبَتِ لِمَ تَعۡبُدُ مَا لَا يَسۡمَعُ وَلَا يُبۡصِرُ وَلَا يُغۡنِي عَنكَ شَيۡـٔٗا
(Akumbutse) pamene iye adauza bambo wake: “E inu bambo wanga! Bwanji mukupembedza zomwe sizimva ndiponso sizipenya, ndiponso Zosakupindulitsani chilichonse?”
Las Exégesis Árabes:
يَٰٓأَبَتِ إِنِّي قَدۡ جَآءَنِي مِنَ ٱلۡعِلۡمِ مَا لَمۡ يَأۡتِكَ فَٱتَّبِعۡنِيٓ أَهۡدِكَ صِرَٰطٗا سَوِيّٗا
“E inu bambo wanga! Ndithu ine zandidzera nzeru (zomuzindikira Allah) zomwe sizidakudzereni; choncho nditsateni. Ndikutsogolereni ku njira yolungama.”
Las Exégesis Árabes:
يَٰٓأَبَتِ لَا تَعۡبُدِ ٱلشَّيۡطَٰنَۖ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ كَانَ لِلرَّحۡمَٰنِ عَصِيّٗا
“E bambo wanga! Musapembedze satana (potsatira malangizo ake). Ndithu satana ngopandukira (Allah) Mwini chifundo chambiri.”
Las Exégesis Árabes:
يَٰٓأَبَتِ إِنِّيٓ أَخَافُ أَن يَمَسَّكَ عَذَابٞ مِّنَ ٱلرَّحۡمَٰنِ فَتَكُونَ لِلشَّيۡطَٰنِ وَلِيّٗا
E bambo wanga! Ndithu ine ndikuopa kuti chilango chingakukhudzeni chochokera kwa (Allah) Mwini chifundo chambiri, ndipo potero mdzakhala bwenzi la satana.”
Las Exégesis Árabes:
قَالَ أَرَاغِبٌ أَنتَ عَنۡ ءَالِهَتِي يَٰٓإِبۡرَٰهِيمُۖ لَئِن لَّمۡ تَنتَهِ لَأَرۡجُمَنَّكَۖ وَٱهۡجُرۡنِي مَلِيّٗا
(Bambo wake) adati: “Kodi iwe ukuda milungu yanga, E iwe Ibrahim? Ngati susiya (kunyoza milungu yanga) ndikugenda ndi miyala; choncho ndichokere kwa nthawi yaitali (tisaonanenso).”
Las Exégesis Árabes:
قَالَ سَلَٰمٌ عَلَيۡكَۖ سَأَسۡتَغۡفِرُ لَكَ رَبِّيٓۖ إِنَّهُۥ كَانَ بِي حَفِيّٗا
(Ibrahim) adati: “Mtendere ukhale pa inu! Ndikupempherani chikhululuko kwa Mbuye wanga (ngakhale mwandipirikitsa). Ndithu iye amandichitira chisoni kwambiri.”
Las Exégesis Árabes:
وَأَعۡتَزِلُكُمۡ وَمَا تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَأَدۡعُواْ رَبِّي عَسَىٰٓ أَلَّآ أَكُونَ بِدُعَآءِ رَبِّي شَقِيّٗا
“Ndipo ine ndikupatukirani ku zomwe mukuzipembedzazo kusiya Allah ndipo ndipempha Mbuye wanga; ndithu sindikhala watsoka popempha Mbuye wanga.”
Las Exégesis Árabes:
فَلَمَّا ٱعۡتَزَلَهُمۡ وَمَا يَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَۖ وَكُلّٗا جَعَلۡنَا نَبِيّٗا
Ndipo pamene adawapatukira ndi zimene adali kuzipembedza kusiya Allah, tidampatsa iye Ishaq, ndi Ya’qub, ndipo aliyense wa iwo tidampanga kukhala m’neneri.
Las Exégesis Árabes:
وَوَهَبۡنَا لَهُم مِّن رَّحۡمَتِنَا وَجَعَلۡنَا لَهُمۡ لِسَانَ صِدۡقٍ عَلِيّٗا
Ndipo tidawapatsa iwo chifundo Chathu, ndi kuwayikira iwo kutchulidwa kwabwino, kwapamwamba (pakati pa zolengedwa).
Las Exégesis Árabes:
وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مُوسَىٰٓۚ إِنَّهُۥ كَانَ مُخۡلَصٗا وَكَانَ رَسُولٗا نَّبِيّٗا
Ndipo mtchule Mûsa m’buku (ili). Ndithu iye adali wosankhidwa ndi woyeretsedwa: ndipo adali Mtumiki M’neneri.
Las Exégesis Árabes:
وَنَٰدَيۡنَٰهُ مِن جَانِبِ ٱلطُّورِ ٱلۡأَيۡمَنِ وَقَرَّبۡنَٰهُ نَجِيّٗا
Ndipo tidamuitana kumbali yakudzanjadzanja la phiri la Turi, ndipo tidamuyandikitsa ndi kuyankhula Nafe momunong’ oneza.
Las Exégesis Árabes:
وَوَهَبۡنَا لَهُۥ مِن رَّحۡمَتِنَآ أَخَاهُ هَٰرُونَ نَبِيّٗا
Ndipo mwachifundo Chathu tidampatsa (Mûsa) m’bale wake Harun kukhala mneneri (womuthangata)
Las Exégesis Árabes:
وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِسۡمَٰعِيلَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صَادِقَ ٱلۡوَعۡدِ وَكَانَ رَسُولٗا نَّبِيّٗا
Mtchulenso m’buku (ili) Ismaila; ndithu iye adali woona palonjezo, ndipo adali Mtumiki Mneneri.
Las Exégesis Árabes:
وَكَانَ يَأۡمُرُ أَهۡلَهُۥ بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱلزَّكَوٰةِ وَكَانَ عِندَ رَبِّهِۦ مَرۡضِيّٗا
Adali kulamula anthu ake Swala ndi Zakaat, ndipo kwa Mbuye wake adali woyanjidwa.
Las Exégesis Árabes:
وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِدۡرِيسَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صِدِّيقٗا نَّبِيّٗا
Mtchulenso m’buku (ili) Idris, ndithu iye adali wonena zoona zokhazokha, Mneneri.
Las Exégesis Árabes:
وَرَفَعۡنَٰهُ مَكَانًا عَلِيًّا
Ndipo tidamunyamula (kumuika pa) malo apamwamba.
Las Exégesis Árabes:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ أَنۡعَمَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِم مِّنَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ مِن ذُرِّيَّةِ ءَادَمَ وَمِمَّنۡ حَمَلۡنَا مَعَ نُوحٖ وَمِن ذُرِّيَّةِ إِبۡرَٰهِيمَ وَإِسۡرَٰٓءِيلَ وَمِمَّنۡ هَدَيۡنَا وَٱجۡتَبَيۡنَآۚ إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُ ٱلرَّحۡمَٰنِ خَرُّواْۤ سُجَّدٗاۤ وَبُكِيّٗا۩
Iwowo ndi omwe adawadalitsa Allah, mwa aneneri mu ana a Adam, ndi (m’mbumba ya) amene tidawatenga pamodzi ndi Nuh (m’chombo), ndi m’mbumba ya Ibrahim ndi Israyeli, ndi amene tidawaongola ndi kuwasankha. Ndipo zikawerengedwa kwa iwo Ayah za (Allah) Mwini chifundo chambiri, amagwa ndi kulambira uku akulira.
Las Exégesis Árabes:
۞ فَخَلَفَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡ خَلۡفٌ أَضَاعُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَٱتَّبَعُواْ ٱلشَّهَوَٰتِۖ فَسَوۡفَ يَلۡقَوۡنَ غَيًّا
Koma pambuyo pa iwo padadza anthu oipa. Adasokoneza Swala (adasiya kupemphera) natsatira zilakolako zoipa; choncho adzakumana ndi chilango choipa.
Las Exégesis Árabes:
إِلَّا مَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحٗا فَأُوْلَٰٓئِكَ يَدۡخُلُونَ ٱلۡجَنَّةَ وَلَا يُظۡلَمُونَ شَيۡـٔٗا
Kupatula amene ati alape ndikukhulupirira ndikuchita zabwino; iwowo adzalowa ku Munda wamtendere ndipo sadzachitidwa chinyengo pa chilichonse.
Las Exégesis Árabes:
جَنَّٰتِ عَدۡنٍ ٱلَّتِي وَعَدَ ٱلرَّحۡمَٰنُ عِبَادَهُۥ بِٱلۡغَيۡبِۚ إِنَّهُۥ كَانَ وَعۡدُهُۥ مَأۡتِيّٗا
Munda wamuyaya umene (Allah) Wachifundo chambiri walonjeza akapolo Ake mobisika, ndithu lonjezo Lake ndilakudza.
Las Exégesis Árabes:
لَّا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوًا إِلَّا سَلَٰمٗاۖ وَلَهُمۡ رِزۡقُهُمۡ فِيهَا بُكۡرَةٗ وَعَشِيّٗا
Sakamva m’menemo mawu achibwana, koma mawu a mtendere; ndipo akapeza rizq (chakudya) lawo m’menemo m’mawa ndi madzulo.
Las Exégesis Árabes:
تِلۡكَ ٱلۡجَنَّةُ ٱلَّتِي نُورِثُ مِنۡ عِبَادِنَا مَن كَانَ تَقِيّٗا
Umenewo ndiwo Munda wamtendere umene tikawapatsa ena mwa akapolo athu omwe adali oopa Allah.
Las Exégesis Árabes:
وَمَا نَتَنَزَّلُ إِلَّا بِأَمۡرِ رَبِّكَۖ لَهُۥ مَا بَيۡنَ أَيۡدِينَا وَمَا خَلۡفَنَا وَمَا بَيۡنَ ذَٰلِكَۚ وَمَا كَانَ رَبُّكَ نَسِيّٗا
(Mtumiki adapempha Gabriel kuti akhale akum’bwerera pafupipafupi. Ndipo Gabriel adamuuza kuti): “Ndipo sitimatsika koma mwa lamulo la Mbuye wako. Zapatsogolo pathu ndi zapambuyo pathu ndi zapakati pa zimenezi zonse Nzake (akuzidziwa bwinobwino). Ndipo Mbuye wako sali woiwala.”
Las Exégesis Árabes:
رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا فَٱعۡبُدۡهُ وَٱصۡطَبِرۡ لِعِبَٰدَتِهِۦۚ هَلۡ تَعۡلَمُ لَهُۥ سَمِيّٗا
“Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pa izo: Choncho mpembedze Iye basi. Ndipo pitiriza ndikupirira popembedza Iye. Kodi ukumudziwa (wina) yemwe ali wofanana Naye (Allah)?”
Las Exégesis Árabes:
وَيَقُولُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَءِذَا مَا مِتُّ لَسَوۡفَ أُخۡرَجُ حَيًّا
Ndipo munthu (wokanira) amanena: “Kodi ndikadzafa nzoonadi kuti Ndidzatulutsidwa (m’manda) nkukhala wamoyo?”
Las Exégesis Árabes:
أَوَلَا يَذۡكُرُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَنَّا خَلَقۡنَٰهُ مِن قَبۡلُ وَلَمۡ يَكُ شَيۡـٔٗا
Kodi munthu sakumbukira kuti tidamulenga kale pomwe sadali chilichonse?
Las Exégesis Árabes:
فَوَرَبِّكَ لَنَحۡشُرَنَّهُمۡ وَٱلشَّيَٰطِينَ ثُمَّ لَنُحۡضِرَنَّهُمۡ حَوۡلَ جَهَنَّمَ جِثِيّٗا
Choncho ndikulumbira Mbuye wako, ndithu tidzawasonkhanitsa iwo pamodzi ndi asatana; ndipo tidzawafikitsa m’mphepete mwa Jahannam uku atagwada.
Las Exégesis Árabes:
ثُمَّ لَنَنزِعَنَّ مِن كُلِّ شِيعَةٍ أَيُّهُمۡ أَشَدُّ عَلَى ٱلرَّحۡمَٰنِ عِتِيّٗا
Kenako, m’gulu lililonse tidzachotsamo yemwe adali wopyola malire polakwira (Allah) Mwini chifundo chambiri.
Las Exégesis Árabes:
ثُمَّ لَنَحۡنُ أَعۡلَمُ بِٱلَّذِينَ هُمۡ أَوۡلَىٰ بِهَا صِلِيّٗا
Ndipo Ife tikuwazindikira kwambiri amene ali oyenera kulowa m’Moto.
Las Exégesis Árabes:
وَإِن مِّنكُمۡ إِلَّا وَارِدُهَاۚ كَانَ عَلَىٰ رَبِّكَ حَتۡمٗا مَّقۡضِيّٗا
Ndipo palibe aliyense mwa inu koma adzaifika (Jahannamyo). Ndithu ili ndi lamulo la Mbuye wako lomwe lidalamulidwa kale.
Las Exégesis Árabes:
ثُمَّ نُنَجِّي ٱلَّذِينَ ٱتَّقَواْ وَّنَذَرُ ٱلظَّٰلِمِينَ فِيهَا جِثِيّٗا
Ndipo kenako tidzawapulumutsa amene ankaopa Allah, ndipo osalungama tidzawasiya m’menemo atagwada.
Las Exégesis Árabes:
وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُنَا بَيِّنَٰتٖ قَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَيُّ ٱلۡفَرِيقَيۡنِ خَيۡرٞ مَّقَامٗا وَأَحۡسَنُ نَدِيّٗا
Ndipo Ayah Zathu zomveka bwino zikawerengedwa kwa iwo, omwe sadakhulupirire amanena kwa omwe akhulupirira: “Ndi gulu liti pa magulu awiri awa, (lanu ndi lathu) lomwe lili ndi pokhala pabwino ndikukhalanso ndi anthu olemekezeka?”
Las Exégesis Árabes:
وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّن قَرۡنٍ هُمۡ أَحۡسَنُ أَثَٰثٗا وَرِءۡيٗا
Ndipo mibadwo yambiri tidaiononga patsogolo pawo, yomwe idali ndi ziwiya zabwino ndi maonekedwe abwino.
Las Exégesis Árabes:
قُلۡ مَن كَانَ فِي ٱلضَّلَٰلَةِ فَلۡيَمۡدُدۡ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ مَدًّاۚ حَتَّىٰٓ إِذَا رَأَوۡاْ مَا يُوعَدُونَ إِمَّا ٱلۡعَذَابَ وَإِمَّا ٱلسَّاعَةَ فَسَيَعۡلَمُونَ مَنۡ هُوَ شَرّٞ مَّكَانٗا وَأَضۡعَفُ جُندٗا
Nena: “Amene ali mkusokera, (Allah) Mwini chifundo chambiri amuonjezera nthawi yamoyo kufikira azione zomwe akulonjezedwa - kapena chilango kapena kudza nthawi (ya Qiyâma) - pamenepo ndipomwe adzadziwa kuti ndani mwini kukhala pamalo poipa, ndi mwini wa ankhondo ofooka (iwo kapena Asilamu)?”
Las Exégesis Árabes:
وَيَزِيدُ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ٱهۡتَدَوۡاْ هُدٗىۗ وَٱلۡبَٰقِيَٰتُ ٱلصَّٰلِحَٰتُ خَيۡرٌ عِندَ رَبِّكَ ثَوَابٗا وَخَيۡرٞ مَّرَدًّا
Ndipo Allah amawaonjezera chiongoko amene aongoka. Ndipo zochita zabwino zonkerankera (mpaka tsiku lachimaliziro), ndizo zili zabwino kwa Mbuye wako monga mphoto, ndiponso ndiko kobwerera kwabwino, (osati za mdziko zomwe anthu osalungama akunyadira).
Las Exégesis Árabes:
أَفَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي كَفَرَ بِـَٔايَٰتِنَا وَقَالَ لَأُوتَيَنَّ مَالٗا وَوَلَدًا
Kodi wamuona yemwe watsutsa Ayah Zathu ndikunena kuti: “Ndithu ndidzapatsidwa chuma ndi ana (pa tsiku lachimaliziro monga momwe andipatsira pano pa dziko?)”
Las Exégesis Árabes:
أَطَّلَعَ ٱلۡغَيۡبَ أَمِ ٱتَّخَذَ عِندَ ٱلرَّحۡمَٰنِ عَهۡدٗا
Kodi adadziwa zamseri, kapena adalandira lonjezo kwa Allah mwini chifundo Chambiri (kotero kuti ali ndi chikhulupiliro pa zimene akunenazo)?.
Las Exégesis Árabes:
كَلَّاۚ سَنَكۡتُبُ مَا يَقُولُ وَنَمُدُّ لَهُۥ مِنَ ٱلۡعَذَابِ مَدّٗا
Sichoncho, ndithu tikulemba zonse zomwe akunena, ndipo tidzamuonjezera nyengo yotalika m’chilango.
Las Exégesis Árabes:
وَنَرِثُهُۥ مَا يَقُولُ وَيَأۡتِينَا فَرۡدٗا
Ndipo tidzamlowa mmalo zimene akunenazi, (chuma ndi anawo), nadzatidzera ali yekhayekha (wopanda chuma ndi zonse zomwe ankanyadira).
Las Exégesis Árabes:
وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ ءَالِهَةٗ لِّيَكُونُواْ لَهُمۡ عِزّٗا
Eti adzipangira milungu ina m’malo mwa Allah kuti milunguyo iwapatse mphamvu (ndi ulemelero).
Las Exégesis Árabes:
كَلَّاۚ سَيَكۡفُرُونَ بِعِبَادَتِهِمۡ وَيَكُونُونَ عَلَيۡهِمۡ ضِدًّا
Iyayi! Idzawakanira mapemphero awo ndikuwaukira.
Las Exégesis Árabes:
أَلَمۡ تَرَ أَنَّآ أَرۡسَلۡنَا ٱلشَّيَٰطِينَ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ تَؤُزُّهُمۡ أَزّٗا
Kodi suona kuti Ife timawatuma asatana kwa osakhulupirira ndipo akuwakhwirizira kwambiri (kuchita zoipa)?
Las Exégesis Árabes:
فَلَا تَعۡجَلۡ عَلَيۡهِمۡۖ إِنَّمَا نَعُدُّ لَهُمۡ عَدّٗا
Choncho, usawachitire changu (kuti alangidwe tsopano), ndithu Ife tikuwawerengera chiwerengero (cha masiku awo; masiku akakwana, tiwalanga).
Las Exégesis Árabes:
يَوۡمَ نَحۡشُرُ ٱلۡمُتَّقِينَ إِلَى ٱلرَّحۡمَٰنِ وَفۡدٗا
(Kumbukira iwe Mtumiki) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa oopa (Allah) kunka nawo kwa Mwini chifundo Chambiri ali m’magulumagulu monga nthumwi (Zake kuti apatsidwe ulemu).
Las Exégesis Árabes:
وَنَسُوقُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ إِلَىٰ جَهَنَّمَ وِرۡدٗا
Ndipo oipa tidzawakusa kunka nawo ku Moto ali ndi ludzu lalikulu monga momwe ziweto zimathamangira kupita kumadzi zikakhala ndi ludzu lalikulu).
Las Exégesis Árabes:
لَّا يَمۡلِكُونَ ٱلشَّفَٰعَةَ إِلَّا مَنِ ٱتَّخَذَ عِندَ ٱلرَّحۡمَٰنِ عَهۡدٗا
Sadzakhala ndi mphamvu yoombolera (ena) koma kupatula omwe adagwiritsa lonjezo la (Allah) Mwini chifundo chambiri.
Las Exégesis Árabes:
وَقَالُواْ ٱتَّخَذَ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَلَدٗا
Ndipo (osakhulupirira omwe ndi Ayuda ndi Akhirisitu) akuti: “(Allah) Mwini chifundo chambiri wadzipangira mwana!”
Las Exégesis Árabes:
لَّقَدۡ جِئۡتُمۡ شَيۡـًٔا إِدّٗا
Ndithu mwadza ndi chinthu choipitsitsa (pazimene mukunenazi).
Las Exégesis Árabes:
تَكَادُ ٱلسَّمَٰوَٰتُ يَتَفَطَّرۡنَ مِنۡهُ وَتَنشَقُّ ٱلۡأَرۡضُ وَتَخِرُّ ٱلۡجِبَالُ هَدًّا
Thambo layandikira kusweka ndi mawuwo, ndipo nthaka kuphwasuka, ndipo mapiri kugwa ndikudukaduka.
Las Exégesis Árabes:
أَن دَعَوۡاْ لِلرَّحۡمَٰنِ وَلَدٗا
Chifukwa chakumunamizira (Allah) Mwini chifundo chambiri kuti ali ndi mwana.
Las Exégesis Árabes:
وَمَا يَنۢبَغِي لِلرَّحۡمَٰنِ أَن يَتَّخِذَ وَلَدًا
Ndipo nkosayenera kwa (Allah) Mwini Chifundo chambiri kudzipangira mwana.
Las Exégesis Árabes:
إِن كُلُّ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ إِلَّآ ءَاتِي ٱلرَّحۡمَٰنِ عَبۡدٗا
Palibe aliyense yemwe ali kumwamba ndi pansi koma adzadza kwa (Allah) Mwini Chifundo chambiri ali kapolo (Wake).
Las Exégesis Árabes:
لَّقَدۡ أَحۡصَىٰهُمۡ وَعَدَّهُمۡ عَدّٗا
Ndithu (Allah) wawadziwa mokwanira ndipo adzawawerenga aliyense payekhapayekha.
Las Exégesis Árabes:
وَكُلُّهُمۡ ءَاتِيهِ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فَرۡدًا
Ndipo, aliyense wa iwo adzadza kwa Iye (Allah) ali payekhapayekha.
Las Exégesis Árabes:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ سَيَجۡعَلُ لَهُمُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وُدّٗا
Ndithu amene akhulupirira ndikumachita zabwino, (Allah) Mwini chifundo chambiri adzaika chikondi pakati pawo.
Las Exégesis Árabes:
فَإِنَّمَا يَسَّرۡنَٰهُ بِلِسَانِكَ لِتُبَشِّرَ بِهِ ٱلۡمُتَّقِينَ وَتُنذِرَ بِهِۦ قَوۡمٗا لُّدّٗا
Ndithu taifewetsa (Qur’an) m’chiyankhulo chako kuti ndi iyo uwawuze nkhani zabwino oopa Allah ndipo ndi iyo uwachenjeze anthu amakani.
Las Exégesis Árabes:
وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّن قَرۡنٍ هَلۡ تُحِسُّ مِنۡهُم مِّنۡ أَحَدٍ أَوۡ تَسۡمَعُ لَهُمۡ رِكۡزَۢا
Kodi ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Kodi ukumuona mmodzi wa iwo, kapena ukumva mgugu wawo?
Las Exégesis Árabes:
 
Traducción de significados Capítulo: Sura Maryam
Índice de Capítulos Número de página
 
Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa - Índice de traducciones

Traducción del significado del Corán al chewa por Khaled Ibrahim Betala (ed.2020)

Cerrar