Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa * - Lexique des traductions


Traduction des sens Sourate: AL-MOUMTAHANAH   Verset:

AL-MOUMTAHANAH

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَتَّخِذُواْ عَدُوِّي وَعَدُوَّكُمۡ أَوۡلِيَآءَ تُلۡقُونَ إِلَيۡهِم بِٱلۡمَوَدَّةِ وَقَدۡ كَفَرُواْ بِمَا جَآءَكُم مِّنَ ٱلۡحَقِّ يُخۡرِجُونَ ٱلرَّسُولَ وَإِيَّاكُمۡ أَن تُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ رَبِّكُمۡ إِن كُنتُمۡ خَرَجۡتُمۡ جِهَٰدٗا فِي سَبِيلِي وَٱبۡتِغَآءَ مَرۡضَاتِيۚ تُسِرُّونَ إِلَيۡهِم بِٱلۡمَوَدَّةِ وَأَنَا۠ أَعۡلَمُ بِمَآ أَخۡفَيۡتُمۡ وَمَآ أَعۡلَنتُمۡۚ وَمَن يَفۡعَلۡهُ مِنكُمۡ فَقَدۡ ضَلَّ سَوَآءَ ٱلسَّبِيلِ
E inu amene mwakhulupirira! Musawachite adani Anga ndi adani anu kukhala athandizi anu ndi kumawauza (nkhani zanu) mwa chikondi, pomwe iwo sanakhulupirire choonadi chimene chakudzerani. Adamtulutsa Mtumiki ndi inu nomwe (m’nyumba zanu) chifukwa chakuti mumakhulupirira Allah, Mbuye wanu, (palibe cholakwa chilichonse chimene mudawachitira,) ngati mwatuluka kukachita Jihâd pa njira Yanga ndi kufunafuna chikondi Changa (musapalane nawo ubwenzi). Mukuwatumizira chinsinsi (chanu cha nkhondo) chifukwa cha chikondi (chanu ndi iwo); (musachitenso zimenezi) pomwe Ine ndikudziwa zimene inu mukubisa ndi zimenene mukuzisonyeza (poyera); amene akuchita zimenezi mwa inu, ndiye kuti wataya njira yoongoka.[355]
[355] Inu Asilamu amene mwakhulupilira mwa Allah ndi Mthenga Wake (s.a.w) musawachite makafiri amene ndi adani anga ndiponso adani anu kukhala okondedwa anu ndi abwenzi anu. Chisonyezo cha chikhulupiliro kwa Msilamu ndiko kuwada adani a Allah, osati kuwakonda ndi kupalana nawo ubwenzi.
Les exégèses en arabe:
إِن يَثۡقَفُوكُمۡ يَكُونُواْ لَكُمۡ أَعۡدَآءٗ وَيَبۡسُطُوٓاْ إِلَيۡكُمۡ أَيۡدِيَهُمۡ وَأَلۡسِنَتَهُم بِٱلسُّوٓءِ وَوَدُّواْ لَوۡ تَكۡفُرُونَ
Akakumana nanu (pankhondo) akukhala adani anu ndipo akukutambasulirani manja ndi malirime awo moipa (pokumenyani ndi kukutukwanani); ndipo akulakalaka mukadakhala osakhulupirira (kuti mufanane nawo).
Les exégèses en arabe:
لَن تَنفَعَكُمۡ أَرۡحَامُكُمۡ وَلَآ أَوۡلَٰدُكُمۡۚ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ يَفۡصِلُ بَيۡنَكُمۡۚ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٞ
Abale anu ngakhale ana anu sadzakuthandizani tsiku la Qiyâma (Allah) adzaweruza (pakati panu), ndipo Allah akuona zimene mukuchita.
Les exégèses en arabe:
قَدۡ كَانَتۡ لَكُمۡ أُسۡوَةٌ حَسَنَةٞ فِيٓ إِبۡرَٰهِيمَ وَٱلَّذِينَ مَعَهُۥٓ إِذۡ قَالُواْ لِقَوۡمِهِمۡ إِنَّا بُرَءَٰٓؤُاْ مِنكُمۡ وَمِمَّا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ كَفَرۡنَا بِكُمۡ وَبَدَا بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكُمُ ٱلۡعَدَٰوَةُ وَٱلۡبَغۡضَآءُ أَبَدًا حَتَّىٰ تُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ وَحۡدَهُۥٓ إِلَّا قَوۡلَ إِبۡرَٰهِيمَ لِأَبِيهِ لَأَسۡتَغۡفِرَنَّ لَكَ وَمَآ أَمۡلِكُ لَكَ مِنَ ٱللَّهِ مِن شَيۡءٖۖ رَّبَّنَا عَلَيۡكَ تَوَكَّلۡنَا وَإِلَيۡكَ أَنَبۡنَا وَإِلَيۡكَ ٱلۡمَصِيرُ
Ndithu inu muli ndi chitsanzo chabwino cha (mtumiki) Ibrahim ndi amene adali naye pamene adawauza anzawo (osakhulupirira kuti): “Ndithu ife tapatukana nanu pamodzi ndi milungu yanu imene mukuipembedza kusiya Allah; takukanani, ndipo chidani ndi kusakondana zaonekera poyera pakati pa inu ndi ife mpaka muyaya, kufikira, mutakhulupirira mwa Allah mmodzi (inunso chitani chimodzimodzi, muwakane abale anu amene ali akafiri), kupatula mawu a Ibrahim pamene adamuuza tate wake (kuti): “Ndithu ndikupempherani chikhululuko. Palibe chimene ndingakutetezereni nacho kwa Allah (ngati mutamuphatikiza Allah ndi zina.”) E Mbuye wathu! Kwa Inu tatsamira. Ndipo kwa Inu tatembenukira ndiponso kobwerera nkwa Inu.[356]
[356] Apa akutiuza kuti titsanzire zimene adachita tate wa Shariya amene ndi Ibrahima pamodzi ndi omtsatira ake pamene adadzipatula kwa makolo awo ndi abale awo omwe adali m’chipembedzo chonama. Msilamu amkonde Allah kuposa tate wake, ana ake, mkazi wake, chuma chake ndi thupi lake limene. Atsogoze zofuna za Allah asanachite china chilichonse. Akatero akhala kuti wakhulupilira Allah mwachoonadi.
Les exégèses en arabe:
رَبَّنَا لَا تَجۡعَلۡنَا فِتۡنَةٗ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ وَٱغۡفِرۡ لَنَا رَبَّنَآۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
E Mbuye wathu! Musatichite kukhala mayeso kwa amene sadakhulupirire, tikhululukireni Mbuye wathu! Ndithu Inu, Ndinu Amphamvu zopambana ndiponso Anzeru zakuya.
Les exégèses en arabe:
لَقَدۡ كَانَ لَكُمۡ فِيهِمۡ أُسۡوَةٌ حَسَنَةٞ لِّمَن كَانَ يَرۡجُواْ ٱللَّهَ وَٱلۡيَوۡمَ ٱلۡأٓخِرَۚ وَمَن يَتَوَلَّ فَإِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡغَنِيُّ ٱلۡحَمِيدُ
Ndithu muli nacho inu kwa iwo (Ibrahim ndi omtsatira) chitsanzo chabwino kwa amene akuyembekezera kukumana ndi Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amene anyozere ndithu Allah Ngolemera (ndiponso) Ngotamandika.
Les exégèses en arabe:
۞ عَسَى ٱللَّهُ أَن يَجۡعَلَ بَيۡنَكُمۡ وَبَيۡنَ ٱلَّذِينَ عَادَيۡتُم مِّنۡهُم مَّوَدَّةٗۚ وَٱللَّهُ قَدِيرٞۚ وَٱللَّهُ غَفُورٞ رَّحِيمٞ
Mwina Allah angaike chikondi pakati panu ndi ena mwa amene mumawada (poiongolera mitima yawo kukhulupirira mwa Allah), ndipo Allah Ngokhoza chilichonse ndiponso Allah Ngokhululuka; Ngwachisoni chosatha.
Les exégèses en arabe:
لَّا يَنۡهَىٰكُمُ ٱللَّهُ عَنِ ٱلَّذِينَ لَمۡ يُقَٰتِلُوكُمۡ فِي ٱلدِّينِ وَلَمۡ يُخۡرِجُوكُم مِّن دِيَٰرِكُمۡ أَن تَبَرُّوهُمۡ وَتُقۡسِطُوٓاْ إِلَيۡهِمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلۡمُقۡسِطِينَ
Allah sakukuletsani kuwachitira zabwino ndi chilungamo amene sadakumenyeni ndi kukutulutsani m’nyumba zanu chifukwa cha chipembedzo. Ndithu Allah amakonda achilungamo.[357]
[357] Allah sakutiletsa kuwachitira zabwino anthu amene sali Asilamu, mmalo mwake akutilamula kuti tiwachitire zabwino ngati alibe upandu uliwonse ndi Asilamu.
Les exégèses en arabe:
إِنَّمَا يَنۡهَىٰكُمُ ٱللَّهُ عَنِ ٱلَّذِينَ قَٰتَلُوكُمۡ فِي ٱلدِّينِ وَأَخۡرَجُوكُم مِّن دِيَٰرِكُمۡ وَظَٰهَرُواْ عَلَىٰٓ إِخۡرَاجِكُمۡ أَن تَوَلَّوۡهُمۡۚ وَمَن يَتَوَلَّهُمۡ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ
Allah akukuletsani kugwirizana nawo amene adakumenyani chifukwa cha chipembedzo ndi kukutulutsani m’nyumba zanu, ndi amene adathandiza kukutulutsani. Amene ati agwirizane nawo iwowo ndiwo achinyengo.
Les exégèses en arabe:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا جَآءَكُمُ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتُ مُهَٰجِرَٰتٖ فَٱمۡتَحِنُوهُنَّۖ ٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِإِيمَٰنِهِنَّۖ فَإِنۡ عَلِمۡتُمُوهُنَّ مُؤۡمِنَٰتٖ فَلَا تَرۡجِعُوهُنَّ إِلَى ٱلۡكُفَّارِۖ لَا هُنَّ حِلّٞ لَّهُمۡ وَلَا هُمۡ يَحِلُّونَ لَهُنَّۖ وَءَاتُوهُم مَّآ أَنفَقُواْۚ وَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ أَن تَنكِحُوهُنَّ إِذَآ ءَاتَيۡتُمُوهُنَّ أُجُورَهُنَّۚ وَلَا تُمۡسِكُواْ بِعِصَمِ ٱلۡكَوَافِرِ وَسۡـَٔلُواْ مَآ أَنفَقۡتُمۡ وَلۡيَسۡـَٔلُواْ مَآ أَنفَقُواْۚ ذَٰلِكُمۡ حُكۡمُ ٱللَّهِ يَحۡكُمُ بَيۡنَكُمۡۖ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٞ
E inu amene mwakhulupirira! Akakudzerani okhulupirira aakazi osamuka, ayeseni mayeso (kuti mudziwe chikhulupiliro chawo); Allah ali wodziwa kwambiri za chikhulupiliro chawo; ngati mutawadziwa kuti ndiokhulupirira musawabwezere kwa osakhulupirira. Akaziwo saloledwa kukwatiwa ndi osakhulupirira, iwonso saloledwa kuwakwatira. Abwezereni chiwongo chimene adapereka amuna osakhulupirirawo. Ndipo palibe tchimo kwa inu kuwakwatira, (ngakhale adasiya amuna awo achikafiri (ku Makka) ngati muwapatsa chiwongo chawo. Musakakamire maukwati ndi akazi achikafiri (osakhulupirira amene adatsalira ku Makka). Itanitsani zimene mudapereka kwa akazi anu (achikafiriwo), naonso Akafiri aitanitse zimene adapereka (kwa akazi awo akalowa m’Chisilamu). Limeneli ndi lamulo la Allah limene akulamula pakati panu. Allah ndiwodziwa kwambiri ndiponso Ngwanzeru (poika malamulo).
Les exégèses en arabe:
وَإِن فَاتَكُمۡ شَيۡءٞ مِّنۡ أَزۡوَٰجِكُمۡ إِلَى ٱلۡكُفَّارِ فَعَاقَبۡتُمۡ فَـَٔاتُواْ ٱلَّذِينَ ذَهَبَتۡ أَزۡوَٰجُهُم مِّثۡلَ مَآ أَنفَقُواْۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ ٱلَّذِيٓ أَنتُم بِهِۦ مُؤۡمِنُونَ
Ndipo ngati mmodzi mwa akazi anu atakuthawani kupita kwa Akafiri, ndipo (mwadzidzidzi) mwakachita nkhondo (ndi kupeza chuma chosiya adani anu), apatseni amene awathawa akazi awo chofanana ndi chimene adapereka (pokwatira). Ndipo muopeni Allah amene inu mukumkhulupirira.
Les exégèses en arabe:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ إِذَا جَآءَكَ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتُ يُبَايِعۡنَكَ عَلَىٰٓ أَن لَّا يُشۡرِكۡنَ بِٱللَّهِ شَيۡـٔٗا وَلَا يَسۡرِقۡنَ وَلَا يَزۡنِينَ وَلَا يَقۡتُلۡنَ أَوۡلَٰدَهُنَّ وَلَا يَأۡتِينَ بِبُهۡتَٰنٖ يَفۡتَرِينَهُۥ بَيۡنَ أَيۡدِيهِنَّ وَأَرۡجُلِهِنَّ وَلَا يَعۡصِينَكَ فِي مَعۡرُوفٖ فَبَايِعۡهُنَّ وَٱسۡتَغۡفِرۡ لَهُنَّ ٱللَّهَۚ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٞ
E iwe Mtumiki! Akakudzera akazi okhulupirira kudzakulonjeza kuti samphatikiza Allah ndi chilichonse ndi kuti saziba, sazichita chiwerewere, sazipha ana awo ndi kuti sazinena bodza lamkunkhuniza, lomwe akulipeka pakati pa manja awo ndi miyendo yawo (pompachika mwana kwa wina amene sali tate wake), ndi kutinso sadzakunyoza pa chinthu chabwino (chimene ukuwaitanira), landira lonjezo lawolo, ndipo apemphere chikhululuko kwa Allah. Ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni.
Les exégèses en arabe:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَتَوَلَّوۡاْ قَوۡمًا غَضِبَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمۡ قَدۡ يَئِسُواْ مِنَ ٱلۡأٓخِرَةِ كَمَا يَئِسَ ٱلۡكُفَّارُ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلۡقُبُورِ
E inu amene mwakhulupirira! Musagwirizane ndi anthu amene Allah wawakwiyira. Ndithu iwo ataya mtima wopeza mphoto tsiku lachimaliziro (chifukwa cha machimo awo ochuluka) monga momwe atayira mtima akafiri za kuuka kwa amene ali m’manda.
Les exégèses en arabe:
 
Traduction des sens Sourate: AL-MOUMTAHANAH
Lexique des sourates Numéro de la page
 
Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa - Lexique des traductions

Traduction des sens du noble Coran en langue chewa, par Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ (édition 2020).

Fermeture