Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa * - Lexique des traductions


Traduction des sens Sourate: AZ-ZALZALAH   Verset:

AZ-ZALZALAH

إِذَا زُلۡزِلَتِ ٱلۡأَرۡضُ زِلۡزَالَهَا
Likadzagwedezedwa dziko lapansi kugwedezeka kwake kwamphamvu,
Les exégèses en arabe:
وَأَخۡرَجَتِ ٱلۡأَرۡضُ أَثۡقَالَهَا
Ndipo nthaka idzatulutsa mitolo yake (zinthu zomwe zidali mkati mwake, monga akufa ndi miyala ya mtengo wapatali),
Les exégèses en arabe:
وَقَالَ ٱلۡإِنسَٰنُ مَا لَهَا
Ndipo munthu adzanena (mwa mantha, ndikudabwa nthawi imeneyo). Ha! Yatani nthaka, (kodi Qiyâma yafika)?
Les exégèses en arabe:
يَوۡمَئِذٖ تُحَدِّثُ أَخۡبَارَهَا
Tsiku limenelo idzanena nkhani zake zonse, (zabwino kapena zoipa).[470]
[470] Idzanena nthaka pa tsiku limenelo pamene Allah adzaiuza kuti inene monga momwe amazinenetsera zinthu zimene chikhalire sizilankhula, pakuti Allah ndi Wamphamvu zonse. Kapena m’mene iti idzakhalire nthaka kudzakwanira munthu kudziwa kuti ikutanthauza chakuti, popanda kutulutsa mawu monga momwe timadziwira munthu wosangalala ndi wachisoni; wanjala ndi wokhuta popanda kuyankhula. Nkhani zomwe idzafotokoza nthaka pa tsiku limenelo, monga momwe adanenera Mneneri Muhammad (s.a.w), ndi izi:- Tsiku la chiweruziro nthaka idzamuikira umboni munthu aliyense kapena m’badwo uliwonse pa chimene adachita pamwamba pake (pamwamba pa nthaka). Limeneli ndilo tanthauzo la mawu aja oti “ Nthaka idzanena nkhani zake.”
Les exégèses en arabe:
بِأَنَّ رَبَّكَ أَوۡحَىٰ لَهَا
Pakuti Mbuye wako adzailamula kutero (kuti igwedezeke ndikunena zimene zinkachitika pamwamba pake).
Les exégèses en arabe:
يَوۡمَئِذٖ يَصۡدُرُ ٱلنَّاسُ أَشۡتَاتٗا لِّيُرَوۡاْ أَعۡمَٰلَهُمۡ
Tsiku limenelo anthu adzachoka (m’manda) ali m’magulu obalalika kuti akasonyezedwe ntchito zawo (ndikudziwa chiwerengero chawo chimene chili kwa Allah).
Les exégèses en arabe:
فَمَن يَعۡمَلۡ مِثۡقَالَ ذَرَّةٍ خَيۡرٗا يَرَهُۥ
Choncho, amene angachite chabwino cholemera ngati kanjere kakang’ono, adzaona malipiro ake.[471]
[471] (Ndime 7-8) Ma Ayah awiriwa akutidziwitsa kuti munthu adzalipidwa pa chilichonse chimene akuchita, chabwino kapena choipa, ngakhale chikhale chochepa monga kulemera kwa kanjere kochepa kwambiri.
Les exégèses en arabe:
وَمَن يَعۡمَلۡ مِثۡقَالَ ذَرَّةٖ شَرّٗا يَرَهُۥ
Ndipo amene angachite choipa cholemera ngati kanjere kakang’ono, adzaona malipiro ake. (Allah sachitira chinyengo aliyense).
Les exégèses en arabe:
 
Traduction des sens Sourate: AZ-ZALZALAH
Lexique des sourates Numéro de la page
 
Traduction des sens du Noble Coran - Traduction en chewa - Lexique des traductions

Traduction des sens du noble Coran en langue chewa, par Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ (édition 2020).

Fermeture