Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fasaara da Yaren Pashto * - Teburin Bayani kan wasu Fassarori


Fassarar Ma'anoni Sura: Suratu Houd   Aya:

Suratu Houd

الٓرۚ كِتَٰبٌ أُحۡكِمَتۡ ءَايَٰتُهُۥ ثُمَّ فُصِّلَتۡ مِن لَّدُنۡ حَكِيمٍ خَبِيرٍ
Alif-Lam-Ra. Ili ndi buku lomwe ndime zake zakonzedwa bwino ndipo zafotokozedwa mwatsatanetsatane kuchokera kwa Allah Mwini nzeru zakuya Wodziwa chilichonse.
Tafsiran larabci:
أَلَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّا ٱللَّهَۚ إِنَّنِي لَكُم مِّنۡهُ نَذِيرٞ وَبَشِيرٞ
(Wachita zimenezi) kuti musampembedze wina wake koma Allah yekha. Ndithudi ine kwa inu ndimchenjezi wochokera kwa Iye ndiponso wokuuzani nkhani zabwino.
Tafsiran larabci:
وَأَنِ ٱسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّكُمۡ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِ يُمَتِّعۡكُم مَّتَٰعًا حَسَنًا إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗى وَيُؤۡتِ كُلَّ ذِي فَضۡلٖ فَضۡلَهُۥۖ وَإِن تَوَلَّوۡاْ فَإِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ عَذَابَ يَوۡمٖ كَبِيرٍ
Ndikuti mupemphe chikhululuko kwa Mbuye wanu ndipo mulape kwa Iye. Akupatsani chisangalalo chabwino mpakana m’nthawi yoikidwa. Ndipo adzampatsa (tsiku lachimaliziro) aliyense wochita zabwino ubwino wake. Koma, ngati mupotoka ine kwanga nkukuoperani za chilango cha tsiku lalikulu.
Tafsiran larabci:
إِلَى ٱللَّهِ مَرۡجِعُكُمۡۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٌ
Kobwerera kwanu nkwa Allah basi. Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse.
Tafsiran larabci:
أَلَآ إِنَّهُمۡ يَثۡنُونَ صُدُورَهُمۡ لِيَسۡتَخۡفُواْ مِنۡهُۚ أَلَا حِينَ يَسۡتَغۡشُونَ ثِيَابَهُمۡ يَعۡلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعۡلِنُونَۚ إِنَّهُۥ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ
Tamverani! Iwo akubisa zimene zili m’mitima yawo kuti amubise Iye (Allah). Mverani! Ndithudi pamene akuzifunda nsalu zawo Iye akudziwa zimene akuzibisa ndi zimene akuzionetsa. Ndithudi Iye ndiwodziwa za mzifuwa.
Tafsiran larabci:
۞ وَمَا مِن دَآبَّةٖ فِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا عَلَى ٱللَّهِ رِزۡقُهَا وَيَعۡلَمُ مُسۡتَقَرَّهَا وَمُسۡتَوۡدَعَهَاۚ كُلّٞ فِي كِتَٰبٖ مُّبِينٖ
۞ Ndipo palibe nyama iliyonse panthaka koma rizq lake lili kwa Allah; ndipo (Iye) akudziwa mbuto yake yamuyaya ndi mbuto yake yakungodutsapo (yomwe ndi pano padziko lapansi). Zonse zili m’buku lofotokoza chilichonse.[219]
[219] Mawu oti “Riziki lake lili kwa Allah’’ nkuti Allah wapatsa chilichonse mphamvu zofunira riziki lake (zoyendetsa moyo wake). Ndimeyi siitanthauza kuti munthu angokhala popanda kugwira ntchito nayembekezera kuti riziki lichokera kumwamba. Koma munthu agwire ntchito molimbikira kuti apeze chuma cha Allah. Zotere nzimene Qur’an ikutilangiza.
Tafsiran larabci:
وَهُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ وَكَانَ عَرۡشُهُۥ عَلَى ٱلۡمَآءِ لِيَبۡلُوَكُمۡ أَيُّكُمۡ أَحۡسَنُ عَمَلٗاۗ وَلَئِن قُلۡتَ إِنَّكُم مَّبۡعُوثُونَ مِنۢ بَعۡدِ ٱلۡمَوۡتِ لَيَقُولَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٞ مُّبِينٞ
Ndipo Iye ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo Arsh Yake (Mpando Wake wachifumu) idali pa madzi. (Adakulengani) kuti akuyeseni mayeso, ndani mwa inu ali wochita zabwino. Koma ukanena (kwa iwo kuti): “Inu mudzaukitsidwa pambuyo pa imfa,” amene sadakhulupirire akuti: “Izi sikanthu koma ndi matsenga oonekera.”[220]
[220] Kunena kwakuti thambo ndi nthaka zidalengedwa m’masiku asanu ndi limodzi, amene akudziwa za masiku asanu ndi limodziwo momwe adalili ndi Allah yekha. Ndiponso mpandowo sitikudziwa tsatanetsatane wake. Chimene chilipo kwa ife nkukhulupilira basi.
Tafsiran larabci:
وَلَئِنۡ أَخَّرۡنَا عَنۡهُمُ ٱلۡعَذَابَ إِلَىٰٓ أُمَّةٖ مَّعۡدُودَةٖ لَّيَقُولُنَّ مَا يَحۡبِسُهُۥٓۗ أَلَا يَوۡمَ يَأۡتِيهِمۡ لَيۡسَ مَصۡرُوفًا عَنۡهُمۡ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Ndipo ngati titawachedwetsera chilango mpaka m’nthawi yodziwika (ndi kukhazikitsidwa ndi Ife), akunena (mwamwano): “Nchiyani chikumanga chilangocho (kuti chidze)? “Tamverani! Tsiku lomwe chidzawadzera, sichidzachotsedwa kwa iwo ndipo zomwe adali kuzichita mwachibwana zidzawazinga.
Tafsiran larabci:
وَلَئِنۡ أَذَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِنَّا رَحۡمَةٗ ثُمَّ نَزَعۡنَٰهَا مِنۡهُ إِنَّهُۥ لَيَـُٔوسٞ كَفُورٞ
Ndipo munthu tikamulawitsa mtendere wochokera kwa Ife, kenako nkuuchotsa kwa iye, ndithu amakhala wotaya mtima kwambiri ndikukhala wosathokoza.
Tafsiran larabci:
وَلَئِنۡ أَذَقۡنَٰهُ نَعۡمَآءَ بَعۡدَ ضَرَّآءَ مَسَّتۡهُ لَيَقُولَنَّ ذَهَبَ ٱلسَّيِّـَٔاتُ عَنِّيٓۚ إِنَّهُۥ لَفَرِحٞ فَخُورٌ
Koma ngati titamulawitsa mtendere pambuyo pa masautso omwe adamkhudza, amati: “Masautso andichoka,”(ndipo sakhala wotanganidwa ndi ntchito zabwino zosonyeza kuyamika Allah), ndithudi iye amakhala wosangalala, wodzitukumula.
Tafsiran larabci:
إِلَّا ٱلَّذِينَ صَبَرُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُم مَّغۡفِرَةٞ وَأَجۡرٞ كَبِيرٞ
Koma amene apirira ndi kumachita ntchito zabwino, iwowo ndiwo adzapeza chikhululuko ndi malipiro aakulu (kwa Allah).
Tafsiran larabci:
فَلَعَلَّكَ تَارِكُۢ بَعۡضَ مَا يُوحَىٰٓ إِلَيۡكَ وَضَآئِقُۢ بِهِۦ صَدۡرُكَ أَن يَقُولُواْ لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡهِ كَنزٌ أَوۡ جَآءَ مَعَهُۥ مَلَكٌۚ إِنَّمَآ أَنتَ نَذِيرٞۚ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ وَكِيلٌ
Mwina usiya zina mwa zomwe zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndikubanika nazo mchifuwa mwako chifukwa chakuti akunena: “Bwanji sizidatsitsidwe kwa iye nkhokwe za chuma kapena bwanji mngelo osadza pamodzi ndi iye?” Koma ndithu iwe ndiwe mchenjezi basi ndipo Allah ndiye muyang’aniri wa chinthu chilichonse.[221]
[221] Ophatikiza Allah ndi zina zake adali kupereka maganizo kwa Mtumiki akuti ampemphe Allah kuti adzetse milumilu ya chuma kapena amutumizire angelo kuti aziyenda naye limodzi. Ndipo adalinso kumaichitira Qur’an chibwana Mtumiki akawawerengera. Potero Mtumiki (s.a.w) adali kubanika mu mtima mwake akafuna kufikitsa uthenga kwa iwo chifukwa chakuopa kutsutsidwa ndi kumchitira chibwana.
Tafsiran larabci:
أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰهُۖ قُلۡ فَأۡتُواْ بِعَشۡرِ سُوَرٖ مِّثۡلِهِۦ مُفۡتَرَيَٰتٖ وَٱدۡعُواْ مَنِ ٱسۡتَطَعۡتُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Kapena akunena kuti: “Waipeka Qur’an?” Nena: “Tabweretsani sura khumi zopekedwa zomwe zingafanane ndi iyi (Qur’an) ndipo aitaneni amene mungathe (kuwaitana) kupatula Allah. (Adze akuthandizeni kulemba bukulo) ngati mukunena zoona!”
Tafsiran larabci:
فَإِلَّمۡ يَسۡتَجِيبُواْ لَكُمۡ فَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّمَآ أُنزِلَ بِعِلۡمِ ٱللَّهِ وَأَن لَّآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ فَهَلۡ أَنتُم مُّسۡلِمُونَ
“Ngati sakuyankhani, choncho, dziwani kuti yavumbulutsidwa (Qur’aniyo) m’kudziwa kwa Allah, ndikuti kulibe mulungu wina koma Iye. Nanga kodi inu simugonjera (Iye)?”
Tafsiran larabci:
مَن كَانَ يُرِيدُ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا وَزِينَتَهَا نُوَفِّ إِلَيۡهِمۡ أَعۡمَٰلَهُمۡ فِيهَا وَهُمۡ فِيهَا لَا يُبۡخَسُونَ
Amene akufuna moyo wa dziko lapansi ndi zokometsera zake, tiwapatsa pompo pa dziko lapansi (malipiro a) zochita zawo mokwanira, ndipo iwo m’menemo sachepetseredwa chilichonse.
Tafsiran larabci:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ لَيۡسَ لَهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ إِلَّا ٱلنَّارُۖ وَحَبِطَ مَا صَنَعُواْ فِيهَا وَبَٰطِلٞ مَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Iwo ndi omwe sadzakhala ndi kanthu tsiku lachimaliziro koma Moto basi. Ndipo zimene adachita m’menemo zidzaonongeka, ndiponso nzopanda phindu zimene ankachita.
Tafsiran larabci:
أَفَمَن كَانَ عَلَىٰ بَيِّنَةٖ مِّن رَّبِّهِۦ وَيَتۡلُوهُ شَاهِدٞ مِّنۡهُ وَمِن قَبۡلِهِۦ كِتَٰبُ مُوسَىٰٓ إِمَامٗا وَرَحۡمَةًۚ أُوْلَٰٓئِكَ يُؤۡمِنُونَ بِهِۦۚ وَمَن يَكۡفُرۡ بِهِۦ مِنَ ٱلۡأَحۡزَابِ فَٱلنَّارُ مَوۡعِدُهُۥۚ فَلَا تَكُ فِي مِرۡيَةٖ مِّنۡهُۚ إِنَّهُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يُؤۡمِنُونَ
Nanga kodi munthu yemwe ali ndi chisonyezo choonekera chochokera kwa Mbuye wake (kotero kuti m’moyo mwake akuyenda molungama; yemwe ndi mneneri Muhammad {s.a.w}), ndipo Mboni ili naye pamodzi ikumtsata yochokera kwa Iye (Mbuye wake yomwe ndi Qur’an kapena Gaburiel), ndipo patsogolo pake padali buku la Mûsa lomwe lidali chitsanzo chabwino ndi mtendere, (wotereyu angafanane ndi yemwe ali mum’dima wa umbuli yemwenso sadziwa cholinga chakulengedwa kwake?) Awa (amene aongoka) akulikhulupirira (buku ili la Qur’an), ndipo amene ati asalikhulupirire m’magulu (a adani), Moto ndiwo malo awo alonjezo. Choncho, usakhale ndi chipeneko pa ichi; ndithudi ichi ndi choona chochokera kwa Mbuye Wako koma anthu ambiri sakhulupirira.
Tafsiran larabci:
وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ يُعۡرَضُونَ عَلَىٰ رَبِّهِمۡ وَيَقُولُ ٱلۡأَشۡهَٰدُ هَٰٓؤُلَآءِ ٱلَّذِينَ كَذَبُواْ عَلَىٰ رَبِّهِمۡۚ أَلَا لَعۡنَةُ ٱللَّهِ عَلَى ٱلظَّٰلِمِينَ
Ndipo palibe oipitsitsa kuposa yemwe wapeka bodza pakumnamizira Allah (kuti ali ndi mwana ndi athandizi). Iwo adzabweretsedwa kwa Mbuye wawo (tsiku la Qiyâma) ndipo mboni (zomwe ndi angelo) zidzanena: “Awa ndi omwe adapekera Mbuye wawo bodza. Mverani! Tembelero la Allah lili pa ochita zoipa.”
Tafsiran larabci:
ٱلَّذِينَ يَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَيَبۡغُونَهَا عِوَجٗا وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ كَٰفِرُونَ
Omwe akutsekereza anthu kutsata njira ya Allah ndi kufuna kuikhotetsa (njirayo). Ndiponso iwo sakhulupirira za tsiku lachimaliziro.
Tafsiran larabci:
أُوْلَٰٓئِكَ لَمۡ يَكُونُواْ مُعۡجِزِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا كَانَ لَهُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ مِنۡ أَوۡلِيَآءَۘ يُضَٰعَفُ لَهُمُ ٱلۡعَذَابُۚ مَا كَانُواْ يَسۡتَطِيعُونَ ٱلسَّمۡعَ وَمَا كَانُواْ يُبۡصِرُونَ
Iwowa sangathe kumulepheretsa (Allah) m’dziko, ndiponso alibe atetezi pambuyo pa Allah. Chilango chawo chidzaonjezeredwa (chifukwa cha zoipa zawo). Sadali kutha kumva ngakhale kuona (chifukwa cha mkwiyo umene udali m’mitima mwawo wokwiira choonadi).
Tafsiran larabci:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ وَضَلَّ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ
Awa ndi omwe adziononga okha ndipo zomwe adali kuzipeka zidzawataika.
Tafsiran larabci:
لَا جَرَمَ أَنَّهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ هُمُ ٱلۡأَخۡسَرُونَ
Zoonadi, iwo ndiotaika kwakukulu pa tsiku lachimaliziro.
Tafsiran larabci:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَأَخۡبَتُوٓاْ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndi kumadzichepetsa kwa Mbuye wawo, iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere. M’menemo adzakhala nthawi yaitali.
Tafsiran larabci:
۞ مَثَلُ ٱلۡفَرِيقَيۡنِ كَٱلۡأَعۡمَىٰ وَٱلۡأَصَمِّ وَٱلۡبَصِيرِ وَٱلسَّمِيعِۚ هَلۡ يَسۡتَوِيَانِ مَثَلًاۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ
Fanizo la magulu awiriwa (okhulupirira ndi osakhulupirira), lili ngati (munthu) wakhungu ndi gonthi, ndi (munthu) wopenya ndi wakumva. Kodi awiriwa angakhale ofanana (pa chikhalidwe chawo)? Bwanji simukuganiza?[222]
[222] Imam Zamakhashari adati: “Adawafanizira osakhulupilira ngati akhungu ndi agonthi, ndipo okhulupilira ngati openya ndi akumva.”
Tafsiran larabci:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوۡمِهِۦٓ إِنِّي لَكُمۡ نَذِيرٞ مُّبِينٌ
Ndipo ndithu Ife tidamtuma Nuh (monga Mtumiki) kwa anthu ake (kuti akawauze): “Ine kwa inu ndine mchenjezi owonekera poyera.”
Tafsiran larabci:
أَن لَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّا ٱللَّهَۖ إِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ عَذَابَ يَوۡمٍ أَلِيمٖ
“Ndikuti musapembedze aliyense koma Allah basi. Ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lopweteka.”
Tafsiran larabci:
فَقَالَ ٱلۡمَلَأُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن قَوۡمِهِۦ مَا نَرَىٰكَ إِلَّا بَشَرٗا مِّثۡلَنَا وَمَا نَرَىٰكَ ٱتَّبَعَكَ إِلَّا ٱلَّذِينَ هُمۡ أَرَاذِلُنَا بَادِيَ ٱلرَّأۡيِ وَمَا نَرَىٰ لَكُمۡ عَلَيۡنَا مِن فَضۡلِۭ بَلۡ نَظُنُّكُمۡ كَٰذِبِينَ
Ndipo pompo akuluakulu mwa omwe sadakhulupirire mwa anthu ake, adati: “Sitikukuona koma ndiwe munthu monga ife, ndipo sitikukuona koma kuti akutsata anthu a pansi pathu ofooka pa nzeru (omwe sadalingalire mozama za iwe). Ndipo sitikukuonani kuti muli ndi ulemelero ndi ubwino wochuluka kuposa ife. Koma tikukuganizirani kuti ndinu onama.”
Tafsiran larabci:
قَالَ يَٰقَوۡمِ أَرَءَيۡتُمۡ إِن كُنتُ عَلَىٰ بَيِّنَةٖ مِّن رَّبِّي وَءَاتَىٰنِي رَحۡمَةٗ مِّنۡ عِندِهِۦ فَعُمِّيَتۡ عَلَيۡكُمۡ أَنُلۡزِمُكُمُوهَا وَأَنتُمۡ لَهَا كَٰرِهُونَ
(Iye) adati: “E inu anthu anga! Kodi muona bwanji ngati ndili ndi chisonyezo chowonekera chochokera kwa Mbuye wanga ndipo wandipatsa chifundo chochokera kwa Iye (monga uneneri), ndipo chabisika kwa inu, kodi tingakukakamizeni kuvomereza pomwe simukuchifuna?”
Tafsiran larabci:
وَيَٰقَوۡمِ لَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مَالًاۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَى ٱللَّهِۚ وَمَآ أَنَا۠ بِطَارِدِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْۚ إِنَّهُم مُّلَٰقُواْ رَبِّهِمۡ وَلَٰكِنِّيٓ أَرَىٰكُمۡ قَوۡمٗا تَجۡهَلُونَ
“Ndipo E inu anthu anga! Ine sindikukupemphani chuma pa uthengawu. Palibe malipiro anga, koma ali kwa Allah basi. Ndipo ine sindingathamangitse amene akhulupirira (monga momwe mudandipemphera kuti ndiwathamangitse anthu ofooka kuti inu mulowe m’malo mwawo), ndithu iwo adzakumana ndi Mbuye wawo, ndipo ine ndikukuonani monga anthu osazindikira (mbuli).”
Tafsiran larabci:
وَيَٰقَوۡمِ مَن يَنصُرُنِي مِنَ ٱللَّهِ إِن طَرَدتُّهُمۡۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ
“Ndipo E inu anthu anga! Ndani angandithandize kwa Allah ngati nditawathamangitsa? Kodi simuganiza?”
Tafsiran larabci:
وَلَآ أَقُولُ لَكُمۡ عِندِي خَزَآئِنُ ٱللَّهِ وَلَآ أَعۡلَمُ ٱلۡغَيۡبَ وَلَآ أَقُولُ إِنِّي مَلَكٞ وَلَآ أَقُولُ لِلَّذِينَ تَزۡدَرِيٓ أَعۡيُنُكُمۡ لَن يُؤۡتِيَهُمُ ٱللَّهُ خَيۡرًاۖ ٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا فِيٓ أَنفُسِهِمۡ إِنِّيٓ إِذٗا لَّمِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ
“Ndipo ine sindikukuuzani kuti ndili ndi nkhokwe za chuma cha Allah kapena kuti ine ndikudziwa zinthu zamseli, ndiponso sindikunena kuti ndine m’ngelo. Ndiponso sindikunena kwa omwe maso anu akuwachepetsa kuti Allah sadzawapatsa chabwino. Allah akudziwa zam’mitima mwawo. (Ngati nditatero) ndiye kuti ine pamenepo ndili m’gulu la oipa.”
Tafsiran larabci:
قَالُواْ يَٰنُوحُ قَدۡ جَٰدَلۡتَنَا فَأَكۡثَرۡتَ جِدَٰلَنَا فَأۡتِنَا بِمَا تَعِدُنَآ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ
(Iwo) adati: “E iwe Nuh! Watsutsana nafe, ndipo wachulukitsa kutsutsana nafe. Choncho bweretsa kwa ife chimene ukutilonjezacho, ngati ulidi mwa onena zoona.
Tafsiran larabci:
قَالَ إِنَّمَا يَأۡتِيكُم بِهِ ٱللَّهُ إِن شَآءَ وَمَآ أَنتُم بِمُعۡجِزِينَ
Adati: “Ndithu Allah achibweretsa kwa inu ngati afuna, ndipo inu simungathe kumulepheretsa (chimene wafuna).”
Tafsiran larabci:
وَلَا يَنفَعُكُمۡ نُصۡحِيٓ إِنۡ أَرَدتُّ أَنۡ أَنصَحَ لَكُمۡ إِن كَانَ ٱللَّهُ يُرِيدُ أَن يُغۡوِيَكُمۡۚ هُوَ رَبُّكُمۡ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
“Ndipo kulangiza kwanga sikungakuthandizeni ngati ntafuna kukulangizani, ngati Allah akufuna kukulekelerani kusokera. Iye ndiye Mbuye wanu. Ndipo kwa Iye mudzabwezedwa.”
Tafsiran larabci:
أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰهُۖ قُلۡ إِنِ ٱفۡتَرَيۡتُهُۥ فَعَلَيَّ إِجۡرَامِي وَأَنَا۠ بَرِيٓءٞ مِّمَّا تُجۡرِمُونَ
Kapena akunena (osakhulupirira a m’Makka kuti: “Muhammad) waipeka (Qur’an mwa iye yekha)?” Nena: “ngati ndayipeka ndiye kuti machimo ake (akupekawo) ali pa ine. Ndipo ine ndili kutali ndi zoipa zimene mukuchita.”
Tafsiran larabci:
وَأُوحِيَ إِلَىٰ نُوحٍ أَنَّهُۥ لَن يُؤۡمِنَ مِن قَوۡمِكَ إِلَّا مَن قَدۡ ءَامَنَ فَلَا تَبۡتَئِسۡ بِمَا كَانُواْ يَفۡعَلُونَ
Ndipo tidamuululira Nuh kuti: “(Tsopano) sakhulupirira aliyense mwa anthu ako kupatula okhawo akhulupirira kale. Choncho, usadandaule pa zimene adali kuchita.”
Tafsiran larabci:
وَٱصۡنَعِ ٱلۡفُلۡكَ بِأَعۡيُنِنَا وَوَحۡيِنَا وَلَا تُخَٰطِبۡنِي فِي ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ إِنَّهُم مُّغۡرَقُونَ
“Ndipo khoma chombo moyang’aniridwa ndi Ife, ndi ulangizi wathu (satha kukuchitira choipa), ndipo usandiyankhulitse za iwo amene achita zoipa (kuti ndiwakhululukire). Ndithudi, iwo amizidwa.”
Tafsiran larabci:
وَيَصۡنَعُ ٱلۡفُلۡكَ وَكُلَّمَا مَرَّ عَلَيۡهِ مَلَأٞ مِّن قَوۡمِهِۦ سَخِرُواْ مِنۡهُۚ قَالَ إِن تَسۡخَرُواْ مِنَّا فَإِنَّا نَسۡخَرُ مِنكُمۡ كَمَا تَسۡخَرُونَ
Ndipo adayamba kukhoma chombo. Nthawi iliyonse akamdutsa akuluakulu a mwa anthu ake, adali kumchitira chipongwe. Naye ankanena (kuti): “Ngati inu Mukutichitira chipongwe, nafenso tidzakuchitirani chipongwe monga momwe mukutichitira chipongwe.”
Tafsiran larabci:
فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ مَن يَأۡتِيهِ عَذَابٞ يُخۡزِيهِ وَيَحِلُّ عَلَيۡهِ عَذَابٞ مُّقِيمٌ
“Posachedwa mudziwa kuti ndani chimdzere chilango chomuyalutsa ndi kumtsikira chilango chopitilira.”
Tafsiran larabci:
حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَ أَمۡرُنَا وَفَارَ ٱلتَّنُّورُ قُلۡنَا ٱحۡمِلۡ فِيهَا مِن كُلّٖ زَوۡجَيۡنِ ٱثۡنَيۡنِ وَأَهۡلَكَ إِلَّا مَن سَبَقَ عَلَيۡهِ ٱلۡقَوۡلُ وَمَنۡ ءَامَنَۚ وَمَآ ءَامَنَ مَعَهُۥٓ إِلَّا قَلِيلٞ
Kufikira pamene lidadza lamulo lathu, madzi naphulika mu uvuni, (chomwe chidali chisonyezo cha Nuh chosonyeza kudza kwa lamulo loona kwa anthu ake) tidamuuza (kuti): “Kweza m’menemo (m’chombo) mtundu uliwonse (wa nyama), ziwiriziwiri, (yaikazi ndi yaimuna), ndi anthu a kubanja lako kupatula omwe chiweruzo (cha Allah) chatsimikizidwa pa iwo (kuti aonongeke), ndipo (atengenso onse) amene akhulupirira.” Komatu ndi ochepa kwambiri amene adakhulupirira pamodzi ndi iye.
Tafsiran larabci:
۞ وَقَالَ ٱرۡكَبُواْ فِيهَا بِسۡمِ ٱللَّهِ مَجۡر۪ىٰهَا وَمُرۡسَىٰهَآۚ إِنَّ رَبِّي لَغَفُورٞ رَّحِيمٞ
Ndipo (Nuh) adati: “Kwerani m’menemo mwadzina la Allah mkuyenda kwake ndi mkukocheza kwake. Ndithu Mbuye wanga Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi.”
Tafsiran larabci:
وَهِيَ تَجۡرِي بِهِمۡ فِي مَوۡجٖ كَٱلۡجِبَالِ وَنَادَىٰ نُوحٌ ٱبۡنَهُۥ وَكَانَ فِي مَعۡزِلٖ يَٰبُنَيَّ ٱرۡكَب مَّعَنَا وَلَا تَكُن مَّعَ ٱلۡكَٰفِرِينَ
Ndipo (chombocho) chidali kuyenda nawo m’mafunde onga mapiri, ndipo Nuh adaitana mwana wake yemwe adali patali (atakana kulowa m’chombo): “Mwana wanga! Kwera pamodzi ndi ife usakhale pamodzi ndi osakhulupirira.”
Tafsiran larabci:
قَالَ سَـَٔاوِيٓ إِلَىٰ جَبَلٖ يَعۡصِمُنِي مِنَ ٱلۡمَآءِۚ قَالَ لَا عَاصِمَ ٱلۡيَوۡمَ مِنۡ أَمۡرِ ٱللَّهِ إِلَّا مَن رَّحِمَۚ وَحَالَ بَيۡنَهُمَا ٱلۡمَوۡجُ فَكَانَ مِنَ ٱلۡمُغۡرَقِينَ
(Iye) adati: “Ndithawira kuphiri likanditeteza ku madziwa.” Nuh adati: “Lero palibe otetezedwa ku lamulo la Allah kupatula yemwe Allah wamchitira chifundo.” Pompo mafunde adatchinga pakati pawo. Choncho adali mgulu la omizidwa.
Tafsiran larabci:
وَقِيلَ يَٰٓأَرۡضُ ٱبۡلَعِي مَآءَكِ وَيَٰسَمَآءُ أَقۡلِعِي وَغِيضَ ٱلۡمَآءُ وَقُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ وَٱسۡتَوَتۡ عَلَى ٱلۡجُودِيِّۖ وَقِيلَ بُعۡدٗا لِّلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ
Ndipo (pambuyo poonongeka onse ndi zonse zomwe Allah adafuna kuti zionongeke), kudanenedwa: “E iwe nthaka! Meza madzi ako. Ndipo iwe thambo! Amange (madzi ako amvula).” Choncho, madzi adaphwa ndipo lamulo lidakwaniritsidwa (loononga anthu oipa). Ndipo (chombo) chidaima pamwamba pa (phiri lotchedwa) Judi, ndipo kudanenedwa: “Aonongeke onse ochita zoipa.”
Tafsiran larabci:
وَنَادَىٰ نُوحٞ رَّبَّهُۥ فَقَالَ رَبِّ إِنَّ ٱبۡنِي مِنۡ أَهۡلِي وَإِنَّ وَعۡدَكَ ٱلۡحَقُّ وَأَنتَ أَحۡكَمُ ٱلۡحَٰكِمِينَ
Ndipo Nuh adafuulira Mbuye wake nati. “E Mbuye wanga! Ndithu mwana wanga ali mgulu la akubanja langa (akuonongedwa). Ndipo ndithu lonjezo lanu ndiloona, ndipo Inu Ndinu Woweruza mwachoonadi kuposa aweruzi onse.”
Tafsiran larabci:
قَالَ يَٰنُوحُ إِنَّهُۥ لَيۡسَ مِنۡ أَهۡلِكَۖ إِنَّهُۥ عَمَلٌ غَيۡرُ صَٰلِحٖۖ فَلَا تَسۡـَٔلۡنِ مَا لَيۡسَ لَكَ بِهِۦ عِلۡمٌۖ إِنِّيٓ أَعِظُكَ أَن تَكُونَ مِنَ ٱلۡجَٰهِلِينَ
(Allah) adati: “E iwe Nuh! Ndithu iyeyo si (mwana) wa m’banja lako. Iye zochita zake sizili zabwino. Choncho usandipemphe zomwe siukuzidziwa, Ine ndikukulangiza kuti usakhale m’gulu la osazindikira (mbuli).”
Tafsiran larabci:
قَالَ رَبِّ إِنِّيٓ أَعُوذُ بِكَ أَنۡ أَسۡـَٔلَكَ مَا لَيۡسَ لِي بِهِۦ عِلۡمٞۖ وَإِلَّا تَغۡفِرۡ لِي وَتَرۡحَمۡنِيٓ أَكُن مِّنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ
(Nuh) adati: “E Mbuye wanga! Ndikudziteteza mwa Inu kuti ndisakupempheninso zomwe sindikuzidziwa. Ngati simundikhululukira ndi kundichitira chifundo, ndikhala mwa anthu otaika.”
Tafsiran larabci:
قِيلَ يَٰنُوحُ ٱهۡبِطۡ بِسَلَٰمٖ مِّنَّا وَبَرَكَٰتٍ عَلَيۡكَ وَعَلَىٰٓ أُمَمٖ مِّمَّن مَّعَكَۚ وَأُمَمٞ سَنُمَتِّعُهُمۡ ثُمَّ يَمَسُّهُم مِّنَّا عَذَابٌ أَلِيمٞ
Kudanenedwa: “E iwe Nuh! Tsika (pa nthaka youma) mwamtendere wochokera kwa Ife, ndipo madalitso ambiri akhale pa iwe ndi pa anthu omwe ali nawe; ndipo kudzakhala mibadwo ina (yoipa pambuyo pako) yomwe tidzaisangalatsa, ndipo kenako chidzaikhudza chilango chowawa chochokera kwa Ife.”
Tafsiran larabci:
تِلۡكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ ٱلۡغَيۡبِ نُوحِيهَآ إِلَيۡكَۖ مَا كُنتَ تَعۡلَمُهَآ أَنتَ وَلَا قَوۡمُكَ مِن قَبۡلِ هَٰذَاۖ فَٱصۡبِرۡۖ إِنَّ ٱلۡعَٰقِبَةَ لِلۡمُتَّقِينَ
Izi ndi zina mwa nkhani zobisika zomwe tikukuululira iwe. Siudali kuzidziwa, iwe ngakhale anthu ako, patsogolo pa ichi, (Qur’an isadadze). Choncho, pirira. Ndithu mathero abwino adzakhala kwa anthu oopa Allah.
Tafsiran larabci:
وَإِلَىٰ عَادٍ أَخَاهُمۡ هُودٗاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥٓۖ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا مُفۡتَرُونَ
Ndipo anthu (amtundu) wa Âdi, tidawatumizira m’bale wawo Hûd. Adati: “E inu anthu anga! Pembedzani Allah! (Siyani kupembedza mafano). Mulibe mulungu wina koma Iye. Inu simuli kanthu koma ndinu opeka bodza (m’kunena kwanu kwakuti mafano ndi anzake a Allah).”
Tafsiran larabci:
يَٰقَوۡمِ لَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ أَجۡرًاۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَى ٱلَّذِي فَطَرَنِيٓۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ
“E inu anthu anga! Sindikukupemphani malipiro pa ichi (uthengawu). Palibe Malipiro anga koma ali kwaYemwe adandilenga. Kodi mulibe nzeru?”
Tafsiran larabci:
وَيَٰقَوۡمِ ٱسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّكُمۡ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِ يُرۡسِلِ ٱلسَّمَآءَ عَلَيۡكُم مِّدۡرَارٗا وَيَزِدۡكُمۡ قُوَّةً إِلَىٰ قُوَّتِكُمۡ وَلَا تَتَوَلَّوۡاْ مُجۡرِمِينَ
“Ndipo E inu anthu anga! Pemphani chikhululuko kwa Mbuye wanu, (pa machimo omwe mwakhala mukuchita), kenako lapani kwa Iye. Akutumizirani mitambo yodzetsa mvula yambiri, ndipo akuonjezerani mphamvu pa mphamvu zanu (zomwe muli nazo). Choncho, musatembenuke kukhala oipa.”
Tafsiran larabci:
قَالُواْ يَٰهُودُ مَا جِئۡتَنَا بِبَيِّنَةٖ وَمَا نَحۡنُ بِتَارِكِيٓ ءَالِهَتِنَا عَن قَوۡلِكَ وَمَا نَحۡنُ لَكَ بِمُؤۡمِنِينَ
(Iwo) adati: “E iwe Hûd! Sudatibweretsere chisonyezo chooneka (chosonyeza kuti ndiwe Mneneri), ndipo ife sitisiya (kupembedza) milungu yathu chifukwa cha zoyankhula zakozo. Ndipo ife sitikukhulupirira.”
Tafsiran larabci:
إِن نَّقُولُ إِلَّا ٱعۡتَرَىٰكَ بَعۡضُ ءَالِهَتِنَا بِسُوٓءٖۗ قَالَ إِنِّيٓ أُشۡهِدُ ٱللَّهَ وَٱشۡهَدُوٓاْ أَنِّي بَرِيٓءٞ مِّمَّا تُشۡرِكُونَ
“Sitinena kanthu, koma kuti (mwina) milungu yathu ina yakulodza misala.” (Iye) adati: “Ndithu ine ndikupereka umboni kwa Allah ndipo inunso perekani umboni kuti ine ndili kutali ndi zimene mukumphatikiza nazo (Allah pomazipembedza).”
Tafsiran larabci:
مِن دُونِهِۦۖ فَكِيدُونِي جَمِيعٗا ثُمَّ لَا تُنظِرُونِ
“Kusiya Iye; (milungu yanuyo sindikuiopa ngati ili ndi mphamvu pamodzi ndi inu), tero ndichitireni chiwembu nonsenu, ndipo kenako musandiyembekezere (musandipatse nthawi).”
Tafsiran larabci:
إِنِّي تَوَكَّلۡتُ عَلَى ٱللَّهِ رَبِّي وَرَبِّكُمۚ مَّا مِن دَآبَّةٍ إِلَّا هُوَ ءَاخِذُۢ بِنَاصِيَتِهَآۚ إِنَّ رَبِّي عَلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
“Ndithu ine ndatsamira kwa Allah, Mbuye wanga yemwenso ali Mbuye wanu. Palibe chinyama chilichonse koma Allah wachigwira tsumba lake (ndikuchiyendetsa mmene akufunira). Ndithudi, Mbuye wanga Ngwachilungamo.”
Tafsiran larabci:
فَإِن تَوَلَّوۡاْ فَقَدۡ أَبۡلَغۡتُكُم مَّآ أُرۡسِلۡتُ بِهِۦٓ إِلَيۡكُمۡۚ وَيَسۡتَخۡلِفُ رَبِّي قَوۡمًا غَيۡرَكُمۡ وَلَا تَضُرُّونَهُۥ شَيۡـًٔاۚ إِنَّ رَبِّي عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ حَفِيظٞ
“Ngati munyoza (kulandira chimene ndakuuzani palibe vuto kwa ine); ndithu ndafikitsa kwa inu chimene ndatumidwa. Ndipo Mbuye wanga (awaononga osakhulupirira, ndipo) abweretsa anthu ena m’malo mwanu, ndipo inu simungamusautse konse. Ndithu Mbuye wanga ndi Msungi wa chilichonse.”
Tafsiran larabci:
وَلَمَّا جَآءَ أَمۡرُنَا نَجَّيۡنَا هُودٗا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥ بِرَحۡمَةٖ مِّنَّا وَنَجَّيۡنَٰهُم مِّنۡ عَذَابٍ غَلِيظٖ
Ndipo pamene lamulo lathu lidafika (lakuwaononga), tidampulumutsa Hûd ndi amene adakhulupirira pamodzi naye, mwachifundo Chathu, ndipo tidawapulumutsa kuchilango chokhwima.[223]
[223] Chilangocho chidali chimphepo choononga chomwe chinagumula nyumba ndi kulowa m’mphuno za adani a Allah ndi kutulukira kokhalira kwawo. Chinkangowagwetsa chafufumimba kotero kuti anthu adali lambilambi ngati mathunthu a mitengo ya kanjedza.
Tafsiran larabci:
وَتِلۡكَ عَادٞۖ جَحَدُواْ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ وَعَصَوۡاْ رُسُلَهُۥ وَٱتَّبَعُوٓاْ أَمۡرَ كُلِّ جَبَّارٍ عَنِيدٖ
Ndipo awa ndi Âdi. Adatsutsa Ayah (ndime) za Mbuye wawo ndi kunyoza atumiki Ake; ndipo adatsata lamulo la yense wodzikweza, wamakani.
Tafsiran larabci:
وَأُتۡبِعُواْ فِي هَٰذِهِ ٱلدُّنۡيَا لَعۡنَةٗ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۗ أَلَآ إِنَّ عَادٗا كَفَرُواْ رَبَّهُمۡۗ أَلَا بُعۡدٗا لِّعَادٖ قَوۡمِ هُودٖ
Ndipo adatsatizidwa ndi tembelero pa moyo wapano padziko lapansi ndi tsiku la Qiyâma (tsiku la chiweruziro). Dziwani! Ndithu Âdi adakana Mbuye wawo. Ha! Adaonongeka Âdi, anthu a Hûd!.
Tafsiran larabci:
۞ وَإِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمۡ صَٰلِحٗاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥۖ هُوَ أَنشَأَكُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ وَٱسۡتَعۡمَرَكُمۡ فِيهَا فَٱسۡتَغۡفِرُوهُ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِۚ إِنَّ رَبِّي قَرِيبٞ مُّجِيبٞ
Ndipo kwa anthu (a mtundu) wa Samud, (tidatuma) m’bale wawo Swaleh. Adati: “E inu anthu anga! Lambirani Allah. Mulibe mulungu wina koma Iye Yekha. Iye adakuumbani ndi nthaka ndi kukukhazikani m’menemo. Ndipo mpempheni chikhululuko (pa zolakwa zanu), kenako tembenukirani kwa Iye. Ndithu Mbuye wanga ali pafupi (ndi akapolo Ake). Ndipo Ngovomera mapempho (aopempha).”
Tafsiran larabci:
قَالُواْ يَٰصَٰلِحُ قَدۡ كُنتَ فِينَا مَرۡجُوّٗا قَبۡلَ هَٰذَآۖ أَتَنۡهَىٰنَآ أَن نَّعۡبُدَ مَا يَعۡبُدُ ءَابَآؤُنَا وَإِنَّنَا لَفِي شَكّٖ مِّمَّا تَدۡعُونَآ إِلَيۡهِ مُرِيبٖ
Iwo adati: “E iwe Swaleh! Ndithudi, udali woyembekezeka (kukhala mfumu kwa ife) patsogolo pa izi (usanabwere ndi izi). Ha! Kodi ukutiletsa kulambira zomwe makolo athu adali kulambira? Ndithu ife tili m’chikaiko chokaikira zomwe ukutiitanirazo.”
Tafsiran larabci:
قَالَ يَٰقَوۡمِ أَرَءَيۡتُمۡ إِن كُنتُ عَلَىٰ بَيِّنَةٖ مِّن رَّبِّي وَءَاتَىٰنِي مِنۡهُ رَحۡمَةٗ فَمَن يَنصُرُنِي مِنَ ٱللَّهِ إِنۡ عَصَيۡتُهُۥۖ فَمَا تَزِيدُونَنِي غَيۡرَ تَخۡسِيرٖ
(Iye) adati: “E inu anthu anga! Mukuona bwanji ngati ndili ndi chisonyezo choonekera chochokera kwa Mbuye wanga (chosonyeza kuona kwa zimenezi), nandipatsanso chifundo chochokera kwa Iye. Nanga ndi yani angandipulumutse ku chilango cha Allah ngati nditamunyoza? Choncho, simungandionjezere china chake koma kutaika basi.”
Tafsiran larabci:
وَيَٰقَوۡمِ هَٰذِهِۦ نَاقَةُ ٱللَّهِ لَكُمۡ ءَايَةٗۖ فَذَرُوهَا تَأۡكُلۡ فِيٓ أَرۡضِ ٱللَّهِۖ وَلَا تَمَسُّوهَا بِسُوٓءٖ فَيَأۡخُذَكُمۡ عَذَابٞ قَرِيبٞ
“Ndipo E inu anthu anga! Iyi ngamira ya Allah ndi chisonyezo kwa inu. Ilekeni izidya panthaka ya Allah, ndipo musaikhudze ndi choipa kuopa kuti chilango chomwe chili pafupi chingakuonongeni.”[224]
[224] Asamudu adampempha chozizwitsa Mneneri wawo Swalih chotsimikiza kuti iye adalidi Mneneri wa Allah. Chozizwitsa chomwe adampempha nkuti atulutse ngamira patanthwe. Choncho mwa mphamvu za Allah ngamira idatuluka m’tanthwemo. Ndipo adawauza kuti asaichitire choipa. Aisiye izingodzidyera m’dziko la Allah. Koma iwo adaipha, ndipo chilango cha Allah chidawatsikira.
Tafsiran larabci:
فَعَقَرُوهَا فَقَالَ تَمَتَّعُواْ فِي دَارِكُمۡ ثَلَٰثَةَ أَيَّامٖۖ ذَٰلِكَ وَعۡدٌ غَيۡرُ مَكۡذُوبٖ
Koma adaipha. Choncho (Swaleh) adati: “Sangalalani m’midzi yanuyi pamasiku atatu. (Kenako mulangidwa). Limenelo ndi lonjezo osati labodza.”
Tafsiran larabci:
فَلَمَّا جَآءَ أَمۡرُنَا نَجَّيۡنَا صَٰلِحٗا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥ بِرَحۡمَةٖ مِّنَّا وَمِنۡ خِزۡيِ يَوۡمِئِذٍۚ إِنَّ رَبَّكَ هُوَ ٱلۡقَوِيُّ ٱلۡعَزِيزُ
Choncho pamene lamulo Lathu lidadza (lakuononga midziyo), tidampulumutsa Swalih ndi anthu amene adakhulupirira naye, kukuyaluka kwa tsiku limenelo, mwa chifundo Chathu. Ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu, Ngopambana.
Tafsiran larabci:
وَأَخَذَ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ ٱلصَّيۡحَةُ فَأَصۡبَحُواْ فِي دِيَٰرِهِمۡ جَٰثِمِينَ
Ndipo amene adadzichitira okha zoipa phokoso lalikulu lidawaononga, tero kudawachera m’nyumba zawo ali lambilambi (atafa).
Tafsiran larabci:
كَأَن لَّمۡ يَغۡنَوۡاْ فِيهَآۗ أَلَآ إِنَّ ثَمُودَاْ كَفَرُواْ رَبَّهُمۡۗ أَلَا بُعۡدٗا لِّثَمُودَ
Ngati kuti iwo mudalibemo m’menemo. Mverani! Ndithu Asamudu adamkana Mbuye wawo. Choncho Asamudu adaonongeka.
Tafsiran larabci:
وَلَقَدۡ جَآءَتۡ رُسُلُنَآ إِبۡرَٰهِيمَ بِٱلۡبُشۡرَىٰ قَالُواْ سَلَٰمٗاۖ قَالَ سَلَٰمٞۖ فَمَا لَبِثَ أَن جَآءَ بِعِجۡلٍ حَنِيذٖ
Ndipo ndithu atumiki athu (angelo) adadza kwa Ibrahim ndi uthenga wabwino. (Iwo) adati: “Mtendere!” (Iye) adayankha: “Mtendere (ukhale pa inu!)” Ndipo (Ibrahim) sadakhalitse (adafulumira) kudza nayo nyama yootcha ya thole (mwana wa ng’ombe).
Tafsiran larabci:
فَلَمَّا رَءَآ أَيۡدِيَهُمۡ لَا تَصِلُ إِلَيۡهِ نَكِرَهُمۡ وَأَوۡجَسَ مِنۡهُمۡ خِيفَةٗۚ قَالُواْ لَا تَخَفۡ إِنَّآ أُرۡسِلۡنَآ إِلَىٰ قَوۡمِ لُوطٖ
Koma pamene adaona kuti manja awo sakuwatambasula kuchakudya adawadodoma, nadzadzidwa nawo mantha. (Iwo) Adati: “Usaope; ndithu ife tatumidwa kwa anthu a Luti (kuti tikawaononge ndiponso kukupatsa nkhani yabwino).”
Tafsiran larabci:
وَٱمۡرَأَتُهُۥ قَآئِمَةٞ فَضَحِكَتۡ فَبَشَّرۡنَٰهَا بِإِسۡحَٰقَ وَمِن وَرَآءِ إِسۡحَٰقَ يَعۡقُوبَ
Ndipo (m’menemo nkuti) mkazi wake (wa Ibrahim) ali chiimire, ndipo adaseka. Kenaka tidamuuza uthenga wabwino (wakubadwa kwa) Ishaq ndipo pambuyo pa Ishaq, Ya’qub.
Tafsiran larabci:
قَالَتۡ يَٰوَيۡلَتَىٰٓ ءَأَلِدُ وَأَنَا۠ عَجُوزٞ وَهَٰذَا بَعۡلِي شَيۡخًاۖ إِنَّ هَٰذَا لَشَيۡءٌ عَجِيبٞ
(Iye) adati: “Kalanga ine! Ndibereka pomwe ine ndili nkhalamba, ndiponso uyu mwamuna wanga ndi nkhalamba? Ndithudi, ichi ndi chinthu chododometsa.”
Tafsiran larabci:
قَالُوٓاْ أَتَعۡجَبِينَ مِنۡ أَمۡرِ ٱللَّهِۖ رَحۡمَتُ ٱللَّهِ وَبَرَكَٰتُهُۥ عَلَيۡكُمۡ أَهۡلَ ٱلۡبَيۡتِۚ إِنَّهُۥ حَمِيدٞ مَّجِيدٞ
(Angelowo) adati: “Ukudabwa ndi lamulo la Allah? Chisomo cha Allah ndi madalitso ake zili pa inu, E inu eni nyumba iyi! Iye Ngoyamikidwa, Mwini ulemelero!”
Tafsiran larabci:
فَلَمَّا ذَهَبَ عَنۡ إِبۡرَٰهِيمَ ٱلرَّوۡعُ وَجَآءَتۡهُ ٱلۡبُشۡرَىٰ يُجَٰدِلُنَا فِي قَوۡمِ لُوطٍ
Ndipo pamene Ibrahim mantha adamchokera ndikumufikira uthenga wabwino, adayamba kutidandaulira za anthu a Luti (kuti tisawaononge).
Tafsiran larabci:
إِنَّ إِبۡرَٰهِيمَ لَحَلِيمٌ أَوَّٰهٞ مُّنِيبٞ
Ndithu Ibrahim adali wodekha, wodandaulira Allah komanso wobwerera kwa Iye mwachangu (polapa).
Tafsiran larabci:
يَٰٓإِبۡرَٰهِيمُ أَعۡرِضۡ عَنۡ هَٰذَآۖ إِنَّهُۥ قَدۡ جَآءَ أَمۡرُ رَبِّكَۖ وَإِنَّهُمۡ ءَاتِيهِمۡ عَذَابٌ غَيۡرُ مَرۡدُودٖ
(Tidamuuza): “E iwe Ibrahim! Siya ichi. Lamulo la Mbuye wako, ndithu ladza. Ndipo ndithu iwo chiwadzera chilango chosabwezedwa.”
Tafsiran larabci:
وَلَمَّا جَآءَتۡ رُسُلُنَا لُوطٗا سِيٓءَ بِهِمۡ وَضَاقَ بِهِمۡ ذَرۡعٗا وَقَالَ هَٰذَا يَوۡمٌ عَصِيبٞ
Ndipo atumiki athu pamene adafika kwa Luti, iye anadandaula za iwo ndi kubanika nao mu mtima (chifukwa chosowa njira yowatetezera kwa anthu oipa pomwe iye sadadziwe kuti alendowo ndi angelo), nati: “Lino ndi tsiku lovuta.”
Tafsiran larabci:
وَجَآءَهُۥ قَوۡمُهُۥ يُهۡرَعُونَ إِلَيۡهِ وَمِن قَبۡلُ كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ٱلسَّيِّـَٔاتِۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ هَٰٓؤُلَآءِ بَنَاتِي هُنَّ أَطۡهَرُ لَكُمۡۖ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَلَا تُخۡزُونِ فِي ضَيۡفِيٓۖ أَلَيۡسَ مِنكُمۡ رَجُلٞ رَّشِيدٞ
Ndipo anthu ake adadza akuthamangira kwa iye (ku nyumba kwake kuti adzachite zauve ndi alendowo). Ndipo kalenso ankachita zoipa zokhazokhazi, (Luti) adati: “E anthu anga! Nawa asungwana anga; ngoyenera kwa inu (kuwakwatira, osati amuna anzanu) choncho, opani Allah, ndipo musandiyalutse pamaso pa alendo anga. Kodi mwa inu mulibe munthu woongoka?”
Tafsiran larabci:
قَالُواْ لَقَدۡ عَلِمۡتَ مَا لَنَا فِي بَنَاتِكَ مِنۡ حَقّٖ وَإِنَّكَ لَتَعۡلَمُ مَا نُرِيدُ
(Iwo) adati: “Ndithu ukudziwa bwino kuti tilibe khumbo ndi atsikana ako. Ndipo ndithu iwe ukudziwa bwino chimene tifuna.”
Tafsiran larabci:
قَالَ لَوۡ أَنَّ لِي بِكُمۡ قُوَّةً أَوۡ ءَاوِيٓ إِلَىٰ رُكۡنٖ شَدِيدٖ
(Iye) adati: “Ndikadakhala nayo mphamvu (yomenyana nanu) kapena kotsamira kolimba kwamphamvu (ndikadalimbana nanu kuti musachite zauve ndi alendowa).”
Tafsiran larabci:
قَالُواْ يَٰلُوطُ إِنَّا رُسُلُ رَبِّكَ لَن يَصِلُوٓاْ إِلَيۡكَۖ فَأَسۡرِ بِأَهۡلِكَ بِقِطۡعٖ مِّنَ ٱلَّيۡلِ وَلَا يَلۡتَفِتۡ مِنكُمۡ أَحَدٌ إِلَّا ٱمۡرَأَتَكَۖ إِنَّهُۥ مُصِيبُهَا مَآ أَصَابَهُمۡۚ إِنَّ مَوۡعِدَهُمُ ٱلصُّبۡحُۚ أَلَيۡسَ ٱلصُّبۡحُ بِقَرِيبٖ
(Athengawa) adati: “E iwe Luti! Ife ndi athenga a Mbuye wako. Safika kwa iwe (ndi chilichonse choipa). Ndipo choka pamodzi ndi banja lako m’gawo la usiku, ndipo aliyense wa inu asatembenuke (kuyang’ana m’mbuyo akamva mkokomo wa kudza kwa chilangocho), kupatula mkazi wako; iye chimpeza chimene chiwapeze anthu enawo. Ndithu lonjezo lawo ndi m’mawa. Kodi m’mawa suudayandikire?”
Tafsiran larabci:
فَلَمَّا جَآءَ أَمۡرُنَا جَعَلۡنَا عَٰلِيَهَا سَافِلَهَا وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهَا حِجَارَةٗ مِّن سِجِّيلٖ مَّنضُودٖ
Choncho, pamene lidadza lamulo lathu, tidaugadabula (m’zindawo) kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba, ndipo tidawavumbwitsira mvula ya sangalawe zopangika ndi dongo lotentheka ndi moto, zogwirana kwambiri.
Tafsiran larabci:
مُّسَوَّمَةً عِندَ رَبِّكَۖ وَمَا هِيَ مِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ بِبَعِيدٖ
(Sangalawezo) zokhala ndi zizindikiro kwa Mbuye wako. (Sangalawe iliyonse idali ndi mwini wake); ndipo chilango chimenechi sichili kutali ndi anthu oipa.
Tafsiran larabci:
۞ وَإِلَىٰ مَدۡيَنَ أَخَاهُمۡ شُعَيۡبٗاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥۖ وَلَا تَنقُصُواْ ٱلۡمِكۡيَالَ وَٱلۡمِيزَانَۖ إِنِّيٓ أَرَىٰكُم بِخَيۡرٖ وَإِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ عَذَابَ يَوۡمٖ مُّحِيطٖ
Ndipo, ku Madiyan tidamtuma m’bale wawo Shuaib, iye adati: “E inu anthu anga! Pembedzani Allah; mulibe mulungu wina koma Iye. Ndipo musachepetse mulingo wa mbale ndi wasikelo (powapimira anthu), ine ndikukuonani kuti ndinu opeza bwino, ndipo ndikukuoperani chilango cha tsiku (lalikulu) lomwe lidzakuzingani.”
Tafsiran larabci:
وَيَٰقَوۡمِ أَوۡفُواْ ٱلۡمِكۡيَالَ وَٱلۡمِيزَانَ بِٱلۡقِسۡطِۖ وَلَا تَبۡخَسُواْ ٱلنَّاسَ أَشۡيَآءَهُمۡ وَلَا تَعۡثَوۡاْ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُفۡسِدِينَ
“Ndipo E inu anthu anga! Kwaniritsani mulingo wa mbale ndi wasikelo mwachilungamo, ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo (mwachinyengo). Ndipo musafalitse zoipa pa dziko ndi cholinga chodzetsa chisokonezo.”
Tafsiran larabci:
بَقِيَّتُ ٱللَّهِ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَۚ وَمَآ أَنَا۠ عَلَيۡكُم بِحَفِيظٖ
“Chuma chimene wakusiirani Allah (m’njira yovomerezeka) ndicho chabwino kwa inu ngati muli okhulupirira. Ndipo ine sindine msungi wanu.”
Tafsiran larabci:
قَالُواْ يَٰشُعَيۡبُ أَصَلَوٰتُكَ تَأۡمُرُكَ أَن نَّتۡرُكَ مَا يَعۡبُدُ ءَابَآؤُنَآ أَوۡ أَن نَّفۡعَلَ فِيٓ أَمۡوَٰلِنَا مَا نَشَٰٓؤُاْۖ إِنَّكَ لَأَنتَ ٱلۡحَلِيمُ ٱلرَّشِيدُ
Adati: “E iwe Shuaib! Kodi mapemphero ako akukulamula (kuti utilamule) kuti tisiye zimene makolo athu ankapembedza, kapena kuti tisiye kuchita zimene tifuna pachuma chathu? (Adati mwachipongwe) ndithudi, iwe ndiwe wanzeru, ndi wolungama.”
Tafsiran larabci:
قَالَ يَٰقَوۡمِ أَرَءَيۡتُمۡ إِن كُنتُ عَلَىٰ بَيِّنَةٖ مِّن رَّبِّي وَرَزَقَنِي مِنۡهُ رِزۡقًا حَسَنٗاۚ وَمَآ أُرِيدُ أَنۡ أُخَالِفَكُمۡ إِلَىٰ مَآ أَنۡهَىٰكُمۡ عَنۡهُۚ إِنۡ أُرِيدُ إِلَّا ٱلۡإِصۡلَٰحَ مَا ٱسۡتَطَعۡتُۚ وَمَا تَوۡفِيقِيٓ إِلَّا بِٱللَّهِۚ عَلَيۡهِ تَوَكَّلۡتُ وَإِلَيۡهِ أُنِيبُ
(Iye) adati: “E inu anthu anga! Mukuona bwanji ngati ndili ndi umboni wowonekera wochokera kwa Mbuye wanga, ndipo nkundipatsa rizq labwino (lahalali) lochokera kwa Iye, (ndisiye zimenezi ndi kusankha njira yokhota)? Ndipo sindifuna kusiyana nanu pochita chimene ndakuletsani. Sindifuna china, koma kukonza mmene ndingathere; ndipo kupambana kwanga (pazimenezi) kuli kwa Allah. Kwa Iye ndatsamira, ndipo kwa Iye ndikutembenukira.”
Tafsiran larabci:
وَيَٰقَوۡمِ لَا يَجۡرِمَنَّكُمۡ شِقَاقِيٓ أَن يُصِيبَكُم مِّثۡلُ مَآ أَصَابَ قَوۡمَ نُوحٍ أَوۡ قَوۡمَ هُودٍ أَوۡ قَوۡمَ صَٰلِحٖۚ وَمَا قَوۡمُ لُوطٖ مِّنكُم بِبَعِيدٖ
“Ndipo E inu anthu anga! Kutsutsana nane kusakuchimwitseni kuopera kuti chingakupezeni chonga chimene chidawapeza anthu a Nuh kapena anthu a Hûd kapenanso anthu a Swaleh; ndipo anthu a Luti sali kutali ndi inu.”
Tafsiran larabci:
وَٱسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّكُمۡ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِۚ إِنَّ رَبِّي رَحِيمٞ وَدُودٞ
“Ndipo mpempheni chikhululuko Mbuye wanu ndipo lapani kwa Iye (posiya machimo ndikuchita zabwino). Ndithu Mbuye wanga Ngwachisoni Ngwachikondi chochuluka (kwa anthu Ake).”
Tafsiran larabci:
قَالُواْ يَٰشُعَيۡبُ مَا نَفۡقَهُ كَثِيرٗا مِّمَّا تَقُولُ وَإِنَّا لَنَرَىٰكَ فِينَا ضَعِيفٗاۖ وَلَوۡلَا رَهۡطُكَ لَرَجَمۡنَٰكَۖ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡنَا بِعَزِيزٖ
(Iwo) adati: “E iwe Shuaib! Sitikumvetsa zambiri mwa zomwe ukunena. Ndipo ife tikukuona wofooka mwa ife. Pakadapanda akubanja lako, tikadakugenda ndi miyala. Ndipo ulibe ulemelero pa ife (koma tikusunga ulemu wa anthu akubanja lako).”[225]
[225] Anthu ake ankamuuza izi zoti sakumvetsa zomwe iye anawauza mwachibwana, nawafanizira malangizo akewo monga malangizo a munthu wozunguzika.
Tafsiran larabci:
قَالَ يَٰقَوۡمِ أَرَهۡطِيٓ أَعَزُّ عَلَيۡكُم مِّنَ ٱللَّهِ وَٱتَّخَذۡتُمُوهُ وَرَآءَكُمۡ ظِهۡرِيًّاۖ إِنَّ رَبِّي بِمَا تَعۡمَلُونَ مُحِيطٞ
(Iye) adati: “E inu anthu anga! Kodi anthu akubanja kwanga ndiwo olemekezeka kwambiri kwa inu kuposa Allah? Ndipo mwamuyika Iye (Allah) kukhala kumbuyo kwa misana yanu. Ndithu Mbuye wanga zonse zimene mukuchita akuzidziwa bwinobwino.”
Tafsiran larabci:
وَيَٰقَوۡمِ ٱعۡمَلُواْ عَلَىٰ مَكَانَتِكُمۡ إِنِّي عَٰمِلٞۖ سَوۡفَ تَعۡلَمُونَ مَن يَأۡتِيهِ عَذَابٞ يُخۡزِيهِ وَمَنۡ هُوَ كَٰذِبٞۖ وَٱرۡتَقِبُوٓاْ إِنِّي مَعَكُمۡ رَقِيبٞ
“Ndipo E anthu anga! Chitani (zimene mufuna) mmene mungathere; inenso ndichita chimodzimodzi (mmene ndingathere). Posachedwapa mudziwa ndani chimufike chilango chomsambula, ndipo ndani wabodza. Ndipo dikirani inenso ndidikira pamodzi ndi inu.”
Tafsiran larabci:
وَلَمَّا جَآءَ أَمۡرُنَا نَجَّيۡنَا شُعَيۡبٗا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥ بِرَحۡمَةٖ مِّنَّا وَأَخَذَتِ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ ٱلصَّيۡحَةُ فَأَصۡبَحُواْ فِي دِيَٰرِهِمۡ جَٰثِمِينَ
Ndipo pamene lamulo Lathu lidadza, tidampulumutsa Shuaib pamodzi ndi amene adakhulupirira naye, mwachifundo Chathu. Ndipo amene adachita zoipa, phokoso lidawachotsa moyo, tero kudawachera m’nyumba zawo ali lambilambi (atafa).
Tafsiran larabci:
كَأَن لَّمۡ يَغۡنَوۡاْ فِيهَآۗ أَلَا بُعۡدٗا لِّمَدۡيَنَ كَمَا بَعِدَتۡ ثَمُودُ
Ndiye ngati sadakhalemo. Tamverani! Adaonongeka (anthu) a ku Madiyan monga momwe adaonongekera Asamudu!
Tafsiran larabci:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَا وَسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٍ
Ndipo ndithu tidamtuma Mûsa pamodzi ndi zozizwitsa zathu ndi umboni woonekera.
Tafsiran larabci:
إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَٱتَّبَعُوٓاْ أَمۡرَ فِرۡعَوۡنَۖ وَمَآ أَمۡرُ فِرۡعَوۡنَ بِرَشِيدٖ
Kwa Farawo ndi nduna zake. Koma iwo adatsata lamulo la Farawo, ndipo lamulo la Farawo siloongoka.
Tafsiran larabci:
يَقۡدُمُ قَوۡمَهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فَأَوۡرَدَهُمُ ٱلنَّارَۖ وَبِئۡسَ ٱلۡوِرۡدُ ٱلۡمَوۡرُودُ
Tsiku la Qiyâma, (Farawo) adzawatsogolera anthu ake ndi kuwafikitsa ku Moto. Ndipo taonani pamalo poipa kufikirapo.
Tafsiran larabci:
وَأُتۡبِعُواْ فِي هَٰذِهِۦ لَعۡنَةٗ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ بِئۡسَ ٱلرِّفۡدُ ٱلۡمَرۡفُودُ
Iwo adatsatizidwa ndi tembelero pano pa dziko lapansi ndipo pa tsiku la Qiyâma (adzatsatizidwanso). Taonani kuipa mphoto (yawo) yopatsidwa!
Tafsiran larabci:
ذَٰلِكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ ٱلۡقُرَىٰ نَقُصُّهُۥ عَلَيۡكَۖ مِنۡهَا قَآئِمٞ وَحَصِيدٞ
Izi ndi zina mwa nkhani za m’mizinda (zomwe) tikukusimbira. Ina mwa iyo ikadalipobe, ndipo ina idatha.
Tafsiran larabci:
وَمَا ظَلَمۡنَٰهُمۡ وَلَٰكِن ظَلَمُوٓاْ أَنفُسَهُمۡۖ فَمَآ أَغۡنَتۡ عَنۡهُمۡ ءَالِهَتُهُمُ ٱلَّتِي يَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مِن شَيۡءٖ لَّمَّا جَآءَ أَمۡرُ رَبِّكَۖ وَمَا زَادُوهُمۡ غَيۡرَ تَتۡبِيبٖ
Ndipo sitidawachitire choipa (powaononga). Koma adadzichitira okha zoipa (pakusakhulupirira Allah ndi kupembedza mafano ndikuipitsa pa dziko), milungu yawo yomwe ankaipembedza kusiya Allah siidawathandize chilichonse pamene lidadza lamulo la Mbuye wako (la kuwaononga). Ndipo (milunguyo) siidawaonjezere (china chake) koma chionongeko basi.
Tafsiran larabci:
وَكَذَٰلِكَ أَخۡذُ رَبِّكَ إِذَآ أَخَذَ ٱلۡقُرَىٰ وَهِيَ ظَٰلِمَةٌۚ إِنَّ أَخۡذَهُۥٓ أَلِيمٞ شَدِيدٌ
Ndipo mmenemo ndi momwe kumakhalira kulanga kwa Mbuye wako pamene alanga anthu a m’mizinda akakhala oipa (pa makhalidwe). Ndithu kulanga kwake (Allah) nkowawa, nkwaukali.
Tafsiran larabci:
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّمَنۡ خَافَ عَذَابَ ٱلۡأٓخِرَةِۚ ذَٰلِكَ يَوۡمٞ مَّجۡمُوعٞ لَّهُ ٱلنَّاسُ وَذَٰلِكَ يَوۡمٞ مَّشۡهُودٞ
Ndithu m’zimenezi muli lingaliro kwa yemwe akuopa chilango cha tsiku lachimaliziro. Limenelo ndi tsiku losonkhanitsidwa anthu. Ndipo limenelo ndi tsiku lochitiridwa umboni (ndi zolengedwa zonse).
Tafsiran larabci:
وَمَا نُؤَخِّرُهُۥٓ إِلَّا لِأَجَلٖ مَّعۡدُودٖ
Ndipo sitikulichedwetsa koma m’nthawi yowerengeka (kwa Allah, ngakhale kuti kwa anthu likuoneka kuti lili kutali.)
Tafsiran larabci:
يَوۡمَ يَأۡتِ لَا تَكَلَّمُ نَفۡسٌ إِلَّا بِإِذۡنِهِۦۚ فَمِنۡهُمۡ شَقِيّٞ وَسَعِيدٞ
Tsiku lakudza (zoopsa zake), sadzayankhula aliyense koma mwachilolezo Chake (Allah). Ena adzakhala oipa, ndipo (ena) adzakhala abwino.
Tafsiran larabci:
فَأَمَّا ٱلَّذِينَ شَقُواْ فَفِي ٱلنَّارِ لَهُمۡ فِيهَا زَفِيرٞ وَشَهِيقٌ
Tsono amene adzakhala oipa kobwerera kwawo nkumoto. Iwo adzakhala m’menemo akufuula potulutsa mawu ndi kuwabweza (monga kulira kwa bulu).
Tafsiran larabci:
خَٰلِدِينَ فِيهَا مَا دَامَتِ ٱلسَّمَٰوَٰتُ وَٱلۡأَرۡضُ إِلَّا مَا شَآءَ رَبُّكَۚ إِنَّ رَبَّكَ فَعَّالٞ لِّمَا يُرِيدُ
Adzakhala m’menemo nthawi yaitali momwe thambo ndi nthaka zidzakhalire, kupatula Mbuye wako akadzafuna. Ndithu Mbuye wako Ngochita chimene wafuna.
Tafsiran larabci:
۞ وَأَمَّا ٱلَّذِينَ سُعِدُواْ فَفِي ٱلۡجَنَّةِ خَٰلِدِينَ فِيهَا مَا دَامَتِ ٱلسَّمَٰوَٰتُ وَٱلۡأَرۡضُ إِلَّا مَا شَآءَ رَبُّكَۖ عَطَآءً غَيۡرَ مَجۡذُوذٖ
Tsono amene adzakhale abwino adzakhala m’Munda wamtendere. Adzakhala mmenemo nthawi yaitali momwe thambo ndi nthaka zidzakhalire, kupatula Mbuye wako akadzafuna; zopatsa (za Mbuye wako ndizo zopatsa) zosatha.
Tafsiran larabci:
فَلَا تَكُ فِي مِرۡيَةٖ مِّمَّا يَعۡبُدُ هَٰٓؤُلَآءِۚ مَا يَعۡبُدُونَ إِلَّا كَمَا يَعۡبُدُ ءَابَآؤُهُم مِّن قَبۡلُۚ وَإِنَّا لَمُوَفُّوهُمۡ نَصِيبَهُمۡ غَيۡرَ مَنقُوصٖ
Choncho, usakhale ndi chipeneko pa zimene awa akuzipembedza (kuti ndimilungu yabodza). Sapembedza koma momwe amapembedzera makolo awo kale. Ndipo ndithu Ife tiwapatsa gawo lawo (la chilango) mokwanira popanda kuchepetsa.
Tafsiran larabci:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ فَٱخۡتُلِفَ فِيهِۚ وَلَوۡلَا كَلِمَةٞ سَبَقَتۡ مِن رَّبِّكَ لَقُضِيَ بَيۡنَهُمۡۚ وَإِنَّهُمۡ لَفِي شَكّٖ مِّنۡهُ مُرِيبٖ
Ndipo ndithu tidampatsa buku Mûsa, koma kusiyana kudabuka mmenemo (pakatanthauzidwe ka bukulo pambuyo pa Mûsa). Pakadapanda mawu a Mbuye wako omwe adatsogola (oti sadzawalanga nthawi isanafike), ndithu kukadaweruzidwa pakati pawo. Ndipo ndithu iwo ali m’kukaika ndi kupeneka (kwakukulu) pa zimenezo.
Tafsiran larabci:
وَإِنَّ كُلّٗا لَّمَّا لَيُوَفِّيَنَّهُمۡ رَبُّكَ أَعۡمَٰلَهُمۡۚ إِنَّهُۥ بِمَا يَعۡمَلُونَ خَبِيرٞ
Ndipo ndithu Mbuye wako adzawapatsa onsewo mphoto ya zochita zawo mokwanira. Ndithu Iye Ngodziwa (zonse) zimene akuchita.
Tafsiran larabci:
فَٱسۡتَقِمۡ كَمَآ أُمِرۡتَ وَمَن تَابَ مَعَكَ وَلَا تَطۡغَوۡاْۚ إِنَّهُۥ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٞ
Choncho (E iwe Mtumiki!) Pitiriza kulungama monga momwe akulamulira (iwe) pamodzi ndi omwe atembenukira (kwa Allah), ndipo musapyole malire. Ndithu Iye akuona zonse zimene muchita.[226]
[226] Apa akutanthauza kuti ngati chikhalidwe cha mibadwo yakale chidali chonchi, mibadwo yomwe adaitumizira buku lake, natsutsana ndi bukuli, ena a iwo nalitaya kutali, iweyo pitiriza ndi Asilamu omwe uli nawo kugwira njira yolungama monga momwe Allah wakulamulira. Usapyole malire ponyozera chimene chili choyenera iwe kuchichita, kapena kudzikakamiza chimene sungathe kuchichita. Allah tu akudziwa zonse zomwe muchita ndipo adzakulipirani.
Tafsiran larabci:
وَلَا تَرۡكَنُوٓاْ إِلَى ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ فَتَمَسَّكُمُ ٱلنَّارُ وَمَا لَكُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ مِنۡ أَوۡلِيَآءَ ثُمَّ لَا تُنصَرُونَ
Ndipo musapendekere kwa amene sali olungama kuopa kuti chilango cha Moto chingakukhudzeni; ndipo simudzakhala ndi atetezi kwa Allah, ndipo potero simudzathandizidwa (chilichonse).
Tafsiran larabci:
وَأَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ طَرَفَيِ ٱلنَّهَارِ وَزُلَفٗا مِّنَ ٱلَّيۡلِۚ إِنَّ ٱلۡحَسَنَٰتِ يُذۡهِبۡنَ ٱلسَّيِّـَٔاتِۚ ذَٰلِكَ ذِكۡرَىٰ لِلذَّٰكِرِينَ
Ndipo pemphera Swala nsonga ziwiri za usana ndi nthawi za usiku zomwe zili pafupi ndi usana. Ndithu zabwino zimachotsa zoipa. Ichi ndi chikumbutso kwa okumbukira.
Tafsiran larabci:
وَٱصۡبِرۡ فَإِنَّ ٱللَّهَ لَا يُضِيعُ أَجۡرَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ
Ndipo pirira (E iwe Mtumiki! Pokwaniritsa malamulo a Mbuye wako)! Ndithu Allah sataya malipiro a ochita zabwino.
Tafsiran larabci:
فَلَوۡلَا كَانَ مِنَ ٱلۡقُرُونِ مِن قَبۡلِكُمۡ أُوْلُواْ بَقِيَّةٖ يَنۡهَوۡنَ عَنِ ٱلۡفَسَادِ فِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا قَلِيلٗا مِّمَّنۡ أَنجَيۡنَا مِنۡهُمۡۗ وَٱتَّبَعَ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مَآ أُتۡرِفُواْ فِيهِ وَكَانُواْ مُجۡرِمِينَ
Kodi bwanji sadakhalepo, mu mibadwo ya anthu akale, eni nzeru (omvera akalangizidwa), oletsa kuononga pa dziko kupatula ochepa amene tidawapulumutsa mwa iwo? Ndipo amene adadzichitira okha zoipa adatsata zomwe adasangalatsidwa nazo, choncho, adali ochita zoipa.
Tafsiran larabci:
وَمَا كَانَ رَبُّكَ لِيُهۡلِكَ ٱلۡقُرَىٰ بِظُلۡمٖ وَأَهۡلُهَا مُصۡلِحُونَ
Ndipo Mbuye wako sali woononga midzi mopanda chilungamo pomwe eni ake (midziyo) ali ochita zabwino.
Tafsiran larabci:
وَلَوۡ شَآءَ رَبُّكَ لَجَعَلَ ٱلنَّاسَ أُمَّةٗ وَٰحِدَةٗۖ وَلَا يَزَالُونَ مُخۡتَلِفِينَ
Ndipo Mbuye wako akadafuna, anthu onse akadawachita kukhala mpingo umodzi. Choncho saleka kukhala osiyana (maganizo).[227]
[227] Akadawakakamiza onse kukhala mpingo umodzi. Koma adawapatsa nzeru ndi mphamvu yozindikilira zinthu kuti asankhe chomwe afuna, chabwino kapena choipa.
Tafsiran larabci:
إِلَّا مَن رَّحِمَ رَبُّكَۚ وَلِذَٰلِكَ خَلَقَهُمۡۗ وَتَمَّتۡ كَلِمَةُ رَبِّكَ لَأَمۡلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنَ ٱلۡجِنَّةِ وَٱلنَّاسِ أَجۡمَعِينَ
Kupatula omwe Mbuye wako wawachitira chifundo; ndipo chifukwa cha chifundocho, adawalenga (koma okha akusankha zoipa). Ndipo mawu a Mbuye wako akwaniritsidwa (akuti): “Ndithudi, ndizadzadzitsa Jahannam ndi ziwanda ndi anthu onse pamodzi (omwe adali oipa).”
Tafsiran larabci:
وَكُلّٗا نَّقُصُّ عَلَيۡكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ ٱلرُّسُلِ مَا نُثَبِّتُ بِهِۦ فُؤَادَكَۚ وَجَآءَكَ فِي هَٰذِهِ ٱلۡحَقُّ وَمَوۡعِظَةٞ وَذِكۡرَىٰ لِلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndipo tikukusimbira zonse mwa nkhani za atumiki zomwe tikukulimbikitsa nazo mtima. Ndipo m’zimenezi choonadi chakufika ndi ulaliki ndiponso chikumbutso kwa okhulupirira.
Tafsiran larabci:
وَقُل لِّلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ ٱعۡمَلُواْ عَلَىٰ مَكَانَتِكُمۡ إِنَّا عَٰمِلُونَ
Ndipo auze amene sadakhulupirire (kuti): “Chitani mmene mungathere; nafenso tichita (mmene tingathere).”
Tafsiran larabci:
وَٱنتَظِرُوٓاْ إِنَّا مُنتَظِرُونَ
“Ndipo dikirani (chiweruzo cha Allah) nafenso tikudikira.”
Tafsiran larabci:
وَلِلَّهِ غَيۡبُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَإِلَيۡهِ يُرۡجَعُ ٱلۡأَمۡرُ كُلُّهُۥ فَٱعۡبُدۡهُ وَتَوَكَّلۡ عَلَيۡهِۚ وَمَا رَبُّكَ بِغَٰفِلٍ عَمَّا تَعۡمَلُونَ
Zonse zobisika za kumwamba ndi pansi nza Allah ndipo zidzabwezedwa kwa Iye. Choncho, mpembedzeni ndi kutsamira kwa Iye. Ndithu Mbuye wako siwonyalanyaza zimene mukuchita.
Tafsiran larabci:
 
Fassarar Ma'anoni Sura: Suratu Houd
Teburin Jerin Sunayen Surori Lambar shafi
 
Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fasaara da Yaren Pashto - Teburin Bayani kan wasu Fassarori

Fassarar Maanonin Alurani mai girma zuwa Yaren shishiwa wanda Khalid Ibrahim Bitala kwafi na Shekarar 2020 Miladiyya

Rufewa