Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa * - Indice Traduzioni


Traduzione dei significati Sura: Ar-Rûm   Versetto:

Ar-Rûm

الٓمٓ
Alif-Lâm-Mîm.[306]
[306] Surayi yayamba ndi zilembo za alifabeti posonyeza kuti Qur’an yalembedwa kupyolera m’malemba amenewa omwe Arabu amawayankhula mofewa. Koma Aquraish adalephera kulemba Buku limeneli pomwe malembo ake akuwadziwa.
Esegesi in lingua araba:
غُلِبَتِ ٱلرُّومُ
Aroma agonjetsedwa (ndi Aperezi)[307]
[307] Surayi idapatsidwa dzina loti Rum chifukwa chakuti idalosera kuti Aroma adzagonjetsa Aperezi. M’menemo nkuti pamene Surayi inkavumbulutsidwa ndi kulosera kupambana kwa Aroma iwo adali atagonjetsedwa kale ndi Aperezi, kugonjetsedwa zedi kotero kuti maiko awo ambiri adalandidwa ndi Apereziwo. Surayi idavumbulutsidwa ku Makka m’chaka chachisanu nchimodzi (6) kapena chisanu ndichiwiri (7) Mtumiki asanasamuke. Aroma ndi anthu akale zedi; amalamulira maiko ambiri. Mzinda wawo waukulu umatchedwa Roma m’dziko la Italy.
Padali mkangano pakati pa mafumu awiri: Mfumu ya Aroma ndi Mfumu ya Aperezi. Mkanganowo udayamba m’chaka cha 602 A.D, ndipo pamene adamenyana nkhondo Aperezi adagonjetsa Aroma ndipo kupambana kwa Aperezi kutamveka m’Makka, Arabu opembedza mafano adakondwa kwambiri poti naonso Aperezi adali kupembedza mafano ngati iwo. Arabu opembedza mafanowo adati kwa Asilamu ndi Akhrisitu: “Anthu a mabuku ngati inu mwagonjetsedwa ndi anzathu opembedza mafano, choncho nafenso tikugonjetsani inu Asilamu posachedwa.”
Qur’an idalengeza ndime izi ziwiri zomwe mkati mwake muli ulosi uwiri: Ulosi woyamba nkuti m’nyengo yosapyolera zaka zisanu ndi zinayi (9) Aperezi adzagonjetsedwa ndi Aroma. Ndipo ulosi wachiwiri ukuti Asilamu adzagonjetsa Arabu opembedza mafano a mu mzinda wa Makka. M’chaka cha 624, Hiraqla, mfumu ya Aroma adagonjetsa mzinda wa Madiyana m’dziko la Aperezi. Ndipo m’chaka chomwecho naonso Asilamu omwe adali 313 adagonjetsa gulu lankhondo la Arabu opembedza mafano omwe kuchuluka kwawo kudali 1,000 pa nkhondo yomwe idachitikira pamalo wotchedwa Badri.
Ndipo opembedza mafanowo adagonjetsedwa moipa. Potero ulosi umene Qur’an idalosera udakwaniritsidwa. Ndipo ichi chidali chinthu chozizwitsa zedi, chomwe chimasonyeza kuti Qur’an ndi mawudi a Allah.
Esegesi in lingua araba:
فِيٓ أَدۡنَى ٱلۡأَرۡضِ وَهُم مِّنۢ بَعۡدِ غَلَبِهِمۡ سَيَغۡلِبُونَ
M’dziko loyandikira (kwa Arabu lomwe ndi dziko la Sham). Nawonso pambuyo pogonjetsedwa kwawo, adzagonjetsa (Aperezi).
Esegesi in lingua araba:
فِي بِضۡعِ سِنِينَۗ لِلَّهِ ٱلۡأَمۡرُ مِن قَبۡلُ وَمِنۢ بَعۡدُۚ وَيَوۡمَئِذٖ يَفۡرَحُ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ
Mzaka zochepa (zosapyolera 10). Zonse nza Allah, pambuyo ndi patsogolo (pankhondoyo). Ndipo tsiku limenelo okhulupirira adzasangalala.
Esegesi in lingua araba:
بِنَصۡرِ ٱللَّهِۚ يَنصُرُ مَن يَشَآءُۖ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Ndi chithandizo cha Allah (chimene iwo adzapatsidwa, chomwe ndikugonjetsa Aquraish tsiku lomwelo). (Allah) amamthandiza amene wamfuna, ndipo Iye Ngwamphamvu zoposa; Ngwachisoni chosatha.
Esegesi in lingua araba:
وَعۡدَ ٱللَّهِۖ لَا يُخۡلِفُ ٱللَّهُ وَعۡدَهُۥ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ
Ili ndilonjezo la Allah (loona pa okhulupirira). Allah saswa lonjezo Lake. Koma anthu ambiri sadziwa.
Esegesi in lingua araba:
يَعۡلَمُونَ ظَٰهِرٗا مِّنَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَهُمۡ عَنِ ٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ غَٰفِلُونَ
Akudziwa zoonekera (zokhazokha) za moyo wa dziko lapansi (zomwe amadalira pa moyo wawo. Monga ulimi, malonda, zomangamanga ndi zina zotero). Ndipo iwo salabadira za tsiku la chimaliziro.
Esegesi in lingua araba:
أَوَلَمۡ يَتَفَكَّرُواْ فِيٓ أَنفُسِهِمۗ مَّا خَلَقَ ٱللَّهُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَآ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَأَجَلٖ مُّسَمّٗىۗ وَإِنَّ كَثِيرٗا مِّنَ ٱلنَّاسِ بِلِقَآيِٕ رَبِّهِمۡ لَكَٰفِرُونَ
Kodi salingalira mwa iwo okha (nkuona kuti) Allah sadalenge thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, koma mwachilungamo, ndiponso kwa nthawi yoikidwa? Ndithu anthu ambiri ngotsutsa za kukumana ndi Mbuye wawo.
Esegesi in lingua araba:
أَوَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۚ كَانُوٓاْ أَشَدَّ مِنۡهُمۡ قُوَّةٗ وَأَثَارُواْ ٱلۡأَرۡضَ وَعَمَرُوهَآ أَكۡثَرَ مِمَّا عَمَرُوهَا وَجَآءَتۡهُمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِۖ فَمَا كَانَ ٱللَّهُ لِيَظۡلِمَهُمۡ وَلَٰكِن كَانُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ
Kodi sadayende pa dziko nkuona momwe adalili malekezero a omwe adaliko patsogolo pawo? Adali anyonga zambiri kuposa iwo. Adailima nthaka ndi kumangapo zomangamanga kuposa momwe iwo adamangirapo. Ndipo aneneri awo adawadzera ndi zizindikiro zoonekera (koma adawatsutsa, ndipo Allah adawawononga). Choncho Allah sadali owapondereza koma iwo ankadzipondereza okha.
Esegesi in lingua araba:
ثُمَّ كَانَ عَٰقِبَةَ ٱلَّذِينَ أَسَٰٓـُٔواْ ٱلسُّوٓأَىٰٓ أَن كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَكَانُواْ بِهَا يَسۡتَهۡزِءُونَ
Kenako malekezero a amene adaipitsa adali chilango choipa kamba koti adatsutsa Ayah za Allah ndipo ankazichitira chipongwe.
Esegesi in lingua araba:
ٱللَّهُ يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥ ثُمَّ إِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Allah amayambitsa kulenga (zolengedwa), kenako adzabwerezanso (kulengako pambuyo pa imfa yawo), kenako mudzabwezedwa kwa Iye (kuti mudzaweruzidwe).
Esegesi in lingua araba:
وَيَوۡمَ تَقُومُ ٱلسَّاعَةُ يُبۡلِسُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ
Ndipo tsiku limene nthawi ya chiweruziro (Qiyâma) idzakwana, oipa adzataya mtima (zakupeza mtendere wa Allah).
Esegesi in lingua araba:
وَلَمۡ يَكُن لَّهُم مِّن شُرَكَآئِهِمۡ شُفَعَٰٓؤُاْ وَكَانُواْ بِشُرَكَآئِهِمۡ كَٰفِرِينَ
Ndipo sadzakhala ndi aomboli ochokera m’mafano awo, ndipo mafano awowo adzawakana.
Esegesi in lingua araba:
وَيَوۡمَ تَقُومُ ٱلسَّاعَةُ يَوۡمَئِذٖ يَتَفَرَّقُونَ
Ndipo tsiku limene nthawi ya chiweruziro (Qiyâma) idzakwana, tsiku limenelo adzalekana (ena kukalowa ku Munda wamtendere, pomwe ena akalowa ku Moto).
Esegesi in lingua araba:
فَأَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَهُمۡ فِي رَوۡضَةٖ يُحۡبَرُونَ
Koma amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala m’minda ya zipatso ndi maluwa akusangalatsidwa.
Esegesi in lingua araba:
وَأَمَّا ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَلِقَآيِٕ ٱلۡأٓخِرَةِ فَأُوْلَٰٓئِكَ فِي ٱلۡعَذَابِ مُحۡضَرُونَ
Ndipo amene sadakhulupirire ndi kutsutsa Ayah Zathu ndi za kukumana ndi tsiku lachimaliziro, iwo adzaperekedwa ku chilango cha Moto.
Esegesi in lingua araba:
فَسُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ حِينَ تُمۡسُونَ وَحِينَ تُصۡبِحُونَ
Choncho, lemekezani Allah pamene mukulowa m’nthawi za usiku (popemphera Magrbi ndi Isha); ndi pamene mukulowa m’nthawi ya m’bandakucha (popemphera pemphero la Fajr).
Esegesi in lingua araba:
وَلَهُ ٱلۡحَمۡدُ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَعَشِيّٗا وَحِينَ تُظۡهِرُونَ
Kutamandidwa konse, kumwamba ndi pansi nkwa Allah. Ndipo (mulemekezeni) m’nthawi ya madzulo (popemphera Asr) ndi pomwe mukulowa m’nthawi yamasana (Dhuhr).
Esegesi in lingua araba:
يُخۡرِجُ ٱلۡحَيَّ مِنَ ٱلۡمَيِّتِ وَيُخۡرِجُ ٱلۡمَيِّتَ مِنَ ٱلۡحَيِّ وَيُحۡيِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَاۚ وَكَذَٰلِكَ تُخۡرَجُونَ
(Iye) amatulutsa chamoyo kuchokera mchakufa, ndipo amatulutsa chakufa kuchokera m’chamoyo, ndipo amaukitsa nthaka pambuyo pa kufa kwake. Ndipo momwemonso mudzatulutsidwa (m’manda).
Esegesi in lingua araba:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦٓ أَنۡ خَلَقَكُم مِّن تُرَابٖ ثُمَّ إِذَآ أَنتُم بَشَرٞ تَنتَشِرُونَ
Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza mphamvu Zake zoposa), ndiko kukulengani kuchokera ku dothi kenako inu nkukhala anthu omwe mukufala (ponseponse).
Esegesi in lingua araba:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦٓ أَنۡ خَلَقَ لَكُم مِّنۡ أَنفُسِكُمۡ أَزۡوَٰجٗا لِّتَسۡكُنُوٓاْ إِلَيۡهَا وَجَعَلَ بَيۡنَكُم مَّوَدَّةٗ وَرَحۡمَةًۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَتَفَكَّرُونَ
Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza chifundo Chake kwa inu) ndiko kukulengerani akazi a mtundu wanu kuti mukhazikike (mitima yanu) kwa iwo, ndipo adaika pakati panu chikondi ndi chisoni. Ndithu mzimenezi muli zizindikiro kwa anthu amene amalingalira.
Esegesi in lingua araba:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦ خَلۡقُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَٱخۡتِلَٰفُ أَلۡسِنَتِكُمۡ وَأَلۡوَٰنِكُمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّلۡعَٰلِمِينَ
Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza kukhoza Kwake) ndiko kulenga kwa thambo ndi nthaka ndikusiyana kwa ziyankhulo zanu ndi utoto (wa makungu anu; chikhalirecho mudalengedwa kuchokera kwa munthu m’modzi). Ndithu m’zimenezi muli zizindikiro kwa odziwa.
Esegesi in lingua araba:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦ مَنَامُكُم بِٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ وَٱبۡتِغَآؤُكُم مِّن فَضۡلِهِۦٓۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَسۡمَعُونَ
Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza luntha Lake), ndiko kukupatsani mpumulo watulo usiku, ndi (kudzuka) usana ndi kufunafuna kwanu zabwino Zake. Ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa anthu amene amamva (ndi kuthandizidwa ndikumvako).
Esegesi in lingua araba:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦ يُرِيكُمُ ٱلۡبَرۡقَ خَوۡفٗا وَطَمَعٗا وَيُنَزِّلُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَيُحۡيِۦ بِهِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَآۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَعۡقِلُونَ
Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza mphamvu Zake zoposa) ndiko kukusonyezani kung’anima komwe kumakuchititsani mantha, ndi kukupatsani chiyembekezero (chakudza kwa mvula). Ndipo amatsitsa madzi kuchokera kumwamba. Kotero kuti amaukitsa nthaka ndi madziwo pambuyo pa kufa kwake (nthakayo). Ndithu m’zimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira.
Esegesi in lingua araba:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦٓ أَن تَقُومَ ٱلسَّمَآءُ وَٱلۡأَرۡضُ بِأَمۡرِهِۦۚ ثُمَّ إِذَا دَعَاكُمۡ دَعۡوَةٗ مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ إِذَآ أَنتُمۡ تَخۡرُجُونَ
Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza kukhoza kwake), ndiko kuti thambo ndi nthaka zaima mwa lamulo Lake. Kenako akadzakuitanani; kuitana kumodzi nthawi imeneyo inu mudzatuluka m’nthaka.
Esegesi in lingua araba:
وَلَهُۥ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ كُلّٞ لَّهُۥ قَٰنِتُونَ
Ndipo onse akumwamba ndi a pa dziko lapansi, Ngake. Onse amamvera Iye.
Esegesi in lingua araba:
وَهُوَ ٱلَّذِي يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥ وَهُوَ أَهۡوَنُ عَلَيۡهِۚ وَلَهُ ٱلۡمَثَلُ ٱلۡأَعۡلَىٰ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Ndipo Iye ndiamene adayambitsa zolengedwa. Ndipo ndi Yemwe adzazibwerezenso (kachiwiri). Ndipo kuzibwerezako, nkosavuta kwa Iye, ndipo ali ndi mbiri yabwino kumwmba ndi pansi. Ndiponso Iye Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.
Esegesi in lingua araba:
ضَرَبَ لَكُم مَّثَلٗا مِّنۡ أَنفُسِكُمۡۖ هَل لَّكُم مِّن مَّا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُم مِّن شُرَكَآءَ فِي مَا رَزَقۡنَٰكُمۡ فَأَنتُمۡ فِيهِ سَوَآءٞ تَخَافُونَهُمۡ كَخِيفَتِكُمۡ أَنفُسَكُمۡۚ كَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٖ يَعۡقِلُونَ
Wapereka kwa inu fanizo la chikhalidwe chanu. Kodi (akapolo) amene manja anu akumanja apeza ali ndi gawo pa chuma chimene takupatsani kotero kuti mumagawana chimenecho molingana? Kodi mumawaopa monga momwe muoperana wina ndi mzake? (Nanga nchotani inu kuti mumuyese Allah kuti ali ndi amzake mwa akapolo Ake?) Umo ndimomwe tikulongosolera Ayah (ndime Zathu) kwa anthu ozindikira.
Esegesi in lingua araba:
بَلِ ٱتَّبَعَ ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ أَهۡوَآءَهُم بِغَيۡرِ عِلۡمٖۖ فَمَن يَهۡدِي مَنۡ أَضَلَّ ٱللَّهُۖ وَمَا لَهُم مِّن نَّٰصِرِينَ
Koma amene adadzichitira zoipa okha, atsata zofuna zawo popanda kudziwa. Kodi ndiyani angamulungamitse amene Allah wamsiya kuti asokere (chifukwa chakusafuna kwake kuongoka)? Ndipo iwo sadzakhala ndi apulumutsi.
Esegesi in lingua araba:
فَأَقِمۡ وَجۡهَكَ لِلدِّينِ حَنِيفٗاۚ فِطۡرَتَ ٱللَّهِ ٱلَّتِي فَطَرَ ٱلنَّاسَ عَلَيۡهَاۚ لَا تَبۡدِيلَ لِخَلۡقِ ٱللَّهِۚ ذَٰلِكَ ٱلدِّينُ ٱلۡقَيِّمُ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ
Choncho lunjika nkhope yako ku chipembedzo moyenera; (pewa kusokera kwa okana Allah. Dzikakamize ku) chilengedwe chimene Allah adalengera anthu. (Ichi nchipembedzo cha Chisilamu chomwe nchoyenerana ndi chilengedwe cha munthu). Palibe kusintha m’kalengedwe ka zolengedwa za Allah. Ichi ndi chipembedzo choona (cholungama). Koma anthu ambiri sadziwa.
Esegesi in lingua araba:
۞ مُنِيبِينَ إِلَيۡهِ وَٱتَّقُوهُ وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَلَا تَكُونُواْ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ
(Lunjikani nkhope zanu) modzichepetsa kwa Iye ndipo muopeni (potsatira malamulo Ake). Pempherani Swala moyenera, ndipo musakhale mwa opembedza mafano.
Esegesi in lingua araba:
مِنَ ٱلَّذِينَ فَرَّقُواْ دِينَهُمۡ وَكَانُواْ شِيَعٗاۖ كُلُّ حِزۡبِۭ بِمَا لَدَيۡهِمۡ فَرِحُونَ
Mwa omwe agawa chipembedzo chawo nkukhala mipatukomipatuko; gulu lililonse likusangalalira chomwe lili nacho.
Esegesi in lingua araba:
وَإِذَا مَسَّ ٱلنَّاسَ ضُرّٞ دَعَوۡاْ رَبَّهُم مُّنِيبِينَ إِلَيۡهِ ثُمَّ إِذَآ أَذَاقَهُم مِّنۡهُ رَحۡمَةً إِذَا فَرِيقٞ مِّنۡهُم بِرَبِّهِمۡ يُشۡرِكُونَ
Ndipo mavuto akawakhudza anthu, amampempha Mbuye wawo modzichepetsa kwa Iye. Kenako akawalawitsa mtendere wochokera kwa Iye, pamenepo ena a iwo amamuphatikiza Mbuye wawo (ndi mafano).
Esegesi in lingua araba:
لِيَكۡفُرُواْ بِمَآ ءَاتَيۡنَٰهُمۡۚ فَتَمَتَّعُواْ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ
Posathokoza zimene tawapatsa. Choncho sangalalani (ndi zimene mukuzifunazo); posachedwapa mudziwa (kuipa kwake).
Esegesi in lingua araba:
أَمۡ أَنزَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ سُلۡطَٰنٗا فَهُوَ يَتَكَلَّمُ بِمَا كَانُواْ بِهِۦ يُشۡرِكُونَ
Kodi kapena tidawatsitsira umboni womwe ukufotokoza zomwe adali kumuphatikiza nazo Iye (Allah)?
Esegesi in lingua araba:
وَإِذَآ أَذَقۡنَا ٱلنَّاسَ رَحۡمَةٗ فَرِحُواْ بِهَاۖ وَإِن تُصِبۡهُمۡ سَيِّئَةُۢ بِمَا قَدَّمَتۡ أَيۡدِيهِمۡ إِذَا هُمۡ يَقۡنَطُونَ
Ndipo anthu tikawalawitsa mtendere, amausangalalira. Koma choipa chikawapeza, chifukwa cha zomwe manja awo atsogoza, pamenepo iwo amataya mtima (kuti sangapezenso zabwino za Allah).
Esegesi in lingua araba:
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّ ٱللَّهَ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ وَيَقۡدِرُۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ
Kodi saona kuti Allah amamchulukitsira rizq yemwe wamfuna, ndi kumchepetsera (yemwe wamfuna)? Ndithu m’zimenezi, muli zisonyezo kwa anthu okhulupirira.
Esegesi in lingua araba:
فَـَٔاتِ ذَا ٱلۡقُرۡبَىٰ حَقَّهُۥ وَٱلۡمِسۡكِينَ وَٱبۡنَ ٱلسَّبِيلِۚ ذَٰلِكَ خَيۡرٞ لِّلَّذِينَ يُرِيدُونَ وَجۡهَ ٱللَّهِۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ
Choncho mpatseni gawo lake wachibale, m’mphawi ndi wapaulendo (amene alibe chokamfikitsa kwawo). Zimenezo nzabwino kwa amene akufuna chiyanjo cha Allah, ndipo iwo ndiwo opambana.
Esegesi in lingua araba:
وَمَآ ءَاتَيۡتُم مِّن رِّبٗا لِّيَرۡبُوَاْ فِيٓ أَمۡوَٰلِ ٱلنَّاسِ فَلَا يَرۡبُواْ عِندَ ٱللَّهِۖ وَمَآ ءَاتَيۡتُم مِّن زَكَوٰةٖ تُرِيدُونَ وَجۡهَ ٱللَّهِ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُضۡعِفُونَ
Ndipo chuma chimene mukupatsana m’njira yamphatso kuti chichuluke m’chuma cha anthu, kwa Allah sichichuluka. Koma (chuma) chimene mukuchipereka m’njira ya Zakaat uku mukufuna chiyanjo cha Allah (chimachuluka). Iwowo ndi amene adzapeza mphoto yochuluka.
Esegesi in lingua araba:
ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَكُمۡ ثُمَّ رَزَقَكُمۡ ثُمَّ يُمِيتُكُمۡ ثُمَّ يُحۡيِيكُمۡۖ هَلۡ مِن شُرَكَآئِكُم مَّن يَفۡعَلُ مِن ذَٰلِكُم مِّن شَيۡءٖۚ سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ
Allah ndi Yemwe adakulengani. Kenako adakupatsani (zokuthandizani kuti mukhale ndi moyo). Kenako adzakupatsani imfa (kuti mulowe m’manda). Ndipo kenako adzakuukitsani (kuti mukaweruzidwe pa zomwe mumachita). Kodi mwa amene mukuwaphatikiza (ndi Allah), alipo yemwe angachite chilichonse m’zimenezi? Wayera Iye (Allah) ndipo watukuka ku zimene akumphatikiza.
Esegesi in lingua araba:
ظَهَرَ ٱلۡفَسَادُ فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ بِمَا كَسَبَتۡ أَيۡدِي ٱلنَّاسِ لِيُذِيقَهُم بَعۡضَ ٱلَّذِي عَمِلُواْ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ
Chisokonezo chaonekera pamtunda ndi panyanja chifukwa cha zimene manja a anthu achita, kuti awalawitse (chilango cha) zina zomwe adachita; kuti iwo atembenukire (kwa Allah).
Esegesi in lingua araba:
قُلۡ سِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَٱنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلُۚ كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّشۡرِكِينَ
Nena: “Yendani padziko ndi kuyang’ana momwe adalili mathero a omwe adalipo kale. Ambiri a iwo adali ophatikiza (Allah ndi mafano).”
Esegesi in lingua araba:
فَأَقِمۡ وَجۡهَكَ لِلدِّينِ ٱلۡقَيِّمِ مِن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَ يَوۡمٞ لَّا مَرَدَّ لَهُۥ مِنَ ٱللَّهِۖ يَوۡمَئِذٖ يَصَّدَّعُونَ
Choncho lunjika nkhope yako ku chipembedzo choongoka lisadadze tsiku losabwezedwa lochokera kwa Allah. Tsiku limenelo (anthu) adzagawikana, (abwino akalowa ku Munda wamtendere, pomwe oipa akalowa ku Moto).
Esegesi in lingua araba:
مَن كَفَرَ فَعَلَيۡهِ كُفۡرُهُۥۖ وَمَنۡ عَمِلَ صَٰلِحٗا فَلِأَنفُسِهِمۡ يَمۡهَدُونَ
Amene sanakhulupirire, kuipa kwa kusakhulupirira kwake kuli pa iye (mwini). Ndipo amene achita zabwino iwo akudzikonzera okha (zabwino).
Esegesi in lingua araba:
لِيَجۡزِيَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ مِن فَضۡلِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ لَا يُحِبُّ ٱلۡكَٰفِرِينَ
Kuti awalipire zabwino Zake amene akhulupirira ndi kuchita zabwino. Ndithu Iye sakonda akafiri (osakhulupirira).
Esegesi in lingua araba:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦٓ أَن يُرۡسِلَ ٱلرِّيَاحَ مُبَشِّرَٰتٖ وَلِيُذِيقَكُم مِّن رَّحۡمَتِهِۦ وَلِتَجۡرِيَ ٱلۡفُلۡكُ بِأَمۡرِهِۦ وَلِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦ وَلَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ
Ndipo zina mwa zisonyezo Zake (zosonyeza mphamvu Zake ndi chifundo Chake) ndiko kutumiza mphepo yodza ndi nkhani yabwino (yakuti mvula ivumba) ndi kuti akulawitseni chifundo Chake, ndi kuti zombo ziyende (panyanja) mwa lamulo Lake, ndi kuti mufunefune zabwino Zake ndi kutinso muthokoze (mtendere Wake pomumvera ndi kumpembedza Iye Yekha).
Esegesi in lingua araba:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ رُسُلًا إِلَىٰ قَوۡمِهِمۡ فَجَآءُوهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَٱنتَقَمۡنَا مِنَ ٱلَّذِينَ أَجۡرَمُواْۖ وَكَانَ حَقًّا عَلَيۡنَا نَصۡرُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndipo, ndithu tidatuma aneneri kwa anthu awo patsogolo pako. Choncho (mneneri aliyense) adawadzera anthu ake ndi maumboni oonekera poyera (osonyeza kuona kwawo, koma adawakana). Tero tidawawononga amene adalakwa. Ndikofunika kwa Ife kupulumutsa okhulupirira.
Esegesi in lingua araba:
ٱللَّهُ ٱلَّذِي يُرۡسِلُ ٱلرِّيَٰحَ فَتُثِيرُ سَحَابٗا فَيَبۡسُطُهُۥ فِي ٱلسَّمَآءِ كَيۡفَ يَشَآءُ وَيَجۡعَلُهُۥ كِسَفٗا فَتَرَى ٱلۡوَدۡقَ يَخۡرُجُ مِنۡ خِلَٰلِهِۦۖ فَإِذَآ أَصَابَ بِهِۦ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦٓ إِذَا هُمۡ يَسۡتَبۡشِرُونَ
Allah ndiyemwe akutumiza mphepo yomwe imagwedeza mitambo mwamphamvu, ndipo akuibalalitsa kumwamba mmene akufunira. Amaigawa zigawozigawo (kufikira) uyiona mvula ikutuluka mkati mwake (mitamboyo). Ndipo (Allah) akaitsitsa kwa amene wamfuna mwa akapolo Ake, pamenepo iwo amakondwa ndi kusangalala.
Esegesi in lingua araba:
وَإِن كَانُواْ مِن قَبۡلِ أَن يُنَزَّلَ عَلَيۡهِم مِّن قَبۡلِهِۦ لَمُبۡلِسِينَ
Ngakhale kuti isadawatsikire, adali otaya mtima (ndi kutekeseka kwambiri).
Esegesi in lingua araba:
فَٱنظُرۡ إِلَىٰٓ ءَاثَٰرِ رَحۡمَتِ ٱللَّهِ كَيۡفَ يُحۡيِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَآۚ إِنَّ ذَٰلِكَ لَمُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
Choncho, yang’ana (molingalira) zizindikiro za chifundo cha Allah momwe akuukitsira nthaka (pomeretsa mmera) pambuyo pa imfa yake. Ndithu Iye Ngoukitsa akufa. Ndipo Iye Ngokhoza chilichonse (palibe chokanika kwa Iye.)
Esegesi in lingua araba:
وَلَئِنۡ أَرۡسَلۡنَا رِيحٗا فَرَأَوۡهُ مُصۡفَرّٗا لَّظَلُّواْ مِنۢ بَعۡدِهِۦ يَكۡفُرُونَ
Ndipo, ndithu tikaatumizira mphepo (yoononga mmera) nkuuona pambuyo pake uli wachikasu, akadakhala akupitiriza kukana (Allah chifukwa chokwiyitsidwa ndi zimenezi.)
Esegesi in lingua araba:
فَإِنَّكَ لَا تُسۡمِعُ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَلَا تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ ٱلدُّعَآءَ إِذَا وَلَّوۡاْ مُدۡبِرِينَ
(Usadandaule ndi makani awo). Ndithu iwe sungachititse kuti amve akufa (kuitana kwako). Ndiponso sungachititse kuti amve agonthi kuitana pamene akutembenukira nakuyang’anitsa msana (osafuna kumva mawu ako).
Esegesi in lingua araba:
وَمَآ أَنتَ بِهَٰدِ ٱلۡعُمۡيِ عَن ضَلَٰلَتِهِمۡۖ إِن تُسۡمِعُ إِلَّا مَن يُؤۡمِنُ بِـَٔايَٰتِنَا فَهُم مُّسۡلِمُونَ
Ndipo iwe sungathe kuwaongolera akhungu m’kusokera kwawo. Sungachititse kuti amve koma okhawo amene akhulupirira Ayah Zathu. Iwowo ndiwo odzipereka.
Esegesi in lingua araba:
۞ ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَكُم مِّن ضَعۡفٖ ثُمَّ جَعَلَ مِنۢ بَعۡدِ ضَعۡفٖ قُوَّةٗ ثُمَّ جَعَلَ مِنۢ بَعۡدِ قُوَّةٖ ضَعۡفٗا وَشَيۡبَةٗۚ يَخۡلُقُ مَا يَشَآءُۚ وَهُوَ ٱلۡعَلِيمُ ٱلۡقَدِيرُ
Allah ndi Yemwe adakulengani kuchokera mkufooka; kenako adakupatsani mphamvu pambuyo pakufooka, ndipo pambuyo pamphamvu adakupatsani kufooka ndi imvi, (Iye) akulenga chimene wafuna. Ndipo Iye Ngodziwa kwambiri, Ngokhoza chilichonse.[308]
[308] M’ndime iyi akufotokoza kuti adalenga anthu kuchokera m’madzi ofooka. Ndipo kuchokera pamenepo chilengedwe chimasinthasintha pokhala khanda, mnyamata kenako nkukhala wamkulu wanyongazake ndipo mapeto ake nkukhala nkhalamba ya imvi, yofooka. Zonsezi zimachitika mwa chifuniro cha Allah popanda munthu kuikapo dzanja.
Esegesi in lingua araba:
وَيَوۡمَ تَقُومُ ٱلسَّاعَةُ يُقۡسِمُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ مَا لَبِثُواْ غَيۡرَ سَاعَةٖۚ كَذَٰلِكَ كَانُواْ يُؤۡفَكُونَ
Ndipo tsiku limene chiweruziro (Qiyâma) chidzachitika, oipa adzakhala akulumbira (kuti) sadakhale (pa dziko lapansi kapena mmanda) koma ola limodzi. Umo ndimomwe amatembenuzidwira (kuchokera ku njira ya choonadi).[309]
[309] Ndime iyi ikufotokozera kuti anthu ochita zoipa akadzaukitsidwa m’manda ndi kuona zoopsa zothetsa nzeru, adzaganiza kuti pamoyo wa padziko lapansi sadakhale nthawi yaitali koma ola limodzi basi. Izi nchifukwa chamavuto omwe adzakumana nawo patsiku limenelo.
Esegesi in lingua araba:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ وَٱلۡإِيمَٰنَ لَقَدۡ لَبِثۡتُمۡ فِي كِتَٰبِ ٱللَّهِ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡبَعۡثِۖ فَهَٰذَا يَوۡمُ ٱلۡبَعۡثِ وَلَٰكِنَّكُمۡ كُنتُمۡ لَا تَعۡلَمُونَ
Ndipo amene apatsidwa nzeru ndi chikhulupiliro, adzanena: “Ndithu inu mudakhala m’chilamulo cha Allah kufikira tsiku louka ku imfa; choncho ili ndi tsiku louka ku imfa koma inu simunali kudziwa.”
Esegesi in lingua araba:
فَيَوۡمَئِذٖ لَّا يَنفَعُ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مَعۡذِرَتُهُمۡ وَلَا هُمۡ يُسۡتَعۡتَبُونَ
Choncho tsiku limenelo, madandaulo a omwe adzichitira chinyengo sadzawathandiza ndipo sadzafunsidwa kuti amukondweretse Allah (ndi kulapa kwawo.)
Esegesi in lingua araba:
وَلَقَدۡ ضَرَبۡنَا لِلنَّاسِ فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ مِن كُلِّ مَثَلٖۚ وَلَئِن جِئۡتَهُم بِـَٔايَةٖ لَّيَقُولَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا مُبۡطِلُونَ
Ndipo ndithu tawapatsa anthu mafanizo a mtundu uliwonse m’Qur’an iyi. Ndipo, ndithu ukawabweretsera mtsutso uliwonse, anena omwe sadakhulupirire: “Inu sikanthu, koma ndinu anthu ochita zachabe.”
Esegesi in lingua araba:
كَذَٰلِكَ يَطۡبَعُ ٱللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِ ٱلَّذِينَ لَا يَعۡلَمُونَ
Mmenemo ndi momwe Allah akudindira (chidindo) m’mitima mwa amene sazindikira.
Esegesi in lingua araba:
فَٱصۡبِرۡ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞۖ وَلَا يَسۡتَخِفَّنَّكَ ٱلَّذِينَ لَا يُوقِنُونَ
Choncho pirira (iwe Mtumiki ku masautso awo). Ndithu lonjezo la Allah, nloona, ndipo asakugwetse mphwayi amene alibe chikhulupiriro chotsimikizika.
Esegesi in lingua araba:
 
Traduzione dei significati Sura: Ar-Rûm
Indice delle Sure Numero di pagina
 
Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa - Indice Traduzioni

Traduzione dei significati del Nobile Corano in lingua chicheŵa, a cura di Khaled Ibrahim Beitala، ed. 2020

Chiudi