Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa * - Indice Traduzioni


Traduzione dei significati Sura: Fâtir   Versetto:

Fâtir

ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ فَاطِرِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ جَاعِلِ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ رُسُلًا أُوْلِيٓ أَجۡنِحَةٖ مَّثۡنَىٰ وَثُلَٰثَ وَرُبَٰعَۚ يَزِيدُ فِي ٱلۡخَلۡقِ مَا يَشَآءُۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
Kuyamikidwa konse nkwa Allah (Yekha) Muumbi wa thambo ndi nthaka (popanda chofanizira), amene adachita angelo kukhala atumwi eni mapiko, awiriawiri; atatuatatu; ndi anayianayi. Amaonjezera mkulenga monga momwe afunira, (palibe chimene chingakanike kwa Iye). Ndithu Allah Ngokhoza chilichonse.[338]
[338] (Ndime 1-2) Iye Allah ali ndi mphamvu pa chilichonse; chimene afuna kuti chichitike chimachitika. Ndipo palibe chimene chingakanike kulengeka ndi Iye ngati atafuna kuti chilengeke. Allah wadzitamanda m’ndime ziwirizi ndi makhalidwe Ake awiri a pamwamba. Khalidwe loyamba, ndikukhoza komwe ndikusalephera chilichonse chimene wafuna. Khalidwe Lake lachiwiri ndikupereka madalitso osiyanasiyana pa zolengedwa Zake. Allah adalenga thambo ndi nthaka popanda chofanizira, natukula thambo kumwamba popanda mzati nalikongoletsa ndi nyenyezi. Iye ndi Yemwe adayalanso nthaka naika mmenemo mmera monga chakudya cha za moyo, nang’ambamo nyanja ndi mitsinje ndi akasupe ndi zina zotero zomwe zikusonyeza mphamvu Zake zoposa ndi luso Lake. Ndime yachiwiriyi ikutiphunzitsa kuti chimene Allah wachipereka kwa munthu monga chuma kukhala ndi moyo wangwiro, kukhala ndi nzeru zakuthwa, palibe amene angazitsekereze zimenezi. Ndipo chimene Allah wam’mana munthu, palibe amene angathe kuchipereka kwa iye.
Esegesi in lingua araba:
مَّا يَفۡتَحِ ٱللَّهُ لِلنَّاسِ مِن رَّحۡمَةٖ فَلَا مُمۡسِكَ لَهَاۖ وَمَا يُمۡسِكۡ فَلَا مُرۡسِلَ لَهُۥ مِنۢ بَعۡدِهِۦۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Chifundo chimene Allah angatsekule kwa anthu, palibe amene angachitsekereze. Ndipo chimene angachiletse palibe amene angachipereke kupatula Iye. Ndipo Iye ndi Mwini mphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.
Esegesi in lingua araba:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ٱذۡكُرُواْ نِعۡمَتَ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡۚ هَلۡ مِنۡ خَٰلِقٍ غَيۡرُ ٱللَّهِ يَرۡزُقُكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِۚ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ فَأَنَّىٰ تُؤۡفَكُونَ
E inu anthu! Kumbukirani chisomo cha Allah chomwe chili pa inu (pomthokoza). Kodi alipo Mlengi wina osati Allah amene angakupatseni rizq kuchokera kumwamba ndi pansi? Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi, koma Iye. Nanga mukutembenuzidwira kuti?
Esegesi in lingua araba:
وَإِن يُكَذِّبُوكَ فَقَدۡ كُذِّبَتۡ رُسُلٞ مِّن قَبۡلِكَۚ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرۡجَعُ ٱلۡأُمُورُ
Ndipo ngati angakutsutse ndithu adatsutsidwanso atumiki amene adalipo patsogolo pako. Ndipo zinthu zonse zidzabwezedwa kwa Allah.
Esegesi in lingua araba:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞۖ فَلَا تَغُرَّنَّكُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا وَلَا يَغُرَّنَّكُم بِٱللَّهِ ٱلۡغَرُورُ
E inu anthu! Ndithu lonjezo la Allah ndi loona. Choncho usakunyengeni moyo wa dziko lapansi, ngakhale mdyerekezi uja wamkulu (Iblis), asakunyengeni pa za Allah.[339]
[339] M’ndime iyi Allah akutichenjeza kuti tisanyengedwe ndi malangizo a Satana akuti: “Chitani mmene mungafunire, Allah Wachifundo chambiri adzakukhululukirani.”
Esegesi in lingua araba:
إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ لَكُمۡ عَدُوّٞ فَٱتَّخِذُوهُ عَدُوًّاۚ إِنَّمَا يَدۡعُواْ حِزۡبَهُۥ لِيَكُونُواْ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلسَّعِيرِ
Ndithu satana ndi mdani wanu; choncho mchiteni kukhala mdani. Iye amaliitanira gulu lake kuti likhale gulu la anthu a ku Moto.[340]
[340] Allah watifotokozera kuti satana ndi mdani wathu wakalekale; iye ndi amene adatulutsitsa tate wathu Adam m’Munda wa mtendere pomulakwitsa. Ndipo iye adalumbira kuti adzapitiriza kutisokeretsa.
Esegesi in lingua araba:
ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَهُمۡ عَذَابٞ شَدِيدٞۖ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُم مَّغۡفِرَةٞ وَأَجۡرٞ كَبِيرٌ
Amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake), pa iwo padzakhala chilango chaukali; koma amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, iwo adzapeza chikhululuko ndi malipiro aakulu.
Esegesi in lingua araba:
أَفَمَن زُيِّنَ لَهُۥ سُوٓءُ عَمَلِهِۦ فَرَءَاهُ حَسَنٗاۖ فَإِنَّ ٱللَّهَ يُضِلُّ مَن يَشَآءُ وَيَهۡدِي مَن يَشَآءُۖ فَلَا تَذۡهَبۡ نَفۡسُكَ عَلَيۡهِمۡ حَسَرَٰتٍۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمُۢ بِمَا يَصۡنَعُونَ
Kodi amene zochita zake zoipa zakometsedwa kwa iye nkumaziona kuti nzabwino, (ngolingana ndi amene waongoka ndi chiongoko cha Allah kotero kuti chabwino nkuchiyesa chabwino; choipa nkuchiyesa choipa?) Ndithu Allah akumlekelera kuti asokere yemwe wamfuna (chifukwa chakuti safuna kuongoka), ndipo akuongola amene wam’funa. Choncho moyo wako usaonongeke chifukwa chowadandaula iwo. Ndithu Allah Ngodziwa zonse zimene (iwo) akuchita.
Esegesi in lingua araba:
وَٱللَّهُ ٱلَّذِيٓ أَرۡسَلَ ٱلرِّيَٰحَ فَتُثِيرُ سَحَابٗا فَسُقۡنَٰهُ إِلَىٰ بَلَدٖ مَّيِّتٖ فَأَحۡيَيۡنَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَاۚ كَذَٰلِكَ ٱلنُّشُورُ
Ndipo Allah ndiamene amatumiza mphepo; choncho imagwedeza mitambo (ya mvula) ndipo timaifikitsa ku dziko lakufa. Ndipo kupyolera m’madzi otuluka mmitamboyo; timaiwukitsa nthaka pambuyo pakufa kwake, momwemonso ndimmene kudzakhalira kutuluka akufa (m’manda tsiku la chiweruziro).
Esegesi in lingua araba:
مَن كَانَ يُرِيدُ ٱلۡعِزَّةَ فَلِلَّهِ ٱلۡعِزَّةُ جَمِيعًاۚ إِلَيۡهِ يَصۡعَدُ ٱلۡكَلِمُ ٱلطَّيِّبُ وَٱلۡعَمَلُ ٱلصَّٰلِحُ يَرۡفَعُهُۥۚ وَٱلَّذِينَ يَمۡكُرُونَ ٱلسَّيِّـَٔاتِ لَهُمۡ عَذَابٞ شَدِيدٞۖ وَمَكۡرُ أُوْلَٰٓئِكَ هُوَ يَبُورُ
Amene akufuna ulemelero, (amvere Allah), chifukwa ulemelero wonse ngwa Allah. Kwa Iye amakwera mawu abwino. Ndipo zochita zabwino ndi zimene zimakweza mawu abwinowo. Ndipo amene akuchita ndale zoipa, adzapeza chilango chaukali; ndipo ndale zawo nzoonongeka.
Esegesi in lingua araba:
وَٱللَّهُ خَلَقَكُم مِّن تُرَابٖ ثُمَّ مِن نُّطۡفَةٖ ثُمَّ جَعَلَكُمۡ أَزۡوَٰجٗاۚ وَمَا تَحۡمِلُ مِنۡ أُنثَىٰ وَلَا تَضَعُ إِلَّا بِعِلۡمِهِۦۚ وَمَا يُعَمَّرُ مِن مُّعَمَّرٖ وَلَا يُنقَصُ مِنۡ عُمُرِهِۦٓ إِلَّا فِي كِتَٰبٍۚ إِنَّ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرٞ
Ndipo Allah adakulengani ndi dothi; kenako ndi dontho la umuna; kenako adakupangani amuna ndi akazi. Ndipo mkazi aliyense satenga mimba ndiponso sabala koma kupyolera m’kudziwa Kwake (Allah). Ndipo amene wapatsidwa moyo, sapatsidwa moyo wautali ndiponso sachepetsedwa moyo wake, koma zonsezo zili m’buku (la Allah). Ndithu zimenezo kwa Allah nzosavuta.
Esegesi in lingua araba:
وَمَا يَسۡتَوِي ٱلۡبَحۡرَانِ هَٰذَا عَذۡبٞ فُرَاتٞ سَآئِغٞ شَرَابُهُۥ وَهَٰذَا مِلۡحٌ أُجَاجٞۖ وَمِن كُلّٖ تَأۡكُلُونَ لَحۡمٗا طَرِيّٗا وَتَسۡتَخۡرِجُونَ حِلۡيَةٗ تَلۡبَسُونَهَاۖ وَتَرَى ٱلۡفُلۡكَ فِيهِ مَوَاخِرَ لِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦ وَلَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ
Ndipo nyanja ziwiri (ya madzi ozizira ndi yamadzi amchere) sizili zofanana, iyi yamadzi okoma, ozuna, ndi omweka bwino kamwedwe kake; ndi iyi (ya madzi) amchere owawa. Ndipo kuchokera m’zonsezi, mumadya nyama yamatumbi (nsomba zaziwisi). Ndipo mumatulutsa zodzikongoletsera (zimene) mumazivala; ndipo m’menemo ukuona zombo zikung’amba madzi kuti mufunefune ubwino Wake (wa Allah) ndi kutinso inu muthokoze.
Esegesi in lingua araba:
يُولِجُ ٱلَّيۡلَ فِي ٱلنَّهَارِ وَيُولِجُ ٱلنَّهَارَ فِي ٱلَّيۡلِ وَسَخَّرَ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَۖ كُلّٞ يَجۡرِي لِأَجَلٖ مُّسَمّٗىۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡ لَهُ ٱلۡمُلۡكُۚ وَٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ مَا يَمۡلِكُونَ مِن قِطۡمِيرٍ
Amalowetsa usiku mu usana, ndi kulowetsa usana mu usiku; dzuwa ndi mwezi adazichita kuti zigonjere (malamulo Ake). Zonse zikuyenda (usana ndi usiku) kufikira nthawi yake yodziwika. Ameneyo ndi Allah, Mbuye wanu, Mwini ufumu. Ndipo amene mukuwapembedza, osati Iye, alibe ngakhale khoko la chipatso cha kanjedza.
Esegesi in lingua araba:
إِن تَدۡعُوهُمۡ لَا يَسۡمَعُواْ دُعَآءَكُمۡ وَلَوۡ سَمِعُواْ مَا ٱسۡتَجَابُواْ لَكُمۡۖ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ يَكۡفُرُونَ بِشِرۡكِكُمۡۚ وَلَا يُنَبِّئُكَ مِثۡلُ خَبِيرٖ
Ngati mutawapempha (mafanowo), sangamve kuitana kwanu, ndipo ngati atamva sangakuyankheni (chifukwa alibe kukhoza kulikonse). Ndipo pa tsiku lomalizira, adzakana kuphatikiza kwanu. Ndipo palibe (aliyense) angakuuze monga momwe akukuuzira (Allah) Wodziwa kwambiri.
Esegesi in lingua araba:
۞ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ أَنتُمُ ٱلۡفُقَرَآءُ إِلَى ٱللَّهِۖ وَٱللَّهُ هُوَ ٱلۡغَنِيُّ ٱلۡحَمِيدُ
E inu anthu! Inu ndiosaukira (chinthu chilichonse) kwa Allah; koma Allah Ngwachikwanekwane (sasaukira chilichonse kwa inu); Wotamandidwa (ndi zolengedwa zonse).
Esegesi in lingua araba:
إِن يَشَأۡ يُذۡهِبۡكُمۡ وَيَأۡتِ بِخَلۡقٖ جَدِيدٖ
Ngati atafuna angakuchotseni ndi kubweretsa zolengedwa zatsopano.
Esegesi in lingua araba:
وَمَا ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ بِعَزِيزٖ
Ndipo zimenezo sizili zovuta kwa Allah.
Esegesi in lingua araba:
وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٞ وِزۡرَ أُخۡرَىٰۚ وَإِن تَدۡعُ مُثۡقَلَةٌ إِلَىٰ حِمۡلِهَا لَا يُحۡمَلۡ مِنۡهُ شَيۡءٞ وَلَوۡ كَانَ ذَا قُرۡبَىٰٓۗ إِنَّمَا تُنذِرُ ٱلَّذِينَ يَخۡشَوۡنَ رَبَّهُم بِٱلۡغَيۡبِ وَأَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَۚ وَمَن تَزَكَّىٰ فَإِنَّمَا يَتَزَكَّىٰ لِنَفۡسِهِۦۚ وَإِلَى ٱللَّهِ ٱلۡمَصِيرُ
Ndipo wosenza, sadzasenza mtolo wa wina. (Aliyense adzasenza mtolo wa machimo ake). Ngakhale amene walemedwa ndi mtolo wake ataitana (wina) chifukwa cha mtolo wake kuti amsenzere silidzatengedwa ngakhale gawo pang’ono la mtolowo (ndi munthu ameneyo), ngakhale atakhala m’bale wake. Ndithu ukuchenjeza okhawo amene akuopa Mbuye wawo pomwe sakumuona, ndipo akupemphera Swala moyenera, ndipo yemwe akudziyeretsa, ndithu akudziyeretsa yekha, (ubwino wake umubwerera iye mwini); ndipo mabwelero (a zolengedwa zonse) ndi kwa Allah (basi).
Esegesi in lingua araba:
وَمَا يَسۡتَوِي ٱلۡأَعۡمَىٰ وَٱلۡبَصِيرُ
Ndipo wakhungu ndi wopenya ngosafanana, (woyenda pa njira ya choona ndi wosokera ngosafanana).
Esegesi in lingua araba:
وَلَا ٱلظُّلُمَٰتُ وَلَا ٱلنُّورُ
Ngakhale mdima ndi kuunika (nzosafanana).
Esegesi in lingua araba:
وَلَا ٱلظِّلُّ وَلَا ٱلۡحَرُورُ
Ngakhale mthunzi ndi kutentha (nzosafanana).
Esegesi in lingua araba:
وَمَا يَسۡتَوِي ٱلۡأَحۡيَآءُ وَلَا ٱلۡأَمۡوَٰتُۚ إِنَّ ٱللَّهَ يُسۡمِعُ مَن يَشَآءُۖ وَمَآ أَنتَ بِمُسۡمِعٖ مَّن فِي ٱلۡقُبُورِ
Ndipo amoyo ndi akufa safanana (amene mitima yawo ili ndi moyo pokhala ndi chikhulupiliro, ndi amene mitima yawo ili yakufa posakhala ndi chikhulupiliro, ngosafanana). Ndithu Allah akumumveretsa amene wam’funa; koma iwe sungathe kumumveretsa amene ali m’manda.
Esegesi in lingua araba:
إِنۡ أَنتَ إِلَّا نَذِيرٌ
Iwe sindiwe chinthu china, koma ndiwe mchenjezi.
Esegesi in lingua araba:
إِنَّآ أَرۡسَلۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ بَشِيرٗا وَنَذِيرٗاۚ وَإِن مِّنۡ أُمَّةٍ إِلَّا خَلَا فِيهَا نَذِيرٞ
Ndithu Ife takutuma mwachoona kuti unene nkhani yabwino (yokalowa ku Munda wamtendere kwa amene akhulupirira), ndi kuti uchenjeze (za chilango cha Moto kwa amene sadakhulupirire). Ndipo palibe m’badwo uliwonse koma mchenjezi adapitamo.
Esegesi in lingua araba:
وَإِن يُكَذِّبُوكَ فَقَدۡ كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ جَآءَتۡهُمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ وَبِٱلزُّبُرِ وَبِٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُنِيرِ
Ndipo ngati angakutsutse (sichachilendo), ndithu amene adali patsogolo pawo adatsutsanso. Aneneri awo adawadzera ndi zizindikiro zoonekera poyera, ndi malemba ndi buku lounikira (njira yabwino).
Esegesi in lingua araba:
ثُمَّ أَخَذۡتُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۖ فَكَيۡفَ كَانَ نَكِيرِ
Kenako ndidawalanga (ndidawaononga) amene adatsutsa. Nanga chidali bwanji chilango Changa (pa iwo).
Esegesi in lingua araba:
أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَخۡرَجۡنَا بِهِۦ ثَمَرَٰتٖ مُّخۡتَلِفًا أَلۡوَٰنُهَاۚ وَمِنَ ٱلۡجِبَالِ جُدَدُۢ بِيضٞ وَحُمۡرٞ مُّخۡتَلِفٌ أَلۡوَٰنُهَا وَغَرَابِيبُ سُودٞ
Kodi sudaone kuti Allah amatsitsa madzi kuchokera ku mitambo? Choncho kupyolera m’madziwo tatulutsa zipatso zautoto wosiyanasiyana (zakuda, zofiira, zachikasu, zobiriwira, pomwe madzi ake ndiamodzi omwewo). Ndipo m’mapiri muli timizere; toyera ndi tofiira tosiyana utoto wake, ndi (tina) takuda kwambiri.
Esegesi in lingua araba:
وَمِنَ ٱلنَّاسِ وَٱلدَّوَآبِّ وَٱلۡأَنۡعَٰمِ مُخۡتَلِفٌ أَلۡوَٰنُهُۥ كَذَٰلِكَۗ إِنَّمَا يَخۡشَى ٱللَّهَ مِنۡ عِبَادِهِ ٱلۡعُلَمَٰٓؤُاْۗ إِنَّ ٱللَّهَ عَزِيزٌ غَفُورٌ
Ndipo mwa anthu ndi nyama zokwawa, ndi ziweto, nchimodzimodzinso; nzosiyana maonekedwe ake (utoto wake). Ndithu odziwa ndi amene amamuopa Allah mwa akapolo Ake. Ndithu Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngokhululuka kwambiri.
Esegesi in lingua araba:
إِنَّ ٱلَّذِينَ يَتۡلُونَ كِتَٰبَ ٱللَّهِ وَأَقَامُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَأَنفَقُواْ مِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ سِرّٗا وَعَلَانِيَةٗ يَرۡجُونَ تِجَٰرَةٗ لَّن تَبُورَ
Ndithu amene akuwerenga buku la Allah uku nkumapemphera Swala moyenera napereka m’zimene tawapatsa mwanseri ndi moonetsera, iwo akuyembekezera malonda osaonongeka.
Esegesi in lingua araba:
لِيُوَفِّيَهُمۡ أُجُورَهُمۡ وَيَزِيدَهُم مِّن فَضۡلِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ غَفُورٞ شَكُورٞ
Kuti akawakwaniritsire malipiro awo ndi kuwaonjezera zabwino Zake; ndithu Iye Ngokhululuka kwabasi; Ngothokoza kwambiri.
Esegesi in lingua araba:
وَٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ مِنَ ٱلۡكِتَٰبِ هُوَ ٱلۡحَقُّ مُصَدِّقٗا لِّمَا بَيۡنَ يَدَيۡهِۗ إِنَّ ٱللَّهَ بِعِبَادِهِۦ لَخَبِيرُۢ بَصِيرٞ
Ndipo buku limene takuvumbulutsira, nloona; likutsimikizira za mabuku omwe adali patsogolo pake. Ndithu Allah kwa akapolo Ake Ngodziwa kwambiri ndiponso akuwaona bwino.
Esegesi in lingua araba:
ثُمَّ أَوۡرَثۡنَا ٱلۡكِتَٰبَ ٱلَّذِينَ ٱصۡطَفَيۡنَا مِنۡ عِبَادِنَاۖ فَمِنۡهُمۡ ظَالِمٞ لِّنَفۡسِهِۦ وَمِنۡهُم مُّقۡتَصِدٞ وَمِنۡهُمۡ سَابِقُۢ بِٱلۡخَيۡرَٰتِ بِإِذۡنِ ٱللَّهِۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَضۡلُ ٱلۡكَبِيرُ
Kenako tidawapatsa buku (Qur’an) amene tidawasankha mwa akapolo Athu, koma alipo ena mwa iwo odzichitira okha chinyengo (pochulukitsa machimo), ena mwa iwo ngaapakatikati; ndipo ena mwa iwo ngopikisana pochita zabwino mwa chifuniro cha Allah. Kuteroko ndiwo ubwino waukulu.
Esegesi in lingua araba:
جَنَّٰتُ عَدۡنٖ يَدۡخُلُونَهَا يُحَلَّوۡنَ فِيهَا مِنۡ أَسَاوِرَ مِن ذَهَبٖ وَلُؤۡلُؤٗاۖ وَلِبَاسُهُمۡ فِيهَا حَرِيرٞ
Adzailowa minda yamuyaya; m’menemo adzakongoletsedwa povekedwa zibangiri zagolide ndi ngale; nsalu ya silika ndicho chovala chawo m’menemo.
Esegesi in lingua araba:
وَقَالُواْ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِيٓ أَذۡهَبَ عَنَّا ٱلۡحَزَنَۖ إِنَّ رَبَّنَا لَغَفُورٞ شَكُورٌ
Ndipo adzanena (pakuthokoza kwawo): “Kutamandidwa konse nkwa Allah Amene watichotsera madandaulo; ndithu Mbuye wathu Ngokhululuka kwambiri, Ngothokoza kwabasi.”
Esegesi in lingua araba:
ٱلَّذِيٓ أَحَلَّنَا دَارَ ٱلۡمُقَامَةِ مِن فَضۡلِهِۦ لَا يَمَسُّنَا فِيهَا نَصَبٞ وَلَا يَمَسُّنَا فِيهَا لُغُوبٞ
“Yemwe, chifukwa cha ubwino Wake, watikhazika m’nyumba yamuyaya; m’menemo mavuto satikhudza, ndiponso m’menemo kutopa sikutikhudza.”
Esegesi in lingua araba:
وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَهُمۡ نَارُ جَهَنَّمَ لَا يُقۡضَىٰ عَلَيۡهِمۡ فَيَمُوتُواْ وَلَا يُخَفَّفُ عَنۡهُم مِّنۡ عَذَابِهَاۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي كُلَّ كَفُورٖ
Koma amene sadakhulupirire, wawo ndi moto wa Jahannam sikudzaweruzidwa kwa iwo kuti afe, ngakhale chilango chake sichidzachepetsedwa pa iwo. Umo ndimmene tikumlipirira aliyense wokanira (mtendere wa Allah).
Esegesi in lingua araba:
وَهُمۡ يَصۡطَرِخُونَ فِيهَا رَبَّنَآ أَخۡرِجۡنَا نَعۡمَلۡ صَٰلِحًا غَيۡرَ ٱلَّذِي كُنَّا نَعۡمَلُۚ أَوَلَمۡ نُعَمِّرۡكُم مَّا يَتَذَكَّرُ فِيهِ مَن تَذَكَّرَ وَجَآءَكُمُ ٱلنَّذِيرُۖ فَذُوقُواْ فَمَا لِلظَّٰلِمِينَ مِن نَّصِيرٍ
Ndipo m’menemo iwo adzakuwa (adzalira uku akunena): “Mbuye wathu! Titulutseni (m’Moto ndi kutibweza pa dziko lapansi); tikachita ntchito zabwino, osati zija tinkachita.” (Allah adzawauza): “Kodi sitidakupatseni moyo wokwanira wotheka kukumbuka kwa wokumbuka? Ndiponso mchenjezi adakudzerani. Choncho lawani (chilango). Ndipo anthu ochita zoipa alibe mpulumutsi.”
Esegesi in lingua araba:
إِنَّ ٱللَّهَ عَٰلِمُ غَيۡبِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ إِنَّهُۥ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ
Ndithu Allah Ngodziwa zobisika za kumwamba ndi za pansi. Iye Ngodziwa kwambiri za m’zifuwa.
Esegesi in lingua araba:
هُوَ ٱلَّذِي جَعَلَكُمۡ خَلَٰٓئِفَ فِي ٱلۡأَرۡضِۚ فَمَن كَفَرَ فَعَلَيۡهِ كُفۡرُهُۥۖ وَلَا يَزِيدُ ٱلۡكَٰفِرِينَ كُفۡرُهُمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ إِلَّا مَقۡتٗاۖ وَلَا يَزِيدُ ٱلۡكَٰفِرِينَ كُفۡرُهُمۡ إِلَّا خَسَارٗا
Iye ndi Yemwe wakuchitani kukhala osiyirana pa dziko lapansi (akufa ena, ena nkulowa m’malo mwawo). Ndipo amene sadakhulupirire, kuipa kwa kusakhulupirirako kuli kwa iye mwini. Ndipo kusakhulupirira kwa osakhulupirira sikuwaonjezera chilichonse kwa Mbuye wawo, koma mkwiyo basi. Ndiponso kusakhulupirira kwa osakhulupirira sikuwaonjezera chilichonse, koma kutayika basi.
Esegesi in lingua araba:
قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ شُرَكَآءَكُمُ ٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَرُونِي مَاذَا خَلَقُواْ مِنَ ٱلۡأَرۡضِ أَمۡ لَهُمۡ شِرۡكٞ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ أَمۡ ءَاتَيۡنَٰهُمۡ كِتَٰبٗا فَهُمۡ عَلَىٰ بَيِّنَتٖ مِّنۡهُۚ بَلۡ إِن يَعِدُ ٱلظَّٰلِمُونَ بَعۡضُهُم بَعۡضًا إِلَّا غُرُورًا
Nena: “Kodi mwawaona aphatikizi anu (awa) amene mukuwapembedza m’malo mwa Allah? Tandionetsani, ndimbali iti ya nthaka adalenga; kapena iwo ali ndi gawo m’thambo; (gawo lakulenga thambo?) Kapena tidawapatsa buku (Qur’an iyi isadadze) kotero kuti ali ndi umboni wapoyera wochokera m’menemo (wotsimikizira chipembedzo chawo chamafano)? Koma ochita zoipa salonjezana ena kwa ena china chake koma zachinyengo basi.
Esegesi in lingua araba:
۞ إِنَّ ٱللَّهَ يُمۡسِكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ أَن تَزُولَاۚ وَلَئِن زَالَتَآ إِنۡ أَمۡسَكَهُمَا مِنۡ أَحَدٖ مِّنۢ بَعۡدِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ كَانَ حَلِيمًا غَفُورٗا
Ndithu Allah amagwira thambo ndi nthaka kuti zisachoke. Ndipo ngati zitachoka, palibe aliyense amene angazigwire kupatula Iye. Ndithu Iye Ngoleza; Ngokhululuka kwabasi.
Esegesi in lingua araba:
وَأَقۡسَمُواْ بِٱللَّهِ جَهۡدَ أَيۡمَٰنِهِمۡ لَئِن جَآءَهُمۡ نَذِيرٞ لَّيَكُونُنَّ أَهۡدَىٰ مِنۡ إِحۡدَى ٱلۡأُمَمِۖ فَلَمَّا جَآءَهُمۡ نَذِيرٞ مَّا زَادَهُمۡ إِلَّا نُفُورًا
Ndipo (awa osakhulupirira, kale) adalumbilira Allah, kulumbira kwawo kwakukulu, kuti ngati adzawadzera mchenjezi, adzakhala oongoka kuposa mbadwo uliwonse. Koma pamene mchenjezi adawadzera, palibe chilichonse chidaonjezeka kwa iwo, koma kukana (choonadicho).
Esegesi in lingua araba:
ٱسۡتِكۡبَارٗا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَكۡرَ ٱلسَّيِّيِٕۚ وَلَا يَحِيقُ ٱلۡمَكۡرُ ٱلسَّيِّئُ إِلَّا بِأَهۡلِهِۦۚ فَهَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّا سُنَّتَ ٱلۡأَوَّلِينَۚ فَلَن تَجِدَ لِسُنَّتِ ٱللَّهِ تَبۡدِيلٗاۖ وَلَن تَجِدَ لِسُنَّتِ ٱللَّهِ تَحۡوِيلًا
Chifukwa cha kudzikweza pa dziko ndi kuchita chiwembu choipa. Ndipo chiwembu choipa sichingamuzinge aliyense koma mwini (yemwe) wachitayo. Kodi akuyembekeza china chosakhala machitidwe (a Allah) amene adawapititsa pa anthu akale. Koma supeza kusintha pa machitidwe a Allah. Ndipo supeza kutembenuka pa machitidwe a Allah.
Esegesi in lingua araba:
أَوَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ وَكَانُوٓاْ أَشَدَّ مِنۡهُمۡ قُوَّةٗۚ وَمَا كَانَ ٱللَّهُ لِيُعۡجِزَهُۥ مِن شَيۡءٖ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَلَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ إِنَّهُۥ كَانَ عَلِيمٗا قَدِيرٗا
Kodi sadayende pa dziko nkuona momwe adalili mathero a omwe adali patsogolo pawo? Ndipo adali anyonga kwambiri kuposa iwo? Ndipo palibe chinthu chonkanika Allah kumwamba ndi pansi. Ndithudi Iye Ngodziwa kwabasi Wokhoza.
Esegesi in lingua araba:
وَلَوۡ يُؤَاخِذُ ٱللَّهُ ٱلنَّاسَ بِمَا كَسَبُواْ مَا تَرَكَ عَلَىٰ ظَهۡرِهَا مِن دَآبَّةٖ وَلَٰكِن يُؤَخِّرُهُمۡ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗىۖ فَإِذَا جَآءَ أَجَلُهُمۡ فَإِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِعِبَادِهِۦ بَصِيرَۢا
Ndipo Allah akadamalanga anthu chifukwa cha zomwe alakwa, sakadasiya pamwamba pake (pa nthaka) chamoyo chilichonse; koma Iye amawalekelera mpaka nthawi yomwe adaiikayo. Choncho nthawi yawo ikadzawadzera, (pompo adzalangidwa). Ndithu Allah akuwadziwa bwino akapolo Ake.
Esegesi in lingua araba:
 
Traduzione dei significati Sura: Fâtir
Indice delle Sure Numero di pagina
 
Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa - Indice Traduzioni

Traduzione dei significati del Nobile Corano in lingua chicheŵa, a cura di Khaled Ibrahim Beitala، ed. 2020

Chiudi