クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 * - 対訳の目次


対訳 章: 人間章   節:

人間章

هَلۡ أَتَىٰ عَلَى ٱلۡإِنسَٰنِ حِينٞ مِّنَ ٱلدَّهۡرِ لَمۡ يَكُن شَيۡـٔٗا مَّذۡكُورًا
Ndithu munthu idampita nthawi yaitali kwambiri (asanauziridwe mzimu) pomwe sadali chinthu chotchulidwa.
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّا خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِن نُّطۡفَةٍ أَمۡشَاجٖ نَّبۡتَلِيهِ فَجَعَلۡنَٰهُ سَمِيعَۢا بَصِيرًا
Ndithu Ife tamlenga munthu kuchokera ku mbewu ya munthu yosakanikirana (ya mkazi ndi ya mwamuna) kuti timuyese mayeso (ndi malamulo Athu); choncho tidampanga kukhala wakumva ndi wopenya; (amve mawu a Allah ndi kuti aone zisonyezo Zake).
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّا هَدَيۡنَٰهُ ٱلسَّبِيلَ إِمَّا شَاكِرٗا وَإِمَّا كَفُورًا
Ndithu Ife tidamlongosolera njira yoongoka: kukhala wokhulupirira kapena wotsutsa (Zonse zili kwa iye).
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّآ أَعۡتَدۡنَا لِلۡكَٰفِرِينَ سَلَٰسِلَاْ وَأَغۡلَٰلٗا وَسَعِيرًا
Ndithu Ife okana tawakonzera unyolo (wam’miyendo yawo) ndi magoli (am’manja ndi m’makosi awo) ndi Moto waukali woyaka.
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّ ٱلۡأَبۡرَارَ يَشۡرَبُونَ مِن كَأۡسٖ كَانَ مِزَاجُهَا كَافُورًا
Ndithu ochita zabwino adzamwa vinyo, chosakanizira chake chidzakhala (madzi a) kaafura.
アラビア語 クルアーン注釈:
عَيۡنٗا يَشۡرَبُ بِهَا عِبَادُ ٱللَّهِ يُفَجِّرُونَهَا تَفۡجِيرٗا
(Kaafura ameneyo) ndikasupe amene adzikamwapo akapolo a Allah ndi kumtulutsa (paliponse pamene afuna) kumtulutsa mofewa.
アラビア語 クルアーン注釈:
يُوفُونَ بِٱلنَّذۡرِ وَيَخَافُونَ يَوۡمٗا كَانَ شَرُّهُۥ مُسۡتَطِيرٗا
(Amene) akukwaniritsa zimene adalonjeza (okha kwa Allah), ndiponso akuopa tsiku (lalikulu) limene zoipa zake zidzakhala zofalikira ponseponse.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَيُطۡعِمُونَ ٱلطَّعَامَ عَلَىٰ حُبِّهِۦ مِسۡكِينٗا وَيَتِيمٗا وَأَسِيرًا
Ndipo amadyetsa chakudya masikini, amasiye ndi ogwidwa pa nkhondo, pomwe iwo akuchifunanso.
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّمَا نُطۡعِمُكُمۡ لِوَجۡهِ ٱللَّهِ لَا نُرِيدُ مِنكُمۡ جَزَآءٗ وَلَا شُكُورًا
Amanena (chamumtima akamapereka chakudyacho): “Tikukudyetsani chifukwa chofuna chikondi cha Allah basi; sitikufuna kwa inu malipiro kapena kuthokoza.
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّا نَخَافُ مِن رَّبِّنَا يَوۡمًا عَبُوسٗا قَمۡطَرِيرٗا
Ndithu ife tikuopa kwa Mbuye wathu tsiku lokhwinyata nkhope ndi mavuto akulu.”
アラビア語 クルアーン注釈:
فَوَقَىٰهُمُ ٱللَّهُ شَرَّ ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمِ وَلَقَّىٰهُمۡ نَضۡرَةٗ وَسُرُورٗا
Ndipo Allah adzawateteza mu mavuto a tsiku limenelo ndiponso adzawapatsa mtendere ndi chisangalalo.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَجَزَىٰهُم بِمَا صَبَرُواْ جَنَّةٗ وَحَرِيرٗا
Ndipo adzawalipira chifukwa cha kupirira kwawo Munda wamtendere ndi nsalu zaveleveti.
アラビア語 クルアーン注釈:
مُّتَّكِـِٔينَ فِيهَا عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِۖ لَا يَرَوۡنَ فِيهَا شَمۡسٗا وَلَا زَمۡهَرِيرٗا
Atatsamira m’menemo pa makama (amtengo wapatali); sadzamva m’menemo kutentha kwa dzuwa kapena kuzizira.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَدَانِيَةً عَلَيۡهِمۡ ظِلَٰلُهَا وَذُلِّلَتۡ قُطُوفُهَا تَذۡلِيلٗا
Mithunzi yake ikawayandikira iwo ndipo mikoko yazipatso idzatewa pafupi (moti munthu atha kuthyola ali chigonere).
アラビア語 クルアーン注釈:
وَيُطَافُ عَلَيۡهِم بِـَٔانِيَةٖ مِّن فِضَّةٖ وَأَكۡوَابٖ كَانَتۡ قَوَارِيرَا۠
Ndipo adzakhala akuzunguliridwa (ndi otumikira) uku atatenga zomwera za siliva ndi matambula onyezimira ndiponso olangala.
アラビア語 クルアーン注釈:
قَوَارِيرَاْ مِن فِضَّةٖ قَدَّرُوهَا تَقۡدِيرٗا
Zolangala zopangidwa ku siliva, atalinga bwino zakumwazo (malinga ndi kufuna kwawo).
アラビア語 クルアーン注釈:
وَيُسۡقَوۡنَ فِيهَا كَأۡسٗا كَانَ مِزَاجُهَا زَنجَبِيلًا
Ndipo (anthu abwino) akamwetsedwa kumeneko vinyo, chosakanizira chake chikafanana ndi Zanjabila (chikasu).
アラビア語 クルアーン注釈:
عَيۡنٗا فِيهَا تُسَمَّىٰ سَلۡسَبِيلٗا
M’menemo muli kasupe wotchedwa Salisabila,
アラビア語 クルアーン注釈:
۞ وَيَطُوفُ عَلَيۡهِمۡ وِلۡدَٰنٞ مُّخَلَّدُونَ إِذَا رَأَيۡتَهُمۡ حَسِبۡتَهُمۡ لُؤۡلُؤٗا مَّنثُورٗا
Ndipo azikawazungulira anyamata osasinthika (chilengedwe chawo,) utawaona (chifukwa cha kukongola kwawo ndi kuwala kwa nkhope zawo) ungawaganizire kuti ndi ngale zomwazidwa.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَإِذَا رَأَيۡتَ ثَمَّ رَأَيۡتَ نَعِيمٗا وَمُلۡكٗا كَبِيرًا
Ndipo ukadzaona kumeneko (ku Jannah) ukaona mtendere ndi ufumu waukulu.
アラビア語 クルアーン注釈:
عَٰلِيَهُمۡ ثِيَابُ سُندُسٍ خُضۡرٞ وَإِسۡتَبۡرَقٞۖ وَحُلُّوٓاْ أَسَاوِرَ مِن فِضَّةٖ وَسَقَىٰهُمۡ رَبُّهُمۡ شَرَابٗا طَهُورًا
Pamwamba pawo padzakhala nsalu zaveleveti zopyapyala, zobiriwira ndi nsalu zaveleveti zochindikala, akavekedwa m’manja mwawo zibangiri zasiliva; Mbuye wawo akawamwetsa chakumwa china choyera kwambiri.
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّ هَٰذَا كَانَ لَكُمۡ جَزَآءٗ وَكَانَ سَعۡيُكُم مَّشۡكُورًا
(Akawauza kuti:) “Ndithu iyi ndi mphoto yanu ndipo ntchito zanu ndi zolandiridwa.”
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّا نَحۡنُ نَزَّلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡقُرۡءَانَ تَنزِيلٗا
Ndithu Ife taivumbulutsa kwa iwe Qur’an mwapang’onopang’ono (kuti uisunge bwino, usaiwale).
アラビア語 クルアーン注釈:
فَٱصۡبِرۡ لِحُكۡمِ رَبِّكَ وَلَا تُطِعۡ مِنۡهُمۡ ءَاثِمًا أَوۡ كَفُورٗا
Choncho, pirira ndi lamulo la Mbuye wako ndipo usamvere wamachimo kapena wokanira aliyense mwa iwo.
アラビア語 クルアーン注釈:
وَٱذۡكُرِ ٱسۡمَ رَبِّكَ بُكۡرَةٗ وَأَصِيلٗا
Ndipo kumbukira dzina la Mbuye wako; mmawa, ndi madzulo (Swala za Subuhi, Dhuhr ndi Asri).
アラビア語 クルアーン注釈:
وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَٱسۡجُدۡ لَهُۥ وَسَبِّحۡهُ لَيۡلٗا طَوِيلًا
Ndipo usiku mlambire Iye, (Swala ya Maghrib ndi Isha); ndiponso umulemekeze usiku nthawi yaitali (popemphera sunna za tahajjudi).
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ يُحِبُّونَ ٱلۡعَاجِلَةَ وَيَذَرُونَ وَرَآءَهُمۡ يَوۡمٗا ثَقِيلٗا
Ndithu awa akukonda moyo wa dziko lapansi, ndipo akulisiya kumbuyo kwao tsiku lovuta.
アラビア語 クルアーン注釈:
نَّحۡنُ خَلَقۡنَٰهُمۡ وَشَدَدۡنَآ أَسۡرَهُمۡۖ وَإِذَا شِئۡنَا بَدَّلۡنَآ أَمۡثَٰلَهُمۡ تَبۡدِيلًا
Ife ndi amene tidawalenga ndipo tidalimbika kalengedwe kawo; ndipo titafuna tingabweretse ena onga iwo (omvera Allah) kulowa m’malo mwawo.
アラビア語 クルアーン注釈:
إِنَّ هَٰذِهِۦ تَذۡكِرَةٞۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ سَبِيلٗا
Ndithu ichi ndichikumbutso choncho amene afuna atsata njira yopitira kwa Mbuye wake (pomukhulupirira ndi kumumvera).
アラビア語 クルアーン注釈:
وَمَا تَشَآءُونَ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلِيمًا حَكِيمٗا
Koma simungafune nokha chilichonse pokhapokha atafuna Allah, ndithu Allah ndi Wodziwa zedi, Wanzeru zakuya.
アラビア語 クルアーン注釈:
يُدۡخِلُ مَن يَشَآءُ فِي رَحۡمَتِهِۦۚ وَٱلظَّٰلِمِينَ أَعَدَّ لَهُمۡ عَذَابًا أَلِيمَۢا
Akumlowetsa amene wamfuna ku chifundo Chake; koma oyipa wawalinganizira chilango chowawa kwambiri.
アラビア語 クルアーン注釈:
 
対訳 章: 人間章
章名の目次 ページ番号
 
クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - 対訳の目次

クルアーン・チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

閉じる