വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ പരിഭാഷ * - വിവർത്തനങ്ങളുടെ സൂചിക


പരിഭാഷ അദ്ധ്യായം: സൂറത്തുൽ ഖസസ്   ആയത്ത്:

സൂറത്തുൽ ഖസസ്

طسٓمٓ
Tâ-Sîn-Mîm.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ
Izi ndi Ayah (ndime) za m’buku (la Qur’an) lofotokoza (chilichonse chofunika pa Chipembedzo).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
نَتۡلُواْ عَلَيۡكَ مِن نَّبَإِ مُوسَىٰ وَفِرۡعَوۡنَ بِٱلۡحَقِّ لِقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ
Tikukulakatulira (iwe Mtumiki) nkhani za Mûsa ndi Farawo m’njira yoona kwa anthu okhulupirira. (Koma osakhulupirira sangapindule kanthu ndi nkhanizi).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
إِنَّ فِرۡعَوۡنَ عَلَا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَجَعَلَ أَهۡلَهَا شِيَعٗا يَسۡتَضۡعِفُ طَآئِفَةٗ مِّنۡهُمۡ يُذَبِّحُ أَبۡنَآءَهُمۡ وَيَسۡتَحۡيِۦ نِسَآءَهُمۡۚ إِنَّهُۥ كَانَ مِنَ ٱلۡمُفۡسِدِينَ
Ndithu Farawo adadzikuza pa dziko, ndipo adawakhazika (anthu a m’dzikolo) m’magulumagulu; gulu lina la mwa iwo adalifooketsa (poliyesa akapolo) ndi kupha ana awo achimuna, ndi kuwasiya a moyo ana awo achikazi. Ndithu iye adali mmodzi wa oononga kwambiri.[297]
[297] Farawo adauzidwa ndi mlosi kuti kudzabadwa mwana mwa Aisraeli wamwamuna yemwe adzathetsa ufumu wake. Pamene adamva izi adalamula kuti makanda onse achimuna a Aisraeli aphedwe. Choncho ana amuna ongobadwa kumene amaphedwa.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَنُرِيدُ أَن نَّمُنَّ عَلَى ٱلَّذِينَ ٱسۡتُضۡعِفُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَنَجۡعَلَهُمۡ أَئِمَّةٗ وَنَجۡعَلَهُمُ ٱلۡوَٰرِثِينَ
Ndipo tidafuna kuwachitira zabwino amene adafooketsedwa m’dziko (la Iguputo), ndi kuwachita kukhala atsogoleri ndi kuwachitanso kukhala amlowa mmalo ( a Baiti Al-Makadasi).[298]
[298] Chimene Allah wafuna chimachitika ngakhale anthu atayesetsa m’njira izi ndi izi kuti achizembe.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَنُمَكِّنَ لَهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَنُرِيَ فِرۡعَوۡنَ وَهَٰمَٰنَ وَجُنُودَهُمَا مِنۡهُم مَّا كَانُواْ يَحۡذَرُونَ
Ndi kuwapatsa mphamvu za pa dziko (kuti azichita mmene angafunire) ndi kuti timuonetse Farawo ndi Hamana ndi magulu awo ankhondo kuchokera kwa iwo (ana a Israel), zomwe amaziwopa (kuti zingawathetsere ufumu wawo).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰٓ أُمِّ مُوسَىٰٓ أَنۡ أَرۡضِعِيهِۖ فَإِذَا خِفۡتِ عَلَيۡهِ فَأَلۡقِيهِ فِي ٱلۡيَمِّ وَلَا تَخَافِي وَلَا تَحۡزَنِيٓۖ إِنَّا رَآدُّوهُ إِلَيۡكِ وَجَاعِلُوهُ مِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Ndipo tidamzindikiritsa mayi wa Mûsa (tinati): “Muyamwitse (mwana wako), ndipo ukamuopera (chiwembu cha Farawo), mponye mu mtsinje usaope, ndipo usadandaule ndithu Ife tidzamubwezera kwa iwe, ndipo tidzamchita kukhala mmodzi wa atumiki.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَٱلۡتَقَطَهُۥٓ ءَالُ فِرۡعَوۡنَ لِيَكُونَ لَهُمۡ عَدُوّٗا وَحَزَنًاۗ إِنَّ فِرۡعَوۡنَ وَهَٰمَٰنَ وَجُنُودَهُمَا كَانُواْ خَٰطِـِٔينَ
Choncho adamtola anthu a Farawo kuti mapeto ake adzakhale m’dani kwa iwo ndi odandaulitsa. Ndithu Farawo ndi Hamana ndi magulu awo ankhondo adali olakwa.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَقَالَتِ ٱمۡرَأَتُ فِرۡعَوۡنَ قُرَّتُ عَيۡنٖ لِّي وَلَكَۖ لَا تَقۡتُلُوهُ عَسَىٰٓ أَن يَنفَعَنَآ أَوۡ نَتَّخِذَهُۥ وَلَدٗا وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ
Ndipo mkazi wa Farawo adati: “(Musamuphe, akhale) chosangalatsa diso langa ndi lako; musamuphe mwina angatithandize, kapena tingam’chite kukhala mwana (wathu.” Adanena izi) iwo asakudziwa (kuti adzakhala m’dani wawo).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَأَصۡبَحَ فُؤَادُ أُمِّ مُوسَىٰ فَٰرِغًاۖ إِن كَادَتۡ لَتُبۡدِي بِهِۦ لَوۡلَآ أَن رَّبَطۡنَا عَلَىٰ قَلۡبِهَا لِتَكُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndipo mu mtima mwa mayi wa Mûsa mudali mopanda kanthu (mudalibe maganizo ena koma maganizo a mwana wake). Padatsala pang’ono kuti aonetse (chinsinsi cha mwanayo ponena kuti adali mwana wake), tikadapanda kulimbitsa mtima wake, kuti akhale mmodzi mwa okhulupirira (lonjezo la Allah).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَقَالَتۡ لِأُخۡتِهِۦ قُصِّيهِۖ فَبَصُرَتۡ بِهِۦ عَن جُنُبٖ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ
Ndipo (mayi wa Musayo) adauza mlongo wake (wa Mûsa): “Mtsatire, (komwe madzi akupita naye).” Choncho iye ankamuyang’ana chapatali pomwe iwo samadziwa (za ichi).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
۞ وَحَرَّمۡنَا عَلَيۡهِ ٱلۡمَرَاضِعَ مِن قَبۡلُ فَقَالَتۡ هَلۡ أَدُلُّكُمۡ عَلَىٰٓ أَهۡلِ بَيۡتٖ يَكۡفُلُونَهُۥ لَكُمۡ وَهُمۡ لَهُۥ نَٰصِحُونَ
Ndipo poyamba tidamuletsa kuti asayamwe mawere a woyamwitsa, (kufikira pomwe mlongo wake) adati: “Kodi ndikusonyezeni eni nyumba omwe angakulelereni ndi kukhala naye momteteza bwino mwanayo?”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَرَدَدۡنَٰهُ إِلَىٰٓ أُمِّهِۦ كَيۡ تَقَرَّ عَيۡنُهَا وَلَا تَحۡزَنَ وَلِتَعۡلَمَ أَنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
Choncho tidamubwezera kwa mayi wake kuti maso ake atonthole, (mtima wake ukhazikike) ndi kuti asadandaule; ndi kuti adziwe kuti lonjezo la Allah ndi loona. Koma ambiri a iwo sadziwa.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَلَمَّا بَلَغَ أَشُدَّهُۥ وَٱسۡتَوَىٰٓ ءَاتَيۡنَٰهُ حُكۡمٗا وَعِلۡمٗاۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
Ndipo (Mûsa) pamene adakula nsinkhu wake ndi kulingana bwino tidampatsa nzeru ndi maphunziro. Ndipo umo ndimomwe timawalipirira ochita zabwino.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَدَخَلَ ٱلۡمَدِينَةَ عَلَىٰ حِينِ غَفۡلَةٖ مِّنۡ أَهۡلِهَا فَوَجَدَ فِيهَا رَجُلَيۡنِ يَقۡتَتِلَانِ هَٰذَا مِن شِيعَتِهِۦ وَهَٰذَا مِنۡ عَدُوِّهِۦۖ فَٱسۡتَغَٰثَهُ ٱلَّذِي مِن شِيعَتِهِۦ عَلَى ٱلَّذِي مِنۡ عَدُوِّهِۦ فَوَكَزَهُۥ مُوسَىٰ فَقَضَىٰ عَلَيۡهِۖ قَالَ هَٰذَا مِنۡ عَمَلِ ٱلشَّيۡطَٰنِۖ إِنَّهُۥ عَدُوّٞ مُّضِلّٞ مُّبِينٞ
Ndipo (tsiku lina) adalowa mu mzinda mozemba, eni m’zindawo osadziwa. Ndipo adapeza m’menemo anthu awiri akumenyana, mmodzi wochokera ku gulu lake, ndipo winayo wochokera kwa adani ake. Tsono wa kugulu lake uja adampempha chithandizo pa mdani wake uja, ndipo Mûsa adammenya chibagera mpaka kumupha (mdaniyo). Adanena: “Iyi (ndachitayi) ndintchito ya satana; ndithu iye ndimdani wosokeretsa, woonekera.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قَالَ رَبِّ إِنِّي ظَلَمۡتُ نَفۡسِي فَٱغۡفِرۡ لِي فَغَفَرَ لَهُۥٓۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ
Adati: “E Mbuye wanga! Ndithu ndadzichitira zoipa ndekha! Choncho ndikhululukireni!” Tero (Allah) adamkhululukira (chifukwa sadalinge kupha). Ndithu Iye (Allah) Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قَالَ رَبِّ بِمَآ أَنۡعَمۡتَ عَلَيَّ فَلَنۡ أَكُونَ ظَهِيرٗا لِّلۡمُجۡرِمِينَ
Adati: “E Mbuye wanga! Chifukwa cha kuti mwandidalitsa, sindidzakhala mthangati wa oipa.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَأَصۡبَحَ فِي ٱلۡمَدِينَةِ خَآئِفٗا يَتَرَقَّبُ فَإِذَا ٱلَّذِي ٱسۡتَنصَرَهُۥ بِٱلۡأَمۡسِ يَسۡتَصۡرِخُهُۥۚ قَالَ لَهُۥ مُوسَىٰٓ إِنَّكَ لَغَوِيّٞ مُّبِينٞ
Choncho kudamuchera mu mzindamo (m’mawa mwake) uku ali wodzazidwa ndi mantha akuyembekezera (kuti chiyani chimpeze pa zimene zidachitika); pompo munthu uja adampempha dzulo chithandizo ankamuitana (kuti amthandize kumenyana ndi m’dani wake wina). Mûsa adamuuza: “Ndithudi ndiwe wopotoka owonekera.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَلَمَّآ أَنۡ أَرَادَ أَن يَبۡطِشَ بِٱلَّذِي هُوَ عَدُوّٞ لَّهُمَا قَالَ يَٰمُوسَىٰٓ أَتُرِيدُ أَن تَقۡتُلَنِي كَمَا قَتَلۡتَ نَفۡسَۢا بِٱلۡأَمۡسِۖ إِن تُرِيدُ إِلَّآ أَن تَكُونَ جَبَّارٗا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا تُرِيدُ أَن تَكُونَ مِنَ ٱلۡمُصۡلِحِينَ
Choncho pamene adafuna kumpanda, yemwe ndi mdani wa awiriwo, (uja wofuna chithandizo kwa Mûsa adaganiza kuti Mûsa afuna kuti ampande iye), ndipo adati: “E iwe Mûsa! Kodi ukufuna kundipha monga momwe udaphera munthu uja dzulo? Iwe sufuna china koma kukhala wodzitukumula (wankhanza) pa dziko, ndipo sukufuna kukhala mmodzi mwa ochita zabwino (oyanjanitsa okangana ndi kukonza zinthu).”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَجَآءَ رَجُلٞ مِّنۡ أَقۡصَا ٱلۡمَدِينَةِ يَسۡعَىٰ قَالَ يَٰمُوسَىٰٓ إِنَّ ٱلۡمَلَأَ يَأۡتَمِرُونَ بِكَ لِيَقۡتُلُوكَ فَٱخۡرُجۡ إِنِّي لَكَ مِنَ ٱلنَّٰصِحِينَ
(Farawo zitamfika mphekesera kuti Mûsa wapha munthu pothangata mu Israyeli, adalamula kuti Mûsa paliponse pomwe angapezeke, agwidwe ndi kuphedwa). Choncho munthu adadza akuthamanga kuchokera kumalekezero a m’zindawo. Adati: “E iwe Mûsa! Akuluakulu akukuchitira upo kuti akuphe choncho choka (m’dziko muno). Ndithu ine ndine mmodzi mwa okufunira iwe zabwino.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَخَرَجَ مِنۡهَا خَآئِفٗا يَتَرَقَّبُۖ قَالَ رَبِّ نَجِّنِي مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ
Ndipo adachoka mu mzindawo ali woopa uku akuyembekezera (kumpeza choipa kuchokera kwa adani ake). Adati: “E Mbuye wanga! Ndipulumutseni kwa anthu ochita zoipa.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَلَمَّا تَوَجَّهَ تِلۡقَآءَ مَدۡيَنَ قَالَ عَسَىٰ رَبِّيٓ أَن يَهۡدِيَنِي سَوَآءَ ٱلسَّبِيلِ
Ndipo pamene adalunjika (kumka) ku Madiyan adati: “Mwina Mbuye wanga andiongolera kunjira yoyenera.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَلَمَّا وَرَدَ مَآءَ مَدۡيَنَ وَجَدَ عَلَيۡهِ أُمَّةٗ مِّنَ ٱلنَّاسِ يَسۡقُونَ وَوَجَدَ مِن دُونِهِمُ ٱمۡرَأَتَيۡنِ تَذُودَانِۖ قَالَ مَا خَطۡبُكُمَاۖ قَالَتَا لَا نَسۡقِي حَتَّىٰ يُصۡدِرَ ٱلرِّعَآءُۖ وَأَبُونَا شَيۡخٞ كَبِيرٞ
Ndipo pamene adawafika madzi a ku Madiyan (pomwe anthu kumeneko ankatungapo madzi), adapeza gulu la anthu likumwetsa (ziweto zawo), ndipo pambali (pa gululo) adapeza akazi awiri akuletsa (ziweto zawo kuti zisapite kukamwa ndi ziweto zinazo). (Mûsa) adati: “Kodi mwatani? (Bwanji simukuzimwetsa ziweto zanu?)” Iwo Adati: “Sitingamwetse (ziweto zathu) mpaka abusa atachotsa (ziweto zawo, chifukwa sitingathe kulimbana nawo). Ndipo bambo wathu ndinkhalamba yaikulu kwabasi.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَسَقَىٰ لَهُمَا ثُمَّ تَوَلَّىٰٓ إِلَى ٱلظِّلِّ فَقَالَ رَبِّ إِنِّي لِمَآ أَنزَلۡتَ إِلَيَّ مِنۡ خَيۡرٖ فَقِيرٞ
Choncho (Mûsa) adawamwetsera (ziweto zawo); kenako adapita pamthunzi, ndipo adati: “E Mbuye wanga! Ndithu ine ndiwosaukira chabwino chimene munditsitsire.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَجَآءَتۡهُ إِحۡدَىٰهُمَا تَمۡشِي عَلَى ٱسۡتِحۡيَآءٖ قَالَتۡ إِنَّ أَبِي يَدۡعُوكَ لِيَجۡزِيَكَ أَجۡرَ مَا سَقَيۡتَ لَنَاۚ فَلَمَّا جَآءَهُۥ وَقَصَّ عَلَيۡهِ ٱلۡقَصَصَ قَالَ لَا تَخَفۡۖ نَجَوۡتَ مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ
Kenako mmodzi mwa asungwana aja adadza kwa iye uku akuyenda mwa manyazi. (Msungwanayo) adati: “Ndithu tate wanga akukuitana kuti akakupatse malipiro pakutimwetsera (ziweto zathu).” Choncho pamene adamdzera, (mneneri Shuaib) ndikumulongosolera nkhani, adati: “Usaope; wapulumuka kwa anthu oipa.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قَالَتۡ إِحۡدَىٰهُمَا يَٰٓأَبَتِ ٱسۡتَـٔۡجِرۡهُۖ إِنَّ خَيۡرَ مَنِ ٱسۡتَـٔۡجَرۡتَ ٱلۡقَوِيُّ ٱلۡأَمِينُ
Mmodzi wa iwo (asungwana aja) adanena: “E bambo wanga mulembeni ntchito (kuti akhale woweta ziweto m’malo mwa ife). Ndithu amene alibwino kuti mumulembe ntchito ndi yemwe ali wamphamvu wokhulupirika (zonse ziwiri mwa iyeyu zirimo.)
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قَالَ إِنِّيٓ أُرِيدُ أَنۡ أُنكِحَكَ إِحۡدَى ٱبۡنَتَيَّ هَٰتَيۡنِ عَلَىٰٓ أَن تَأۡجُرَنِي ثَمَٰنِيَ حِجَجٖۖ فَإِنۡ أَتۡمَمۡتَ عَشۡرٗا فَمِنۡ عِندِكَۖ وَمَآ أُرِيدُ أَنۡ أَشُقَّ عَلَيۡكَۚ سَتَجِدُنِيٓ إِن شَآءَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ
(Shuaib) adati (kwa iye): “Ine ndikufuna kukukwatitsa mmodzi mwa asungwana anga awiriwa, chiongo chake ndikundigwilira ntchito zaka zisanu ndi zitatu; ngati utakwaniritsa zaka khumi ndiye kuti nkufuna kwako. Sindikufuna kukuvutitsa (pokuchulukitsira zaka); undipeza, Allah akafuna, kuti ndine mmodzi wa anthu abwino, (wokwaniritsa lonjezo).”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قَالَ ذَٰلِكَ بَيۡنِي وَبَيۡنَكَۖ أَيَّمَا ٱلۡأَجَلَيۡنِ قَضَيۡتُ فَلَا عُدۡوَٰنَ عَلَيَّۖ وَٱللَّهُ عَلَىٰ مَا نَقُولُ وَكِيلٞ
(Mûsa) adati: “Zimene mwandilonjezazi zili pakati pa ine ndi inu. Nyengo iriyonse imene ndikwaniritse pa ziwirizi (pogwira ntchitoyo, ndiye kuti ndakwaniritsa lonjezo lanu) musandichitire mtopola. Ndipo Allah ndiye Muyang’aniri pa zomwe tikukambazi.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
۞ فَلَمَّا قَضَىٰ مُوسَى ٱلۡأَجَلَ وَسَارَ بِأَهۡلِهِۦٓ ءَانَسَ مِن جَانِبِ ٱلطُّورِ نَارٗاۖ قَالَ لِأَهۡلِهِ ٱمۡكُثُوٓاْ إِنِّيٓ ءَانَسۡتُ نَارٗا لَّعَلِّيٓ ءَاتِيكُم مِّنۡهَا بِخَبَرٍ أَوۡ جَذۡوَةٖ مِّنَ ٱلنَّارِ لَعَلَّكُمۡ تَصۡطَلُونَ
Mûsa pamene adakwaniritsa nyengoyo, adanyamuka ndi banja lake (kubwerera kwao) adaona moto kumbali ya phiri. Adauza banja lake: “Dikirani ndithudi ine ndaona moto mwina mwake ndingakutengereni nkhani za kumeneko kapena chikuni cha moto kuti muothe.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَلَمَّآ أَتَىٰهَا نُودِيَ مِن شَٰطِيِٕ ٱلۡوَادِ ٱلۡأَيۡمَنِ فِي ٱلۡبُقۡعَةِ ٱلۡمُبَٰرَكَةِ مِنَ ٱلشَّجَرَةِ أَن يَٰمُوسَىٰٓ إِنِّيٓ أَنَا ٱللَّهُ رَبُّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Tsono pamene adaudzera, adaitanidwa kuchokera mbali ya kumanja ya chigwacho, pa malo wodalitsidwa kuchokera mu mtengo, ankati: “E iwe Mûsa! Ndithudi Ine ndi Allah Mbuye wa zolengedwa.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَأَنۡ أَلۡقِ عَصَاكَۚ فَلَمَّا رَءَاهَا تَهۡتَزُّ كَأَنَّهَا جَآنّٞ وَلَّىٰ مُدۡبِرٗا وَلَمۡ يُعَقِّبۡۚ يَٰمُوسَىٰٓ أَقۡبِلۡ وَلَا تَخَفۡۖ إِنَّكَ مِنَ ٱلۡأٓمِنِينَ
“Ndipo ponya (pansi) ndodo yakoyo.” Choncho pamene adayiona ikugwedezeka monga kuti iyo ndi njoka, adatembenuka kuthawa ndipo sadachewuke. (Adauzidwa): “E iwe Mûsa! Bwera kuno, usaope. Ndithu iwe ndiwe mmodzi wokhala ndi mtendere.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
ٱسۡلُكۡ يَدَكَ فِي جَيۡبِكَ تَخۡرُجۡ بَيۡضَآءَ مِنۡ غَيۡرِ سُوٓءٖ وَٱضۡمُمۡ إِلَيۡكَ جَنَاحَكَ مِنَ ٱلرَّهۡبِۖ فَذَٰنِكَ بُرۡهَٰنَانِ مِن رَّبِّكَ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦٓۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمٗا فَٰسِقِينَ
Lowetsa dzanja lako m’thumba mwako (palisani la mkanjo wako), lituluka lili loyera, popanda choipa. Ukachita mantha, fumbata dzanja lako chakukhwapa; (ukatero mantha akuchokera). Izi zidzakhala zizindikiro ziwiri zochokera kwa Mbuye wako kwa Farawo ndi nduna zake. Ndithu iwo ndianthu olakwa.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قَالَ رَبِّ إِنِّي قَتَلۡتُ مِنۡهُمۡ نَفۡسٗا فَأَخَافُ أَن يَقۡتُلُونِ
(Mûsa) adanena (moopa) “E Mbuye wanga! Ine ndidapha munthu mwa iwo, ndipo ndikuopa kuti akandipha.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَأَخِي هَٰرُونُ هُوَ أَفۡصَحُ مِنِّي لِسَانٗا فَأَرۡسِلۡهُ مَعِيَ رِدۡءٗا يُصَدِّقُنِيٓۖ إِنِّيٓ أَخَافُ أَن يُكَذِّبُونِ
“Ndipo m’bale wanga (Haaruni) ndikatswiri pakuyankhula kuposa ine. Mutumizeni pamodzi ndi ine monga mnthandizi, azikandivomereza (pa zimene ndizikanena). Ndithu ine ndikuopa kuti akanditsutsa.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قَالَ سَنَشُدُّ عَضُدَكَ بِأَخِيكَ وَنَجۡعَلُ لَكُمَا سُلۡطَٰنٗا فَلَا يَصِلُونَ إِلَيۡكُمَا بِـَٔايَٰتِنَآۚ أَنتُمَا وَمَنِ ٱتَّبَعَكُمَا ٱلۡغَٰلِبُونَ
(Allah) adati: “Tilimbitsa dzanja lako ndi m’bale wakoyo ndipo tikupatsani kupambana, iwo sangafikitse masautso pa inu; chifukwa cha zozizwitsa zathuzo inu awiri ndi amene akutsatireni, ndinu opambana.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَلَمَّا جَآءَهُم مُّوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَا بَيِّنَٰتٖ قَالُواْ مَا هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٞ مُّفۡتَرٗى وَمَا سَمِعۡنَا بِهَٰذَا فِيٓ ءَابَآئِنَا ٱلۡأَوَّلِينَ
Pamene Mûsa adawadzera ndi zizindikiro zathu zoonekera poyera, adati: “Ichi sichina koma ndi matsenga wopeka; sitidamvepo zimenezi kumakolo athu akale.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَقَالَ مُوسَىٰ رَبِّيٓ أَعۡلَمُ بِمَن جَآءَ بِٱلۡهُدَىٰ مِنۡ عِندِهِۦ وَمَن تَكُونُ لَهُۥ عَٰقِبَةُ ٱلدَّارِۚ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلظَّٰلِمُونَ
Ndipo Mûsa adanena: “Mbuye wanga akumudziwa yemwe wadza ndi chiongoko kuchokera kwa Iye ndi yemwe adzakhala ndi mathero a pokhala pabwino. Ndithu ochita zoipa sakapambana.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَقَالَ فِرۡعَوۡنُ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَأُ مَا عَلِمۡتُ لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرِي فَأَوۡقِدۡ لِي يَٰهَٰمَٰنُ عَلَى ٱلطِّينِ فَٱجۡعَل لِّي صَرۡحٗا لَّعَلِّيٓ أَطَّلِعُ إِلَىٰٓ إِلَٰهِ مُوسَىٰ وَإِنِّي لَأَظُنُّهُۥ مِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ
Ndipo Farawo adati: “E inu nduna (zanga)! Sindidziwa kuti inu muli ndi mulungu (wina) kupatula ine. Choncho, iwe Haamana! Ndiwotchere njerwa tero undimangire chipilala kuti mwina mwake ndingamsuzumire Mulungu wa Mûsa. Ndithu ine ndikumganizira kuti ndi mmodzi wa abodza.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَٱسۡتَكۡبَرَ هُوَ وَجُنُودُهُۥ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّ وَظَنُّوٓاْ أَنَّهُمۡ إِلَيۡنَا لَا يُرۡجَعُونَ
Ndipo iye pamodzi ndi makamu ake ankhondo adadzitukumula pa dziko popanda chilungamo ndipo ankaganiza kuti iwo sadzabwelere kwa Ife.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَأَخَذۡنَٰهُ وَجُنُودَهُۥ فَنَبَذۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡيَمِّۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلظَّٰلِمِينَ
Koma tidamulanga ndi magulu ake ankhondo ndi kuwaponya m’nyanja; yang’ana, kodi adali bwanji mathero a ochita zoipa.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَجَعَلۡنَٰهُمۡ أَئِمَّةٗ يَدۡعُونَ إِلَى ٱلنَّارِۖ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَا يُنصَرُونَ
Ndipo tidawachita kukhala atsogoleri oitanira (anthu) ku Moto; ndipo tsiku la chiweruziro (Qiyâma) sadzathandizidwa.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَأَتۡبَعۡنَٰهُمۡ فِي هَٰذِهِ ٱلدُّنۡيَا لَعۡنَةٗۖ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ هُم مِّنَ ٱلۡمَقۡبُوحِينَ
Tidawatsatiziranso matembelero padziko lino lapansi. Ndipo tsiku la chimaliziro iwo adzakhala oyipitsitsa (ndi kuthamangitsidwa ku chifundo cha Allah).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ مِنۢ بَعۡدِ مَآ أَهۡلَكۡنَا ٱلۡقُرُونَ ٱلۡأُولَىٰ بَصَآئِرَ لِلنَّاسِ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٗ لَّعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ
Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku pambuyo powononga mibadwo yoyamba kuti likhale chiphanulamaso cha anthu (kuti liwaunikire ku njira yolungama), ndi kuti likhale chiongoko ndi chifundo kuti iwo akumbukire.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَمَا كُنتَ بِجَانِبِ ٱلۡغَرۡبِيِّ إِذۡ قَضَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَى ٱلۡأَمۡرَ وَمَا كُنتَ مِنَ ٱلشَّٰهِدِينَ
Ndipo iwe sudali mbali ya kuzambwe (kwa phiri limenelo) pamene tidampatsa Mûsa lamulo; sudalinso mwa amene adalipo (pamalopo).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَلَٰكِنَّآ أَنشَأۡنَا قُرُونٗا فَتَطَاوَلَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡعُمُرُۚ وَمَا كُنتَ ثَاوِيٗا فِيٓ أَهۡلِ مَدۡيَنَ تَتۡلُواْ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتِنَا وَلَٰكِنَّا كُنَّا مُرۡسِلِينَ
Koma ife tidaumba mibadwo yambiri (pambuyo pa Mneneri Mûsa) kotero kuti zaka zidapitapo zambiri pakati pawo. Ndipo sudakhale nawo anthu a Madiyan ndi kumawawerengera Ayah (ndime) Zathu; koma Ife tidali kutuma (atumiki ndi kuwafotokozera zomwe zidachitika patsogolo ndi pambuyo pawo, monga momwe takutumira iwe ndi kukudziwitsa nkhani zakale ndi zimene zikudza pambuyo).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَمَا كُنتَ بِجَانِبِ ٱلطُّورِ إِذۡ نَادَيۡنَا وَلَٰكِن رَّحۡمَةٗ مِّن رَّبِّكَ لِتُنذِرَ قَوۡمٗا مَّآ أَتَىٰهُم مِّن نَّذِيرٖ مِّن قَبۡلِكَ لَعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ
Ndipo sudali kumbali kwa phiri pamene tidamuitana (Mneneri Mûsa). Koma (kutumidwa kwako) ndimtendere wochokera kwa Mbuye wako kuti uwachenjeze anthu omwe mchenjezi sadawadzere (mnthawi yaitali) iwe usadadze, kuti akumbukire.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَلَوۡلَآ أَن تُصِيبَهُم مُّصِيبَةُۢ بِمَا قَدَّمَتۡ أَيۡدِيهِمۡ فَيَقُولُواْ رَبَّنَا لَوۡلَآ أَرۡسَلۡتَ إِلَيۡنَا رَسُولٗا فَنَتَّبِعَ ءَايَٰتِكَ وَنَكُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
(Ndipo sitikadatuma) koma kuti mavuto akawapeza ochokera (ku zoipa) zomwe atsogoza manja awo, amanena: “Mbuye wathu! Bwanji wosatitumizira Mtumiki kuti titsate mawu anu ndi kukhala mwa okhulupirira.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَلَمَّا جَآءَهُمُ ٱلۡحَقُّ مِنۡ عِندِنَا قَالُواْ لَوۡلَآ أُوتِيَ مِثۡلَ مَآ أُوتِيَ مُوسَىٰٓۚ أَوَلَمۡ يَكۡفُرُواْ بِمَآ أُوتِيَ مُوسَىٰ مِن قَبۡلُۖ قَالُواْ سِحۡرَانِ تَظَٰهَرَا وَقَالُوٓاْ إِنَّا بِكُلّٖ كَٰفِرُونَ
Koma choona pamene chidawadzera kuchokera kwa Ife, adati: “Bwanji sadapatsidwe zonga zomwe adapatsidwa Mûsa? (Monga kutembenuza ndodo kukhala njoka, ndi zina zotero).” Kodi kalelo sadazikane zomwe adapatsidwa Mûsa? Nkunena (za Taurati ndi Qur’an): “Ndimatsenga awiri amene akuthandizana.” Ndipo adati: “Ndithu ife tikuwakana onse.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قُلۡ فَأۡتُواْ بِكِتَٰبٖ مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِ هُوَ أَهۡدَىٰ مِنۡهُمَآ أَتَّبِعۡهُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Nena: “Bwerani nalo buku lochokera kwa Allah lomwe lili ndi chiongoko chabwino kuposa awiriwa (Taurati ya Mneneri Mûsa, ndi iyi Qur’an), kuti ndilitsate ngati inu mukunena zoona.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَإِن لَّمۡ يَسۡتَجِيبُواْ لَكَ فَٱعۡلَمۡ أَنَّمَا يَتَّبِعُونَ أَهۡوَآءَهُمۡۚ وَمَنۡ أَضَلُّ مِمَّنِ ٱتَّبَعَ هَوَىٰهُ بِغَيۡرِ هُدٗى مِّنَ ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ
Koma ngati sadakuyankhe, dziwa kuti akutsatira zilakolako zawo. Kodi ndani wasokera kwambiri kuposa yemwe akutsatira zilakolako zake popanda chiongoko chochokera kwa Allah? Ndithu Allah saongola anthu odzichitira zoipa.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
۞ وَلَقَدۡ وَصَّلۡنَا لَهُمُ ٱلۡقَوۡلَ لَعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ
Ndipo ndithu tafikitsa mawu kwa iwo mochulukitsa, mwatsatanetsatane kuti iwo akumbukire.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
ٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ مِن قَبۡلِهِۦ هُم بِهِۦ يُؤۡمِنُونَ
Amene tidawapatsa buku kale ili lisadadze, akulikhulupirira ili (buku la Qur’an).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَإِذَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ قَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِهِۦٓ إِنَّهُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّنَآ إِنَّا كُنَّا مِن قَبۡلِهِۦ مُسۡلِمِينَ
Ndipo likawerengedwa kwa iwo, akuti: “Talikhulupirira; ndithu ichi nchoona chochokera kwa Mbuye wathu; ndithu ilo lisanadze ife tidali Asilamu (ogonjera Allah).”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
أُوْلَٰٓئِكَ يُؤۡتَوۡنَ أَجۡرَهُم مَّرَّتَيۡنِ بِمَا صَبَرُواْ وَيَدۡرَءُونَ بِٱلۡحَسَنَةِ ٱلسَّيِّئَةَ وَمِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ يُنفِقُونَ
Iwo adzapatsidwa malipiro awo kawiri (chifukwa chotsatira Mneneri Mûsa Ndi Mneneri Isa (Yesu), kale; ndipo tsopano ndikumtsatira Mneneri Muhammad{s.a.w}) nchifukwa chakuti adapirira; amachotsa choipa (pochita) chabwino, ndipo m’zimene tawapatsa akupereka chopereka (Sadaka).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَإِذَا سَمِعُواْ ٱللَّغۡوَ أَعۡرَضُواْ عَنۡهُ وَقَالُواْ لَنَآ أَعۡمَٰلُنَا وَلَكُمۡ أَعۡمَٰلُكُمۡ سَلَٰمٌ عَلَيۡكُمۡ لَا نَبۡتَغِي ٱلۡجَٰهِلِينَ
Ndipo akamva zopanda pake amazipewa, ndipo amati (kwa achibwanawo): “Ife tili ndi zochita zathu inunso muli ndi zochita zanu, mtendere ukhale pa inu. Ife sitifuna (kutsutsana) ndi mbuli.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
إِنَّكَ لَا تَهۡدِي مَنۡ أَحۡبَبۡتَ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ يَهۡدِي مَن يَشَآءُۚ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُهۡتَدِينَ
Ndithu iwe sungathe kumuongola amene ukumfuna, koma Allah amamuongola amene wamfuna. Ndipo Iye akudziwa za amene ali oongoka.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَقَالُوٓاْ إِن نَّتَّبِعِ ٱلۡهُدَىٰ مَعَكَ نُتَخَطَّفۡ مِنۡ أَرۡضِنَآۚ أَوَلَمۡ نُمَكِّن لَّهُمۡ حَرَمًا ءَامِنٗا يُجۡبَىٰٓ إِلَيۡهِ ثَمَرَٰتُ كُلِّ شَيۡءٖ رِّزۡقٗا مِّن لَّدُنَّا وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
Ndipo akunena (akafiri a m’ Makka, kuuza Mtumiki): “Ngati titsatira chiongoko (ichi chimene wadza nacho) pamodzi ndi iwe, tifwambidwa m’dziko lathu (potimenya nkhondo mafuko ena a Arabu).” Kodi sitidawakhazike pamalo opatulika ndi pa mtendere pomwe zipatso za mitundumitundu zikudza pamenepo mwaulere (monga rizq) zochokera kwa Ife? Koma ambiri a iwo sadziwa.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِن قَرۡيَةِۭ بَطِرَتۡ مَعِيشَتَهَاۖ فَتِلۡكَ مَسَٰكِنُهُمۡ لَمۡ تُسۡكَن مِّنۢ بَعۡدِهِمۡ إِلَّا قَلِيلٗاۖ وَكُنَّا نَحۡنُ ٱلۡوَٰرِثِينَ
Kodi ndimidzi ingati imene tidaiononga yomwe inkanyadira za moyo wawo (wosavutika ndi wodya bwino)! Umo m’malo mwawo simudakhalidwebe pambuyo pawo koma mochepa basi; ndipo ife tidalowa chokolo m’zimenezi.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَمَا كَانَ رَبُّكَ مُهۡلِكَ ٱلۡقُرَىٰ حَتَّىٰ يَبۡعَثَ فِيٓ أُمِّهَا رَسُولٗا يَتۡلُواْ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتِنَاۚ وَمَا كُنَّا مُهۡلِكِي ٱلۡقُرَىٰٓ إِلَّا وَأَهۡلُهَا ظَٰلِمُونَ
Ndipo Mbuye wako sali owononga midzi pokhapokha akatuma mtumiki mu mzinda wawo waukulu ndi kuwawerengera mawu a m’ndime Zathu, (akakana ndi pamene timawaononga); ndiponso sitili owononga midzi pokhapokha anthu ake atakhala achinyengo.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَمَآ أُوتِيتُم مِّن شَيۡءٖ فَمَتَٰعُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَزِينَتُهَاۚ وَمَا عِندَ ٱللَّهِ خَيۡرٞ وَأَبۡقَىٰٓۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ
Ndipo chilichonse chimene mwapatsidwa nchosangalatsa cha moyo wa pa dziko, ndiponso chokometsera chake (chomwe sichikhalira kutha); koma chomwe chili kwa Allah ndicho chabwino, chamuyaya; kodi bwanji simukuzindikira?
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
أَفَمَن وَعَدۡنَٰهُ وَعۡدًا حَسَنٗا فَهُوَ لَٰقِيهِ كَمَن مَّتَّعۡنَٰهُ مَتَٰعَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا ثُمَّ هُوَ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ مِنَ ٱلۡمُحۡضَرِينَ
Kodi munthu yemwe tamulonjeza lonjezo labwino (kuti akalowa ku Munda wamtendere) kotero kuti iye akakumana nalo (lonjezolo), angafanane ndi yemwe tamsangalatsa ndi zosangalatsa za moyo wa pa dziko basi, kenako iye nkukhala mmodzi okaponyedwa (ku Moto) tsiku la chiweruziro (Qiyâma)?
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَيَوۡمَ يُنَادِيهِمۡ فَيَقُولُ أَيۡنَ شُرَكَآءِيَ ٱلَّذِينَ كُنتُمۡ تَزۡعُمُونَ
Ndipo (akumbutse) tsiku limene (Allah) adzawaitana, adzati: “Ali kuti anzanga aja omwe mumanena (kuti ndianzananga)?”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قَالَ ٱلَّذِينَ حَقَّ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقَوۡلُ رَبَّنَا هَٰٓؤُلَآءِ ٱلَّذِينَ أَغۡوَيۡنَآ أَغۡوَيۡنَٰهُمۡ كَمَا غَوَيۡنَاۖ تَبَرَّأۡنَآ إِلَيۡكَۖ مَا كَانُوٓاْ إِيَّانَا يَعۡبُدُونَ
Adzanena amene mawu (onena za chilango) atsimikizika pa iwo: “Mbuye wathu! Awa ndiamene tidawasokeretsa; tidawasokeretsa monga momwe Tidasokelera. tikudzipatula ndi iwo kwa inu; samatilambira ife.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَقِيلَ ٱدۡعُواْ شُرَكَآءَكُمۡ فَدَعَوۡهُمۡ فَلَمۡ يَسۡتَجِيبُواْ لَهُمۡ وَرَأَوُاْ ٱلۡعَذَابَۚ لَوۡ أَنَّهُمۡ كَانُواْ يَهۡتَدُونَ
Ndipo kudzanenedwa: “Itanani aphatikizi anu.” Choncho adzawaitana koma sadzawayankha. Ndipo azawawona mavuto (pa nthawiyo azakhumba) akadakhala oongoka (pa dziko lapansi kotero kuti akadapeza mtendere pa tsiku la chimaliziro).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَيَوۡمَ يُنَادِيهِمۡ فَيَقُولُ مَاذَآ أَجَبۡتُمُ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Ndipo (akumbutse) tsiku limene adzawaitana, nkudzati: “Kodi mudawayankha chiyani Atumiki?”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَعَمِيَتۡ عَلَيۡهِمُ ٱلۡأَنۢبَآءُ يَوۡمَئِذٖ فَهُمۡ لَا يَتَسَآءَلُونَ
Basi tsiku limenelo nkhani zidzawasowa choncho iwo sadzatha kufunsana.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَأَمَّا مَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحٗا فَعَسَىٰٓ أَن يَكُونَ مِنَ ٱلۡمُفۡلِحِينَ
Koma amene walapa ndi kukhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, adzakhala mwa opambana.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَرَبُّكَ يَخۡلُقُ مَا يَشَآءُ وَيَخۡتَارُۗ مَا كَانَ لَهُمُ ٱلۡخِيَرَةُۚ سُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ
Ndipo Mbuye wako amalenga chimene wafuna ndi kuchisankha (chimene wafuna). Iwo alibe chifuniro. Allah wapatukana ndi zonse zochepetsa ulemelero Wake, ndipo watukuka ku zomwe akumphatikiza nazo.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَرَبُّكَ يَعۡلَمُ مَا تُكِنُّ صُدُورُهُمۡ وَمَا يُعۡلِنُونَ
Ndiponso Mbuye wako akudziwa zimene zifuwa zawo zikubisa (maganizo awo) ndi zimene akuwonetsera (poyera).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَهُوَ ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ لَهُ ٱلۡحَمۡدُ فِي ٱلۡأُولَىٰ وَٱلۡأٓخِرَةِۖ وَلَهُ ٱلۡحُكۡمُ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Ndipo Iye ndi Allah; palibe wopembedzedwa m’choonadi koma Iye. Kuyamikidwa konse (kwabwino) pachiyambi ndi kumapeto nkwake; ndipo kulamulanso nkwake, ndipo inu mudzabwerera kwa Iye.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ إِن جَعَلَ ٱللَّهُ عَلَيۡكُمُ ٱلَّيۡلَ سَرۡمَدًا إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ مَنۡ إِلَٰهٌ غَيۡرُ ٱللَّهِ يَأۡتِيكُم بِضِيَآءٍۚ أَفَلَا تَسۡمَعُونَ
Nena: “Tandiuzani ngati Allah atakupangirani usiku kuti usachoke mpaka tsiku la chiweruziro (Qiyâma), kodi ndimulungu wanji osati Allah amene angakudzetsereni kuunika? Kodi simumva?”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ إِن جَعَلَ ٱللَّهُ عَلَيۡكُمُ ٱلنَّهَارَ سَرۡمَدًا إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ مَنۡ إِلَٰهٌ غَيۡرُ ٱللَّهِ يَأۡتِيكُم بِلَيۡلٖ تَسۡكُنُونَ فِيهِۚ أَفَلَا تُبۡصِرُونَ
Nena: “Tandiuzani ngati Allah ataupanga usana kuti usachoke mpaka tsiku la chiweruziro (Qiyâma), kodi ndimulungu wanji osati Allah amene angakudzetsereni usiku m’mene mumapumulamo? Kodi simuona (chifundo cha Allah)?”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَمِن رَّحۡمَتِهِۦ جَعَلَ لَكُمُ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ لِتَسۡكُنُواْ فِيهِ وَلِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦ وَلَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ
Ndipo mu chifundo Chake, adakupangirani usiku ndi usana kuti muzipumulamo ndi kufunafuna zabwino Zake (masana) kuti muthokoze.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَيَوۡمَ يُنَادِيهِمۡ فَيَقُولُ أَيۡنَ شُرَكَآءِيَ ٱلَّذِينَ كُنتُمۡ تَزۡعُمُونَ
Ndipo tsiku limene (Allah) adzawaitana, adzati: “Ali kuti anzanga aja amene mumati ndimilungu inzanga?”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَنَزَعۡنَا مِن كُلِّ أُمَّةٖ شَهِيدٗا فَقُلۡنَا هَاتُواْ بُرۡهَٰنَكُمۡ فَعَلِمُوٓاْ أَنَّ ٱلۡحَقَّ لِلَّهِ وَضَلَّ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ
Ndipo mumpingo uliwonse tidzatulutsa mboni (yawo yowaikira umboni), ndipo tidzawauza: “Bwerani ndi umboni wanu.” Pamenepo adzadziwa kuti choonadi ncha Allah, ndipo zidzawasowa zimene amapeka.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
۞ إِنَّ قَٰرُونَ كَانَ مِن قَوۡمِ مُوسَىٰ فَبَغَىٰ عَلَيۡهِمۡۖ وَءَاتَيۡنَٰهُ مِنَ ٱلۡكُنُوزِ مَآ إِنَّ مَفَاتِحَهُۥ لَتَنُوٓأُ بِٱلۡعُصۡبَةِ أُوْلِي ٱلۡقُوَّةِ إِذۡ قَالَ لَهُۥ قَوۡمُهُۥ لَا تَفۡرَحۡۖ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ ٱلۡفَرِحِينَ
Ndithu Qaruni adali mwa anthu a Mûsa; koma adazikweza kwa iwo, ndipo tidampatsa nkhokwe za chuma zomwe makiyi ake ngolemetsa kagulu ka anthu anyonga (kuwasenza). Anthu ake adamuuza: “Usanyade; ndithu Allah sakonda onyada.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَٱبۡتَغِ فِيمَآ ءَاتَىٰكَ ٱللَّهُ ٱلدَّارَ ٱلۡأٓخِرَةَۖ وَلَا تَنسَ نَصِيبَكَ مِنَ ٱلدُّنۡيَاۖ وَأَحۡسِن كَمَآ أَحۡسَنَ ٱللَّهُ إِلَيۡكَۖ وَلَا تَبۡغِ ٱلۡفَسَادَ فِي ٱلۡأَرۡضِۖ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ ٱلۡمُفۡسِدِينَ
“Ndipo uyifunefune kupyolera m’zomwe Allah wakupatsa, nyumba yabwino yomaliza, usaiwale gawo lako la m’dziko; chita zabwino monga momwe Allah wakuchitira zabwino, ndipo usafune kuononga pa dziko; ndithu Allah sakonda oononga.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
قَالَ إِنَّمَآ أُوتِيتُهُۥ عَلَىٰ عِلۡمٍ عِندِيٓۚ أَوَلَمۡ يَعۡلَمۡ أَنَّ ٱللَّهَ قَدۡ أَهۡلَكَ مِن قَبۡلِهِۦ مِنَ ٱلۡقُرُونِ مَنۡ هُوَ أَشَدُّ مِنۡهُ قُوَّةٗ وَأَكۡثَرُ جَمۡعٗاۚ وَلَا يُسۡـَٔلُ عَن ذُنُوبِهِمُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ
Adati: “Ndithu ndapatsidwa izi chifukwa cha kudziwa kwanga komwe ndili nako.” Kodi iye sadadziwe kuti Allah adawaononga anthu patsogolo pake omwe adali anyonga kwambiri kuposa iye, komanso osonkhanitsa chuma chambiri? Ndipo oipa sadzafunsidwa zolakwa zawo. (Allah akudziwa zonse za iwo)!
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَخَرَجَ عَلَىٰ قَوۡمِهِۦ فِي زِينَتِهِۦۖ قَالَ ٱلَّذِينَ يُرِيدُونَ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا يَٰلَيۡتَ لَنَا مِثۡلَ مَآ أُوتِيَ قَٰرُونُ إِنَّهُۥ لَذُو حَظٍّ عَظِيمٖ
Choncho, adatulukira kwa anthu ake (monyada) uku atadzikongoletsa. Amene akufuna moyo wa pa dziko adanena (mokhumbira): “Kalanga ife! Tikadapatsidwa monga wapatsidwa Qaruna! Ndithu iye ngodala kwakukulu.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ وَيۡلَكُمۡ ثَوَابُ ٱللَّهِ خَيۡرٞ لِّمَنۡ ءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحٗاۚ وَلَا يُلَقَّىٰهَآ إِلَّا ٱلصَّٰبِرُونَ
Ndipo amene adapatsidwa kuzindikira adanena: “Tsoka lanu! Malipiro a Allah ngabwino kwa yemwe wakhulupirira ndi kuchita zabwino, (kuposa izi ali nazo Qaruni); ndipo sadzapatsidwa zimenezi koma okhawo ali opirira.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
فَخَسَفۡنَا بِهِۦ وَبِدَارِهِ ٱلۡأَرۡضَ فَمَا كَانَ لَهُۥ مِن فِئَةٖ يَنصُرُونَهُۥ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَمَا كَانَ مِنَ ٱلۡمُنتَصِرِينَ
Kenako tidamdidimiza m’nthaka iye ndi nyumba yake; ndipo adalibe gulu lililonse lomuthangata popikisana ndi Allah, ndipo sadali mwa odzipulumutsa okha.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَأَصۡبَحَ ٱلَّذِينَ تَمَنَّوۡاْ مَكَانَهُۥ بِٱلۡأَمۡسِ يَقُولُونَ وَيۡكَأَنَّ ٱللَّهَ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦ وَيَقۡدِرُۖ لَوۡلَآ أَن مَّنَّ ٱللَّهُ عَلَيۡنَا لَخَسَفَ بِنَاۖ وَيۡكَأَنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلۡكَٰفِرُونَ
Ndipo amene ankalakalaka ulemelero wake dzulo adayamba kunena: “E zoonadi Allah amamuonjezera chuma amene akumfuna mwa akapolo Ake (chingakhale ali oipa wosayanjidwa ndi Iye), ndipo amamuchepetsera chuma (amene wamfuna kotero ngakhale ali woyanjidwa ndi Iye.) Pakadapanda Allah kutimvera chisoni. (Mkukhumbira kwathu pa zimene adampatsa Qaruna akadatikwilira m’nthaka. Ha! Zoonadi osakhulupirira sangapambane.”
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
تِلۡكَ ٱلدَّارُ ٱلۡأٓخِرَةُ نَجۡعَلُهَا لِلَّذِينَ لَا يُرِيدُونَ عُلُوّٗا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا فَسَادٗاۚ وَٱلۡعَٰقِبَةُ لِلۡمُتَّقِينَ
Nyumba yomalizirayo tikawapangira amene sakufuna kudzikweza pa dziko ndi kuononga. Ndipo malekezero abwino adzakhala a wanthu owopa (Allah).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
مَن جَآءَ بِٱلۡحَسَنَةِ فَلَهُۥ خَيۡرٞ مِّنۡهَاۖ وَمَن جَآءَ بِٱلسَّيِّئَةِ فَلَا يُجۡزَى ٱلَّذِينَ عَمِلُواْ ٱلسَّيِّـَٔاتِ إِلَّا مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Amene achite chabwino, adzapeza mphoto yoposa chimene adachitacho ndipo amene achite choipa sadzalipidwa (china chake) koma zoipa zomwezo zimene adali kuzichita.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
إِنَّ ٱلَّذِي فَرَضَ عَلَيۡكَ ٱلۡقُرۡءَانَ لَرَآدُّكَ إِلَىٰ مَعَادٖۚ قُل رَّبِّيٓ أَعۡلَمُ مَن جَآءَ بِٱلۡهُدَىٰ وَمَنۡ هُوَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
Ndithudi yemwe wakulamula kuitsata Qur’an, mwachoonadi adzakubwezera pa malo pobwerera. Nena! “Mbuye wanga ndi yemwe akudziwa amene wadza ndi chiongoko ndi yemwe ali m’kusokera koonekera poyera.’’
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَمَا كُنتَ تَرۡجُوٓاْ أَن يُلۡقَىٰٓ إِلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبُ إِلَّا رَحۡمَةٗ مِّن رَّبِّكَۖ فَلَا تَكُونَنَّ ظَهِيرٗا لِّلۡكَٰفِرِينَ
Ndipo iwe sudali kulakalaka kuti ungapatsidwe buku (pamodzi ndi uneneri) koma izi zidachitika pa chifundo chochokera kwa Mbuye wako; choncho usakhale m’thandizi wa anthu osakhulupirira (Allah).
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَلَا يَصُدُّنَّكَ عَنۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ بَعۡدَ إِذۡ أُنزِلَتۡ إِلَيۡكَۖ وَٱدۡعُ إِلَىٰ رَبِّكَۖ وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ
Ndipo asakutsekereze kutsatira ndime za (mawu a) Allah pa mbuyo povumbulutsidwa pa iwe, ndipo aitanire anthu kwa Mbuye wako, komatu usakhale m’gulu la anthu omphatikiza Allah ndi mafano.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
وَلَا تَدۡعُ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَۘ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۚ كُلُّ شَيۡءٍ هَالِكٌ إِلَّا وَجۡهَهُۥۚ لَهُ ٱلۡحُكۡمُ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Ndipo usapemphe mulungu wina pa modzi ndi Allah. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye Yekha. Chinthu chilichonse chidzaonongeka kupatula Nkhope Yake. Ulamuliro (wazinthu zonse) uli kwa Iye ndipo kwa Iye ndi kumene mudzabwerera nonsenu.
അറബി ഖുർആൻ വിവരണങ്ങൾ:
 
പരിഭാഷ അദ്ധ്യായം: സൂറത്തുൽ ഖസസ്
സൂറത്തുകളുടെ സൂചിക പേജ് നമ്പർ
 
വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ പരിഭാഷ - വിവർത്തനങ്ങളുടെ സൂചിക

പരിശുദ്ധ ഖുർആൻ ആശയ വിവർത്തനം ചെവ്വ ഭാഷയിൽ, പരിഭാഷ: ഖാലിദ് ഇബ്റാഹീം പെറ്റാല, 2020 പതിപ്പ്

അടക്കുക