ߞߎ߬ߙߣߊ߬ ߞߟߊߒߞߋ ߞߘߐ ߟߎ߬ ߘߟߊߡߌߘߊ - ߛ߭ߌߛ߭ߌߦߏߥߊߞߊ߲ ߘߟߊߡߌߘߊ * - ߘߟߊߡߌߘߊ ߟߎ߫ ߦߌ߬ߘߊ߬ߥߟߊ


ߞߘߐ ߟߎ߬ ߘߟߊߡߌ߬ߘߊ߬ߟߌ ߝߐߘߊ ߘߏ߫: ߛߋ߲߬ߓߊ ߝߐߘߊ   ߟߝߊߙߌ ߘߏ߫:

ߛߋ߲߬ߓߊ ߝߐߘߊ

أَلَمۡ تَرَ كَيۡفَ فَعَلَ رَبُّكَ بِأَصۡحَٰبِ ٱلۡفِيلِ
Kodi sudaone momwe Mbuye wako adawachitira eni njovu?[485]
[485] Sura imeneyi ikufotokoza mbiri imene idachitika pafupi ndi mzinda wa Makka mchaka cha 570 A.C. Dziko la Yemen lidali kulamulidwa ndi anthu a mtundu wa Ahabashi (ochokera ku Ethiopia). Iwowo pa nthawi imemeyo adali Akhristu. Bwana Mkubwa (Gavanala) waku Yemen pa nthawiyo adali Abraha. Abrahayu adafuna kuwaletsa Arabu kuti asamapite ku Makka kukayendera Kaaba. Pa chifukwa ichi adamanga tchalichi lalikulu kwambiri ndiponso lokongola lomwe lidali mu mzinda wa Sana‘a. Adawakakamiza Arabu kuyendera tchalichilo m’malo mopita ku Al-Kaaba. Pamene Arabu adamva zimenezi zidawanyansa. Ndipo adadza munthu wina wochokera ku fuko la Kinaana ndikukalowa m’tchalichimo ndikuchitiramo chimbudzi. Adatenga chimbudzicho ndikupakapaka m’zipupa za tchalichi lija chifukwa chonyansidwa ndi nyumbayo kuti siidali yoyenera kulowa m’malo mwa Kaaba. Pamene adaona izi, Abraha adakwiya kwambiri ndipo adalumbira kuti sachitira mwina koma kukagumula Kaaba. Adasonkhanitsa gulu la nkhondo lalikulu momwe mudalinso njovu zakuti zikamthandize kugumula Al-Kaaba. Choncho adauyatsa ulendo kupita ku mzinda wa Makka. Abraha pamene adafika ku Makka, adatumiza munthu kwa Arabu kuti awafotokozere kuti iye sadadze kudzawathira nkhondo, koma adadzera kudzagumula Al-Kaaba. Choncho adawapempha kuti amupatse danga kuti atero. Abdul Mutwalib adalamula anthu ake onse kuti achoke mu mzindawo apite ku mapiri. Iye adakalowa Mnyumba ya Kaaba ndipo adapempha Allah kuti ayipulumutse nyumba Yake yopatulika. Kenaka nayenso adawatsatira anzake ku mapiri kuja ndipo adangokhala phee, kuti amuone bwino yemwe adali kulimbana ndi Allah pomugumulira nyumba Yake. Abraha pamene adadziwa kuti Arabu atuluka mu mzindamo adakonzeka kulowa m’Makka ndi kugumula Al-Kaaba. Koma Allah Wamphamvu zonse adamutumizira gulu Lake la nkhondo monga momwe mukuwerengera pa Ayah yachitatu. Ankhondo a Abraha ena adafera pompo koma ena pamodzi ndi iye mwini, adathawa ndikukafera kwawo ku Yemen. pa chifukwa chimenechi Arabu ankachitcha chaka chimenechi kuti “chaka cha njovu.” Choncho mwana aliyense wobadwa m’chakachi ankatchedwa mwana wobadwa m’chaka cha njovu. Ndipo Mneneri Muhammad (s.a.w) adabadwa m’chaka chimenechi ndipo ankadziwikanso monga mwana wobadwa m’chaka cha njovu.
ߊߙߊߓߎߞߊ߲ߡߊ ߞߘߐߦߌߘߊ ߟߎ߬:
أَلَمۡ يَجۡعَلۡ كَيۡدَهُمۡ فِي تَضۡلِيلٖ
Kodi sadachichite chiwembu chawo kukhala chosokera (chopanda phindu?)
ߊߙߊߓߎߞߊ߲ߡߊ ߞߘߐߦߌߘߊ ߟߎ߬:
وَأَرۡسَلَ عَلَيۡهِمۡ طَيۡرًا أَبَابِيلَ
Ndipo adawatumizira magulumagulu a mbalame otsatizana. (ndipo adawazungulira mbali zonse).
ߊߙߊߓߎߞߊ߲ߡߊ ߞߘߐߦߌߘߊ ߟߎ߬:
تَرۡمِيهِم بِحِجَارَةٖ مِّن سِجِّيلٖ
Zimawagenda ndi miyala ya moto.
ߊߙߊߓߎߞߊ߲ߡߊ ߞߘߐߦߌߘߊ ߟߎ߬:
فَجَعَلَهُمۡ كَعَصۡفٖ مَّأۡكُولِۭ
Choncho adawachita ngati m’mera wodyedwa (ndi nyama ndi kulavulidwa).
ߊߙߊߓߎߞߊ߲ߡߊ ߞߘߐߦߌߘߊ ߟߎ߬:
 
ߞߘߐ ߟߎ߬ ߘߟߊߡߌ߬ߘߊ߬ߟߌ ߝߐߘߊ ߘߏ߫: ߛߋ߲߬ߓߊ ߝߐߘߊ
ߝߐߘߊ ߟߎ߫ ߦߌ߬ߘߊ߬ߥߟߊ ߞߐߜߍ ߝߙߍߕߍ
 
ߞߎ߬ߙߣߊ߬ ߞߟߊߒߞߋ ߞߘߐ ߟߎ߬ ߘߟߊߡߌߘߊ - ߛ߭ߌߛ߭ߌߦߏߥߊߞߊ߲ ߘߟߊߡߌߘߊ - ߘߟߊߡߌߘߊ ߟߎ߫ ߦߌ߬ߘߊ߬ߥߟߊ

ߞߎ߬ߙߣߊ߬ ߞߟߊߒߞߋ ߞߘߐ ߟߎ߬ ߘߟߊߡߌߘߊ ߛ߭ߌߛ߭ߌߦߏߥߊߞߊ߲ ߘߐ߫߸ ߞ߭ߊ߯ߟߌߘߎ߫ ߌߓߑߙߊ߬ߤߌ߯ߡߎ߫ ߔߌߕߊߟߊ߯ ߟߊ߫ ߘߟߊߡߌߘߊߟߌ ߟߋ߬. ߊ߬ ߓߊ ߟߊߘߊ߲ߣߍ߲߫ ߌߡ. ߂߀߂߀ ߟߋ߬ ߟߊ߫.

ߘߊߕߎ߲߯ߠߌ߲