அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு * - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை


மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: ஸூரா யூனுஸ்   வசனம்:

ஸூரா யூனுஸ்

الٓرۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡحَكِيمِ
Alif-Lam-Ra. Izi ndi Ayah za m’buku lanzeru. (Lokamba zanzeru zokhazokha).
அரபு விரிவுரைகள்:
أَكَانَ لِلنَّاسِ عَجَبًا أَنۡ أَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ رَجُلٖ مِّنۡهُمۡ أَنۡ أَنذِرِ ٱلنَّاسَ وَبَشِّرِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَنَّ لَهُمۡ قَدَمَ صِدۡقٍ عِندَ رَبِّهِمۡۗ قَالَ ٱلۡكَٰفِرُونَ إِنَّ هَٰذَا لَسَٰحِرٞ مُّبِينٌ
Kodi nchodabwitsa kwa anthu kuti tamuvumbulutsira (chivumbulutso) munthu wochokera mwa iwo (yemwe ndi Muhammad {s.a.w}) kuti: “Chenjeza anthu ndipo awuze nkhani yabwino amene akhulupirira kuti iwo adzapeza ulemelero waukulu kwa Mbuye wawo?” Osakhulupirira adati: “Ndithudi uyu ndi wa matsenga (mfiti) wowonekera.’’[214]
[214] Allah akuti: Sikunayenere kwa anthu kudabwa ndi kutsutsa chivumbulutso chathu kwa munthu wochokera mwa iwo yemwe cholinga chake nkuti achenjeze anthu za chilango cha Allah ndi kuti awauze nkhani zabwino amene mwa iwo akhulupilira. Ndiponso nkosayenera kwa iwo kumunenera Muhammadi (s.a.w), Mtumiki wathu, kuti iye ndi wa matsenga.
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ رَبَّكُمُ ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ يُدَبِّرُ ٱلۡأَمۡرَۖ مَا مِن شَفِيعٍ إِلَّا مِنۢ بَعۡدِ إِذۡنِهِۦۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُوهُۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ
Ndithu Mbuye wanu ndi Allah Amene adalenga thambo ndi nthaka (ndi zonse za m’menemo) m’masiku asanu ndi limodzi; (masiku omwe palibe yemwe akuwadziwa kutalika kwake koma Iye Yekha), kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu, kukhazikika kwake akukudziwa ndi Iye Yekha basi). Amayendetsa zinthu (za zolengedwa Zake). Palibe muomboli (woombola wina) koma pambuyo pa chilolezo Chake (Allah). Uyo ndiye Allah Mbuye wanu; choncho mupembedzeni Iye. Kodi simungakumbukire (kuti mafanowo si milungu)?
அரபு விரிவுரைகள்:
إِلَيۡهِ مَرۡجِعُكُمۡ جَمِيعٗاۖ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقًّاۚ إِنَّهُۥ يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥ لِيَجۡزِيَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ بِٱلۡقِسۡطِۚ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَهُمۡ شَرَابٞ مِّنۡ حَمِيمٖ وَعَذَابٌ أَلِيمُۢ بِمَا كَانُواْ يَكۡفُرُونَ
Kobwerera kwanu nonsenu ndi kwa Iye. Ili ndilonjezo la Allah loona. Ndithu Iye ndi Yemwe adayamba kulenga (zolengedwa), ndiponso ndi Yemwe adzazibwereza (pambuyo pa imfa) kuti adzawalipire amene adakhulupirira ndi kumachita zabwino mwa chilungamo. Ndipo amene sadakhulupirire, akapeza zakumwa za madzi owira ndi chilango chopweteka chifukwa cha kusakhulupirira kwawo.
அரபு விரிவுரைகள்:
هُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ ٱلشَّمۡسَ ضِيَآءٗ وَٱلۡقَمَرَ نُورٗا وَقَدَّرَهُۥ مَنَازِلَ لِتَعۡلَمُواْ عَدَدَ ٱلسِّنِينَ وَٱلۡحِسَابَۚ مَا خَلَقَ ٱللَّهُ ذَٰلِكَ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۚ يُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٖ يَعۡلَمُونَ
Iye (Allah) ndiYemwe adapanga dzuwa kukhala lowala, ndi mwezi kukhala wounika; ndipo adaukonzera mbuto (masitesheni) kuti mudziwe kuchuluka kwa zaka ndi chiwerengero chake. Allah sadalenge zimenezo koma mwachoonadi (ndi cholinga cha nzeru). Akufotokoza Ayah (Zake) kwa anthu ozindikira.[215]
[215] Mbuye wanu ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka. Ndipo dzuwa adalipanga kuti lizipereka kuwala ku zolengedwa; naonso mwezi kuti uzitumiza kuunika. Ndipo mwezi adaupangira njira momwe umayenda. Ndipo kuunika kwake kumakhala kosiyanasiyana chifukwa cha masitesheniwa. Izi nkuti zikuthangateni powerengera nthawi, ndikuti mudziwe chiwerengero cha zaka. Allah adalenga zimenezi ncholinga chanzeru zakuya.
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ فِي ٱخۡتِلَٰفِ ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ وَمَا خَلَقَ ٱللَّهُ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَتَّقُونَ
Ndithu m’kusinthanasinthana kwa usiku ndi usana, ndi zomwe Allah walenga kumwamba ndi pansi, ndithudi, ndi zisonyezo kwa anthu oopa (Allah).
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ ٱلَّذِينَ لَا يَرۡجُونَ لِقَآءَنَا وَرَضُواْ بِٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَٱطۡمَأَنُّواْ بِهَا وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَنۡ ءَايَٰتِنَا غَٰفِلُونَ
Ndithu amene sayembekeza kukumana Nafe, nakondetsetsa umoyo wapadziko lapansi ndi kukhazikika (mtima) ndi za mmenemo, ndi omwe akunyozera Ayah Zathu,
அரபு விரிவுரைகள்:
أُوْلَٰٓئِكَ مَأۡوَىٰهُمُ ٱلنَّارُ بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Iwowo (onse) malo awo ndi ku Moto chifukwa cha zomwe adazipeza (m’njira zosayenera).
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ يَهۡدِيهِمۡ رَبُّهُم بِإِيمَٰنِهِمۡۖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهِمُ ٱلۡأَنۡهَٰرُ فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ
Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, Mbuye wawo awaongola chifukwa cha chikhulupiliro chawo. Pansi (ndi patsogolo) pawo mitsinje ikuyenda m’Minda yamtendere.
அரபு விரிவுரைகள்:
دَعۡوَىٰهُمۡ فِيهَا سُبۡحَٰنَكَ ٱللَّهُمَّ وَتَحِيَّتُهُمۡ فِيهَا سَلَٰمٞۚ وَءَاخِرُ دَعۡوَىٰهُمۡ أَنِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Mapemphero awo m’menemo adzakhala kunena: “Subuhanaka Lahuma’ Ulemelero ndi Wanu, E Inu Allah!” Ndipo kulonjerana kwawo m’menemo kudzakhala kunena: “Salaam (alayikum’) Mtendere (ukhale pa inu).” Ndipo duwa yawo yomaliza (idzakhala kuyamika ponena kuti) “Alham’du Lillah Rabil a’lamin’. Kuyamikidwa konse nkwa Allah Mbuye wa zolengedwa.”[216]
[216] Pemphero la okhulupilira lidzakhala kumuyeretsa Allah kuzimene adali kumunenera osakhulupilira pa dziko lapansi. Nayenso Allah adzakhala akuwalonjera. Ndipo nawo adzakhala akulonjerananso wina ndi mnzake. Uku nkutsimikizira mtendere ndi kukhazikika kopanda kutekeseka ndi china chilichonse. Ndipo nthawi zonse kothera kwa mapemphero awo ndi kuthokoza Allah powalimbikitsa pa chikhulupiliro.
அரபு விரிவுரைகள்:
۞ وَلَوۡ يُعَجِّلُ ٱللَّهُ لِلنَّاسِ ٱلشَّرَّ ٱسۡتِعۡجَالَهُم بِٱلۡخَيۡرِ لَقُضِيَ إِلَيۡهِمۡ أَجَلُهُمۡۖ فَنَذَرُ ٱلَّذِينَ لَا يَرۡجُونَ لِقَآءَنَا فِي طُغۡيَٰنِهِمۡ يَعۡمَهُونَ
Ndipo Allah akadakhala kuti akuwapatsa anthu zoipa mwachangu (zomwe iwo akuzifulumizitsa) monga mmene amawapatsira mwachangu zabwino (akamupemphamo, ndiye kuti) ikadalamulidwa nthawi yawo (yowaonongera koma Allah amawamvera chisoni), koma amene saopa kukumana Nafe tikuwasiya akuyumbayumba m’zoipa zawo.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِذَا مَسَّ ٱلۡإِنسَٰنَ ٱلضُّرُّ دَعَانَا لِجَنۢبِهِۦٓ أَوۡ قَاعِدًا أَوۡ قَآئِمٗا فَلَمَّا كَشَفۡنَا عَنۡهُ ضُرَّهُۥ مَرَّ كَأَن لَّمۡ يَدۡعُنَآ إِلَىٰ ضُرّٖ مَّسَّهُۥۚ كَذَٰلِكَ زُيِّنَ لِلۡمُسۡرِفِينَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Ndipo vuto likamkhuza munthu amatipempha (m’kakhalidwe kake konse), chogona, chokhala kapena choimilira. Koma tikamchotsera vuto lomwe lidampeza, amayenda ngati sanatipempheko pa vuto Iomwe Iidamkhudza. Momwemo ndimo zakometseredwa kwa opyola malire zomwe ankachita.[217]
[217] Munthu vuto likamkhudza mthupi mwake, kapena pachuma chake ndi mwina motero apo mpomwe amazindikira za kufooka kwake. Amayamba kumkuwira Mbuye wake Allah ndi kumpempha m‘kakhalidwe kake konse- chogona, chokhala, choimilira kuti amchotsere mliri umene wamgwera. Koma Allah akamuyankha namchotsera vutolo amamfulatira Allah napitiriza kumlakwira naiwala ubwino wa Allah ngati kuti vuto silidamkhudze, ngati kutinso sadampempheko Allah. Ichi ndicho chikhalidwe cha anthu ambiri. Amadziwa Allah pomwe mavuto akawagwera. Koma akakhala pamtendere Allah amamuiwala.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَقَدۡ أَهۡلَكۡنَا ٱلۡقُرُونَ مِن قَبۡلِكُمۡ لَمَّا ظَلَمُواْ وَجَآءَتۡهُمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ وَمَا كَانُواْ لِيُؤۡمِنُواْۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡمُجۡرِمِينَ
Ndipo ndithu tidaiononga mibadwo yambiri patsogolo panu pamene idachita zoipa. Komatu atumiki awo adawadzera ndi zisonyezo zoonekera, koma sadali oti nkukhulupirira. Umo ndi momwenso tidzawalipire anthu ochita zoipa!
அரபு விரிவுரைகள்:
ثُمَّ جَعَلۡنَٰكُمۡ خَلَٰٓئِفَ فِي ٱلۡأَرۡضِ مِنۢ بَعۡدِهِمۡ لِنَنظُرَ كَيۡفَ تَعۡمَلُونَ
Kenako takupangani inu (Asilamu) kukhala olowa m’malo mwawo pa dziko pambuyo pawo kuti tione mmene mungachitire (zabwino kapena zoipa).
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَاتُنَا بَيِّنَٰتٖ قَالَ ٱلَّذِينَ لَا يَرۡجُونَ لِقَآءَنَا ٱئۡتِ بِقُرۡءَانٍ غَيۡرِ هَٰذَآ أَوۡ بَدِّلۡهُۚ قُلۡ مَا يَكُونُ لِيٓ أَنۡ أُبَدِّلَهُۥ مِن تِلۡقَآيِٕ نَفۡسِيٓۖ إِنۡ أَتَّبِعُ إِلَّا مَا يُوحَىٰٓ إِلَيَّۖ إِنِّيٓ أَخَافُ إِنۡ عَصَيۡتُ رَبِّي عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٖ
Ndipo Ayah Zathu zomveka bwino zikawerengedwa kwa iwo, akunena amene sayembekezera kukumana ndi Ife: “Bwera ndi Qur’an (yogwirizana ndi zofuna zathu) osati iyi, kapena uyisinthe (pang’ono).” Nena: “Nkosatheka kwa ine kuisintha mwachifuniro changa. Sinditsata koma zimene zikuvumbulutsidwa kwa ine. Ndithu ine ndikuopa chilango cha tsiku lalikulu ngati ndinyoza Mbuye wanga.”
அரபு விரிவுரைகள்:
قُل لَّوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَا تَلَوۡتُهُۥ عَلَيۡكُمۡ وَلَآ أَدۡرَىٰكُم بِهِۦۖ فَقَدۡ لَبِثۡتُ فِيكُمۡ عُمُرٗا مِّن قَبۡلِهِۦٓۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ
Nena: “Allah akadafuna, sindikadakuwerengerani Qur’aniyi ndiponso sakadakudziwitsani Qur’aniyo, ndidakhala pakati panu moyo wanga (zaka zambiri) isadavumbulutsidwe, (simudandimve ndikunena chilichonse cha utumiki). Kodi mulibe nzeru?”
அரபு விரிவுரைகள்:
فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا أَوۡ كَذَّبَ بِـَٔايَٰتِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ
Ndani woipitsitsa woposa yemwe akumpekera Allah bodza, ndi yemwe akutsutsa Ayah Zake? Ndithudi, sangapambane wochita zoipa.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَيَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَضُرُّهُمۡ وَلَا يَنفَعُهُمۡ وَيَقُولُونَ هَٰٓؤُلَآءِ شُفَعَٰٓؤُنَا عِندَ ٱللَّهِۚ قُلۡ أَتُنَبِّـُٔونَ ٱللَّهَ بِمَا لَا يَعۡلَمُ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَلَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ
Ndipo iwo akupembedza milungu yina kusiya Allah, yomwe singathe kuwapatsa masautso (ngati atasiya kuipembedza) ndiponso siyingathe kuwapatsa chithandizo (ngati atalimbika kuipembedza) ndipo akunena: “Iwo (mafanowo) ndi aomboli athu kwa Allah.” Nena: “Kodi mukumuuza Allah zomwe sakudziwa kumwamba ndi pansi? Wapatukana Allah Ndipo watukuka kuzimene akum’phatikiza nazo.”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمَا كَانَ ٱلنَّاسُ إِلَّآ أُمَّةٗ وَٰحِدَةٗ فَٱخۡتَلَفُواْۚ وَلَوۡلَا كَلِمَةٞ سَبَقَتۡ مِن رَّبِّكَ لَقُضِيَ بَيۡنَهُمۡ فِيمَا فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ
Ndipo ndithudi anthu kalero (m’nthawi ya Adam) adali mpingo umodzi (opembedza Allah), koma adasiyana (pambuyo pake). Ndipo pakadapanda liwu lochokera kwa Mbuye wako, lomwe lidatsogola (lakuti adzawalanga tsiku la Qiyâma), ndithu kukadaweruzidwa pakati pawo m’zomwe adali kusiyana.[218]
[218] Ndithudi, anthu mchilengedwe chawo adali a mpingo umodzi wogonjera Allah mwa chilengedwe. Kenako Allah adawatumizira aneneri kuti awatsogolere kunjira Yake molingana ndi chilamulo chake Allah. Koma ngakhale zili tere anthu adali ndi ufulu mwa chilengedwe chawo kulandira choipa kapena chabwino. Potero, choipa chidawagonjetsa ena a iwo natsata zilakolako za satana. Nasiyana ndi anzawo chifukwa chazimenezo. Komatu padali lamulo la Allah la pachiyambi loti oipa sadzawalanga mwachangu koma kufikira nthawi yawo itakwana. Pakadapanda lamuloli ndiye kuti onse akadawalanga nthawi yomweyo.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَيَقُولُونَ لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡهِ ءَايَةٞ مِّن رَّبِّهِۦۖ فَقُلۡ إِنَّمَا ٱلۡغَيۡبُ لِلَّهِ فَٱنتَظِرُوٓاْ إِنِّي مَعَكُم مِّنَ ٱلۡمُنتَظِرِينَ
Ndipo akunena: “Kukadakhala kuti chinatsitsidwa kwa iye chizindikiro (chotsimikizira uneneri wake) chochokera kwa Mbuye wake (chomwe takhala tikuchipempha nthawi ndi nthawi).” Nena (kwa iwo): “Ndithu kudziwa zobisika nkwa Allah Yekha. Choncho dikirani (chiweruzo cha Allah) inenso pamodzi nanu ndine mmodzi wa odikira.”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِذَآ أَذَقۡنَا ٱلنَّاسَ رَحۡمَةٗ مِّنۢ بَعۡدِ ضَرَّآءَ مَسَّتۡهُمۡ إِذَا لَهُم مَّكۡرٞ فِيٓ ءَايَاتِنَاۚ قُلِ ٱللَّهُ أَسۡرَعُ مَكۡرًاۚ إِنَّ رُسُلَنَا يَكۡتُبُونَ مَا تَمۡكُرُونَ
Ndipo tikawalawitsa anthu mtendere pambuyo pa masautso omwe adawakhudza, pompo iwo amayamba kuzichitira ndale Ayah Zathu. Nena: “Allah ngwachangu kwambiri poononga ndale (zawo).” Ndithu amithenga athu (angelo) akulemba ziwembu zanu (zonse) zimene mukuchita.
அரபு விரிவுரைகள்:
هُوَ ٱلَّذِي يُسَيِّرُكُمۡ فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِۖ حَتَّىٰٓ إِذَا كُنتُمۡ فِي ٱلۡفُلۡكِ وَجَرَيۡنَ بِهِم بِرِيحٖ طَيِّبَةٖ وَفَرِحُواْ بِهَا جَآءَتۡهَا رِيحٌ عَاصِفٞ وَجَآءَهُمُ ٱلۡمَوۡجُ مِن كُلِّ مَكَانٖ وَظَنُّوٓاْ أَنَّهُمۡ أُحِيطَ بِهِمۡ دَعَوُاْ ٱللَّهَ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ لَئِنۡ أَنجَيۡتَنَا مِنۡ هَٰذِهِۦ لَنَكُونَنَّ مِنَ ٱلشَّٰكِرِينَ
Iye ndi Yemwe amakuyendetsani pa ntunda ndi pa nyanja; kufikira pomwe mumakhala m’zombo; ndipo zimayenda nawo (zombozo) ndi mphepo yabwino, naisangalalira. (Mwadzidzidzi) namondwe nkuzidzera (zombozo) ndipo mafunde nkuwadzera mbali zonse natsimikiza kuti azingidwa (ndi chionongeko); amampempha Allah modzipereka kwa Iye mukupempha kwawo (uku akunena): “Ngati mutipulumutsa pa ichi, tidzakhala m’gulu la oyamika (nthawi zonse)!”
அரபு விரிவுரைகள்:
فَلَمَّآ أَنجَىٰهُمۡ إِذَا هُمۡ يَبۡغُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّۗ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِنَّمَا بَغۡيُكُمۡ عَلَىٰٓ أَنفُسِكُمۖ مَّتَٰعَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ ثُمَّ إِلَيۡنَا مَرۡجِعُكُمۡ فَنُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Koma akawapulumutsa, pompo akuyamba kudzitukumula ndi kuononga pa dziko popanda chowayenereza (kutero). E inu anthu! Ndithu kuononga kwanu kukubweretserani masautso inu nokha. Ndipo chisangalalo (chake) cha moyo wa dziko lapansi (nchochepa). Kenako kobwerera kwanu ndi kwa Ife, ndipo tidzakuuzani zomwe munkachita.
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّمَا مَثَلُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا كَمَآءٍ أَنزَلۡنَٰهُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ فَٱخۡتَلَطَ بِهِۦ نَبَاتُ ٱلۡأَرۡضِ مِمَّا يَأۡكُلُ ٱلنَّاسُ وَٱلۡأَنۡعَٰمُ حَتَّىٰٓ إِذَآ أَخَذَتِ ٱلۡأَرۡضُ زُخۡرُفَهَا وَٱزَّيَّنَتۡ وَظَنَّ أَهۡلُهَآ أَنَّهُمۡ قَٰدِرُونَ عَلَيۡهَآ أَتَىٰهَآ أَمۡرُنَا لَيۡلًا أَوۡ نَهَارٗا فَجَعَلۡنَٰهَا حَصِيدٗا كَأَن لَّمۡ تَغۡنَ بِٱلۡأَمۡسِۚ كَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٖ يَتَفَكَّرُونَ
Ndithu fanizo la moyo wadziko lapansi lili ngati madzi amvula, tawatsitsa kuchokera ku mitambo nkusakanikirana ndi zomera za m’nthaka zomwe anthu ndi nyama amadya; kufikira nthaka ikakwaniritsa kukongola kwake ndi kudzikometsa ndipo eni (nthaka) nkuganiza kuti iwo ali ndi mphamvu pa nthakayo (pokolola zomwe zili pamenepo). Mwadzidzidzi nkuzidzera lamulo Lathu (za pa nthakazo), usiku kapena masana, nkuzichita kukhala ngati zokololedwa ngati kuti sizidalipo dzulo (lake). Motere tikufotokoza Ayah kwa anthu olingalira.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَٱللَّهُ يَدۡعُوٓاْ إِلَىٰ دَارِ ٱلسَّلَٰمِ وَيَهۡدِي مَن يَشَآءُ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Ndipo Allah akuitanira (anthu Ake) ku Nyumba yamtendere. Ndipo amamuongolera kunjira yolungama amene wamfuna (ngati ali wotheka kuongoka).
அரபு விரிவுரைகள்:
۞ لِّلَّذِينَ أَحۡسَنُواْ ٱلۡحُسۡنَىٰ وَزِيَادَةٞۖ وَلَا يَرۡهَقُ وُجُوهَهُمۡ قَتَرٞ وَلَا ذِلَّةٌۚ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Ndipo omwe achita zabwino, adzapata (malipiro) abwino ndi zoonjezera. Ndipo fumbi silikavindikira nkhope zawo. Ndiponso kunyozeka sikukawapeza. Iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere; mmenemo akakhala nthawi yaitali.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَٱلَّذِينَ كَسَبُواْ ٱلسَّيِّـَٔاتِ جَزَآءُ سَيِّئَةِۭ بِمِثۡلِهَا وَتَرۡهَقُهُمۡ ذِلَّةٞۖ مَّا لَهُم مِّنَ ٱللَّهِ مِنۡ عَاصِمٖۖ كَأَنَّمَآ أُغۡشِيَتۡ وُجُوهُهُمۡ قِطَعٗا مِّنَ ٱلَّيۡلِ مُظۡلِمًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Ndipo amene akolola zoipa (kuchokera m’zochita zawo zoipa) mphoto ya choipa ndiyofanana ndi icho; ndipo kunyozeka kudzawapeza; sadzakhala ndi aliyense wotha kuwateteza ku chilango cha Allah. Nkhope zawo zidzakhala ngati zaphimbidwa ndi zidutswa za usiku wa m’dima, (zidzakhala zakuda kwambiri); awo ndiwo anthu a ku Moto. Iwo mmenemo adzakhala nthawi yaitali.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَيَوۡمَ نَحۡشُرُهُمۡ جَمِيعٗا ثُمَّ نَقُولُ لِلَّذِينَ أَشۡرَكُواْ مَكَانَكُمۡ أَنتُمۡ وَشُرَكَآؤُكُمۡۚ فَزَيَّلۡنَا بَيۡنَهُمۡۖ وَقَالَ شُرَكَآؤُهُم مَّا كُنتُمۡ إِيَّانَا تَعۡبُدُونَ
Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa onse. Kenako tidzawauza amene ankaphatikiza (Allah ndi mafano kuti): “Imani pompo inu pamodzi ndi aphatikizi anuwo.” Ndipo tidzawasiyanitsa pakati pawo; koma aphatikizi awowo adzati: “Simudali kutipembedza ife (koma mudali kupembedza zilakolako zanu).”
அரபு விரிவுரைகள்:
فَكَفَىٰ بِٱللَّهِ شَهِيدَۢا بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكُمۡ إِن كُنَّا عَنۡ عِبَادَتِكُمۡ لَغَٰفِلِينَ
“Allah akukwanira kukhala mboni pakati pathu ndi pakati panu. Ndithu ife sitidali kuzindikira za mapemphero anu. (Sitinkazindikira kuti inu mukutipembedza).”
அரபு விரிவுரைகள்:
هُنَالِكَ تَبۡلُواْ كُلُّ نَفۡسٖ مَّآ أَسۡلَفَتۡۚ وَرُدُّوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ مَوۡلَىٰهُمُ ٱلۡحَقِّۖ وَضَلَّ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ
Kumeneko munthu aliyense adzadziwa zimene adatsogoza; ndipo adzabwezedwa kwa Allah, Mbuye wawo Woona ndipo zidzawasowa zimene adali kupeka.
அரபு விரிவுரைகள்:
قُلۡ مَن يَرۡزُقُكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ أَمَّن يَمۡلِكُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَمَن يُخۡرِجُ ٱلۡحَيَّ مِنَ ٱلۡمَيِّتِ وَيُخۡرِجُ ٱلۡمَيِّتَ مِنَ ٱلۡحَيِّ وَمَن يُدَبِّرُ ٱلۡأَمۡرَۚ فَسَيَقُولُونَ ٱللَّهُۚ فَقُلۡ أَفَلَا تَتَّقُونَ
Nena: “Kodi ndani akukupatsani (zopatsa) kuchokera kumwamba (povumbwitsa mvula), ndi pansi (pomeretsa mmera)? Nanga ndani amakupatsani kumva ndi kupenya? Nanga ndani amene akutulutsa chamoyo kuchokera m’chakufa, ndi kutulutsa chakufa kuchokera m’chamoyo? Nanga ndani akukonza zinthu zonse?” Anena: “Ndi Allah.” Choncho, nena: “Kodi bwanji simukumuopa?”
அரபு விரிவுரைகள்:
فَذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمُ ٱلۡحَقُّۖ فَمَاذَا بَعۡدَ ٱلۡحَقِّ إِلَّا ٱلضَّلَٰلُۖ فَأَنَّىٰ تُصۡرَفُونَ
Uyo ndi Allah, Mbuye wanu Woona; nanga pali chiyani pambuyo poleka choonadi, sikusokera basi? Kodi nanga mukutembenuzidwa chotani (kusiya choonadi)?
அரபு விரிவுரைகள்:
كَذَٰلِكَ حَقَّتۡ كَلِمَتُ رَبِّكَ عَلَى ٱلَّذِينَ فَسَقُوٓاْ أَنَّهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Momwemo liwu la Mbuye wako latsimikizika kwa amene adatuluka m’chilamulo cha Allah kuti iwo sadzakhulupirira.
அரபு விரிவுரைகள்:
قُلۡ هَلۡ مِن شُرَكَآئِكُم مَّن يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥۚ قُلِ ٱللَّهُ يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥۖ فَأَنَّىٰ تُؤۡفَكُونَ
Nena: “Kodi alipo mwa aphatikizi anu (mafano) amene angayambitse kulenga zolengedwa; kenako (zitafa) ndikuzibweza?” Nena: “Allah ndi Yemwe akuyambitsa zolengedwa kenaka ndi kuzibweza (pambuyo poonongeka). Nanga mukunamizidwa chotani (kusiya chikhulupiliro)?”
அரபு விரிவுரைகள்:
قُلۡ هَلۡ مِن شُرَكَآئِكُم مَّن يَهۡدِيٓ إِلَى ٱلۡحَقِّۚ قُلِ ٱللَّهُ يَهۡدِي لِلۡحَقِّۗ أَفَمَن يَهۡدِيٓ إِلَى ٱلۡحَقِّ أَحَقُّ أَن يُتَّبَعَ أَمَّن لَّا يَهِدِّيٓ إِلَّآ أَن يُهۡدَىٰۖ فَمَا لَكُمۡ كَيۡفَ تَحۡكُمُونَ
Nena: “Kodi alipo mwa aphatikizi anu (mafano) woongolera kuchoonadi?” Nena: “Allah ndi Yemwe akuongolera ku choonadi. Kodi amene akutsogolera ku choonadi sindiye woyenera kwambiri kutsatidwa kapena (woyenera kutsatidwa ndi) yemwe sakutha kudziongola pokhapokha atawongoledwa ndi wina wake? Nanga mwatani kodi, kodi mukuweruza bwanji?”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمَا يَتَّبِعُ أَكۡثَرُهُمۡ إِلَّا ظَنًّاۚ إِنَّ ٱلظَّنَّ لَا يُغۡنِي مِنَ ٱلۡحَقِّ شَيۡـًٔاۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمُۢ بِمَا يَفۡعَلُونَ
Ndipo ambiri a iwo satsatira (china) koma zoganizira basi, (osati chomwe afufuza ndikuchizindikira ndi nzeru zawo). Ndithu choganizira sichithandiza ngakhale pang’ono ku choonadi. Ndithu Allah akudziwa zonse zimene akuchita.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمَا كَانَ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانُ أَن يُفۡتَرَىٰ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلَٰكِن تَصۡدِيقَ ٱلَّذِي بَيۡنَ يَدَيۡهِ وَتَفۡصِيلَ ٱلۡكِتَٰبِ لَا رَيۡبَ فِيهِ مِن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo sikotheka Qur’an iyi kukhala yopekedwa, yosachokera kwa Allah (monga momwe munenera). Koma (yachokera kwa Allah) kutsimikizira zomwe zidalipo patsogolo pake, ndi kulongosola za buku (lakale). Palibe chikaiko m’menemo (kuti) yachokera kwa Mbuye wa zolengedwa.
அரபு விரிவுரைகள்:
أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰهُۖ قُلۡ فَأۡتُواْ بِسُورَةٖ مِّثۡلِهِۦ وَٱدۡعُواْ مَنِ ٱسۡتَطَعۡتُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Kapena akunena kuti waipeka? Nena: “Tabwerani ndi sura (imodzi) yofanana ndi iyo, ndipo itanani amene mungathe (kuwaitana kuti akuthandizeni) kupatula Allah, ngati inu mukunena zoona (kuti Qur’aniyi waipeka Muhammad {s.a.w}).”
அரபு விரிவுரைகள்:
بَلۡ كَذَّبُواْ بِمَا لَمۡ يُحِيطُواْ بِعِلۡمِهِۦ وَلَمَّا يَأۡتِهِمۡ تَأۡوِيلُهُۥۚ كَذَٰلِكَ كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلظَّٰلِمِينَ
Koma atsutsa zomwe sakuzizindikira (m’mene zilili) ngakhale tanthauzo lake (la kuona kwake kapena kunama kwake) lisanawafike. Momwemonso adatsutsa omwe adalipo patsogolo pawo. Choncho, taona momwe mathero a anthu ochimwa adalili.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمِنۡهُم مَّن يُؤۡمِنُ بِهِۦ وَمِنۡهُم مَّن لَّا يُؤۡمِنُ بِهِۦۚ وَرَبُّكَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُفۡسِدِينَ
Ndipo mwa iwo pali ena omwe akuikhulupirira (Qur’an), ndipo ena mwa iwo sakuikhulupirira. Ndipo Mbuye wako akuwadziwa bwino oononga.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِن كَذَّبُوكَ فَقُل لِّي عَمَلِي وَلَكُمۡ عَمَلُكُمۡۖ أَنتُم بَرِيٓـُٔونَ مِمَّآ أَعۡمَلُ وَأَنَا۠ بَرِيٓءٞ مِّمَّا تَعۡمَلُونَ
Ndipo ngati apitiriza kukutsutsa, nena: “Ine ndili ndi ntchito yanga, inunso muli ndi ntchito yanu. Inu mwatalikirana nazo zimene ndikuchita, inenso ndatalikirana nazo zimene mukuchita!”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمِنۡهُم مَّن يَسۡتَمِعُونَ إِلَيۡكَۚ أَفَأَنتَ تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ وَلَوۡ كَانُواْ لَا يَعۡقِلُونَ
Ndipo mwa iwo alipo ena amene akumvetsera kwa iwe, (koma osati ndi cholinga choti adziwe). Kodi iwe ungathe kuwamveretsa agonthi, chikhalirecho nzeru alibe?
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمِنۡهُم مَّن يَنظُرُ إِلَيۡكَۚ أَفَأَنتَ تَهۡدِي ٱلۡعُمۡيَ وَلَوۡ كَانُواْ لَا يُبۡصِرُونَ
Ndipo alipo ena mwa iwo amene akukutong’olera maso (kukuyang’ana monyoza). Kodi iwe ungathe kuwatsogolera akhungu, chikhalirecho sali openya?
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَظۡلِمُ ٱلنَّاسَ شَيۡـٔٗا وَلَٰكِنَّ ٱلنَّاسَ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ
Ndithu Allah sachitira anthu choipa chilichonse. Koma anthu akudzichitira okha zoipa. (Adapatsidwa nzeru, koma sazigwiritsa ntchito).
அரபு விரிவுரைகள்:
وَيَوۡمَ يَحۡشُرُهُمۡ كَأَن لَّمۡ يَلۡبَثُوٓاْ إِلَّا سَاعَةٗ مِّنَ ٱلنَّهَارِ يَتَعَارَفُونَ بَيۡنَهُمۡۚ قَدۡ خَسِرَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِلِقَآءِ ٱللَّهِ وَمَا كَانُواْ مُهۡتَدِينَ
Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe adzawasonkhanitsa (onse) ngati kuti sadakhale (pa dziko lapansi) koma ola limodzi la usana (atathedwa nzeru). Adzazindikirana pakati pawo; (koma aliyense sadzalabadira mnzake). Ndithu aonongeka amene adatsutsa za kukumana ndi Allah ndipo sadali oongoka.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِمَّا نُرِيَنَّكَ بَعۡضَ ٱلَّذِي نَعِدُهُمۡ أَوۡ نَتَوَفَّيَنَّكَ فَإِلَيۡنَا مَرۡجِعُهُمۡ ثُمَّ ٱللَّهُ شَهِيدٌ عَلَىٰ مَا يَفۡعَلُونَ
Ndipo ngati tingakusonyeze (pompano pa dziko lapansi) zina mwa zomwe tikuwalonjeza ndikuwachenjeza nazo, kapena kukubweretsera imfa (usadazione zimenezo), kobwerera kwawo nkwa Ife basi. Kenako Allah ndi mboni pa zomwe akuchita.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلِكُلِّ أُمَّةٖ رَّسُولٞۖ فَإِذَا جَآءَ رَسُولُهُمۡ قُضِيَ بَيۡنَهُم بِٱلۡقِسۡطِ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ
Ndipo fuko lililonse lili ndi Mtumiki ndipo akazabwera Mtumiki wawo (tsiku la chiweruziro), kudzaweruzidwa pakati pawo mwa chilungamo ndipo sadzaponderezedwa.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Ndipo akunena (osakhulupirira): “Kodi lonjezo ili lidzachitika liti ngati mukunena zoona?”
அரபு விரிவுரைகள்:
قُل لَّآ أَمۡلِكُ لِنَفۡسِي ضَرّٗا وَلَا نَفۡعًا إِلَّا مَا شَآءَ ٱللَّهُۗ لِكُلِّ أُمَّةٍ أَجَلٌۚ إِذَا جَآءَ أَجَلُهُمۡ فَلَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ سَاعَةٗ وَلَا يَسۡتَقۡدِمُونَ
Nena: “Ndilibe mphamvu mwandekha pa (kudzichotsera) vuto ngakhale (kudzibweretsera) thandizo. (Nanga za zimenezo ndingadziweponji)? Koma chimene Allah wafuna (ndi chomwe chimachitika). M’badwo uli wonse uli ndi nthawi yake (yofera). Nthawi yawo (yofera) ikadza sangathe kuichedwetsa ola limodzi ngakhale kuifulumizitsa.”
அரபு விரிவுரைகள்:
قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ إِنۡ أَتَىٰكُمۡ عَذَابُهُۥ بَيَٰتًا أَوۡ نَهَارٗا مَّاذَا يَسۡتَعۡجِلُ مِنۡهُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ
Nena: “Kodi mukuona bwanji, ngati chilango chakecho chitakudzerani usiku kapena usana (mungathe kuthawa)? Nanga bwanji ochimwa akuchifulumizitsa (kuti chidze mwachangu)?”
அரபு விரிவுரைகள்:
أَثُمَّ إِذَا مَا وَقَعَ ءَامَنتُم بِهِۦٓۚ ءَآلۡـَٰٔنَ وَقَدۡ كُنتُم بِهِۦ تَسۡتَعۡجِلُونَ
“Kodi chikadza ndipamene mudzachikhulupirire?” Panthawiyo mudzauzidwa): “Kodi tsopano (ndi pamene mukukhulupirira), chikhalirecho mudali kuchifulumizitsa (kale)?”
அரபு விரிவுரைகள்:
ثُمَّ قِيلَ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ ذُوقُواْ عَذَابَ ٱلۡخُلۡدِ هَلۡ تُجۡزَوۡنَ إِلَّا بِمَا كُنتُمۡ تَكۡسِبُونَ
Kenako kudzanenedwa kwa amene adachita zoipa: “Lawani chilango chamuyaya! Kodi mungalipidwe zina osakhala zomwe mudazipata (kuchokera m’zochita zanu zoipa)?”
அரபு விரிவுரைகள்:
۞ وَيَسۡتَنۢبِـُٔونَكَ أَحَقٌّ هُوَۖ قُلۡ إِي وَرَبِّيٓ إِنَّهُۥ لَحَقّٞۖ وَمَآ أَنتُم بِمُعۡجِزِينَ
Eti akukufunsa: “Kodi nzoona izo (zimene ukunena)?” Nena: “Inde! Ndikulumbira kwa Mbuye wanga, zimenezo ndi zoona. Ndipo inu simuli olepheretsa (Allah).”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَوۡ أَنَّ لِكُلِّ نَفۡسٖ ظَلَمَتۡ مَا فِي ٱلۡأَرۡضِ لَٱفۡتَدَتۡ بِهِۦۗ وَأَسَرُّواْ ٱلنَّدَامَةَ لَمَّا رَأَوُاْ ٱلۡعَذَابَۖ وَقُضِيَ بَيۡنَهُم بِٱلۡقِسۡطِ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ
Ndipo kukadakhala kuti munthu aliyense amene adachita zoipa, nkukhala nazo zonse zam’dziko akadapereka zonse kuti adziombole nazo (pamene adzaona kuopsa kwa chilango cha tsikulo). Ndipo akadzachiona chilango, adzayesetsa kubisa madandaulo (awo; koma adzaonekera poyera). Ndipo kudzaweruzidwa mwachilungamo pakati pawo, ndipo iwo sadzaponderezedwa.
அரபு விரிவுரைகள்:
أَلَآ إِنَّ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ أَلَآ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
Tamverani! Ndithu zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah. Tamverani! Ndithu lonjezo la Allah ndi loona, koma ambiri a iwo sadziwa.
அரபு விரிவுரைகள்:
هُوَ يُحۡيِۦ وَيُمِيتُ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Iye (Allah ndi amene) amapereka moyo ndi imfa. Ndipo kwa Iye (nonsenu) mudzabwezedwa.
அரபு விரிவுரைகள்:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ قَدۡ جَآءَتۡكُم مَّوۡعِظَةٞ مِّن رَّبِّكُمۡ وَشِفَآءٞ لِّمَا فِي ٱلصُّدُورِ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٞ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ
E inu anthu! Ndithu ulaliki wakudzerani kuchokera kwa Mbuye wanu ndi machiritso a matenda omwe ali m’mitima mwanu, ndiponso nchiongoko ndi chifundo kwa okhulupirira.
அரபு விரிவுரைகள்:
قُلۡ بِفَضۡلِ ٱللَّهِ وَبِرَحۡمَتِهِۦ فَبِذَٰلِكَ فَلۡيَفۡرَحُواْ هُوَ خَيۡرٞ مِّمَّا يَجۡمَعُونَ
Nena: “Chifukwa cha ubwino wa Allah ndi chifundo Chake (mwapeza zimenezi), choncho asangalalire zimenezi.” Izi ndizabwino kwambiri kuposa zimene akusonkhanitsa (m’zinthu za dziko lapansi).
அரபு விரிவுரைகள்:
قُلۡ أَرَءَيۡتُم مَّآ أَنزَلَ ٱللَّهُ لَكُم مِّن رِّزۡقٖ فَجَعَلۡتُم مِّنۡهُ حَرَامٗا وَحَلَٰلٗا قُلۡ ءَآللَّهُ أَذِنَ لَكُمۡۖ أَمۡ عَلَى ٱللَّهِ تَفۡتَرُونَ
Nena: “Kodi mukuona bwanji, rizq lomwe Allah wakutsitsirani? Kenako inu lina mwa ilo mwalichita kukhala loletsedwa (la haramu), ndipo lina mwa ilo kukhala lololedwa (la halali).” Nena: “Kodi Allah adakulolezani (kuchita zimenezo), kapena mukumpekera Allah bodza?”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمَا ظَنُّ ٱلَّذِينَ يَفۡتَرُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۗ إِنَّ ٱللَّهَ لَذُو فَضۡلٍ عَلَى ٱلنَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَشۡكُرُونَ
Kodi ali ndi ganizo lotani amene akumpekera Allah bodza pa za tsiku la Qiyâma? Ndithu Allah Ndi mwini ubwino wochuluka kwa anthu. Koma ambiri a iwo sathokoza.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمَا تَكُونُ فِي شَأۡنٖ وَمَا تَتۡلُواْ مِنۡهُ مِن قُرۡءَانٖ وَلَا تَعۡمَلُونَ مِنۡ عَمَلٍ إِلَّا كُنَّا عَلَيۡكُمۡ شُهُودًا إِذۡ تُفِيضُونَ فِيهِۚ وَمَا يَعۡزُبُ عَن رَّبِّكَ مِن مِّثۡقَالِ ذَرَّةٖ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا فِي ٱلسَّمَآءِ وَلَآ أَصۡغَرَ مِن ذَٰلِكَ وَلَآ أَكۡبَرَ إِلَّا فِي كِتَٰبٖ مُّبِينٍ
Ndipo siutanganidwa ndi ntchito iliyonse, ndiponso simuwerenga m’menemo (chinthu chilichonse) cha m’Qur’an ndipo simuchita ntchito ina iliyonse (inu anthu) koma Ife timakhala mboni pa inu pamene mukutanganidwa nayo. Ndipo sichibisika kwa Mbuye wako chinthu chilichonse ngakhale cholemera ngati nyelere, m’nthaka ngakhale kumwamba. Ndipo ngakhale chocheperapo zedi kuposa pamenepo kapena chokulirapo koma chili m’kuku (la Allah) lofotokoza chilichonse.
அரபு விரிவுரைகள்:
أَلَآ إِنَّ أَوۡلِيَآءَ ٱللَّهِ لَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ
Tamverani! Ndithu okondedwa a Allah sadzakhala ndi mantha (pa tsiku la Qiyâma), ndipo sadzadandaula.
அரபு விரிவுரைகள்:
ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَكَانُواْ يَتَّقُونَ
(Amenewo ndi) amene adakhulupirira ndi kumuopa (Allah).
அரபு விரிவுரைகள்:
لَهُمُ ٱلۡبُشۡرَىٰ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَفِي ٱلۡأٓخِرَةِۚ لَا تَبۡدِيلَ لِكَلِمَٰتِ ٱللَّهِۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
Iwo ali ndi zabwino pa moyo wa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro. Palibe kusintha pa mawu a Allah. Uku ndiko kupambana kwakukulu.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَا يَحۡزُنكَ قَوۡلُهُمۡۘ إِنَّ ٱلۡعِزَّةَ لِلَّهِ جَمِيعًاۚ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
Ndipo (iwe, Mtumiki) zisakudandaulitse zonena zawo (zomwe akukunenera monyoza). Ndithu ulemelero ndi mphamvu zonse nza Allah. Iye Ngwakumva, Ngodziwa.
அரபு விரிவுரைகள்:
أَلَآ إِنَّ لِلَّهِ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِۗ وَمَا يَتَّبِعُ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ شُرَكَآءَۚ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّ وَإِنۡ هُمۡ إِلَّا يَخۡرُصُونَ
Tamverani! Ndithu (zonse) za kumwamba ndi za pansi, nza Allah. Ndipo amene akupembedza zina kusiya Allah, satsatira aphatikizi (a Allah). Akungotsatira zoganizira, ndipo iwo sanena china koma bodza basi.
அரபு விரிவுரைகள்:
هُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلَّيۡلَ لِتَسۡكُنُواْ فِيهِ وَٱلنَّهَارَ مُبۡصِرًاۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَسۡمَعُونَ
Iye (Allah) ndi Yemwe adakupangirani usiku kuti muzipumamo, ndi (adakupangirani) usana kukhala wowala (kuti mupenye). Ndithu m’zimene muli zisonyezo (zosonyeza chifundo cha Allah pa zolengedwa Zake) kwa anthu akumva.
அரபு விரிவுரைகள்:
قَالُواْ ٱتَّخَذَ ٱللَّهُ وَلَدٗاۗ سُبۡحَٰنَهُۥۖ هُوَ ٱلۡغَنِيُّۖ لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ إِنۡ عِندَكُم مِّن سُلۡطَٰنِۭ بِهَٰذَآۚ أَتَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ
Akunena: “Allah wadzipangira mwana.” Wapatukana ndi zimenezo! Iye Ngokwanira, (salakalaka mwana ngakhale mthangati aliyense). NdiZake (zonse) za kumwamba ndi za pansi. Inu mulibe umboni pa zimenezi. Kodi mukumnenera Allah zomwe simukuzidziwa?
அரபு விரிவுரைகள்:
قُلۡ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَفۡتَرُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ لَا يُفۡلِحُونَ
Nena: “Ndithu amene akumpekera Allah bodza, sadzapambana.”
அரபு விரிவுரைகள்:
مَتَٰعٞ فِي ٱلدُّنۡيَا ثُمَّ إِلَيۡنَا مَرۡجِعُهُمۡ ثُمَّ نُذِيقُهُمُ ٱلۡعَذَابَ ٱلشَّدِيدَ بِمَا كَانُواْ يَكۡفُرُونَ
Ndichisangalalo chochepa basi m’dziko lapansi. Kenako kwa Ife ndiwo mabwelero awo. Kenako tidzawalawitsa chilango chaukali chifukwa cha kusakhulupirira kwawo.
அரபு விரிவுரைகள்:
۞ وَٱتۡلُ عَلَيۡهِمۡ نَبَأَ نُوحٍ إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ إِن كَانَ كَبُرَ عَلَيۡكُم مَّقَامِي وَتَذۡكِيرِي بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ فَعَلَى ٱللَّهِ تَوَكَّلۡتُ فَأَجۡمِعُوٓاْ أَمۡرَكُمۡ وَشُرَكَآءَكُمۡ ثُمَّ لَا يَكُنۡ أَمۡرُكُمۡ عَلَيۡكُمۡ غُمَّةٗ ثُمَّ ٱقۡضُوٓاْ إِلَيَّ وَلَا تُنظِرُونِ
Ndipo awerengere (molakatula) nkhani za Nuh pamene adanena kwa anthu ake: “E inu anthu anga! Ngati kukhala kwanga pamodzi ndi inu ndi kukumbutsa kwanga Ayah za Allah kukukukulirani, ine ndatsamira kwa Allah (sindisiya ntchito yangayi). Choncho sonkhanitsani zinthu zanu pamodzi ndi milungu yanuyo; (sonkhanani kuti mundichitire choipa, ine sindilabadira chilichonse). Ndipo chinthu chanucho chisabisike kwa inu, (chitani moonekera. Ine sinditekeseka ndi chilichonse). Kenako chitani pa ine (chimene mufuna kuchita) ndipo musandipatse danga.
அரபு விரிவுரைகள்:
فَإِن تَوَلَّيۡتُمۡ فَمَا سَأَلۡتُكُم مِّنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَى ٱللَّهِۖ وَأُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ
Ngati mutembenuka ndikunyoza, (ndikufuna kwanu). Ine sindinakupempheni malipiro. Malipiro anga kulibe kulikonse (kumene ndingalandire) koma kwa Allah, ndipo ndalamulidwa kuti ndikhale mmodzi mwa Asilamu (ogonjera Iye).”
அரபு விரிவுரைகள்:
فَكَذَّبُوهُ فَنَجَّيۡنَٰهُ وَمَن مَّعَهُۥ فِي ٱلۡفُلۡكِ وَجَعَلۡنَٰهُمۡ خَلَٰٓئِفَ وَأَغۡرَقۡنَا ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَاۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُنذَرِينَ
Koma adamutsutsa. Choncho tidampulumutsa pamodzi ndi amene adali naye m’chombo. Ndipo tidawasankha iwo kukhala otsala (pa dziko anzawo ataonongeka). Ndipo tidawamiza amene adatsutsa Ayah Zathu. Choncho taona momwe mapeto a ochenjezedwa adalili!
அரபு விரிவுரைகள்:
ثُمَّ بَعَثۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِۦ رُسُلًا إِلَىٰ قَوۡمِهِمۡ فَجَآءُوهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَمَا كَانُواْ لِيُؤۡمِنُواْ بِمَا كَذَّبُواْ بِهِۦ مِن قَبۡلُۚ كَذَٰلِكَ نَطۡبَعُ عَلَىٰ قُلُوبِ ٱلۡمُعۡتَدِينَ
Pambuyo pake tidawatumiza atumiki (ambiri) kwa anthu awo. Adawadzera ndi zisonyezo zoonekera poyera koma sadali okhulupirira zimene ena adazitsutsa kale, (adatsatira njira zomwezo za anzawo). Umo ndi momwe tikudindira zidindo m’mitima ya anthu opyola malire.
அரபு விரிவுரைகள்:
ثُمَّ بَعَثۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِم مُّوسَىٰ وَهَٰرُونَ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ بِـَٔايَٰتِنَا فَٱسۡتَكۡبَرُواْ وَكَانُواْ قَوۡمٗا مُّجۡرِمِينَ
Kenako pambuyo pawo tidamtuma Mûsa ndi Haarun pamodzi ndi zizindikiro zathu kwa Farawo ndi nduna zake, koma adadzikweza. Tero adali anthu ochita zoipa.
அரபு விரிவுரைகள்:
فَلَمَّا جَآءَهُمُ ٱلۡحَقُّ مِنۡ عِندِنَا قَالُوٓاْ إِنَّ هَٰذَا لَسِحۡرٞ مُّبِينٞ
Ndipo pamene choonadi chidawadzera kuchokera kwa Ife, adanena: “Ndithu awa ndimatsenga oonekera.”
அரபு விரிவுரைகள்:
قَالَ مُوسَىٰٓ أَتَقُولُونَ لِلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَكُمۡۖ أَسِحۡرٌ هَٰذَا وَلَا يُفۡلِحُ ٱلسَّٰحِرُونَ
Mûsa adati: “Mukutero pa choonadi pamene chakudzerani? Kodi matsenga ali chonchi? Ndipo amatsenga sangapambane (ngakhale zitatani).”
அரபு விரிவுரைகள்:
قَالُوٓاْ أَجِئۡتَنَا لِتَلۡفِتَنَا عَمَّا وَجَدۡنَا عَلَيۡهِ ءَابَآءَنَا وَتَكُونَ لَكُمَا ٱلۡكِبۡرِيَآءُ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا نَحۡنُ لَكُمَا بِمُؤۡمِنِينَ
(Iwo) adati: “Kodi watidzera kuti utichotse ku zimene tidawapeza nazo makolo athu kuti ukulu ukhale wa inu awiri m’dzikoli? Koma ife sitingakukhulupirireni awirinu.”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَقَالَ فِرۡعَوۡنُ ٱئۡتُونِي بِكُلِّ سَٰحِرٍ عَلِيمٖ
Ndipo Farawo adati: “Ndibweretsereni wamatsenga aliyense wodziwa kwambiri (zamatsenga).”
அரபு விரிவுரைகள்:
فَلَمَّا جَآءَ ٱلسَّحَرَةُ قَالَ لَهُم مُّوسَىٰٓ أَلۡقُواْ مَآ أَنتُم مُّلۡقُونَ
Ndipo pamene amatsenga adadza, Mûsa adati kwa iwo: “Ponyani zomwe mufuna kuponya (kuti musonyeze ukatswiri wanu kwa anthu).”
அரபு விரிவுரைகள்:
فَلَمَّآ أَلۡقَوۡاْ قَالَ مُوسَىٰ مَا جِئۡتُم بِهِ ٱلسِّحۡرُۖ إِنَّ ٱللَّهَ سَيُبۡطِلُهُۥٓ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُصۡلِحُ عَمَلَ ٱلۡمُفۡسِدِينَ
Pamene adaponya, Mûsa adati: “Zomwe mwabweretsa ndi matsenga. Allah awaononga pompano. Ndithu Allah sakonza ntchito za oononga.”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَيُحِقُّ ٱللَّهُ ٱلۡحَقَّ بِكَلِمَٰتِهِۦ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡمُجۡرِمُونَ
“Ndipo Allah achilimbikitsa choonadi ndi mau Ake, ngakhale oipa anyansidwe nazo.”
அரபு விரிவுரைகள்:
فَمَآ ءَامَنَ لِمُوسَىٰٓ إِلَّا ذُرِّيَّةٞ مِّن قَوۡمِهِۦ عَلَىٰ خَوۡفٖ مِّن فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِمۡ أَن يَفۡتِنَهُمۡۚ وَإِنَّ فِرۡعَوۡنَ لَعَالٖ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَإِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلۡمُسۡرِفِينَ
Sadamkhulupirire Mûsa kupatula achinyamata a mwa anthu ake, chifukwa choopa Farawo ndi nduna zake kuti angawazunze. Ndithu Farawo adali wodzikuza pa dziko, ndithudi, adali m’modzi mwa opyola malire.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَقَالَ مُوسَىٰ يَٰقَوۡمِ إِن كُنتُمۡ ءَامَنتُم بِٱللَّهِ فَعَلَيۡهِ تَوَكَّلُوٓاْ إِن كُنتُم مُّسۡلِمِينَ
Ndipo Mûsa adati: “E inu anthu anga! Ngati inu mwakhulupirira Allah, choncho tsamirani kwa Iye ngati mulidi Asilamu (owona).
அரபு விரிவுரைகள்:
فَقَالُواْ عَلَى ٱللَّهِ تَوَكَّلۡنَا رَبَّنَا لَا تَجۡعَلۡنَا فِتۡنَةٗ لِّلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ
Choncho (iwo) adati: “Tayadzamira kwa Allah. E Mbuye wathu! Musatichite kukhala mayetsero kwa anthu oipa.”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَنَجِّنَا بِرَحۡمَتِكَ مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡكَٰفِرِينَ
“Ndipo tipulumutseni mwa chifundo Chanu ku anthu osakhulupirira.”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰ وَأَخِيهِ أَن تَبَوَّءَا لِقَوۡمِكُمَا بِمِصۡرَ بُيُوتٗا وَٱجۡعَلُواْ بُيُوتَكُمۡ قِبۡلَةٗ وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndipo tidavumbulutsa kwa Mûsa ndi m’bale wake mawu Athu (oti): “Apangireni nyumba anthu anu mu Eguputo ndipo nyumba zanu zichiteni kukhala misikiti (pakuti simungathe kukhala ndi misikiti yoonekera), ndipo pempherani Swala. Ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira (kuti Allah awapatsa zabwino pa moyo wa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro).”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَقَالَ مُوسَىٰ رَبَّنَآ إِنَّكَ ءَاتَيۡتَ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَأَهُۥ زِينَةٗ وَأَمۡوَٰلٗا فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا رَبَّنَا لِيُضِلُّواْ عَن سَبِيلِكَۖ رَبَّنَا ٱطۡمِسۡ عَلَىٰٓ أَمۡوَٰلِهِمۡ وَٱشۡدُدۡ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ فَلَا يُؤۡمِنُواْ حَتَّىٰ يَرَوُاْ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَلِيمَ
Ndipo Mûsa adati: “Mbuye wathu! Inu mwampatsa Farawo ndi nduna zake zodzikometsera, ndi chuma chambirimbiri pa moyo wa pa dziko. Mbuye wathu, (iwo akugwiritsa ntchito zimenezi) kuti asokeretse anthu pa njira Yanu. Mbuye wathu, wonongani chuma chawo ndipo iumitseni mitima yawo popeza sakhulupirira kufikira ataona chilango chowawa.”
அரபு விரிவுரைகள்:
قَالَ قَدۡ أُجِيبَت دَّعۡوَتُكُمَا فَٱسۡتَقِيمَا وَلَا تَتَّبِعَآنِّ سَبِيلَ ٱلَّذِينَ لَا يَعۡلَمُونَ
(Allah) adati: “Pempho lanu lavomerezedwa! Choncho lungamani mwaubwino, ndipo musatsate njira za omwe sadziwa.”
அரபு விரிவுரைகள்:
۞ وَجَٰوَزۡنَا بِبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱلۡبَحۡرَ فَأَتۡبَعَهُمۡ فِرۡعَوۡنُ وَجُنُودُهُۥ بَغۡيٗا وَعَدۡوًاۖ حَتَّىٰٓ إِذَآ أَدۡرَكَهُ ٱلۡغَرَقُ قَالَ ءَامَنتُ أَنَّهُۥ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا ٱلَّذِيٓ ءَامَنَتۡ بِهِۦ بَنُوٓاْ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَأَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ
Ndipo tidawaolotsa pa nyanja ana a Israyeli. Ndipo Farawo ndi asilikali ake ankhondo adawatsata moipitsa ndi mwamtopola, kufikira pamene kumira kudampeza; (iye) adati: “Ndakhulupirira kuti palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Yemwe ana a Israyeli amkhulupirira. Ndipo ine ndine mmodzi mwa Asilamu (omugonjera monga iwo akumgonjera).”
அரபு விரிவுரைகள்:
ءَآلۡـَٰٔنَ وَقَدۡ عَصَيۡتَ قَبۡلُ وَكُنتَ مِنَ ٱلۡمُفۡسِدِينَ
(Angelo adamuuza kuti:) “Tsopano (ndipamene ukukhulupirira), pomwe kale udanyoza ndikukhala mmodzi wa oononga!”
அரபு விரிவுரைகள்:
فَٱلۡيَوۡمَ نُنَجِّيكَ بِبَدَنِكَ لِتَكُونَ لِمَنۡ خَلۡفَكَ ءَايَةٗۚ وَإِنَّ كَثِيرٗا مِّنَ ٱلنَّاسِ عَنۡ ءَايَٰتِنَا لَغَٰفِلُونَ
“Choncho lero tikupulumutsa (polisunga) thupi lako, kuti ukhale chisonyezo kwa amene akudza m’mbuyo mwako (kuti adziwe kuti sudali mulungu). Koma ndithu anthu ambiri salabadira zisonyezo Zathu.”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَقَدۡ بَوَّأۡنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ مُبَوَّأَ صِدۡقٖ وَرَزَقۡنَٰهُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ فَمَا ٱخۡتَلَفُواْ حَتَّىٰ جَآءَهُمُ ٱلۡعِلۡمُۚ إِنَّ رَبَّكَ يَقۡضِي بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فِيمَا كَانُواْ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ
Ndipo ndithu (pambuyo pake) tidawakonzera mokhala mwabwino ana a Israyeli, ndikuwapatsa zabwino. Sadasiyane kufikira pamene kuzindikira kudawadzera. Ndithu Mbuye wako adzaweruza pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zimene adali kutsutsana.
அரபு விரிவுரைகள்:
فَإِن كُنتَ فِي شَكّٖ مِّمَّآ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكَ فَسۡـَٔلِ ٱلَّذِينَ يَقۡرَءُونَ ٱلۡكِتَٰبَ مِن قَبۡلِكَۚ لَقَدۡ جَآءَكَ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُمۡتَرِينَ
Ngati uli ndi chipeneko pa zimene takuvumbulutsira, afunse amene akuwerenga mabuku akale (Ayuda ndi Akhrisitu amene alowa m’Chisilamu). Ndithu choonadi chakufika kuchokera kwa Mbuye wako. Choncho usakhale mwa amene akukaikira.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ فَتَكُونَ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ
Ndiponso usakhale mwa omwe akutsutsa zizindikiro za Allah, kuopa kuti ungadzakhale m’gulu la otaika.
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ ٱلَّذِينَ حَقَّتۡ عَلَيۡهِمۡ كَلِمَتُ رَبِّكَ لَا يُؤۡمِنُونَ
Ndithu aja amene liwu la Mbuye wako latsimikizika pa iwo, sakhulupirira.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَوۡ جَآءَتۡهُمۡ كُلُّ ءَايَةٍ حَتَّىٰ يَرَوُاْ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَلِيمَ
Ndipo ngakhale kuti chisonyezo chamtundu uliwonse chiwadzere (sangakhulupirirebe), mpaka aone chilango chopweteka.
அரபு விரிவுரைகள்:
فَلَوۡلَا كَانَتۡ قَرۡيَةٌ ءَامَنَتۡ فَنَفَعَهَآ إِيمَٰنُهَآ إِلَّا قَوۡمَ يُونُسَ لَمَّآ ءَامَنُواْ كَشَفۡنَا عَنۡهُمۡ عَذَابَ ٱلۡخِزۡيِ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَمَتَّعۡنَٰهُمۡ إِلَىٰ حِينٖ
Kodi udalipo mudzi (ndi umodzi womwe pakati pa midzi mwa yomwe tidaiwononga), umene udalapa ndi kukhulupirira (pambuyo poona chilango kotero kuti) chikhulupiliro chake nkuuthandiza pa nthawi imeneyo, osati kupatula anthu a Yunus okha? Pamene adakhulupirira, tidawachotsera chilango choyalutsa m’moyo wa padziko lapansi, ndipo tidawasangalatsa kufikira nthawi yawo (yofera).
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَوۡ شَآءَ رَبُّكَ لَأٓمَنَ مَن فِي ٱلۡأَرۡضِ كُلُّهُمۡ جَمِيعًاۚ أَفَأَنتَ تُكۡرِهُ ٱلنَّاسَ حَتَّىٰ يَكُونُواْ مُؤۡمِنِينَ
Ndipo Mbuye wako akadafuna (kuwakakamiza anthu mwamphamvu kuti akhulupirire), onse ali m’dziko lapansi akadakhulupirira (sipakadatsala ndi mmodzi yemwe. Koma Allah safuna kukakamiza anthu mwamphamvu). Nanga kodi iwe uwakakamiza anthu kuti akhale okhulupirira?
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمَا كَانَ لِنَفۡسٍ أَن تُؤۡمِنَ إِلَّا بِإِذۡنِ ٱللَّهِۚ وَيَجۡعَلُ ٱلرِّجۡسَ عَلَى ٱلَّذِينَ لَا يَعۡقِلُونَ
Ndipo palibe munthu angakhulupirire popanda chilolezo cha Allah. Iye amaachitira ukali amene alibe nzeru (amene sagwiritsa ntchito nzeru zawo).
அரபு விரிவுரைகள்:
قُلِ ٱنظُرُواْ مَاذَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَمَا تُغۡنِي ٱلۡأٓيَٰتُ وَٱلنُّذُرُ عَن قَوۡمٖ لَّا يُؤۡمِنُونَ
Nena: “Yang’anani nchiyani chikupezeka kumwamba ndi pansi!” Ndipo zisonyezo zonsezi ndi machenjezo onsewa sangawakwanire (ndi kuwapindulira kanthu) anthu osakhulupirira.
அரபு விரிவுரைகள்:
فَهَلۡ يَنتَظِرُونَ إِلَّا مِثۡلَ أَيَّامِ ٱلَّذِينَ خَلَوۡاْ مِن قَبۡلِهِمۡۚ قُلۡ فَٱنتَظِرُوٓاْ إِنِّي مَعَكُم مِّنَ ٱلۡمُنتَظِرِينَ
Kodi chiliponso chimene akudikira posakhala (kuwadzera) monga masiku (azilango zomwe zidawapeza) amene adapita kale (iwo asadafike)? Nena: “Dikirani nanenso ndili pamodzi nanu mwa odikira.”
அரபு விரிவுரைகள்:
ثُمَّ نُنَجِّي رُسُلَنَا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْۚ كَذَٰلِكَ حَقًّا عَلَيۡنَا نُنجِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Kenako tidzawapulumutsa atumiki Athu ndi amene adakhulupirira. Chotere nkoyenera kwa Ife kuwapulumutsa okhulupirira.
அரபு விரிவுரைகள்:
قُلۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِن كُنتُمۡ فِي شَكّٖ مِّن دِينِي فَلَآ أَعۡبُدُ ٱلَّذِينَ تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلَٰكِنۡ أَعۡبُدُ ٱللَّهَ ٱلَّذِي يَتَوَفَّىٰكُمۡۖ وَأُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Nena: “E inu anthu! Ngati inu muli ndi chipeneko pa chipembedzo changa, (dziwani kuti) sindingapembedze zimene mukuzipembedza kusiya Allah; koma ine ndipembedza Allah (Mmodzi yekha) Yemwe amakupatsani imfa (ndi moyo). Ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi wa okhulupirira.”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَأَنۡ أَقِمۡ وَجۡهَكَ لِلدِّينِ حَنِيفٗا وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ
“Ndiponso (ndauzidwa kuti): ‘Lungamitsa nkhope yako kuchipembedzo momuyeretsera Allah mapemphero Ake, ndipo usakhale mmodzi mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).’
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَا تَدۡعُ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَنفَعُكَ وَلَا يَضُرُّكَۖ فَإِن فَعَلۡتَ فَإِنَّكَ إِذٗا مِّنَ ٱلظَّٰلِمِينَ
‘Ndipo (kuti), usapembedze chimene sichingakupindulitsire zabwino, kapena kukubweretsera masautso, kusiya Allah. Ngati utero ndiye kuti iwe ndi mmodzi wa oipa.”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِن يَمۡسَسۡكَ ٱللَّهُ بِضُرّٖ فَلَا كَاشِفَ لَهُۥٓ إِلَّا هُوَۖ وَإِن يُرِدۡكَ بِخَيۡرٖ فَلَا رَآدَّ لِفَضۡلِهِۦۚ يُصِيبُ بِهِۦ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦۚ وَهُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ
Ndipo ngati Allah atakukhudza ndi masautso, palibe aliyense owachotsa kupatula Iye. Ngatinso atakufunira zabwino, palibe amene angaubweze ubwino Wake. (Iye) amadza ndi ubwinowo kwa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo Iye Ngokhululuka Ngwachisoni zedi.
அரபு விரிவுரைகள்:
قُلۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ قَدۡ جَآءَكُمُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكُمۡۖ فَمَنِ ٱهۡتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهۡتَدِي لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيۡهَاۖ وَمَآ أَنَا۠ عَلَيۡكُم بِوَكِيلٖ
Nena: “E inu anthu! Choonadi chakudzerani kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho amene waongoka, (zabwino zake) zili pa iye mwini. Ndipo amene wasokera, ndithu zotsatira za kusokera zili pa iye mwini. Ndipo ine sindili muyang’aniri pa inu, (udindo wanga ndi kuchenjeza basi).”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَٱتَّبِعۡ مَا يُوحَىٰٓ إِلَيۡكَ وَٱصۡبِرۡ حَتَّىٰ يَحۡكُمَ ٱللَّهُۚ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلۡحَٰكِمِينَ
Ndipo (andiuza kuti): “Tsatira zimene zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndipo pirira kufikira Allah adzaweruze. Iye Ngoweruza bwino kuposa aweruzi onse.”
அரபு விரிவுரைகள்:
 
மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: ஸூரா யூனுஸ்
அத்தியாயங்களின் அட்டவணை பக்க எண்
 
அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை

புனித அல் குர்ஆனுக்கான ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு- காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா மூலம் மொழிபெயர்க்கப்பட்டது.

மூடுக