قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - الترجمة الشيشيوا * - تەرجىمىلەر مۇندەرىجىسى


مەنالار تەرجىمىسى سۈرە: سۈرە پۇسسىلەت   ئايەت:

سۈرە پۇسسىلەت

حمٓ
Hâ-Mîm:
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
تَنزِيلٞ مِّنَ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
(Qur’an iyi) ndichivumbulutso chochokera kwa (Allah) Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
كِتَٰبٞ فُصِّلَتۡ ءَايَٰتُهُۥ قُرۡءَانًا عَرَبِيّٗا لِّقَوۡمٖ يَعۡلَمُونَ
(Ili) ndi buku lomwe ma Ayah ake afotokozedwa (bwino pokhudza malamulo a zamdziko ndi tsiku lachimaliziro); chowerengedwa (chimene chavumbulutsidwa) m’chiyankhulo cha Chiarabu kwa anthu ozindikira (tsatanetsatane wa malamulo ake).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
بَشِيرٗا وَنَذِيرٗا فَأَعۡرَضَ أَكۡثَرُهُمۡ فَهُمۡ لَا يَسۡمَعُونَ
Likunena nkhani yabwino (kwa ochita zabwino) ndi kuchenjeza (anthu ochita zoipa); koma ambiri a iwo (Aquraish) ainyoza kotero kuti sakumva; (kumva kothandizidwa nalo ndi kulilingalira).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَقَالُواْ قُلُوبُنَا فِيٓ أَكِنَّةٖ مِّمَّا تَدۡعُونَآ إِلَيۡهِ وَفِيٓ ءَاذَانِنَا وَقۡرٞ وَمِنۢ بَيۡنِنَا وَبَيۡنِكَ حِجَابٞ فَٱعۡمَلۡ إِنَّنَا عَٰمِلُونَ
Ndipo akunena (kuti): “Mitima yathu (yaphimbidwa) m’zivindikiro, ku zomwe ukutiitanirazo, ndipo m’makutu mwathu muli kulemera kwa ugonthi; choncho pakati pathu ndi pakati pa iwe pali chotsekereza (chotchinga); tero chita (zakozo); nafe tichita (zathu; aliyense wa ife asalowelere za mnzake).”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
قُلۡ إِنَّمَآ أَنَا۠ بَشَرٞ مِّثۡلُكُمۡ يُوحَىٰٓ إِلَيَّ أَنَّمَآ إِلَٰهُكُمۡ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞ فَٱسۡتَقِيمُوٓاْ إِلَيۡهِ وَٱسۡتَغۡفِرُوهُۗ وَوَيۡلٞ لِّلۡمُشۡرِكِينَ
Nena: “Ndithu, ine ndi munthu monga inu; kukuvumbulutsidwa kwa ine (kuchokera kwa Allah) kuti ndithu Mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi; choncho lungamani kwa Iye ndipo mpempheni chikhululuko (pa zimene mwakhala mukumchimwira)” Ndipo kuonongeka kwakukulu kuli pa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ كَٰفِرُونَ
Amene sapereka chopereka (Zakaat), ndiomwe akukanira za tsiku lachimaliziro.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمۡ أَجۡرٌ غَيۡرُ مَمۡنُونٖ
Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, pa iwo padzakhala malipiro osadukiza (osatha).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
۞ قُلۡ أَئِنَّكُمۡ لَتَكۡفُرُونَ بِٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡأَرۡضَ فِي يَوۡمَيۡنِ وَتَجۡعَلُونَ لَهُۥٓ أَندَادٗاۚ ذَٰلِكَ رَبُّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Nena: “Kodi inu mukumkanira yemwe adalenga nthaka mmasiku awiri (okha)? Ndipo mukumpangira milungu (ina)? Iyeyo ndiye Mbuye wa zolengedwa zonse.”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَجَعَلَ فِيهَا رَوَٰسِيَ مِن فَوۡقِهَا وَبَٰرَكَ فِيهَا وَقَدَّرَ فِيهَآ أَقۡوَٰتَهَا فِيٓ أَرۡبَعَةِ أَيَّامٖ سَوَآءٗ لِّلسَّآئِلِينَ
Ndipo adaika pamenepo mapiri ataliatali pamwamba pake, ndi kudalitsapo (ndi madzi, mmera, ndi ziweto), ndipo adayesa mmenemo zakudya zake (za okhala pa nthakapo; zimenezi adadzichita) mmasiku anayi; (izi) nzokwanira kwa ofunsa (zakalengedwe ka nthaka ndi zamkati mwake).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰٓ إِلَى ٱلسَّمَآءِ وَهِيَ دُخَانٞ فَقَالَ لَهَا وَلِلۡأَرۡضِ ٱئۡتِيَا طَوۡعًا أَوۡ كَرۡهٗا قَالَتَآ أَتَيۡنَا طَآئِعِينَ
Kenako adalunjika ku thambo (malunjikidwe ogwirizana ndimomwe Iye alili mosafanana ndi zolengedwa zake), pomwe ilo (thambolo) lidali utsi. Ndipo adati kwa ilo ndi nthaka: “Idzani, mofuna kapena mokakamizidwa (tsatirani lamulo Langa).” Izo zidayankha kuti: “Tadza mofuna.”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
فَقَضَىٰهُنَّ سَبۡعَ سَمَٰوَاتٖ فِي يَوۡمَيۡنِ وَأَوۡحَىٰ فِي كُلِّ سَمَآءٍ أَمۡرَهَاۚ وَزَيَّنَّا ٱلسَّمَآءَ ٱلدُّنۡيَا بِمَصَٰبِيحَ وَحِفۡظٗاۚ ذَٰلِكَ تَقۡدِيرُ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡعَلِيمِ
Choncho adakwaniritsa kulenga thambo zisanu ndi ziwiri mmasiku awiri, ndipo thambo lililonse adalidziwitsa ntchito yake (polilamula zochita zake). Ndipo tidakongoletsa thambo lapafupi (ndi inu) ndi nyenyezi (zounikira dziko lapansi), ndiponso kuti zizilondera kumwamha (kuti ziwanda zisamapite kukamvera za kumwamba). Uwu ndi muyeso wa Mwini mphamvu, Wodziwa kwambiri.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
فَإِنۡ أَعۡرَضُواْ فَقُلۡ أَنذَرۡتُكُمۡ صَٰعِقَةٗ مِّثۡلَ صَٰعِقَةِ عَادٖ وَثَمُودَ
Koma ngati anyozera (kukhulupirira), nena: “Ndikukuchenjezani za chilango monga chilango cha Âdi ndi Samud.”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
إِذۡ جَآءَتۡهُمُ ٱلرُّسُلُ مِنۢ بَيۡنِ أَيۡدِيهِمۡ وَمِنۡ خَلۡفِهِمۡ أَلَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّا ٱللَّهَۖ قَالُواْ لَوۡ شَآءَ رَبُّنَا لَأَنزَلَ مَلَٰٓئِكَةٗ فَإِنَّا بِمَآ أُرۡسِلۡتُم بِهِۦ كَٰفِرُونَ
Pamene aneneri adawadzera patsogolo pawo ndi pambuyo pawo (ndikuwauza): “Musapembedze (milungu ina), koma Allah,” adati: “Mbuye wathu akadafuna, akadatsitsa angelo (kudzatilalikira, osati anthu monga inu). Choncho ndithu ife tikuzikana zimene mwatumidwa nazozo.”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
فَأَمَّا عَادٞ فَٱسۡتَكۡبَرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّ وَقَالُواْ مَنۡ أَشَدُّ مِنَّا قُوَّةًۖ أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّ ٱللَّهَ ٱلَّذِي خَلَقَهُمۡ هُوَ أَشَدُّ مِنۡهُمۡ قُوَّةٗۖ وَكَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يَجۡحَدُونَ
Tsono Âdi adadzikweza pa dziko mosayenera, ndipo adati: “Ndani wamphamvu kuposa ife?” Kodi saona kuti Allah Yemwe adawalenga ndi Mwini mphamvu zambiri kuposa iwo? Koma adapitiriza kukanira zozizwitsa Zathu.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
فَأَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ رِيحٗا صَرۡصَرٗا فِيٓ أَيَّامٖ نَّحِسَاتٖ لِّنُذِيقَهُمۡ عَذَابَ ٱلۡخِزۡيِ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَخۡزَىٰۖ وَهُمۡ لَا يُنصَرُونَ
Choncho tidawatumizira mphepo ya mkuntho yozizira kwabasi mmasiku amatsoka, kuti tiwalawitse chilango chowasambula pamoyo wa pa dziko lapansi; ndipo chilango cha tsiku lachimaliziro ndi choyalutsa kwambiri; ndipo iwo sadzapulumutsidwa.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَأَمَّا ثَمُودُ فَهَدَيۡنَٰهُمۡ فَٱسۡتَحَبُّواْ ٱلۡعَمَىٰ عَلَى ٱلۡهُدَىٰ فَأَخَذَتۡهُمۡ صَٰعِقَةُ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡهُونِ بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Naonso Asamudu tidawasonyeza (njira yabwino ndi njira yoipa), ndipo adakonda ndi kusankha kusokera kusiya chiongoko; ndipo udawapeza nkuwe wa chilango choyalutsa chifukwa cha machimo amene adali kuchita.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَنَجَّيۡنَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَكَانُواْ يَتَّقُونَ
Koma tidawapulumutsa (ku chilango chimenechi) amene adakhulupirira ndipo anali kumuopa (Allah).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَيَوۡمَ يُحۡشَرُ أَعۡدَآءُ ٱللَّهِ إِلَى ٱلنَّارِ فَهُمۡ يُوزَعُونَ
Ndipo (akumbutse, iwe Mtumiki), tsiku lomwe adani a Allah adzasonkhanitsidwa kunka nawo ku Moto, uku akukusidwa (onse, oyamba ndi omalizira),
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
حَتَّىٰٓ إِذَا مَا جَآءُوهَا شَهِدَ عَلَيۡهِمۡ سَمۡعُهُمۡ وَأَبۡصَٰرُهُمۡ وَجُلُودُهُم بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Kufikira pomwe adzaufikira (Moto); makutu awo ndi maso awo ndi khungu lawo zidzawachitira umboni pa zomwe adali kuchita (pa dziko lapansi).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَقَالُواْ لِجُلُودِهِمۡ لِمَ شَهِدتُّمۡ عَلَيۡنَاۖ قَالُوٓاْ أَنطَقَنَا ٱللَّهُ ٱلَّذِيٓ أَنطَقَ كُلَّ شَيۡءٖۚ وَهُوَ خَلَقَكُمۡ أَوَّلَ مَرَّةٖ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Ndipo adzanena (adani a Allah) ku makungu awo: “Bwanji mukutiperekera umboni woipa?” Zidzati: “Allah watiyankhulitsa, Amene amayankhulitsa chilichonse; ndipo Iye ndi Amene adakulengani (mkulenga) koyamba (pomwe simudali kanthu), ndiponso kwa Iye Yekha ndiko mudzabwezedwa.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَمَا كُنتُمۡ تَسۡتَتِرُونَ أَن يَشۡهَدَ عَلَيۡكُمۡ سَمۡعُكُمۡ وَلَآ أَبۡصَٰرُكُمۡ وَلَا جُلُودُكُمۡ وَلَٰكِن ظَنَنتُمۡ أَنَّ ٱللَّهَ لَا يَعۡلَمُ كَثِيرٗا مِّمَّا تَعۡمَلُونَ
Simudathe kubisa (ntchito zanu zoipa ku ziwalo zanu) poopera kuti kumva kwanu ndi kuyang’ana kwanu ndi makungu anu zingakuperekereni umboni woipa! Koma mudali kuganiza kuti Allah sadziwa zambiri zomwe mukuchita (mobisa).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَذَٰلِكُمۡ ظَنُّكُمُ ٱلَّذِي ظَنَنتُم بِرَبِّكُمۡ أَرۡدَىٰكُمۡ فَأَصۡبَحۡتُم مِّنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ
Ndipo amenewo ndi maganizo anu omwe mudali kumganizira (nawo) Mbuye wanu adakuonongani, ndipo (lero tsiku la Qiyâma) muli m’gulu la otaika.”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
فَإِن يَصۡبِرُواْ فَٱلنَّارُ مَثۡوٗى لَّهُمۡۖ وَإِن يَسۡتَعۡتِبُواْ فَمَا هُم مِّنَ ٱلۡمُعۡتَبِينَ
Choncho ngakhalc atapirira (ku zopweteka zawo), moto ndiwo mabwelero awo ndi kokhazikika kwawo kwa muyaya. Ngati atapempha chiyanjo cha Allah pa iwo, iwo sadzakhala m’gulu la oyanjidwa.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
۞ وَقَيَّضۡنَا لَهُمۡ قُرَنَآءَ فَزَيَّنُواْ لَهُم مَّا بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَمَا خَلۡفَهُمۡ وَحَقَّ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقَوۡلُ فِيٓ أُمَمٖ قَدۡ خَلَتۡ مِن قَبۡلِهِم مِّنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِۖ إِنَّهُمۡ كَانُواْ خَٰسِرِينَ
Ndipo tidawakonzera iwo abwenzi oipa (padziko lapansi), choncho adawakometsera zamtsogolo mwawo ndi za pambuyo pawo ndipo liwu la chilango lidatsimikizika pa iwo pamodzi ndi mibadwo yomwe idapita kale ya ziwanda ndi anthu, ndithu iwo adali otaika.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَا تَسۡمَعُواْ لِهَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ وَٱلۡغَوۡاْ فِيهِ لَعَلَّكُمۡ تَغۡلِبُونَ
Akunena okanira (kuuzana okhaokha): “Musamvetsere Qur’an iyi, koma sokoserani pomwe ikuwerengedwa (kuti asaimvere aliyense) kuti mwina mupambane.”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
فَلَنُذِيقَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ عَذَابٗا شَدِيدٗا وَلَنَجۡزِيَنَّهُمۡ أَسۡوَأَ ٱلَّذِي كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Ndithu tiwalawitsa amene akanira chilango choopsa (pa zochita zawo zoipa, makamaka pakuithira Qur’an nkhondo), ndipo ndithu tiwalipira malipiro oipitsitsa chifukwa cha zoipa zomwe adali kuchita.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
ذَٰلِكَ جَزَآءُ أَعۡدَآءِ ٱللَّهِ ٱلنَّارُۖ لَهُمۡ فِيهَا دَارُ ٱلۡخُلۡدِ جَزَآءَۢ بِمَا كَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يَجۡحَدُونَ
Imeneyo ndi mphoto yoyenera ya adani a Allah, yomwe ndi Moto. Mmenemo adzakhala muyaya. Imeneyi ndi mphoto ya zimene adali kuzikanira m’zisonyezo Zathu.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ رَبَّنَآ أَرِنَا ٱلَّذَيۡنِ أَضَلَّانَا مِنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِ نَجۡعَلۡهُمَا تَحۡتَ أَقۡدَامِنَا لِيَكُونَا مِنَ ٱلۡأَسۡفَلِينَ
Ndipo okanira adzanena (ali mkati mwa Moto): “E Mbuye wathu! Tisonyezeni (magulu awiri) amene adatisokeretsa ochokera m’ziwanda ndi anthu kuti tiwaike pansi pa mapazi athu, kuti akhale mwa apansi (mu ulemelero ndi malo).”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
إِنَّ ٱلَّذِينَ قَالُواْ رَبُّنَا ٱللَّهُ ثُمَّ ٱسۡتَقَٰمُواْ تَتَنَزَّلُ عَلَيۡهِمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ أَلَّا تَخَافُواْ وَلَا تَحۡزَنُواْ وَأَبۡشِرُواْ بِٱلۡجَنَّةِ ٱلَّتِي كُنتُمۡ تُوعَدُونَ
Ndithu amene anena (kuti): “Mbuye wathu ndi Allah,” (povomereza umodzi Wake), kenako nkupitiriza kulungama pa malamulo Ake, angelo amawatsikira iwo nthawi yakufa (uku akuti): “Musaope (pa zomwe mukumane nazo). Ndipo musadandaule (pazomwe mwazisiya). Ndipo sangalalani ndi Munda wamtendere umene mudalonjezedwa (kupyolera mmalirime a aneneri).”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
نَحۡنُ أَوۡلِيَآؤُكُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَفِي ٱلۡأٓخِرَةِۖ وَلَكُمۡ فِيهَا مَا تَشۡتَهِيٓ أَنفُسُكُمۡ وَلَكُمۡ فِيهَا مَا تَدَّعُونَ
(Angelo amanena kwa iwo): “Ife ndi athangati anu pamoyo wa pa dziko lapansi (pokulimbikitsani panjira yolungama), ndi tsiku lachimaliziro (pokupempherani chipulumutso kwa Allah); inu mukapeza kumeneko chilichonse chomwe mitima yanu ikafune (zokoma ndi zabwino); ndipo, mukapeza mmenemo chilichonse chomwe mukachilakelake.”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
نُزُلٗا مِّنۡ غَفُورٖ رَّحِيمٖ
(“Limeneli ndi) phwando lochokera kwa (Mbuye) Wokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha.”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَمَنۡ أَحۡسَنُ قَوۡلٗا مِّمَّن دَعَآ إِلَى ٱللَّهِ وَعَمِلَ صَٰلِحٗا وَقَالَ إِنَّنِي مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ
Kodi ndani yemwe ali ndi zonena zabwino kuposa yemwe akuitanira kwa Allah (ndi kumumvera), ndikuchita, (pamodzi ndi zimenezo), zabwino uku akunena: “Ine ndi mmodzi mwa ogonjera (malamulo a Allah).”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَلَا تَسۡتَوِي ٱلۡحَسَنَةُ وَلَا ٱلسَّيِّئَةُۚ ٱدۡفَعۡ بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ فَإِذَا ٱلَّذِي بَيۡنَكَ وَبَيۡنَهُۥ عَدَٰوَةٞ كَأَنَّهُۥ وَلِيٌّ حَمِيمٞ
Ndipo chabwino sichingafanane ndi choipa. Chotsa (choipa) ndi chomwe chili chabwino; mapeto ake akhala kuti yemwe padali chidani pakati pako ndi pakati pake (akhala) ngati mthandizi wodalirika.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَمَا يُلَقَّىٰهَآ إِلَّا ٱلَّذِينَ صَبَرُواْ وَمَا يُلَقَّىٰهَآ إِلَّا ذُو حَظٍّ عَظِيمٖ
Ndipo palibe angapatsidwe zimenezi (zochotsa choipa pochita chabwino) kupatula amene apirira. Ndiponso sangapatsidwe zimenezi kupatula mwini gawo la ubwino waukulu.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَإِمَّا يَنزَغَنَّكَ مِنَ ٱلشَّيۡطَٰنِ نَزۡغٞ فَٱسۡتَعِذۡ بِٱللَّهِۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
Ndipo ngati satana atakusokoneza kuti akuchotse ku zomwe walamulidwa, pempha chitetezo kwa Allah. Ndithu Iye Ngwakumva zonse, Ngodziwa zonse; (adzakuteteza kwa iye).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِ ٱلَّيۡلُ وَٱلنَّهَارُ وَٱلشَّمۡسُ وَٱلۡقَمَرُۚ لَا تَسۡجُدُواْ لِلشَّمۡسِ وَلَا لِلۡقَمَرِ وَٱسۡجُدُواْۤ لِلَّهِۤ ٱلَّذِي خَلَقَهُنَّ إِن كُنتُمۡ إِيَّاهُ تَعۡبُدُونَ
Ndipo zina mwa zisonyezo Zake, ndi usiku, usana, dzuwa ndi mwezi. Musalambire dzuwa ngakhale mwezi, koma lambirani Allah, Amene adazilenga ngati inu mukumpembedza mwachoonadi.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
فَإِنِ ٱسۡتَكۡبَرُواْ فَٱلَّذِينَ عِندَ رَبِّكَ يُسَبِّحُونَ لَهُۥ بِٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ وَهُمۡ لَا يَسۡـَٔمُونَ۩
Koma ngati adzikweza (opembedza mafano ndi kusiya kutsatira lamulo lako, usade nkhawa). Ndipo, amene ali kwa Mbuye wako; (angelo), akulemekeza Iye usiku ndi usana, ndipo iwo satopa (ndi kutamanda Allah).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦٓ أَنَّكَ تَرَى ٱلۡأَرۡضَ خَٰشِعَةٗ فَإِذَآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡهَا ٱلۡمَآءَ ٱهۡتَزَّتۡ وَرَبَتۡۚ إِنَّ ٱلَّذِيٓ أَحۡيَاهَا لَمُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰٓۚ إِنَّهُۥ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٌ
Ndipo zina mwa zisonyezo Zake (zoposa), ndithu iwe umaona nthaka ili youma; koma tikatsitsa madzi pa iyo imagwedezeka ndi kufufuma; ndithu Amene waiukitsa nthaka itauma, Ngoukitsa akufa. Iye Ngwamphamvu zoposa pa chilichonse.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
إِنَّ ٱلَّذِينَ يُلۡحِدُونَ فِيٓ ءَايَٰتِنَا لَا يَخۡفَوۡنَ عَلَيۡنَآۗ أَفَمَن يُلۡقَىٰ فِي ٱلنَّارِ خَيۡرٌ أَم مَّن يَأۡتِيٓ ءَامِنٗا يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ ٱعۡمَلُواْ مَا شِئۡتُمۡ إِنَّهُۥ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٌ
Ndithu amene akupotoza choonadi mzisonyezo Zathu sangabisike kwa Ife. (Ndipo tidzawalipira zimene akuyenerana nazo). Kodi wabwino ndi uti, yemwe adzaponyedwa ku Moto, kapena yemwe adzadza pa tsiku la chiweruziro uku ali wokhazikika mtima? Chitani zimene mukufuna; ndithu Iye Ngopenya chilichonse chimene mukuchita. (Aliyense adzamulipira pa zochita zake).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِٱلذِّكۡرِ لَمَّا جَآءَهُمۡۖ وَإِنَّهُۥ لَكِتَٰبٌ عَزِيزٞ
Ndithu amene atsutsa Qur’an yolemekezeka ikawadzera (popanda kulingalira, kwa iwo kudzakhala chilango chosasimbika). Ndipo ndithu limeneli ndi buku lopambana (chilichonse cholipinga).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
لَّا يَأۡتِيهِ ٱلۡبَٰطِلُ مِنۢ بَيۡنِ يَدَيۡهِ وَلَا مِنۡ خَلۡفِهِۦۖ تَنزِيلٞ مِّنۡ حَكِيمٍ حَمِيدٖ
Silifikidwa ndi chonama patsogolo pake ngakhale pambuyo pake. Ndi lovumbulutsidwa kuchokera kwa Wanzeru zakuya, Woyamikidwa kwambiri (mzochita Zake).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
مَّا يُقَالُ لَكَ إِلَّا مَا قَدۡ قِيلَ لِلرُّسُلِ مِن قَبۡلِكَۚ إِنَّ رَبَّكَ لَذُو مَغۡفِرَةٖ وَذُو عِقَابٍ أَلِيمٖ
Palibe chimene chinenedwa kwa iwe (Mtumiki {s.a.w) kuchokera kwa adani ako) koma chomwe chidanenedwa kwa aneneri akale (kuchokera kwa adani awo). Ndipo Mbuye wako ndi Mwini chikhululuko chambiri (kwa amene walapa kwa Iye), ndiponso Mwini chilango chowawa (kwa yemwe wapitiriza kunyozera).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَلَوۡ جَعَلۡنَٰهُ قُرۡءَانًا أَعۡجَمِيّٗا لَّقَالُواْ لَوۡلَا فُصِّلَتۡ ءَايَٰتُهُۥٓۖ ءَا۬عۡجَمِيّٞ وَعَرَبِيّٞۗ قُلۡ هُوَ لِلَّذِينَ ءَامَنُواْ هُدٗى وَشِفَآءٞۚ وَٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ فِيٓ ءَاذَانِهِمۡ وَقۡرٞ وَهُوَ عَلَيۡهِمۡ عَمًىۚ أُوْلَٰٓئِكَ يُنَادَوۡنَ مِن مَّكَانِۭ بَعِيدٖ
Ndipo tikadaichita Qur’an iyi kukhala mchiyankhulo chachilendo osati Chiarabu, akadanena: “Nchifukwa ninji ma Ayah ake sadafotokozedwe bwino; buku la chilankhulo chachilendo olalikidwa nkukhala mwarabu?” Nena (iwe Mtumiki): “Limeneli ndi chiongoko ndi chochiritsa kwa okhulupirira. Koma kwa amene salikhulupirira, (zili ngati kuti) mmakutu mwawo muli ugonthi (chifukwa cholinyoza) umene ukuwachititsa khungu (chifukwa choti saona chilichonse mmenemo chowapindulira), iwo (okanirawo ali ngati) akuitanidwa (ndi woitana) kuchokera pamtunda wapatali (kuti amkhulupirire).”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ فَٱخۡتُلِفَ فِيهِۚ وَلَوۡلَا كَلِمَةٞ سَبَقَتۡ مِن رَّبِّكَ لَقُضِيَ بَيۡنَهُمۡۚ وَإِنَّهُمۡ لَفِي شَكّٖ مِّنۡهُ مُرِيبٖ
Ndipo ndithu tidampatsa Mûsa buku ((la Tarat)) ndipo (anthu ake) adatsutsana za ilo. Kukadapanda kutsogola liwu lochokera kwa Mbuye wako (loti adzachedwetsa chilango kwa okutsutsa) kukadaweruzidwa pakati pawo (powaononga). Ndithu iwo ali m’chikaiko choikaikira iyo (Qur’an).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
مَّنۡ عَمِلَ صَٰلِحٗا فَلِنَفۡسِهِۦۖ وَمَنۡ أَسَآءَ فَعَلَيۡهَاۗ وَمَا رَبُّكَ بِظَلَّٰمٖ لِّلۡعَبِيدِ
Amene achite chabwino, akudzichitira yekha; ndipo amene akuipitsa (m’zochita zake), machimo ake ali pa iye yekha. Mbuye wako sali wopondereza akapolo (Ake polanga wina ndi tchimo la wina).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
۞ إِلَيۡهِ يُرَدُّ عِلۡمُ ٱلسَّاعَةِۚ وَمَا تَخۡرُجُ مِن ثَمَرَٰتٖ مِّنۡ أَكۡمَامِهَا وَمَا تَحۡمِلُ مِنۡ أُنثَىٰ وَلَا تَضَعُ إِلَّا بِعِلۡمِهِۦۚ وَيَوۡمَ يُنَادِيهِمۡ أَيۡنَ شُرَكَآءِي قَالُوٓاْ ءَاذَنَّٰكَ مَا مِنَّا مِن شَهِيدٖ
۞ Kudziwa kwa tsiku la Qiyâma kukubwezedwa kwa Iye (Allah;) zipatso sizituluka m’mikoko yake ndipo mkazi satenga pakati ndi kubereka popanda Allah kudziwa. (Koma amadziwa zonsezo bwinobwino). Ndipo (kumbukira) tsiku limene Allah adzawaitane (ndi kuwafunsa kuti): “Ali kuti aphatikizi Anga aja (amene mudali kuwapembedza kusiya Ine)?” Adzanena (modandaula): “Tikukudziwitsani, (E Inu Allah)! Palibe aliyense mwa ife angaikire umboni (kuti Inu muli ndi mnzanu).”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَضَلَّ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَدۡعُونَ مِن قَبۡلُۖ وَظَنُّواْ مَا لَهُم مِّن مَّحِيصٖ
Ndipo zomwe adali kuzipembedza kale zidzawasowa. Ndipo adzatsimikiza kuti alibe pothawira.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
لَّا يَسۡـَٔمُ ٱلۡإِنسَٰنُ مِن دُعَآءِ ٱلۡخَيۡرِ وَإِن مَّسَّهُ ٱلشَّرُّ فَيَـُٔوسٞ قَنُوطٞ
Munthu satopa kupempha zabwino (za m’dziko lapansi kwa Mbuye wake). Koma choipa chikamkhudza iye amakhala wotaya mtima kwambiri.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَلَئِنۡ أَذَقۡنَٰهُ رَحۡمَةٗ مِّنَّا مِنۢ بَعۡدِ ضَرَّآءَ مَسَّتۡهُ لَيَقُولَنَّ هَٰذَا لِي وَمَآ أَظُنُّ ٱلسَّاعَةَ قَآئِمَةٗ وَلَئِن رُّجِعۡتُ إِلَىٰ رَبِّيٓ إِنَّ لِي عِندَهُۥ لَلۡحُسۡنَىٰۚ فَلَنُنَبِّئَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِمَا عَمِلُواْ وَلَنُذِيقَنَّهُم مِّنۡ عَذَابٍ غَلِيظٖ
Ndipo ndithu tikamulawitsa chisomo chochokera kwa Ife atapeza mavuto kwambiri amene adamkhudza, ndithu amanena, (monyada): “Izi nzangazanga. (Ndazipeza chifukwa cha khama langa ndi nzeru zanga). Ndipo za tsiku lachimaliziro sindikhulupirira kuti lilipo. Ndipo ngati nditabwezedwa kwa Mbuye wanga, ndiye kuti ine ndidzakhala nazo zabwino kwa Iye.” Choncho tidzawauza omwe adakanira zimene adachita, ndipo tidzawalawitsa chilango chokhwima (chosanjikana china pamwamba pa chinzake).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَإِذَآ أَنۡعَمۡنَا عَلَى ٱلۡإِنسَٰنِ أَعۡرَضَ وَنَـَٔا بِجَانِبِهِۦ وَإِذَا مَسَّهُ ٱلشَّرُّ فَذُو دُعَآءٍ عَرِيضٖ
Ndipo munthu tikam’dalitsa (ndi chisomo Chathu), amanyoza ndi kudziika kutali (ndi chipembedzo Chathu). Koma vuto likam’khudza umuona uyo akuchulukitsa maduwa (mapemphero).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ إِن كَانَ مِنۡ عِندِ ٱللَّهِ ثُمَّ كَفَرۡتُم بِهِۦ مَنۡ أَضَلُّ مِمَّنۡ هُوَ فِي شِقَاقِۭ بَعِيدٖ
Nena (kwa iwo, iwe Mtumiki): “Tandiuzani ngati (Qur’aniyi) ilidi yochokera kwa Allah, kenako inu nkuikanira; (nanga zingakhale bwanji?) Kodi ndiyani wosokera kwambiri kuposa uyo amene ali mu mtsutso wakutali (ndi choona)?”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
سَنُرِيهِمۡ ءَايَٰتِنَا فِي ٱلۡأٓفَاقِ وَفِيٓ أَنفُسِهِمۡ حَتَّىٰ يَتَبَيَّنَ لَهُمۡ أَنَّهُ ٱلۡحَقُّۗ أَوَلَمۡ يَكۡفِ بِرَبِّكَ أَنَّهُۥ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ شَهِيدٌ
Posachedwa tiwaonetsa (awa okanira), zisonyezo Zathu (zosonyeza kuona kwa Qur’an ndi iwe) kumbali zonse, ndi mwa iwo eni kufikira zionekere kwa iwo kuti chimene wadza nachochi nchoona. Kodi Mbuye wako siwokwanira kuti Iye akuona chilichonse?
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
أَلَآ إِنَّهُمۡ فِي مِرۡيَةٖ مِّن لِّقَآءِ رَبِّهِمۡۗ أَلَآ إِنَّهُۥ بِكُلِّ شَيۡءٖ مُّحِيطُۢ
Chenjerani! Ndithu awa ali m’chikaiko za kukumana ndi Mbuye wawo. Ndithu Iye (Mbuye wawo) wachizungulira chinthu chilichonse mkudziwa Kwake.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
 
مەنالار تەرجىمىسى سۈرە: سۈرە پۇسسىلەت
سۈرە مۇندەرىجىسى بەت نومۇرى
 
قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - الترجمة الشيشيوا - تەرجىمىلەر مۇندەرىجىسى

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

تاقاش