Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - Dịch thuật tiếng Chichio * - Mục lục các bản dịch


Ý nghĩa nội dung Chương: Chương Al-Furqan   Câu:

Chương Al-Furqan

تَبَارَكَ ٱلَّذِي نَزَّلَ ٱلۡفُرۡقَانَ عَلَىٰ عَبۡدِهِۦ لِيَكُونَ لِلۡعَٰلَمِينَ نَذِيرًا
Watukuka Mwini kupereka madalitso, Yemwe wavumbulutsa Qur’an kwa kapolo Wake kuti ikhale mchenjezi kwa zolengedwa zonse.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
ٱلَّذِي لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلَمۡ يَتَّخِذۡ وَلَدٗا وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ شَرِيكٞ فِي ٱلۡمُلۡكِ وَخَلَقَ كُلَّ شَيۡءٖ فَقَدَّرَهُۥ تَقۡدِيرٗا
(Allah) Yemwe Ngwake ufumu wa kumwamba ndi wa pansi. Ndipo sadabale mwana ndipo alibenso wothandizana naye pa ufumu (Wake). Adalenga chinthu chilichonse ndikuchilinga mlingo wake.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةٗ لَّا يَخۡلُقُونَ شَيۡـٔٗا وَهُمۡ يُخۡلَقُونَ وَلَا يَمۡلِكُونَ لِأَنفُسِهِمۡ ضَرّٗا وَلَا نَفۡعٗا وَلَا يَمۡلِكُونَ مَوۡتٗا وَلَا حَيَوٰةٗ وَلَا نُشُورٗا
Ndipo m’malo mwa Iye (Mulungu weniweni, osakhulupirira) adzipangira milungu yomwe siilenga chilichonse koma iyo ndiyomwe idalengedwa; ndiponso ilibe mphamvu yodzichotsera masautso ngakhale kudzidzetsera zothandiza. Ndiponso ilibe mphamvu zoperekera irnfa ndi moyo, ngakhale kuukitsa akufa.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّآ إِفۡكٌ ٱفۡتَرَىٰهُ وَأَعَانَهُۥ عَلَيۡهِ قَوۡمٌ ءَاخَرُونَۖ فَقَدۡ جَآءُو ظُلۡمٗا وَزُورٗا
Ndipo osakhulupirira akunena: “Ichi sikanthu (Qur’an imene Muhammad {s.a.w} wadza nayo) koma ndi chonama chimene wachipeka, ndipo pachimenechi amthandiza anthu ena (eni mabuku).” Kunena zoona, iwo (osakhulupirira) adza ndi chinyengo ndi bodza (pazonena zawozi). [292]
[292] Osakhulupilira amumzinda wa Makka adali kuinyoza Qur’an namati ndi buku labodza limene walipeka yekhayekha Muhammad (s.a.w) ndikumamnamizira Allah kuti ndiye walivumbulutsa. Amatinso anthu a mabuku ndiwo adamthandiza kulipeka. Zonena zawozi nzabodza zokhazokha chifukwa Qur’an yomwe Muhammad (s.a.w) akuiwerengayo ili m’Charabu osati m’Chiyuda.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَقَالُوٓاْ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ ٱكۡتَتَبَهَا فَهِيَ تُمۡلَىٰ عَلَيۡهِ بُكۡرَةٗ وَأَصِيلٗا
Ndipo (osakhulupirira) akunena: “Iyi (Qur’an) ndi nthano za anthu akale zomwe (Muhammad {s.a.w}) adazilembetsa. Choncho zikulakatulidwa kwa iye m’mawa ndi madzulo (kuti aloweze).”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
قُلۡ أَنزَلَهُ ٱلَّذِي يَعۡلَمُ ٱلسِّرَّ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ إِنَّهُۥ كَانَ غَفُورٗا رَّحِيمٗا
Nena: “Adaivumbulutsa Yemwe akudziwa zobisika za m’thambo ndi m’nthaka. Ndithu Iye ali Wokhululuka; Wachisoni, (nchifukwa chake sakukulangani mwachangu pazimene mukunenazi).”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَقَالُواْ مَالِ هَٰذَا ٱلرَّسُولِ يَأۡكُلُ ٱلطَّعَامَ وَيَمۡشِي فِي ٱلۡأَسۡوَاقِ لَوۡلَآ أُنزِلَ إِلَيۡهِ مَلَكٞ فَيَكُونَ مَعَهُۥ نَذِيرًا
Ndipo akunena: “Ndi Mtumiki wanji uyu, womadya chakudya nkumayenda m’misika? Kodi bwanji sadatumizidwe mngelo kwa iye kuti azikhala naye limodzi uku akuchenjeza?”[293]
[293] Amamunenera zachipongwe Mtumiki Muhammad (s.a.w) kuti: “Nchiyani watiposa uyu pamene akudzitcha yekha kuti ndi Mtumiki? lye akudya chakudya monga momwe ife tidyera, ndipo akuyendayenda m’misika kunka nafunafuna zokhalira moyo monga anthu ena onse achitira. Akadakhaladi Mtumiki ndiye kuti Allah akadampatsa zosowa zake zonse. Ngati alidi Mtumiki bwanji Allah sadamtsitsire angelo kumwamba kuti azimthandiza? Zikadatero apo tikadamkhulupilira.’’
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
أَوۡ يُلۡقَىٰٓ إِلَيۡهِ كَنزٌ أَوۡ تَكُونُ لَهُۥ جَنَّةٞ يَأۡكُلُ مِنۡهَاۚ وَقَالَ ٱلظَّٰلِمُونَ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا رَجُلٗا مَّسۡحُورًا
“Kapena kuponyeredwa nkhokwe (za chuma), kapena kukhala ndi munda ndikumadya m’menemo?” Ndipo osalungama akuti: “Ndithudi, mukutsatira munthu wolodzedwa.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
ٱنظُرۡ كَيۡفَ ضَرَبُواْ لَكَ ٱلۡأَمۡثَٰلَ فَضَلُّواْ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ سَبِيلٗا
Ona momwe akukuponyera mafanizo (omwe sali oyenerana nawe, nthawi zina akuti ndiwe wolodzedwa wamisala, wabodza, wophunzitsidwa ndi anthu ena) choncho asokera, ndipo sangathe kupeza njira (yoongoka yokunenera).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
تَبَارَكَ ٱلَّذِيٓ إِن شَآءَ جَعَلَ لَكَ خَيۡرٗا مِّن ذَٰلِكَ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ وَيَجۡعَل لَّكَ قُصُورَۢا
Watukuka Mwini kupereka madalitso ambiri, Yemwe akafuna, akuchitira zabwino kuposa zimenezi, (adzakupatsa pa tsiku lachimaliziro) Minda yamtendere yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; ndipo adzakupangira nyumba zikuluzikulu zachifumu.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
بَلۡ كَذَّبُواْ بِٱلسَّاعَةِۖ وَأَعۡتَدۡنَا لِمَن كَذَّبَ بِٱلسَّاعَةِ سَعِيرًا
Koma akutsutsa zanthawi ya Qiyâma. ndipo tawakonzera Moto woyaka (iwo) amene akutsutsa zanthawi ya Qiyâma (ya chimaliziro).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
إِذَا رَأَتۡهُم مِّن مَّكَانِۭ بَعِيدٖ سَمِعُواْ لَهَا تَغَيُّظٗا وَزَفِيرٗا
(Motowo) ukadzawaona (naonso nkuuona) kuchokera pa malo apatali, (iwo) adzamva mkwiyo wa Motowo ndi mkokomo wake.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَإِذَآ أُلۡقُواْ مِنۡهَا مَكَانٗا ضَيِّقٗا مُّقَرَّنِينَ دَعَوۡاْ هُنَالِكَ ثُبُورٗا
Ndipo akadzaponyedwa m’menemo, pamalo opanika uku manja atanjatidwa chakukhosi, pamenepo adzaitana imfa (kuti iwafike, afe apumule ku masautsowo).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
لَّا تَدۡعُواْ ٱلۡيَوۡمَ ثُبُورٗا وَٰحِدٗا وَٱدۡعُواْ ثُبُورٗا كَثِيرٗا
(Tidzawauza): “Lero musaitane imfa imodzi, koma itanani imfa zambiri (ndipo simupeza mpumulo koma mazunzo okhaokha).”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
قُلۡ أَذَٰلِكَ خَيۡرٌ أَمۡ جَنَّةُ ٱلۡخُلۡدِ ٱلَّتِي وُعِدَ ٱلۡمُتَّقُونَۚ كَانَتۡ لَهُمۡ جَزَآءٗ وَمَصِيرٗا
Nena (kwa osakhulupirira): “Kodi izi ndizo zabwino, kapena munda wamuyaya umene alonjezedwa oopa Allah kuti udzakhale mphoto (yabwino) kwa iwo ndi kobwerera (kotamandika)?”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
لَّهُمۡ فِيهَا مَا يَشَآءُونَ خَٰلِدِينَۚ كَانَ عَلَىٰ رَبِّكَ وَعۡدٗا مَّسۡـُٔولٗا
“M’menemo adzapeza chilichonse chomwe adzafune. Adzakhala nthawi yaitali. Mtenderewu ndi lonjezo lochokera kwa Mbuye wako pa iwo lomwe adampempha kuti adzawakwaniritsire.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَيَوۡمَ يَحۡشُرُهُمۡ وَمَا يَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ فَيَقُولُ ءَأَنتُمۡ أَضۡلَلۡتُمۡ عِبَادِي هَٰٓؤُلَآءِ أَمۡ هُمۡ ضَلُّواْ ٱلسَّبِيلَ
Ndipo (kumbuka) tsiku limene adzawasonkhanitse (awa osakhulupirira) ndi omwe adali kuwapembedza (monga Isa (Yesu), Uzairi ndi angelo) kusiya Allah; adzanena (Allah kuuza amene ankalambiridwawo): “Kodi ndinu mudasokeretsa anthu angawa, kapena ndi okha adasokera njira.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
قَالُواْ سُبۡحَٰنَكَ مَا كَانَ يَنۢبَغِي لَنَآ أَن نَّتَّخِذَ مِن دُونِكَ مِنۡ أَوۡلِيَآءَ وَلَٰكِن مَّتَّعۡتَهُمۡ وَءَابَآءَهُمۡ حَتَّىٰ نَسُواْ ٱلذِّكۡرَ وَكَانُواْ قَوۡمَۢا بُورٗا
Adzanena: “E ulemelero ukhale kwa inu! Sizidali zoyenera kwa ife kudzikonzera atetezi mmalo mwa Inu, (nanji kuuza anthu kuti azitipembedza). Koma mudawasangalatsa iwo ndi makolo awo kufikira adaiwala malangizo (Anu). Ndipo adali anthu oonongeka.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
فَقَدۡ كَذَّبُوكُم بِمَا تَقُولُونَ فَمَا تَسۡتَطِيعُونَ صَرۡفٗا وَلَا نَصۡرٗاۚ وَمَن يَظۡلِم مِّنكُمۡ نُذِقۡهُ عَذَابٗا كَبِيرٗا
(Allah adzati): “Ndithu yakutsutsani (milungu yanuyo) pa zimene mwanena (kuti iwo adakusokeretsani). Ndipo simutha kudzichotsera (chilango) ngakhale (kupeza) chithandizo.” Ndipo, ndithudi amene achite zoipa mwa inu, tidzamulawitsa chilango chachikulu.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَمَآ أَرۡسَلۡنَا قَبۡلَكَ مِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ إِلَّآ إِنَّهُمۡ لَيَأۡكُلُونَ ٱلطَّعَامَ وَيَمۡشُونَ فِي ٱلۡأَسۡوَاقِۗ وَجَعَلۡنَا بَعۡضَكُمۡ لِبَعۡضٖ فِتۡنَةً أَتَصۡبِرُونَۗ وَكَانَ رَبُّكَ بَصِيرٗا
Ndipo palibe pamene tidatuma atumiki patsogolo pako koma ndithu iwo, adali kudya chakudya; ankayendanso m’misika. Ndipo tawasankha ena mwa inu kuti akhale mayeso kwa ena (popereka masautso kwa olungama). kodi mupirira? Ndipo, Mbuye wako ali Wopenya (chilichonse).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
۞ وَقَالَ ٱلَّذِينَ لَا يَرۡجُونَ لِقَآءَنَا لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡنَا ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ أَوۡ نَرَىٰ رَبَّنَاۗ لَقَدِ ٱسۡتَكۡبَرُواْ فِيٓ أَنفُسِهِمۡ وَعَتَوۡ عُتُوّٗا كَبِيرٗا
۞ Ndipo amene alibe chiyembekezo chakukumana Nafe akunena: “Bwanji angelo satumidwa kwa ife? Kapena timuone Mbuye wathu (kuti atitsimikizire kuti ndiwedi Mtumiki wake”? Ndipo Allah akunena): “Ndithu adzitukumula mmitima mwawo ndipo anyoza; kunyoza kwakukulu.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يَوۡمَ يَرَوۡنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ لَا بُشۡرَىٰ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُجۡرِمِينَ وَيَقُولُونَ حِجۡرٗا مَّحۡجُورٗا
Tsiku lowaona angelo, sikudzakhala chisangalalo tsiku limenelo kwa ochimwa, (koma lidzakhala tsiku lochoka moyo wawo). Ndipo adzanena (tsiku limenelo): “Ha! Allah atitchinjirize kwambiri.” (Koma mawu awa, sadzathandiza chilichonse).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَقَدِمۡنَآ إِلَىٰ مَا عَمِلُواْ مِنۡ عَمَلٖ فَجَعَلۡنَٰهُ هَبَآءٗ مَّنثُورًا
Ndipo tidzaidzera ntchito iliyonse (yabwino) imene adachita, ndipo tizaichita monga fumbi louluka (ponseponse, yopanda phindu chifukwa cha kusakhulupirira Allah kwawo.)
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِ يَوۡمَئِذٍ خَيۡرٞ مُّسۡتَقَرّٗا وَأَحۡسَنُ مَقِيلٗا
Anthu a ku Munda wamtendere tsiku limenelo adzakhala ndi mokhala mwabwino, ndi pamalo pampumulo wabwino.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَيَوۡمَ تَشَقَّقُ ٱلسَّمَآءُ بِٱلۡغَمَٰمِ وَنُزِّلَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ تَنزِيلًا
Ndipo akumbutse za tsikulo pomwe thambo lidzang’ambika ndikudzetsa mitambo (yomwe idzachititsa chimdima ponseponse). Ndipo angelo adzatsika ambirimbiri.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
ٱلۡمُلۡكُ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡحَقُّ لِلرَّحۡمَٰنِۚ وَكَانَ يَوۡمًا عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ عَسِيرٗا
Tsiku limenelo ufumu wachoonadi ngwa (Allah) Wachifundo chambiri. Ndipo lidzakhala tsiku lovuta kwa osakhulupirira.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَيَوۡمَ يَعَضُّ ٱلظَّالِمُ عَلَىٰ يَدَيۡهِ يَقُولُ يَٰلَيۡتَنِي ٱتَّخَذۡتُ مَعَ ٱلرَّسُولِ سَبِيلٗا
Ndipo tsiku (limenelo), wosalungama adzakukuta zala zake uku akunena: “Kalanga ine! Ndikadatsata njira ya Mtumiki.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يَٰوَيۡلَتَىٰ لَيۡتَنِي لَمۡ أَتَّخِذۡ فُلَانًا خَلِيلٗا
“E tsoka langa! Ndikadapanda kumchita uje kukhala bwenzi wanga. (nkadapulumuka lero).”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
لَّقَدۡ أَضَلَّنِي عَنِ ٱلذِّكۡرِ بَعۡدَ إِذۡ جَآءَنِيۗ وَكَانَ ٱلشَّيۡطَٰنُ لِلۡإِنسَٰنِ خَذُولٗا
“Ndithu adandisokeretsa kufikira ndidasiya ulaliki (wa Allah) utandidzera. Zoonadi, satana amataya munthu (akaona kuti wamgwetsa m’chionongeko).”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَقَالَ ٱلرَّسُولُ يَٰرَبِّ إِنَّ قَوۡمِي ٱتَّخَذُواْ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانَ مَهۡجُورٗا
Ndipo Mtumiki (adasuma kwa Mbuye wake) adati: “E Mbuye wanga! Ndithu anthu anga aisandutsa Qur’aniyi kukhala chinthu chosiidwa, (sakuiwerenga. Ndiponso sakutsata ziphunzitso zake).”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَكَذَٰلِكَ جَعَلۡنَا لِكُلِّ نَبِيٍّ عَدُوّٗا مِّنَ ٱلۡمُجۡرِمِينَۗ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ هَادِيٗا وَنَصِيرٗا
Momwemonso mneneri aliyense tidamkonzera mdani wochokera mwa (anthu) oipa. Ndipo Mbuye wako wakwana kukhala muongoli ndi mthandizi (wako).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوۡلَا نُزِّلَ عَلَيۡهِ ٱلۡقُرۡءَانُ جُمۡلَةٗ وَٰحِدَةٗۚ كَذَٰلِكَ لِنُثَبِّتَ بِهِۦ فُؤَادَكَۖ وَرَتَّلۡنَٰهُ تَرۡتِيلٗا
Ndipo amene sadakhulupirire akunena: “Bwanji Qur’an yonse siidavumbulutsidwe nthawi imodzi kwa iye? Momwemo (ukuoneramo, tikuitumiza pang’onopang’ono) kuti tiulimbikitse mtima wako ndi iyo, ndipo taiyala, mkayalidwe kabwino.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَلَا يَأۡتُونَكَ بِمَثَلٍ إِلَّا جِئۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ وَأَحۡسَنَ تَفۡسِيرًا
Ndipo sangakubweretsere fanizo lililonse koma tikubweretsera choonadi (choyankha fanizolo ndi kukudziwitsa) ndi kumasulira kwabwino.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
ٱلَّذِينَ يُحۡشَرُونَ عَلَىٰ وُجُوهِهِمۡ إِلَىٰ جَهَنَّمَ أُوْلَٰٓئِكَ شَرّٞ مَّكَانٗا وَأَضَلُّ سَبِيلٗا
Amene adzasonkhanitsidwe akukokedwa ndi nkhope zawo kunka ku Jahanama, iwowo adzakhala pamalo oipa ndipo ngosokera njira (yachoonadi).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ وَجَعَلۡنَا مَعَهُۥٓ أَخَاهُ هَٰرُونَ وَزِيرٗا
Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku. Ndipo m’bale wake Harun (Aroni) tidamsankha kukhala nduna (yake).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
فَقُلۡنَا ٱذۡهَبَآ إِلَى ٱلۡقَوۡمِ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا فَدَمَّرۡنَٰهُمۡ تَدۡمِيرٗا
Choncho tidati: “Pitani kwa anthu omwe atsutsa zisonyezo Zathu. Tero, tidawaononga kotheratu.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَقَوۡمَ نُوحٖ لَّمَّا كَذَّبُواْ ٱلرُّسُلَ أَغۡرَقۡنَٰهُمۡ وَجَعَلۡنَٰهُمۡ لِلنَّاسِ ءَايَةٗۖ وَأَعۡتَدۡنَا لِلظَّٰلِمِينَ عَذَابًا أَلِيمٗا
Naonso anthu a Nuh, pamene adatsutsa atumiki, tidawamiza, ndipo tidawachita kukhala phunziro kwa anthu, ndipo anthu osalungama tawakonzera chilango chowawa.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَعَادٗا وَثَمُودَاْ وَأَصۡحَٰبَ ٱلرَّسِّ وَقُرُونَۢا بَيۡنَ ذَٰلِكَ كَثِيرٗا
Nawonso Âdi, Asamudu ndi eni chitsime ndi mibadwo yambiri pakati pa iwo.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَكُلّٗا ضَرَبۡنَا لَهُ ٱلۡأَمۡثَٰلَۖ وَكُلّٗا تَبَّرۡنَا تَتۡبِيرٗا
Ndipo onse tidawaponyera mafanizo; ndiponso onse tidawaononga motheratu (pamene adakana kutsatira malamulo athu).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَلَقَدۡ أَتَوۡاْ عَلَى ٱلۡقَرۡيَةِ ٱلَّتِيٓ أُمۡطِرَتۡ مَطَرَ ٱلسَّوۡءِۚ أَفَلَمۡ يَكُونُواْ يَرَوۡنَهَاۚ بَلۡ كَانُواْ لَا يَرۡجُونَ نُشُورٗا
Ndipo ndithu iwo (Aquraish, m’maulendo awo) adafika pa mudzi (Sodomu ndi Gomora) womwe mvula yoipa (ya sangalabwi) idawavumbwa. Kodi sadali kuuona? Koma sadali kuyembekezera zakuuka ku imfa.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَإِذَا رَأَوۡكَ إِن يَتَّخِذُونَكَ إِلَّا هُزُوًا أَهَٰذَا ٱلَّذِي بَعَثَ ٱللَّهُ رَسُولًا
Ndipo akakuona (iwe Mtumiki Muhammad {s.a.w}), amangokuchitira chipongwe: “Kodi uyu ndi yemwe Allah wamtuma kuti akhale mtumiki?”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
إِن كَادَ لَيُضِلُّنَا عَنۡ ءَالِهَتِنَا لَوۡلَآ أَن صَبَرۡنَا عَلَيۡهَاۚ وَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ حِينَ يَرَوۡنَ ٱلۡعَذَابَ مَنۡ أَضَلُّ سَبِيلًا
“Ndithu adatsala pang’ono kutisokeretsa ku milungu yathu, tikadapanda kupirira pa milunguyo.” Posachedwapa adziwa, pamene adzaona chilango, (kuti) ndani wosokera zedi njira.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
أَرَءَيۡتَ مَنِ ٱتَّخَذَ إِلَٰهَهُۥ هَوَىٰهُ أَفَأَنتَ تَكُونُ عَلَيۡهِ وَكِيلًا
Kodi wamuona yemwe wachichita chilakolako chake (chimene akuchikonda) kukhala mulungu wake? Kodi iweyo ungathe kukhala muyang’aniri wa iye (kotero kuti ungamkakamize chomwe safuna)?
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
أَمۡ تَحۡسَبُ أَنَّ أَكۡثَرَهُمۡ يَسۡمَعُونَ أَوۡ يَعۡقِلُونَۚ إِنۡ هُمۡ إِلَّا كَٱلۡأَنۡعَٰمِ بَلۡ هُمۡ أَضَلُّ سَبِيلًا
Kapena ukuganiza kuti ambiri a iwo akumva kapena kuzindikira? Iwo sali kanthu kena koma ali ngati ziweto. Ndipo iwo asokera kwambiri njira.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
أَلَمۡ تَرَ إِلَىٰ رَبِّكَ كَيۡفَ مَدَّ ٱلظِّلَّ وَلَوۡ شَآءَ لَجَعَلَهُۥ سَاكِنٗا ثُمَّ جَعَلۡنَا ٱلشَّمۡسَ عَلَيۡهِ دَلِيلٗا
Kodi sudaone momwe Mbuye wako wautambasulira mthunzi? Akadafuna, akadauchita kuti ukhale wokhazikika (wosasinthasintha). Ndipo talichita dzuwa kukhala chisonyezo chake. [294]
[294] Apa Allah akuti kodi sukuona luso la Allah pa zopangapanga Zake ndi mphamvu Zake zoposa momwe amautambasulira mthunzi nthawi yamasana kuti munthu akhale pamthunzi ndikupeza mpumulo wabwino kuchoka mkutentha kwa dzuwa. Pakadapanda mthunzi ndiye kuti munthu akadatenthedwa ndi dzuwa ndikusowetsedwa mtendere pa moyo wake. Ndipo Allah akadafuna akadauleka mthunzi kuti ukhale pamalo amodzi. Koma Iye ndi mphamvu Zake zoposa adaupanga kukhala wosinthasintha.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
ثُمَّ قَبَضۡنَٰهُ إِلَيۡنَا قَبۡضٗا يَسِيرٗا
Kenaka tikuufumbata kwa Ife m’kufumbata kwapang’onopang’ono (kufikira wonse wutachoka).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلَّيۡلَ لِبَاسٗا وَٱلنَّوۡمَ سُبَاتٗا وَجَعَلَ ٱلنَّهَارَ نُشُورٗا
Ndipo Iye ndi amene wakuchitirani usiku kukhala monga chovala, ndipo tulo monga mpumulo, ndipo usana wauchita kukhala monga nthawi youka (kuimfa).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَرۡسَلَ ٱلرِّيَٰحَ بُشۡرَۢا بَيۡنَ يَدَيۡ رَحۡمَتِهِۦۚ وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ طَهُورٗا
Iye ndi Yemwe amatumiza mphepo kukhala nkhani yabwino patsogolo pa chifundo chake (mvula), ndipo kuchokera kumitambo tikutsitsa madzi oyera.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
لِّنُحۡـِۧيَ بِهِۦ بَلۡدَةٗ مَّيۡتٗا وَنُسۡقِيَهُۥ مِمَّا خَلَقۡنَآ أَنۡعَٰمٗا وَأَنَاسِيَّ كَثِيرٗا
Kuti ndi madziwo tiukitse dziko lakufa (lachilala), ndikumwetsa zina mwa zimene tidazilenga monga ziweto ndi anthu ochuluka.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَٰهُ بَيۡنَهُمۡ لِيَذَّكَّرُواْ فَأَبَىٰٓ أَكۡثَرُ ٱلنَّاسِ إِلَّا كُفُورٗا
Ndiponso ndithu tikuigawa (mvulayi) pakati pawo kuti akumbukire, ndipo anthu ambiri akukana (kuthokoza Allah) koma kupitiriza kusakhulupirira.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَلَوۡ شِئۡنَا لَبَعَثۡنَا فِي كُلِّ قَرۡيَةٖ نَّذِيرٗا
Ndipo tikadafuna, tikadatuma mchenjezi wawowawo m’mudzi uliwonse, (koma tatuma Muhammad {s.a.w} kuti akhale mchenjezi wa onse).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
فَلَا تُطِعِ ٱلۡكَٰفِرِينَ وَجَٰهِدۡهُم بِهِۦ جِهَادٗا كَبِيرٗا
Choncho usawamvere osakhulupirira koma limbana nawo ndi iyo (Qur’an); kulimbana kwakukulu.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
۞ وَهُوَ ٱلَّذِي مَرَجَ ٱلۡبَحۡرَيۡنِ هَٰذَا عَذۡبٞ فُرَاتٞ وَهَٰذَا مِلۡحٌ أُجَاجٞ وَجَعَلَ بَيۡنَهُمَا بَرۡزَخٗا وَحِجۡرٗا مَّحۡجُورٗا
Ndipo Iye (Allah) ndi Yemwe wazikumanitsa nyanja ziwiri, iyi yamadzi okoma othetsa ludzu ndi iyi yamadzi amchere owawa. Ndipo waika malire ndi chitsekerezo chotsekereza pakati pa izo.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَهُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ مِنَ ٱلۡمَآءِ بَشَرٗا فَجَعَلَهُۥ نَسَبٗا وَصِهۡرٗاۗ وَكَانَ رَبُّكَ قَدِيرٗا
Ndipo Iye ndiye adalenga munthu ndi madzi ndiponso adamchitira chibale cha magazi ndi chibale cha ukwati. Ndipo Mbuye wako ali Wokhoza chilichonse.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَيَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَنفَعُهُمۡ وَلَا يَضُرُّهُمۡۗ وَكَانَ ٱلۡكَافِرُ عَلَىٰ رَبِّهِۦ ظَهِيرٗا
Ndipo (ena mwa anthu) akupembedza zina zake kusiya Allah, zomwe sizingawathandize ndiponso sizingawadzetsere masautso (atasiya kuzipembedza). Ndipo wosakhulupirira ndi mthandizi wa zoipa poukira Mbuye wake.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا مُبَشِّرٗا وَنَذِيرٗا
Ndipo Ife sitidakutume koma kuti ukhale wouza nkhani zabwino (okhulupirira); ndi wochenjeza (osakhulupirira).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
قُلۡ مَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍ إِلَّا مَن شَآءَ أَن يَتَّخِذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ سَبِيلٗا
Nena: “Sindikupemphani malipiro pa zimenezi (zomwe ndikukuphunzitsani) koma amene afuna ayende pa njira yopita kwa Mbuye wake, (popanda chopereka).”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱلۡحَيِّ ٱلَّذِي لَا يَمُوتُ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِهِۦۚ وَكَفَىٰ بِهِۦ بِذُنُوبِ عِبَادِهِۦ خَبِيرًا
Ndipo tsamira kwa (Allah) Wamoyo, Wamuyaya Yemwe saafa. Ndipo mulemekeze pomtamanda ndi mbiri Zake. Ndipo Iye akukwana kudziwa bwinobwino machimo a akapolo Ake.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٖ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ ٱلرَّحۡمَٰنُ فَسۡـَٔلۡ بِهِۦ خَبِيرٗا
Yemwe adalenga thambo ndi nthaka ndi zimene zikupezeka mkati mwake. (Adazilenga) m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu, m’kukhazikika kodziwa Yekha). Iye Ngwachifundo chambiri; mufunseni wodziwa za Iye.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱسۡجُدُواْۤ لِلرَّحۡمَٰنِ قَالُواْ وَمَا ٱلرَّحۡمَٰنُ أَنَسۡجُدُ لِمَا تَأۡمُرُنَا وَزَادَهُمۡ نُفُورٗا۩
Ndipo akauzidwa (kuti): “Mulambireni (Allah) Wachifundo chambiri.” Amati: “Ndani Wachifundo chambiri? Kodi tilambire Yemwe iwe ukutilamula?” (Mawu amenewa) adawaonjezera iwo mwano.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
تَبَارَكَ ٱلَّذِي جَعَلَ فِي ٱلسَّمَآءِ بُرُوجٗا وَجَعَلَ فِيهَا سِرَٰجٗا وَقَمَرٗا مُّنِيرٗا
Watukuka Mwini kupereka madalitso Yemwe adakhazikitsa nyenyezi ku thambo, ndipo m’menemo adaika nyali (dzuwa) ndi mwezi wounika.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ خِلۡفَةٗ لِّمَنۡ أَرَادَ أَن يَذَّكَّرَ أَوۡ أَرَادَ شُكُورٗا
Ndipo Iye ndi Yemwe adapanga usiku ndi usana kuti zizitsatana (ndikusinthana). (Izi zingapindulitse) kwa amene afuna kukumbukira kapena (amene) afuna kuthokoza.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَعِبَادُ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلَّذِينَ يَمۡشُونَ عَلَى ٱلۡأَرۡضِ هَوۡنٗا وَإِذَا خَاطَبَهُمُ ٱلۡجَٰهِلُونَ قَالُواْ سَلَٰمٗا
Ndipo akapolo a (Allah) Wachifundo chambiri ndi omwe akuyenda pa dziko modzichepetsa, ndipo mbuli zikanena kwa iwo (mawu amwano), amaziyankha mawu abwino.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَٱلَّذِينَ يَبِيتُونَ لِرَبِّهِمۡ سُجَّدٗا وَقِيَٰمٗا
Ndi omwe amapititsa nthawi ina ya usiku uku akulambira ndi kuimilira chifukwa cha kulemekeza Mbuye wawo.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَٱلَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَا ٱصۡرِفۡ عَنَّا عَذَابَ جَهَنَّمَۖ إِنَّ عَذَابَهَا كَانَ غَرَامًا
Ndi omwe akunena: “E Mbuye wathu tipewetsereni chilango cha Jahannam; ndithu chilango chake nchosasiyana nacho.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
إِنَّهَا سَآءَتۡ مُسۡتَقَرّٗا وَمُقَامٗا
“Ndithu iyo ndi malo woipa; ndiponso pokhala poipa.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَٱلَّذِينَ إِذَآ أَنفَقُواْ لَمۡ يُسۡرِفُواْ وَلَمۡ يَقۡتُرُواْ وَكَانَ بَيۡنَ ذَٰلِكَ قَوَامٗا
Ndi omwe amati akamagawira anthu ena chuma chawo, samwaza pachabe ndiponso sachita umbombo, koma amachita mwapakatikati.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَٱلَّذِينَ لَا يَدۡعُونَ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ وَلَا يَقۡتُلُونَ ٱلنَّفۡسَ ٱلَّتِي حَرَّمَ ٱللَّهُ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَلَا يَزۡنُونَۚ وَمَن يَفۡعَلۡ ذَٰلِكَ يَلۡقَ أَثَامٗا
Ndi omwe sapembedza milungu ina poiphatikiza ndi Allah, ndiponso saapha munthu yemwe Allah adaletsa kumupha kupatula pakakhala choonadi ndiponso saachita chigololo. Ndipo amene achite zimenezi, apeza masautso (pompano pa dziko lapansi).
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يُضَٰعَفۡ لَهُ ٱلۡعَذَابُ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وَيَخۡلُدۡ فِيهِۦ مُهَانًا
Chilango chidzawonjezeredwa kwa iye tsiku la Qiyâma, ndipo adzakhala m’chilango muyaya uku ali wonyozeka.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
إِلَّا مَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ عَمَلٗا صَٰلِحٗا فَأُوْلَٰٓئِكَ يُبَدِّلُ ٱللَّهُ سَيِّـَٔاتِهِمۡ حَسَنَٰتٖۗ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورٗا رَّحِيمٗا
Kupatula amene walapa, naakhulupirira, ndikuchita ntchito yabwino. Tsono iwowo, Allah adzawasinthira zoipa zawo kukhala zabwino. Ndipo Allah ali Wokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَمَن تَابَ وَعَمِلَ صَٰلِحٗا فَإِنَّهُۥ يَتُوبُ إِلَى ٱللَّهِ مَتَابٗا
Ndipo amene akulapa ndikuchita zabwino, ndithu iye akulapa mwachoonadi kwa Allah.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَٱلَّذِينَ لَا يَشۡهَدُونَ ٱلزُّورَ وَإِذَا مَرُّواْ بِٱللَّغۡوِ مَرُّواْ كِرَامٗا
Omwenso sachitira umboni za bodza, ndipo akadutsa pamalo pa zachibwana, amadutsa mwaulemu.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَٱلَّذِينَ إِذَا ذُكِّرُواْ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ لَمۡ يَخِرُّواْ عَلَيۡهَا صُمّٗا وَعُمۡيَانٗا
Ndiponso omwe amati akakumbutsidwa Ayah za Mbuye wawo, samazigwera mwa ugonthi ndi mwakhungu.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَٱلَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَا هَبۡ لَنَا مِنۡ أَزۡوَٰجِنَا وَذُرِّيَّٰتِنَا قُرَّةَ أَعۡيُنٖ وَٱجۡعَلۡنَا لِلۡمُتَّقِينَ إِمَامًا
Ndi omwenso akunena: “E Mbuye wathu! Tipatseni mwa akazi athu ndi ana athu chotonthoza maso, ndipo tichiteni kukhala atsogoleri a oopa Allah.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
أُوْلَٰٓئِكَ يُجۡزَوۡنَ ٱلۡغُرۡفَةَ بِمَا صَبَرُواْ وَيُلَقَّوۡنَ فِيهَا تَحِيَّةٗ وَسَلَٰمًا
Iwo adzalipidwa zipinda (za pamwamba ku Jannah) chifukwa cha mavuto omwe adawapirira. Ndipo akalandira m’menemo ulemu ndi mtendere.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ حَسُنَتۡ مُسۡتَقَرّٗا وَمُقَامٗا
Akakhala m’menemo nthawi yaitali; akongolerenji malo okhazikika ndi kukhalamo.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
قُلۡ مَا يَعۡبَؤُاْ بِكُمۡ رَبِّي لَوۡلَا دُعَآؤُكُمۡۖ فَقَدۡ كَذَّبۡتُمۡ فَسَوۡفَ يَكُونُ لِزَامَۢا
Nena: “Ndithu Mbuye wanga sakadalabadira chilichonse pa inu pakadapanda mapemphero anu, (akadakulangani pompano pa dziko lapansi.) Komabe inu mwatsutsa (uthenga wa aneneri). Choncho chilango chidzakugweranibe.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
 
Ý nghĩa nội dung Chương: Chương Al-Furqan
Mục lục các chương Kinh Số trang
 
Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - Dịch thuật tiếng Chichio - Mục lục các bản dịch

Bản dịch ý nghĩa nội dung Kinh Qur'an bằng tiếng Chichio, do Khalid Ibrahim Petala dịch thuật, bản dịch năm 2020.

Đóng lại