Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - Dịch thuật tiếng Chichio * - Mục lục các bản dịch


Ý nghĩa nội dung Chương: Chương Al-Saf   Câu:

Chương Al-Saf

سَبَّحَ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
Zonse zakumwamba ndi zapansi zimalemekeza Allah (ndi kumuyeretsa kumakhalidwe osayenera ndi ulemelero Wake). Ndipo Iye Yekha Ngopambana pa chilichonse; Wanzeru zakuya.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لِمَ تَقُولُونَ مَا لَا تَفۡعَلُونَ
E inu amene mwakhulupirira! Bwanji mukunena zimene simuchita?[358]
[358] (Ndime 2-3) Khalidwe la munthu limene limakwiyitsa Allah kwambiri ndiko kunena zokoma chikhalirecho zochita zili zoipa. Amawanyenga anthu ndi mawu otsekemera koma zochita zake ndizachinyengo zokhazokha. Munthu wa makhalidwe otere, malipiro ake ndi kulowa ku nthukutira ya Moto. Choncho zochita zanu zifanane ndi zimene mukuyankhula. Apeweni makhalidwe achiphamaso.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
كَبُرَ مَقۡتًا عِندَ ٱللَّهِ أَن تَقُولُواْ مَا لَا تَفۡعَلُونَ
Nzomuipira zedi Allah kunena zinthu zimene simuchita.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
إِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلَّذِينَ يُقَٰتِلُونَ فِي سَبِيلِهِۦ صَفّٗا كَأَنَّهُم بُنۡيَٰنٞ مَّرۡصُوصٞ
Ndithu Allah amakonda amene akumenya nkhondo pa njira Yake (yofalitsa chipembedzo Chake), ali pa mzere (umodzi) uku ali monga chomanga, chomangika mwamphamvu.[359]
[359] Allah akufuna kuti Asilamu akhale dzanja limodzi pofalitsa Chisilamu, agwire ntchito yokomera gulu lonse mothangatana.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ لِمَ تُؤۡذُونَنِي وَقَد تَّعۡلَمُونَ أَنِّي رَسُولُ ٱللَّهِ إِلَيۡكُمۡۖ فَلَمَّا زَاغُوٓاْ أَزَاغَ ٱللَّهُ قُلُوبَهُمۡۚ وَٱللَّهُ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡفَٰسِقِينَ
Ndipo kumbuka (iwe Mneneri{s.a.w}) pamene Mûsa adanena kwa anthu ake kuti: “Ndichifukwa ninji mukundivutitsa ine pomwe mukudziwa kuti ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu?” Ndipo pamene adapitiriza kupandukira choonadi, Allah adaipinda mitima yawo (kuti isalandire chiongoko); ndipo Allah saongola anthu otuluka m’chilamulo Chake.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَإِذۡ قَالَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ يَٰبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ إِنِّي رَسُولُ ٱللَّهِ إِلَيۡكُم مُّصَدِّقٗا لِّمَا بَيۡنَ يَدَيَّ مِنَ ٱلتَّوۡرَىٰةِ وَمُبَشِّرَۢا بِرَسُولٖ يَأۡتِي مِنۢ بَعۡدِي ٱسۡمُهُۥٓ أَحۡمَدُۖ فَلَمَّا جَآءَهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ قَالُواْ هَٰذَا سِحۡرٞ مُّبِينٞ
Ndiponso (kumbuka) pamene adanena (Mtumiki) Isa (Yesu) mwana wa Mariya, kuti: “E inu ana a Israelil! Ndithu ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu, amene ndikuchitira umboni zimene zidadza patsogolo panga za buku la Chipangano chakale (Torah) ndipo ndikuuzani nkhani yabwino ya mthenga amene adzadze pambuyo panga, dzina lake Ahamad (Muhammad{s.a.w}).” Koma pamene adawadzera (Mtumiki wolonjedzedwayo) ndi zisonyezo zowonekera poyera (kuti iye ndi Mtumiki wa Allah). Adati: “Awa ndi matsenga owonekera.”
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ وَهُوَ يُدۡعَىٰٓ إِلَى ٱلۡإِسۡلَٰمِۚ وَٱللَّهُ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ
Kodi ndani oipitsitsa kuposa yemwe wapekera Allah bodza, pomwe iye akuitanidwira ku Chisilamu (chipembedzo choona ndi chabwino)? Ndipo Allah saongola anthu achinyengo.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يُرِيدُونَ لِيُطۡفِـُٔواْ نُورَ ٱللَّهِ بِأَفۡوَٰهِهِمۡ وَٱللَّهُ مُتِمُّ نُورِهِۦ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡكَٰفِرُونَ
Akufuna kuti azimitse dangalira la Allah ndi pakamwa pawo ndipo Allah Ngokwaniritsa dangalira Lake ngakhale ziwaipire osakhulupirira.[360]
[360] (Ndime 8-9) Allah akulonjeza kuti Chisilamu chidzapambana zipembedzo zonse ngakhale osakhulupilira akuchithira nkhondo.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
هُوَ ٱلَّذِيٓ أَرۡسَلَ رَسُولَهُۥ بِٱلۡهُدَىٰ وَدِينِ ٱلۡحَقِّ لِيُظۡهِرَهُۥ عَلَى ٱلدِّينِ كُلِّهِۦ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡمُشۡرِكُونَ
Iye ndi amene adatuma Mtumiki Wake (Muhammad{s.a.w}) ndi chiongoko ndi chipembedzo choona, kuti achiike pamwamba pa zipembedzo zonse, ngakhale kuti ophatikiza Allah ndi mafano zikuwaipira.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ هَلۡ أَدُلُّكُمۡ عَلَىٰ تِجَٰرَةٖ تُنجِيكُم مِّنۡ عَذَابٍ أَلِيمٖ
E inu amene mwakhulupirira! Kodi ndikudziwitseni malonda amene angakupulumutseni ku chilango chowawa?
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
تُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَتُجَٰهِدُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ بِأَمۡوَٰلِكُمۡ وَأَنفُسِكُمۡۚ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ
Muzimkhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake; ndipo muzichita Jihâd pa njira ya Allah ndi chuma chanu, ndi matupi anu. Zimenezo nzabwino kwa inu ngati muli odziwa.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يَغۡفِرۡ لَكُمۡ ذُنُوبَكُمۡ وَيُدۡخِلۡكُمۡ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ وَمَسَٰكِنَ طَيِّبَةٗ فِي جَنَّٰتِ عَدۡنٖۚ ذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
Akukhululukirani machimo anu ndipo akulowetsani m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake, ndiponso (adzakupatsani) mokhala mwabwino ku minda yamuyaya. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
وَأُخۡرَىٰ تُحِبُّونَهَاۖ نَصۡرٞ مِّنَ ٱللَّهِ وَفَتۡحٞ قَرِيبٞۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndizina zomwe mukuzifuna. Thandizo (lonse) lichokera kwa Allah ndi kugonjetsa kumene kuli pafupi; ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ كُونُوٓاْ أَنصَارَ ٱللَّهِ كَمَا قَالَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ لِلۡحَوَارِيِّـۧنَ مَنۡ أَنصَارِيٓ إِلَى ٱللَّهِۖ قَالَ ٱلۡحَوَارِيُّونَ نَحۡنُ أَنصَارُ ٱللَّهِۖ فَـَٔامَنَت طَّآئِفَةٞ مِّنۢ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَكَفَرَت طَّآئِفَةٞۖ فَأَيَّدۡنَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ عَلَىٰ عَدُوِّهِمۡ فَأَصۡبَحُواْ ظَٰهِرِينَ
E inu amene mwakhulupirira! Khalani othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah (pamene Mtumiki akukuitanani kuti mumthangate) monga momwe adanenera Isa (Yesu) mwana wa Mariya powauza otsatira ake: “Ndani adzandithangata pa ntchito ya Allah (yofalitsa chipembedzo Chake)? Otsatira ake adanena: “Ife ndife othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah.” Choncho gulu lina la ana a Israyeli lidakhululupirira, ndipo gulu lina silidakhululupirire, tero tidawapatsa mphamvu amene adakhulupirira pa adani awo, ndipo adali opambana.
Các Tafsir tiếng Ả-rập:
 
Ý nghĩa nội dung Chương: Chương Al-Saf
Mục lục các chương Kinh Số trang
 
Bản dịch ý nghĩa nội dung Qur'an - Dịch thuật tiếng Chichio - Mục lục các bản dịch

Bản dịch ý nghĩa nội dung Kinh Qur'an bằng tiếng Chichio, do Khalid Ibrahim Petala dịch thuật, bản dịch năm 2020.

Đóng lại