Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 阿迪亚特   段:

Al-’Adiy ât

وَٱلۡعَٰدِيَٰتِ ضَبۡحٗا
Ndikulumbilira akavalo othamanga ali ndi phuma,
阿拉伯语经注:
فَٱلۡمُورِيَٰتِ قَدۡحٗا
Ndi otulutsa moto ku zikhotwa (pomenyetsa miyendo m’miyala),
阿拉伯语经注:
فَٱلۡمُغِيرَٰتِ صُبۡحٗا
Ndi othira nkhondo adani mmawa (dzuwa lisadatuluke),
阿拉伯语经注:
فَأَثَرۡنَ بِهِۦ نَقۡعٗا
Ndi kuulutsa fumbi lambiri (kwa adani) nthawi imeneyo,
阿拉伯语经注:
فَوَسَطۡنَ بِهِۦ جَمۡعًا
Ndikulowelera mkatikati mwa adani.
阿拉伯语经注:
إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لِرَبِّهِۦ لَكَنُودٞ
Ndithu munthu ali wokanira Mbuye wake, (sathokoza Allah pa zimene amdalitsa nazo).[472]
[472] Tanthauzo la “kukanira Mbuye wake” ndi kuukanira mtendere Wake. Ndipo kukanira mtendere ndiko kusagwiritsira ntchito mtenderewo mnjira zabwino, monga m’mapemphero ndi zina zotero.
阿拉伯语经注:
وَإِنَّهُۥ عَلَىٰ ذَٰلِكَ لَشَهِيدٞ
Ndithudi iye pa zimenezi ndi mboni (yodzichitira yekha kupyolera mzochitachita zake).
阿拉伯语经注:
وَإِنَّهُۥ لِحُبِّ ٱلۡخَيۡرِ لَشَدِيدٌ
Ndipo ndithu iye ndiwokonda chuma kwambiri (ndiponso ngwamsulizo).[473]
[473] Kapena kuti ali wofunitsitsa chuma kwambiri; kumeneko ndikumangoti mtima dyokodyoko pachuma. Ukachipeza ndikumachichitira umbombo ndipo ndikumaganiza kuti chumacho nchopambana china chilichonse.
阿拉伯语经注:
۞ أَفَلَا يَعۡلَمُ إِذَا بُعۡثِرَ مَا فِي ٱلۡقُبُورِ
Kodi sakudziwa zikadzatulutsidwa za m’manda,
阿拉伯语经注:
وَحُصِّلَ مَا فِي ٱلصُّدُورِ
Ndikudzasonkhanitsidwa ndi kuonekera poyera zomwe zidali m’mitima?
阿拉伯语经注:
إِنَّ رَبَّهُم بِهِمۡ يَوۡمَئِذٖ لَّخَبِيرُۢ
Ndithu tsiku limenelo Mbuye wawo adzawadziwa kwambiri (ndikuwalongosolera zonse zochita zawo).[474]
[474] “Kuwadziwa kwambiri,” kukutanthauza kuti Iye ngodziwa zazikuluzikulu ndi zazing’onozing’ono zoonekera poyera ndi zobisika. Tsiku limenelo adzawalipira chilichonse chimene adachita.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 阿迪亚特
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭