《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 * - 译解目录


含义的翻译 章: 哈吉拉   段:

哈吉拉

الٓرۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ وَقُرۡءَانٖ مُّبِينٖ
۞ Alif-Lâm-Râ. Izi ndi Aaya (ndime) za m’buku (lomwe lasonkhanitsa chilichonse chofunika,) ndi Qur’an yomveka bwino.
阿拉伯语经注:
رُّبَمَا يَوَدُّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوۡ كَانُواْ مُسۡلِمِينَ
Nthawi zambiri omwe sadakhulupirire (pamene adzakhala m’Moto) adzalakalaka kuti akadakhala okhulupirira (pamoyo wa pa dziko lapansi).
阿拉伯语经注:
ذَرۡهُمۡ يَأۡكُلُواْ وَيَتَمَتَّعُواْ وَيُلۡهِهِمُ ٱلۡأَمَلُۖ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ
Asiye azidya (chakudya monga momwe zidyera nyama) ndi kusangalala; ndipo chiyembekezo chiziwatangwanitsa ndi kuwanyenga; posachedwa adziwa (kuti zimene amaziyembekezerazo nzabodza).
阿拉伯语经注:
وَمَآ أَهۡلَكۡنَا مِن قَرۡيَةٍ إِلَّا وَلَهَا كِتَابٞ مَّعۡلُومٞ
Ndipo sitidaononge mudzi uliwonse (m’midzi yochita zoipa) koma udali ndi nthawi yake (youwonongera) yodziwika.
阿拉伯语经注:
مَّا تَسۡبِقُ مِنۡ أُمَّةٍ أَجَلَهَا وَمَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ
Ndipo palibe mtundu wa anthu umene ungaitsogolere nthawi yake (yofera) kapena kuichedwetsa (itakwana kale).
阿拉伯语经注:
وَقَالُواْ يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِي نُزِّلَ عَلَيۡهِ ٱلذِّكۡرُ إِنَّكَ لَمَجۡنُونٞ
Ndipo (osakhulupirira) akunena (mwachipongwe) “E iwe amene wavumbulutsiridwa ulaliki! Ndithudi ndiwe wamisala.”
阿拉伯语经注:
لَّوۡمَا تَأۡتِينَا بِٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ
“Bwanji iwe osatibweretsera angelo (kuti akuchitire umboni) ngati uli mmodzi waonena zoona?”
阿拉伯语经注:
مَا نُنَزِّلُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَمَا كَانُوٓاْ إِذٗا مُّنظَرِينَ
(Allah akuwauza:) “Ife sititsitsa angelo pokhapokha kutatsimikizika (tikawatuma kukapereka chilango kwa anthu). Ndipo pamenepo sangapatsidwe nthawi.”
阿拉伯语经注:
إِنَّا نَحۡنُ نَزَّلۡنَا ٱلذِّكۡرَ وَإِنَّا لَهُۥ لَحَٰفِظُونَ
Ndithu Ife ndife omwe tavumbulutsa Qur’an, ndipo ndithudi, tiisunga.[244]
[244] Omasulira Qur’an adati Allah Mwini wake adalonjeza udindo woisunga Qur’an ndi kuiteteza kuti anthu asathe kuikapo manja awo posintha ndondomeko ya mawu ake kapena matanthandauzo ake, poonjezerapo malembo ena kapena kuchepetsa monga momwe zidachitikira ndi mabuku ena omwe Allah adawasiira anthu kuti awasunge ndi kuwateteza.
Qur’an yomwe tikuwerenga lero ndi yomweyo imene idalinso kuwerengedwa m’nthawi ya Mtumiki Muhammad (s.a.w). Palibe mawu oonjeza kapena kuchotsa.
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ فِي شِيَعِ ٱلۡأَوَّلِينَ
Ndithudi tidatuma (atumiki) patsogolo pako m’magulu (a anthu) akale, oyamba.
阿拉伯语经注:
وَمَا يَأۡتِيهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Ndipo sadali kuwadzera mtumiki aliyense, koma ankamchitira chipongwe.
阿拉伯语经注:
كَذَٰلِكَ نَسۡلُكُهُۥ فِي قُلُوبِ ٱلۡمُجۡرِمِينَ
Momwemo tikuupititsa (mkhalidwe wachipongwewu) m’mitima mwa oipa.
阿拉伯语经注:
لَا يُؤۡمِنُونَ بِهِۦ وَقَدۡ خَلَتۡ سُنَّةُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Koma saikhulupirira Qur’aniyi chikhalirecho mafanizo a anthu oyamba awadutsa (ndipo aona momwe tidawaonongera).
阿拉伯语经注:
وَلَوۡ فَتَحۡنَا عَلَيۡهِم بَابٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ فَظَلُّواْ فِيهِ يَعۡرُجُونَ
Ndipo tikadawatsekulira (awa osakhulupirira) khomo lakumwamba ndipo nkukhala akukwera m’menemo (ndi kutsika monga momwe amafunira kuti zimenezo zikhale chozizwitsa cha Mtumiki),
阿拉伯语经注:
لَقَالُوٓاْ إِنَّمَا سُكِّرَتۡ أَبۡصَٰرُنَا بَلۡ نَحۡنُ قَوۡمٞ مَّسۡحُورُونَ
Akadati: “Ndithu maso athu aledzera; (iyayi) koma ndife anthu olodzedwa (tikuona zomwe sindizo).”[245]
[245] Allah akuti akadawatsekulira makomo akumwamba monga momwe adafunira nakwerako nkuona ufumu wa Allah ndi angelo ali yakaliyakali, sakadakhulupilirabe chifukwa chakuuma kwa mitima yawo. Chimene akadanena nkuti mitu yazungulira.
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ جَعَلۡنَا فِي ٱلسَّمَآءِ بُرُوجٗا وَزَيَّنَّٰهَا لِلنَّٰظِرِينَ
Ndithudi, kumwamba tidaikako “Buruji” (njira momwe zikuyendamo nyenyezi) ndipo tidakukongoletsa kwa okuwona.
阿拉伯语经注:
وَحَفِظۡنَٰهَا مِن كُلِّ شَيۡطَٰنٖ رَّجِيمٍ
Ndipo tidakuteteza kwa satana aliyense wopirikitsidwa (kumwambako akafuna kukamvetsera zimene zikunenedwa kumeneko).
阿拉伯语经注:
إِلَّا مَنِ ٱسۡتَرَقَ ٱلسَّمۡعَ فَأَتۡبَعَهُۥ شِهَابٞ مُّبِينٞ
Kupatula amene amamvetsera mobera; ndipo pompo chinsakali chamoto choonekera chimamtsata.
阿拉伯语经注:
وَٱلۡأَرۡضَ مَدَدۡنَٰهَا وَأَلۡقَيۡنَا فِيهَا رَوَٰسِيَ وَأَنۢبَتۡنَا فِيهَا مِن كُلِّ شَيۡءٖ مَّوۡزُونٖ
Ndipo nthaka tidaiyala ndi kuikamo mapiri ndipo tameretsa mmera wa chinthu chilichonse m’menemo mwamlingo (wake).
阿拉伯语经注:
وَجَعَلۡنَا لَكُمۡ فِيهَا مَعَٰيِشَ وَمَن لَّسۡتُمۡ لَهُۥ بِرَٰزِقِينَ
Ndipo mmenemo takupangirani zinthu zoyendetsa moyo (wanu zakudya ndi zakumwa ndi zina zotere) ndiponso (tidakupatsani ana ndi ziweto) zomwe inu simungathe kuzidyetsa. (Ife ndife amene tikuzikonzera chakudya chawo, osati inu).
阿拉伯语经注:
وَإِن مِّن شَيۡءٍ إِلَّا عِندَنَا خَزَآئِنُهُۥ وَمَا نُنَزِّلُهُۥٓ إِلَّا بِقَدَرٖ مَّعۡلُومٖ
Ndipo palibe chinthu chilichonse koma gwero lake likuchokera kwa Ife; ndipo sitichitsitsa koma mwamlingo wodziwika (osati mwachisawawa).
阿拉伯语经注:
وَأَرۡسَلۡنَا ٱلرِّيَٰحَ لَوَٰقِحَ فَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَسۡقَيۡنَٰكُمُوهُ وَمَآ أَنتُمۡ لَهُۥ بِخَٰزِنِينَ
Ndipo timazitumiza mphepo zitasenza madzi, ndipo madziwo tikuwatsitsa kuchokera kumitamboyo; kenako tikukumwetsani madziwo (tikukumwetseraninso ziweto zanu, mitengo yanu ndi zina), ndipo inu si amene mukuwasunga (madziwo).
阿拉伯语经注:
وَإِنَّا لَنَحۡنُ نُحۡيِۦ وَنُمِيتُ وَنَحۡنُ ٱلۡوَٰرِثُونَ
Ndipo ndithudi, Ife ndife omwe timapereka moyo, ndi kupereka imfa. Ndiponso Ife ndi Amlowam’malo (a chinthu chilichonse chimene chikusiidwa chopanda mwini).
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ عَلِمۡنَا ٱلۡمُسۡتَقۡدِمِينَ مِنكُمۡ وَلَقَدۡ عَلِمۡنَا ٱلۡمُسۡتَـٔۡخِرِينَ
Ndipo ndithu tikuwadziwa mwa inu amene atsogola (amene adafa kale), ndipo ndithu tikuwadziwanso amene atsalira (ali ndi moyobe ndi amene sanabadwe).
阿拉伯语经注:
وَإِنَّ رَبَّكَ هُوَ يَحۡشُرُهُمۡۚ إِنَّهُۥ حَكِيمٌ عَلِيمٞ
Ndipo ndithu palibe chikaiko, Mbuye wako ndi Yemwe adzawasonkhanitsa (pambuyo pa imfa kuti adzawaweruze). Iye ndi Wanzeru zakuya, Wodziwa chilichonse.
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِن صَلۡصَٰلٖ مِّنۡ حَمَإٖ مَّسۡنُونٖ
Ndipo ndithu tidamlenga munthu ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera, osinthika mtundu;
阿拉伯语经注:
وَٱلۡجَآنَّ خَلَقۡنَٰهُ مِن قَبۡلُ مِن نَّارِ ٱلسَّمُومِ
Ndipo ziwanda tidazilenga kale ndi moto wamphepo yotentha kwambiri.
阿拉伯语经注:
وَإِذۡ قَالَ رَبُّكَ لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِنِّي خَٰلِقُۢ بَشَرٗا مِّن صَلۡصَٰلٖ مِّنۡ حَمَإٖ مَّسۡنُونٖ
Ndipo (kumbuka) pamene Mbuye wako adauza angelo (kuti): “Ndithu Ine ndilenga munthu ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera osinthika mtundu.”
阿拉伯语经注:
فَإِذَا سَوَّيۡتُهُۥ وَنَفَخۡتُ فِيهِ مِن رُّوحِي فَقَعُواْ لَهُۥ سَٰجِدِينَ
“Choncho ndikamkwaniritsa ndikumuuzira mzimu wolengedwa ndi Ine, muweramireni momulemekeza.’’
阿拉伯语经注:
فَسَجَدَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ كُلُّهُمۡ أَجۡمَعُونَ
Choncho angelo onse adamuweramira.
阿拉伯语经注:
إِلَّآ إِبۡلِيسَ أَبَىٰٓ أَن يَكُونَ مَعَ ٱلسَّٰجِدِينَ
Kupatula Iblis; adakana kukhala mmodzi mwa owerama.
阿拉伯语经注:
قَالَ يَٰٓإِبۡلِيسُ مَا لَكَ أَلَّا تَكُونَ مَعَ ٱلسَّٰجِدِينَ
Allah adati: “E iwe Iblis! Chifukwa ninji sudakhale pamodzi ndi owerama?”
阿拉伯语经注:
قَالَ لَمۡ أَكُن لِّأَسۡجُدَ لِبَشَرٍ خَلَقۡتَهُۥ مِن صَلۡصَٰلٖ مِّنۡ حَمَإٖ مَّسۡنُونٖ
Adati: “Sindingamuweramire munthu yemwe mwam’lenga ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera osinthika mtundu.”
阿拉伯语经注:
قَالَ فَٱخۡرُجۡ مِنۡهَا فَإِنَّكَ رَجِيمٞ
(Allah) adati: “Choncho choka m’menemo; ndithu iwe ndiwe wopirikitsidwa (ku chifundo Changa).”
阿拉伯语经注:
وَإِنَّ عَلَيۡكَ ٱللَّعۡنَةَ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلدِّينِ
“Ndipo ndithu matembelero ali pa iwe mpaka tsiku lamalipiro.”
阿拉伯语经注:
قَالَ رَبِّ فَأَنظِرۡنِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ
(Iblis) adati: “Mbuye wanga choncho ndipatseni nthawi mpaka tsiku limene adzaukitsidwe kwa akufa.”
阿拉伯语经注:
قَالَ فَإِنَّكَ مِنَ ٱلۡمُنظَرِينَ
(Allah) adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi mwa opatsidwa nthawi (danga).”
阿拉伯语经注:
إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡوَقۡتِ ٱلۡمَعۡلُومِ
Kufikira tsiku la nthawi yodziwika (ikadzafika nthawi imeneyo, udzafa).”
阿拉伯语经注:
قَالَ رَبِّ بِمَآ أَغۡوَيۡتَنِي لَأُزَيِّنَنَّ لَهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَأُغۡوِيَنَّهُمۡ أَجۡمَعِينَ
(Satana) adati: “Mbuye wanga! Pakuti mwanena kuti ndine wosokera, choncho ndikawakometsera za m’dziko (kufikira kuti akakulakwireni), ndithu ndikawasokeretsa onse.”
阿拉伯语经注:
إِلَّا عِبَادَكَ مِنۡهُمُ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
“Kupatula akapolo anu oyeretsedwa, mwa iwo.”
阿拉伯语经注:
قَالَ هَٰذَا صِرَٰطٌ عَلَيَّ مُسۡتَقِيمٌ
(Allah) adati: “Iyi ndinjira yoongoka yobwerera kwa Ine (ndipo adzandidzera akadzafuna).”
阿拉伯语经注:
إِنَّ عِبَادِي لَيۡسَ لَكَ عَلَيۡهِمۡ سُلۡطَٰنٌ إِلَّا مَنِ ٱتَّبَعَكَ مِنَ ٱلۡغَاوِينَ
Ndithudi akapolo Anga pa iwo sudzakhala ndi mphamvu kupatula okutsata (mwachifuniro chawo) mwa opotoka.”
阿拉伯语经注:
وَإِنَّ جَهَنَّمَ لَمَوۡعِدُهُمۡ أَجۡمَعِينَ
Ndithu Jahannam ndiwo malo awo olonjezedwa kwa onse.
阿拉伯语经注:
لَهَا سَبۡعَةُ أَبۡوَٰبٖ لِّكُلِّ بَابٖ مِّنۡهُمۡ جُزۡءٞ مَّقۡسُومٌ
Ili ndi makomo asanu ndi awiri; khomo lililonse lili ndi gawo logawidwa mwa iwo.
阿拉伯语经注:
إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّٰتٖ وَعُيُونٍ
Ndithudi owopa Allah adzakhala m’minda ndi akasupe (omwe adzakhala patsogolo pawo).
阿拉伯语经注:
ٱدۡخُلُوهَا بِسَلَٰمٍ ءَامِنِينَ
(Ndipo tidzawauza) “Lowani m’menemo mwamtendere, mosatekeseka.”
阿拉伯语经注:
وَنَزَعۡنَا مَا فِي صُدُورِهِم مِّنۡ غِلٍّ إِخۡوَٰنًا عَلَىٰ سُرُرٖ مُّتَقَٰبِلِينَ
Ndipo tidzawachotsera mfundo za chidani zomwe zidali m’mitima mwawo; (adzakhala) mwachibale, (mokondana,) atakhala pa mipando yachifumu atayang’anizana nkhope.
阿拉伯语经注:
لَا يَمَسُّهُمۡ فِيهَا نَصَبٞ وَمَا هُم مِّنۡهَا بِمُخۡرَجِينَ
Mmenemo masautso sakawakhudza, ndiponso sadzatulutsidwamo.
阿拉伯语经注:
۞ نَبِّئۡ عِبَادِيٓ أَنِّيٓ أَنَا ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ
Auze akapolo anga kuti ndithu Ine ndine Wokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha.
阿拉伯语经注:
وَأَنَّ عَذَابِي هُوَ ٱلۡعَذَابُ ٱلۡأَلِيمُ
Ndipo ndithu chilango Changa ndi chilango chopweteka zedi.
阿拉伯语经注:
وَنَبِّئۡهُمۡ عَن ضَيۡفِ إِبۡرَٰهِيمَ
Ndipo auze nkhani ya alendo a (Mneneri) Ibrahim.
阿拉伯语经注:
إِذۡ دَخَلُواْ عَلَيۡهِ فَقَالُواْ سَلَٰمٗا قَالَ إِنَّا مِنكُمۡ وَجِلُونَ
Pamene adalowa kwa iye ndikunena: “Salaman (Mtendere!)” (Iyenso adawayankha: “Mtendere ukhalenso pa inu.” Ndipo Pamene adaona kuti akana chakudya) Adati: “Ndithu ife tikukuopani.”
阿拉伯语经注:
قَالُواْ لَا تَوۡجَلۡ إِنَّا نُبَشِّرُكَ بِغُلَٰمٍ عَلِيمٖ
Iwo adati: “Usaope! Ife tikukuuza nkhani yabwino ya (kuti ubala) mwana wanzeru kwambiri.”
阿拉伯语经注:
قَالَ أَبَشَّرۡتُمُونِي عَلَىٰٓ أَن مَّسَّنِيَ ٱلۡكِبَرُ فَبِمَ تُبَشِّرُونَ
Iye adati: “Ha! Mukundiuza nkhani iyi pomwe ukalamba wandifikira? Kodi nkhani yabwinoyi mukundiuza mnjira yotani?”
阿拉伯语经注:
قَالُواْ بَشَّرۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ فَلَا تَكُن مِّنَ ٱلۡقَٰنِطِينَ
Iwo adati: “Takuuza nkhani yabwinoyi mwachoonadi; choncho, usakhale mwa otaya mtima.”
阿拉伯语经注:
قَالَ وَمَن يَقۡنَطُ مِن رَّحۡمَةِ رَبِّهِۦٓ إِلَّا ٱلضَّآلُّونَ
Iye adati: “(Ine sinditaya mtima ndi chifundo cha Allah. Ndipo) palibe angataye mtima ndi chifundo cha Allah, koma wosokera basi (yemwe sazindikira ukulu wa Allah).”
阿拉伯语经注:
قَالَ فَمَا خَطۡبُكُمۡ أَيُّهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ
Iye adati: “Nanga cholinga chanu china nchiyani, E inu otumidwa?”
阿拉伯语经注:
قَالُوٓاْ إِنَّآ أُرۡسِلۡنَآ إِلَىٰ قَوۡمٖ مُّجۡرِمِينَ
Iwo adati: “Ife tatumidwanso kwa anthu aja oipa (kuti tikawaononge).”
阿拉伯语经注:
إِلَّآ ءَالَ لُوطٍ إِنَّا لَمُنَجُّوهُمۡ أَجۡمَعِينَ
“Kupatula akubanja la Luti, ndithu ife tikawapulumutsa onse.”
阿拉伯语经注:
إِلَّا ٱمۡرَأَتَهُۥ قَدَّرۡنَآ إِنَّهَا لَمِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ
“Koma mkazi wake (wa Luti), tamkonzera kukhala mmodzi wa otsalira pambuyo.”
阿拉伯语经注:
فَلَمَّا جَآءَ ءَالَ لُوطٍ ٱلۡمُرۡسَلُونَ
Ndipo pamene atumikiwo adawadzera anthu a Luti (ali mmaonokedwe amunthu)
阿拉伯语经注:
قَالَ إِنَّكُمۡ قَوۡمٞ مُّنكَرُونَ
(Luti) adati: “Ndithudi, inu ndi anthu osadziwika (sitikudziwani).”
阿拉伯语经注:
قَالُواْ بَلۡ جِئۡنَٰكَ بِمَا كَانُواْ فِيهِ يَمۡتَرُونَ
Iwo adati: “Inde, ife takudzera ndi zomwe (iwo) adali kuzikaikira, (zomwe ndi chilango chawo).”
阿拉伯语经注:
وَأَتَيۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ وَإِنَّا لَصَٰدِقُونَ
“Ndipo tadza kwa iwe ndi (chinthu) choonadicho, ndithu ife ndi owona (pazimene tinenazi).”
阿拉伯语经注:
فَأَسۡرِ بِأَهۡلِكَ بِقِطۡعٖ مِّنَ ٱلَّيۡلِ وَٱتَّبِعۡ أَدۡبَٰرَهُمۡ وَلَا يَلۡتَفِتۡ مِنكُمۡ أَحَدٞ وَٱمۡضُواْ حَيۡثُ تُؤۡمَرُونَ
“Choncho, choka ndi banja lako mkati mwa usiku; ndipo iwe udziwatsata pambuyo pawo; tsono aliyense wa inu asayang’ane kumbuyo (akamva mkokomo wachilango chochokera kumwamba, kuopa kuti angafe), ndipo yendani (mwachangu) kunka komwe mukulamulidwa.”
阿拉伯语经注:
وَقَضَيۡنَآ إِلَيۡهِ ذَٰلِكَ ٱلۡأَمۡرَ أَنَّ دَابِرَ هَٰٓؤُلَآءِ مَقۡطُوعٞ مُّصۡبِحِينَ
Ndipo tidamudziwitsa iyeyo (Luti) lamulo lathu lakuti ndithu phata lawo anthu (ochimwawo) lidzadulidwa kum’banda kucha.
阿拉伯语经注:
وَجَآءَ أَهۡلُ ٱلۡمَدِينَةِ يَسۡتَبۡشِرُونَ
Ndipo adadza (kwa Luti) anthu a m’mudziwo akusangalala (poona kuti kwadza alendo okongola kuti achite nawo zadama).[246]
[246] Anthu a mumzindawo adadza ku nyumba ya Luti akuthamanga mokondwa atamva kuti kwa Luti kwadza alendo achinyamata owoneka bwino zedi.
阿拉伯语经注:
قَالَ إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ ضَيۡفِي فَلَا تَفۡضَحُونِ
(Mneneri Luti) adati: “Ndithu awa ndialendo anga; choncho musandiyalutse (pochita nawo zadama).”
阿拉伯语经注:
وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَلَا تُخۡزُونِ
“Muopeninso Allah, ndipo musandichititse manyazi (pamaso pawo).”
阿拉伯语经注:
قَالُوٓاْ أَوَلَمۡ نَنۡهَكَ عَنِ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Iwo adati (kwa Mneneri Luti): “Kodi sitidakuletse kulandira anthu (achilendo)?”
阿拉伯语经注:
قَالَ هَٰٓؤُلَآءِ بَنَاتِيٓ إِن كُنتُمۡ فَٰعِلِينَ
Iye adati: “Awa (akazi onsewa ali ngati) ana anga. Ngati inu ndinu ochita (chimene chalamulidwa, akwatireni; musachite zauve ndi alendowa).”
阿拉伯语经注:
لَعَمۡرُكَ إِنَّهُمۡ لَفِي سَكۡرَتِهِمۡ يَعۡمَهُونَ
Ndikulumbira moyo wako, ndithu iwo m’kuledzera kwawo (ndi zoipa) akungoyumbayumba.
阿拉伯语经注:
فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّيۡحَةُ مُشۡرِقِينَ
Choncho mkuwe wa chilango udawagwira pamene dzuwa linkatuluka.
阿拉伯语经注:
فَجَعَلۡنَا عَٰلِيَهَا سَافِلَهَا وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهِمۡ حِجَارَةٗ مِّن سِجِّيلٍ
Choncho (midziyo) tidaigadabula kumwamba kukhala pansi, (pansi kukhala kumwamba); ndipo tidawavumbwitsira mvula yamiyala (yotentha) ya moto.
阿拉伯语经注:
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّلۡمُتَوَسِّمِينَ
Ndithudi, (m’nkhani iyi) muli malingaliro (aakulu) kwa anthu olingalira zinthu.
阿拉伯语经注:
وَإِنَّهَا لَبِسَبِيلٖ مُّقِيمٍ
Ndipo (midzi) iyi (yomwe tidaiwononga chotereyi), ili chikhalire m’njira moyenda anthu (ndipo iwo akuona zizindikiro zake).
阿拉伯语经注:
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndithudi, mzimenezi muli phunziro (lalikulu) kwa okhulupirira.
阿拉伯语经注:
وَإِن كَانَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡأَيۡكَةِ لَظَٰلِمِينَ
Ndipo ndithu anthu a m’nkhalango (anthu a Mneneri Shuaib) adali ochita zoipa kwabasi.
阿拉伯语经注:
فَٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡ وَإِنَّهُمَا لَبِإِمَامٖ مُّبِينٖ
Choncho, tidawalanga. Ndipo (maiko) awiriwa ali m’njira zoonekera, (momwe Aquraish amadutsa pa maulendo awo).
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ كَذَّبَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡحِجۡرِ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Ndipo ndithu okhala m’chigwa cha Hijr (Asamuda), Adatsutsa atumiki.
阿拉伯语经注:
وَءَاتَيۡنَٰهُمۡ ءَايَٰتِنَا فَكَانُواْ عَنۡهَا مُعۡرِضِينَ
Tidawapatsa zisonyezo zathu, koma sadazilabadire.
阿拉伯语经注:
وَكَانُواْ يَنۡحِتُونَ مِنَ ٱلۡجِبَالِ بُيُوتًا ءَامِنِينَ
Iwo adali kujoba nyumba m’mapiri mwamtendere (ankaboola mapiri kuwasandutsa nyumba zawo).
阿拉伯语经注:
فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّيۡحَةُ مُصۡبِحِينَ
Choncho, chiphokoso cha chilango chidawapeza m’mawa.
阿拉伯语经注:
فَمَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Sichidawathandize (chuma) chomwe ankachipeza (ngakhalenso zimene ankazichita).
阿拉伯语经注:
وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَآ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۗ وَإِنَّ ٱلسَّاعَةَ لَأٓتِيَةٞۖ فَٱصۡفَحِ ٱلصَّفۡحَ ٱلۡجَمِيلَ
Sitidalenge thambo ndi nthaka ndi (zonse) zapakati pake koma (kulimbikitsa) choonadi. Ndipo palibe chikaiko, Qiyâma idza. Choncho mkhululukire kukhululuka kwabwino (aliyense wokuchitira zoipa).
阿拉伯语经注:
إِنَّ رَبَّكَ هُوَ ٱلۡخَلَّٰقُ ٱلۡعَلِيمُ
Ndithudi, Mbuye wako, Iye ndi Mlengi wa zonse, Wodziwa kwambiri.
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَٰكَ سَبۡعٗا مِّنَ ٱلۡمَثَانِي وَٱلۡقُرۡءَانَ ٱلۡعَظِيمَ
Ndipo ndithu takupatsa (Ayah izi) zisanu ndi ziwiri zomawerenga kawirikawiri, (Sûrat Al-Fatihah), ndi Qur’an yolemekezeka.
阿拉伯语经注:
لَا تَمُدَّنَّ عَيۡنَيۡكَ إِلَىٰ مَا مَتَّعۡنَا بِهِۦٓ أَزۡوَٰجٗا مِّنۡهُمۡ وَلَا تَحۡزَنۡ عَلَيۡهِمۡ وَٱخۡفِضۡ جَنَاحَكَ لِلۡمُؤۡمِنِينَ
Usatong’olere maso ako (kuyang’ana) zimene tawasangalatsa nazo mitundumitundu ya mwa iwo (monga chuma cha anthu osakhulupirira). Usawadandaulirenso iwo ndipo tsitsa phiko lako kwa okhululupirira, (uwafungatire).
阿拉伯语经注:
وَقُلۡ إِنِّيٓ أَنَا ٱلنَّذِيرُ ٱلۡمُبِينُ
Ndipo nena: “Ndithu ine ndine mchenjezi woonekera (sindikubisa chilichonse kuopera kuti chingakutsikireni chilango).”
阿拉伯语经注:
كَمَآ أَنزَلۡنَا عَلَى ٱلۡمُقۡتَسِمِينَ
Monga momwe tidatsitsira (chilango) kwa amene adadzigawa m’magulu.
阿拉伯语经注:
ٱلَّذِينَ جَعَلُواْ ٱلۡقُرۡءَانَ عِضِينَ
Omwe aichita Qur’an kukhala magawomagawo; (zina nkuzikhulupirira, zina nkuzitsutsa).
阿拉伯语经注:
فَوَرَبِّكَ لَنَسۡـَٔلَنَّهُمۡ أَجۡمَعِينَ
(Allah akudzilumbilira kuti:) Pali Mbuye wako, tidzawafunsa onse (tsiku la Qiyâma).
阿拉伯语经注:
عَمَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Pazimene ankachita (padziko lapansi).
阿拉伯语经注:
فَٱصۡدَعۡ بِمَا تُؤۡمَرُ وَأَعۡرِضۡ عَنِ ٱلۡمُشۡرِكِينَ
Choncho, lengeza zimene ukulamulidwa, ndipo uwapewe opembedza mafano, (usaope chilichonse kwa iwo).
阿拉伯语经注:
إِنَّا كَفَيۡنَٰكَ ٱلۡمُسۡتَهۡزِءِينَ
Ndithu Ife tikukwanira kukuteteza ku (zoipa za) achipongwe.
阿拉伯语经注:
ٱلَّذِينَ يَجۡعَلُونَ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَۚ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ
Omwe akupanga milungu ina ndi kuiphatikiza ndi Allah, posachedwapa adziwa (zotsatira zake).
阿拉伯语经注:
وَلَقَدۡ نَعۡلَمُ أَنَّكَ يَضِيقُ صَدۡرُكَ بِمَا يَقُولُونَ
Ndithu Ife tikudziwa kuti chifuwa chako chikubanika ndi zimene akunenazo.
阿拉伯语经注:
فَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ وَكُن مِّنَ ٱلسَّٰجِدِينَ
(Koma pirira), lemekeza Mbuye wako pamodzi ndi kumtamanda (ndi rnbiri Zake zabwino) ndipo khala mwa olambira (Allah.)
阿拉伯语经注:
وَٱعۡبُدۡ رَبَّكَ حَتَّىٰ يَأۡتِيَكَ ٱلۡيَقِينُ
Ndipo mpembedze Mbuye wako mpaka chikufike chitsimikizo (imfa).
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 哈吉拉
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 译解目录

古兰经契瓦文译解,哈利德·伊布拉欣·比德拉翻译,2020年版

关闭