Amene akuyembekezera kukumana ndi Allah, (agwire ntchito yabwino pamoyo wake kuti akakumane Naye ndi zabwino), pakuti ndithu nthawi ya Allah (tsiku la chimaliziro) ikudza (popanda chikaiko). Ndipo Iye Ngwakumva (zonena za akapolo Ake), Ngodziwa (zachinsinsi chawo).[299]
[299] Tanthauzo la ndimeyi nkuti amene akuyembekezera kuti akalandire malipiro abwino kwa Allah, apirire pa moyo wa pa dziko lapansi polimbika kumvera Allah mpaka adzakumane ndi Allah. Ndithudi, kukumana ndi Allah kuli pafupi.
Ndipo amene akuchita khama (polimbana ndi Akafiri, kapena pogonjetsa mtima wake kuti utsatire malamulo a Allah), ndithu zabwino za khamalo zili pa iye mwini. Ndithu Allah siwosaukira chilichonse kwa zolengedwa Zake.
Ndipo alipo ena mwa anthu omwe akunena: “Takhulupirira mwa Allah.” Koma akavutitsidwa chifukwa cha Allah, amawachita masautso a anthu monga chilango cha Allah, (sapirira; iwowa ndi achinyengo (achiphamaso). Ndipo chikadza chipulumutso chochokera kwa Mbuye wako amanena: “Ndithu ife tidali pamodzi ndi inu.” (Koma chikhalirecho akunena zonama). Kodi Allah sadziwa zomwe zili m’zifuwa za zolengedwa?[301]
[301] Alipo ena pakati pa anthu amene amangonena ndi malirime awo okha kuti: “Takhulupilira Allah.” Koma mmodzi wawo akavutitsidwa chifukwa cha chikhulupiliro chakecho, amatuluka m’chipembedzomo. Ndipo masautso a anthu amati ndicho chifukwa chomwe chidawachotsetsa m’chipembedzocho. Komatu chilango cha Allah nchosafanana ndi chilango cha anthu. Chofunika kwa iwo nkupilira ndi kulimba mtima; osatekeseka ndi chilichonse ngakhale choononga moyo wawo.
Ndipo ndithudi, adzasenza mitolo ya machimo ndi mitolo yina yamachimo (ya omwe adawasokeretsa) poiphatikiza ku mitolo yawo ya machimo. (Nawonso osokezedwa, adzasenzanso mitolo ya machimo chifukwa cha kutsatira kwawo anthu owasokezawo). Ndipo pa tsiku la Qiyâma (chimaliziro,) ndithu adzafunsidwa pa zimene amapeka.
Ndipo (akumbutse nkhani ya) Ibrahim pamene adawauza anthu ake: “Mpembedzeni Allah ndi kumuopa. Zimenezo nzabwino kwa inu ngati mukudziwa (kusiyana kwa chabwino ndi choipa).”
Choncho yankho la anthu ake silidali lina koma adangoti: “Mupheni kapena mtentheni ndi moto.” Koma Allah adampulumutsa ku moto. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo (zosonyeza mphamvu za Allah) kwa anthu okhulupirira.
Ndipo adanena: “Ndithu inu mwasankha mafano kukhala milungu kusiya Allah, ndipo mukukondana pakati panu m’moyo wa pa dziko; (pokhalirana pamodzi ndi kupitiriza kupembedza mafanowo mwachimvano). Koma tsiku la Qiyâma, mudzakanana wina ndi mnzake, komanso mudzatembelerana wina ndi mnzake, malo anu adzakhala ku Moto, ndipo simudzapeza okupulumutsani.”
Ndipo tidampatsa (Mneneri Ibrahim) Ishâq ndi Ya’qub, ndipo tidaika uneneri ndi buku pa mbumba yake, ndipo tidampatsa malipiro ake pa dziko lapansi; ndithu iye pa tsiku la chimaliziro adzakhala mwa anthu abwino.[303]
[303] Ibrahim pamene adasamuka ku Iraqi kupita ku Palesitina ndi cholinga chokafalitsa chipembedzo cha Allah kumeneko, Allah adamdalitsa ndi mwana wotchedwa Isihaka ndi mdzukulu wake. Ndipo adasankha mbumba yake kukhala mbumba yotulukamo aneneri ndi atumiki. Ndipo mabuku a kumwamba ankavumbulutsidwa kwa aneneri ochokera m’mbumba yake. Allah adamuchitira izi chifukwa cha kugonjera malamulo Ake kwathunthu.
“Kodi inu mukuchita amuna anzanu ukwati ndi kutseka njira (pakuchita chifwamba) ndi kuchita zoipa m’mabwalo anu osonkhanirana?” Koma yankho la anthu ake silidali lina koma kunena kuti: “Tidzere ndi chilango cha Allah cho ngati uli mmodzi wa owona.”
(Mneneri Ibrahim) adati: “Koma mmenemo muli Luti.” Iwo adati: “Ife ndife odziwa kwambiri za omwe ali m’menemo; ndithu timpulumutsa iye ndi banja lake kupatula mkazi wake; iye ndi mmodzi wa otsalira (woonongeka).”
Ndipo pamene atumiki athu adamdzera Luti, adawadandaulira ndi kuwadera nkhawa; (ndipo iwo) adati: “Usaope ndipo usadandaule. Ndithu ife tikupulumutsa ndi banja lako kupatula mkazi wako; iye ndi mmodzi wa otsalira (woonongeka).”
Momwemonso Kaaruni, Farawo ndi Hamana (adaonongedwa). Ndithu adawadzera Mûsa ndi zozizwitsa (zooneka), koma adadzikweza pa dziko. Komatu sadathe kumpambana (Allah pomulepheretsa kuwalanga).
Choncho aliyense wa iwo tidamlanga ndi machimo ake. Ena a iwo tidawatumizira chimphepo chamiyala; ena a iwo udawaononga mkuwe; ena a iwo tidawadidimiza m’nthaka, ndipo ena a iwo tidawamiza (m’madzi). Si Allah amene adawachitira zoipa, koma adadzichitira okha zoipa.
Fanizo la amene adzipangira milungu yabodza kusiya Allah, lili ngati fanizo la kangaude (yemwe) wadzipangira nyumba (kuti imsunge, pomwe nyumbayo siingathe kumsunga m’nyengo yozizira kapena yotentha), ndithu nyumba yomwe ili yofooka kwambiri ndi nyumba ya kangaude, akadakhala akudziwa.[304]
[304] M’ndime iyi Allah akufanizira munthu wopembedza mafano ndicholinga choti mafanowo adzimthangata pomudzetsera zabwino ndi kumchotsera zoipa, kuti ali ngati kangaude yemwe wamanga nyumba ndi cholinga choti imteteze ku chisanu ndi kutentha pomwe nyumbayo njofooka yomwe siingathe kumteteza ku chisanu kapena kudzuwa. Izi zili chimodzimodzi ndi wopembedza mafano. Mafanowo sangamudzetsere zabwino kapena kumchotsera zoipa.
۞ Ndipo musatsutsane ndi anthu a buku koma kutsutsana kwabwino kupatula amene achita zoipa mwa iwo. Ndipo nenani: “Takhulupirira zomwe zavumbulutsidwa kwa ife ndi zomwe zavumbulutsidwa kwa inu, ndipo Mulungu wathu ndi Mulungu wanu ndi Mmodzi; ndipo ife ndife ogonjera Iye.”
Ndipo umo ndimomwe takuvumbulutsira buku (ili la Qur’an). Choncho amene tidawapatsa buku, (ili lisadadze, monga Taurat ndi Injili), akulikhulupirira; akulikhulupiriranso ena mwa awa (Arabu omwe sitidawapatse buku). Ndipo sangawakane ma Ayah Athu kupatula osakhulupirira.
Ndipo iwe sumawerenga buku lililonse, ili lisanadze; ndipo sudalilembe ndi dzanja lako lakumanja. Zikadatero ndiye kuti anthu achabe akadakaikira.[305]
[305] Ukadakhala kuti umawerenga ndi kulemba pamenepo pakadakhala poyenera kwa osakhulupilira kukaikira Qur’an. Ndime iyi ikufotokoza momveka kuti Mtumiki adali wosadziwa kulemba ndi kuwerenga koma adamdzetsera buku ili lomwe m’kati mwake muli nkhaninso za anthu akale ndi zinthu zina zobisika. Choncho umenewu ndi umboni waukulu wovomereza kuti iye ndi Mtumikidi wa Allah.
Ndipo akunena: “Kodi bwanji sizinatsitsidwe kwa iye zozizwitsa kuchokera kwa Mbuye wake?” Nena: “Zozizwitsa zili kwa Allah; ndipo ine ndine mchenjezi woonekera, (ndilibe mphamvu zokudzetserani zozizwitsa koma pokhapo Allah atafuna).”
Nena: “Allah akukwana kukhala mboni pakati panga ndi inu; akudziwa za kumwamba ndi zapansi ndipo amene akukhulupirira zachabe ndi kukana Allah, iwowo ndiwo otayika.”
Ndipo moyo uwu wa pa dziko lapansi suli kanthu, koma chibwana ndi masewera. Ndipo ndithu nyumba ya tsiku la chimaliziro, ndiwo moyo weniweni, akadakhala akudziwa.
Ndipo akakwera m’chombo (ndi kukumana ndi zoopsa), amampempha Allah modzipereka ndikumuyeretsera pempho. Koma akawapulumutsa ndi kuwafikitsa ku ntunda, iwo amayambanso kumuphatikiza ndi mafano.
Kodi wachinyengo wamkulu ndani woposa amene akupekera bodza Allah, kapena kutsutsa choona chikamdzera? Kodi si mu Jahannam momwe mudzakhala malo a osakhulupirira?
Ndipo amene akulimbikira m’njira yathu, (polimbana ndi satana, ndi mzimu woipa ndi zilakolako zoipa zam’thupi, ndi cholinga chofuna kukondweretsa Allah) ndithu tiwaongolera ku njira Zathu. Ndipo ndithu Allah ali pamodzi ndi ochita zabwino.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
搜索结果:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".