Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 杜哈尼   段:

Ad-Dukhân

حمٓ
Hâ-Mîm.
阿拉伯语经注:
وَٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ
Ndikulumbilira buku lofotokoza momveka.
阿拉伯语经注:
إِنَّآ أَنزَلۡنَٰهُ فِي لَيۡلَةٖ مُّبَٰرَكَةٍۚ إِنَّا كُنَّا مُنذِرِينَ
Ndithu tidaivumbulutsa (Qur’an) mu usiku wodala. Ife ndithu Ndiachenjezi.
阿拉伯语经注:
فِيهَا يُفۡرَقُ كُلُّ أَمۡرٍ حَكِيمٍ
Mu (usiku) umenewu chinthu chilichonse chanzeru chimaweruzidwa ndi kulongosoledwa.
阿拉伯语经注:
أَمۡرٗا مِّنۡ عِندِنَآۚ إِنَّا كُنَّا مُرۡسِلِينَ
Mwa chilamulo chochokera kwa Ife. Ndithu Ife ndife otumiza atumiki (kuti achenjeze anthu).
阿拉伯语经注:
رَحۡمَةٗ مِّن رَّبِّكَۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
(Chifukwa cha) chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndithu Iye Ngwakumva zonse, Wodziwa kwabasi.
阿拉伯语经注:
رَبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَآۖ إِن كُنتُم مُّوقِنِينَ
Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati muli otsimikiza.
阿拉伯语经注:
لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ يُحۡيِۦ وَيُمِيتُۖ رَبُّكُمۡ وَرَبُّ ءَابَآئِكُمُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Palibe wopembedzedwa moona koma Iye basi. Amapereka moyo ndikupereka imfa, Mbuye wanu ndi Mbuye wa makolo anu oyamba.
阿拉伯语经注:
بَلۡ هُمۡ فِي شَكّٖ يَلۡعَبُونَ
Koma iwo (okanira) ali mchikaiko akungosewera, (potsatira zilakolako zawo zoipa).
阿拉伯语经注:
فَٱرۡتَقِبۡ يَوۡمَ تَأۡتِي ٱلسَّمَآءُ بِدُخَانٖ مُّبِينٖ
Basi, yembekezera tsiku limene thambo lidzadze ndi utsi woonekera (konsekonse).
阿拉伯语经注:
يَغۡشَى ٱلنَّاسَۖ هَٰذَا عَذَابٌ أَلِيمٞ
Udzawaphimba anthu onse (ndipo adzakhala akunena:) “Ichi ndi chilango chowawa.
阿拉伯语经注:
رَّبَّنَا ٱكۡشِفۡ عَنَّا ٱلۡعَذَابَ إِنَّا مُؤۡمِنُونَ
E Mbuye wathu! Tichotsereni chilangochi, ndithu ife tikhulupirira.”
阿拉伯语经注:
أَنَّىٰ لَهُمُ ٱلذِّكۡرَىٰ وَقَدۡ جَآءَهُمۡ رَسُولٞ مُّبِينٞ
(Kodi lero) kukumbukira kuwapindulira chiyani iwo? Chikhalirecho mtumiki wolongosola chilichonse adawadzera.
阿拉伯语经注:
ثُمَّ تَوَلَّوۡاْ عَنۡهُ وَقَالُواْ مُعَلَّمٞ مَّجۡنُونٌ
Koma sadamlabadire uku akumnena kuti: “Waphunzitsidwa (ndi anthu), ndiponso wopenga.”
阿拉伯语经注:
إِنَّا كَاشِفُواْ ٱلۡعَذَابِ قَلِيلًاۚ إِنَّكُمۡ عَآئِدُونَ
Ndithu Ife tichotsa chilangocho pang’ono (koma) inu mubwerezanso (machimo anu).
阿拉伯语经注:
يَوۡمَ نَبۡطِشُ ٱلۡبَطۡشَةَ ٱلۡكُبۡرَىٰٓ إِنَّا مُنتَقِمُونَ
(Kumbuka, iwe Mtumiki), tsiku limene tidzawalanga chilango chachikulu; ndithu Ife ndife olanga.
阿拉伯语经注:
۞ وَلَقَدۡ فَتَنَّا قَبۡلَهُمۡ قَوۡمَ فِرۡعَوۡنَ وَجَآءَهُمۡ رَسُولٞ كَرِيمٌ
Ndipo ndithu iwo asadadze, tidawayesa anthu a Farawo. Ndiponso adawadzera mtumiki wolemekezeka,
阿拉伯语经注:
أَنۡ أَدُّوٓاْ إِلَيَّ عِبَادَ ٱللَّهِۖ إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٞ
Kuti: “Ndipatseni akapolo a Allah. Ndithu ine kwa inu ndi Mtumiki wokhulupirika.”
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 杜哈尼
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭