Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 杜哈尼   段:
إِنَّ يَوۡمَ ٱلۡفَصۡلِ مِيقَٰتُهُمۡ أَجۡمَعِينَ
Ndithu tsiku lachiweruziro ndiyo nthawi yawo onse (imene alonjezedwa).
阿拉伯语经注:
يَوۡمَ لَا يُغۡنِي مَوۡلًى عَن مَّوۡلٗى شَيۡـٔٗا وَلَا هُمۡ يُنصَرُونَ
Tsiku limene m’bale sadzathandiza m’bale wake pa chilichonse (ku chilango cha Allah), ngakhale iwo sadzapulumutsidwa.
阿拉伯语经注:
إِلَّا مَن رَّحِمَ ٱللَّهُۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Kupatula amene Allah adzawachitira chifundo. Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa, Ngwachisoni chosatha.
阿拉伯语经注:
إِنَّ شَجَرَتَ ٱلزَّقُّومِ
Ndithu mtengo wa Zakkumi.
阿拉伯语经注:
طَعَامُ ٱلۡأَثِيمِ
Ndi chakudya cha ochimwa.
阿拉伯语经注:
كَٱلۡمُهۡلِ يَغۡلِي فِي ٱلۡبُطُونِ
(Kutentha kwake) ngati mtovu wosungunulidwa, (wotentha kwambiri;) udzakhala ukuwira mmimba.
阿拉伯语经注:
كَغَلۡيِ ٱلۡحَمِيمِ
Monga kuwira kwa madzi otentha kwambiri.
阿拉伯语经注:
خُذُوهُ فَٱعۡتِلُوهُ إِلَىٰ سَوَآءِ ٱلۡجَحِيمِ
(Kudzanenedwa): “Mgwireni; mkokereni (ndi kumponya) pakatikati pa Jahena!”
阿拉伯语经注:
ثُمَّ صُبُّواْ فَوۡقَ رَأۡسِهِۦ مِنۡ عَذَابِ ٱلۡحَمِيمِ
“Kenako mthireni pamwamba pamutu wake chilango chamadzi otentha!”
阿拉伯语经注:
ذُقۡ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡكَرِيمُ
(Adzauzidwa mwachipongwe): “Lawa! Ndithu iwe ndiwe wamphamvu zambiri, wolemekezeka, (monga momwe udali kudzitamira muja).”
阿拉伯语经注:
إِنَّ هَٰذَا مَا كُنتُم بِهِۦ تَمۡتَرُونَ
“Ndithu izi ndi zimene mudali kuzikaikira zija!”
阿拉伯语经注:
إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي مَقَامٍ أَمِينٖ
Ndithu oopa Allah adzakhala pa malo a chitetezo.
阿拉伯语经注:
فِي جَنَّٰتٖ وَعُيُونٖ
Mminda ndi mu akasupe.
阿拉伯语经注:
يَلۡبَسُونَ مِن سُندُسٖ وَإِسۡتَبۡرَقٖ مُّتَقَٰبِلِينَ
Adzavala (nsalu) za silika wopyapyala ndi silika wokhuthala uku atayang’anizana (nkhope).
阿拉伯语经注:
كَذَٰلِكَ وَزَوَّجۡنَٰهُم بِحُورٍ عِينٖ
Umo ndi mmene zidzakhalire; ndipo tidzawakwatitsa ndi akazi okongola amaso aakulu.
阿拉伯语经注:
يَدۡعُونَ فِيهَا بِكُلِّ فَٰكِهَةٍ ءَامِنِينَ
Mmenemo adzakhala akuitanitsa mtundu uliwonse wa zipatso, mwamtendere;
阿拉伯语经注:
لَا يَذُوقُونَ فِيهَا ٱلۡمَوۡتَ إِلَّا ٱلۡمَوۡتَةَ ٱلۡأُولَىٰۖ وَوَقَىٰهُمۡ عَذَابَ ٱلۡجَحِيمِ
Sadzalawa imfa mmenemo, kupatula imfa yoyamba ija; ndipo adzawateteza kuchilango cha Jahena,
阿拉伯语经注:
فَضۡلٗا مِّن رَّبِّكَۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ
Chifundo chochokera kwa Mbuye wako! Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu!
阿拉伯语经注:
فَإِنَّمَا يَسَّرۡنَٰهُ بِلِسَانِكَ لَعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ
Ndithu taifewetsa (Qur’an) mchiyankhulo chako (cha Chiarabu) kuti akumbukire.
阿拉伯语经注:
فَٱرۡتَقِبۡ إِنَّهُم مُّرۡتَقِبُونَ
Choncho yembekeza; iwonso akuyembekezera, (kodi ndani chimtsikire chilango pakati panu).
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 杜哈尼
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭