Check out the new design

Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ. * - Tərcumənin mündəricatı


Mənaların tərcüməsi Surə: Ğafir   Ayə:
۞ وَيَٰقَوۡمِ مَا لِيٓ أَدۡعُوكُمۡ إِلَى ٱلنَّجَوٰةِ وَتَدۡعُونَنِيٓ إِلَى ٱلنَّارِ
“E inu anthu anga! Chifukwa ninji, ine ndikukuitanirani ku chipulumutso ndipo inu mukundiitanira ku Moto?”
Ərəbcə təfsirlər:
تَدۡعُونَنِي لِأَكۡفُرَ بِٱللَّهِ وَأُشۡرِكَ بِهِۦ مَا لَيۡسَ لِي بِهِۦ عِلۡمٞ وَأَنَا۠ أَدۡعُوكُمۡ إِلَى ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡغَفَّٰرِ
“Mukundiitanira kuti ndimkane Allah, ndi kuphatikiza ndi milungu yonama yomwe ine sindikuidziwa, pomwe ine ndikukuitanirani kwa Mwini mphamvu zoposa, Wokhululuka kwambiri?”
Ərəbcə təfsirlər:
لَا جَرَمَ أَنَّمَا تَدۡعُونَنِيٓ إِلَيۡهِ لَيۡسَ لَهُۥ دَعۡوَةٞ فِي ٱلدُّنۡيَا وَلَا فِي ٱلۡأٓخِرَةِ وَأَنَّ مَرَدَّنَآ إِلَى ٱللَّهِ وَأَنَّ ٱلۡمُسۡرِفِينَ هُمۡ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِ
“Palibe chikaiko, ndithu zomwe mukundiitanirazo (kuti ndizipembedze) zilibe (kuyankha) pempho lililonse pano pa dziko lapansi ngakhale tsiku lachimaliziro. Ndipo kobwerera kwathu nkwa Allah basi. Ndipo, wopyola malire (a Allah) iwowo ndiwo anthu a ku Moto.”
Ərəbcə təfsirlər:
فَسَتَذۡكُرُونَ مَآ أَقُولُ لَكُمۡۚ وَأُفَوِّضُ أَمۡرِيٓ إِلَى ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ بَصِيرُۢ بِٱلۡعِبَادِ
“Choncho posachedwa, mudzakumbukira zimene ndikukuuzanizi. Ndipo ine ndikutula zinthu zanga kwa Allah, ndithu Allah akuona za anthu Ake.”
Ərəbcə təfsirlər:
فَوَقَىٰهُ ٱللَّهُ سَيِّـَٔاتِ مَا مَكَرُواْۖ وَحَاقَ بِـَٔالِ فِرۡعَوۡنَ سُوٓءُ ٱلۡعَذَابِ
Choncho Allah adam’teteza ku zoipa zomwe adam’tchera. Ndipo chilango choipa chidawazungulira anthu a Farawo (pamodzi ndi iye mwini.)
Ərəbcə təfsirlər:
ٱلنَّارُ يُعۡرَضُونَ عَلَيۡهَا غُدُوّٗا وَعَشِيّٗاۚ وَيَوۡمَ تَقُومُ ٱلسَّاعَةُ أَدۡخِلُوٓاْ ءَالَ فِرۡعَوۡنَ أَشَدَّ ٱلۡعَذَابِ
Zilango za kumoto zikusonyezedwa kwa iwo mmawa ndi madzulo. Ndipo tsiku lomwe Qiyâma idzafika (kudzanenedwa): “Alowetseni anthu a Farawo ku chilango cha ukali kwambiri (choposa chomwe adalandira mmanda mwawo).”
Ərəbcə təfsirlər:
وَإِذۡ يَتَحَآجُّونَ فِي ٱلنَّارِ فَيَقُولُ ٱلضُّعَفَٰٓؤُاْ لِلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُوٓاْ إِنَّا كُنَّا لَكُمۡ تَبَعٗا فَهَلۡ أَنتُم مُّغۡنُونَ عَنَّا نَصِيبٗا مِّنَ ٱلنَّارِ
Ndipo (akumbutse) pamene azidzatsutsana m’Moto! Pamene ofooka (amene amatsatira) adzanena kwa omwe adali kudzikweza: “Ndithu ife tidali otsatira anu; kodi simungathe kutichotsera gawo lina la chilango cha Moto?”
Ərəbcə təfsirlər:
قَالَ ٱلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُوٓاْ إِنَّا كُلّٞ فِيهَآ إِنَّ ٱللَّهَ قَدۡ حَكَمَ بَيۡنَ ٱلۡعِبَادِ
Awo amene adadzikweza adzati: “Ndithu ife tonse tili mommuno. Ndithu Allah waweruza kale pakati pa akapolo (Ake). (Choncho palibe chilichonse chimene tingaphulepo).”
Ərəbcə təfsirlər:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ فِي ٱلنَّارِ لِخَزَنَةِ جَهَنَّمَ ٱدۡعُواْ رَبَّكُمۡ يُخَفِّفۡ عَنَّا يَوۡمٗا مِّنَ ٱلۡعَذَابِ
Ndipo a ku Moto adzayankhula kwa (angelo) olondera Jahannam: “Mpempheni Mbuye wanu, atipeputsire chilangochi tsiku limodzi.”
Ərəbcə təfsirlər:
 
Mənaların tərcüməsi Surə: Ğafir
Surələrin mündəricatı Səhifənin rəqəmi
 
Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ. - Tərcumənin mündəricatı

Khalid İbrahim Beytala tərəfindən tərcümə.

Bağlamaq