Check out the new design

Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ. * - Tərcumənin mündəricatı


Mənaların tərcüməsi Surə: əl-Ənam   Ayə:
ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَلَمۡ يَلۡبِسُوٓاْ إِيمَٰنَهُم بِظُلۡمٍ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمُ ٱلۡأَمۡنُ وَهُم مُّهۡتَدُونَ
(Palibe chikaiko kwa) amene adakhulupirira ndipo sadasakanize chikhulupiliro chawo ndi kupondereza (shirk), iwowo ali nacho chitetezo. Ndiponso iwo ndi omwe ali oongoka.
Ərəbcə təfsirlər:
وَتِلۡكَ حُجَّتُنَآ ءَاتَيۡنَٰهَآ إِبۡرَٰهِيمَ عَلَىٰ قَوۡمِهِۦۚ نَرۡفَعُ دَرَجَٰتٖ مَّن نَّشَآءُۗ إِنَّ رَبَّكَ حَكِيمٌ عَلِيمٞ
Ndipo izi ndi zizindikiro Zathu (mitsutso Yathu), zomwe tidampatsa Ibrahim pa anthu ake. Timamtukulira ulemelero amene tamfuna. Ndithu Mbuye wako Ngwanzeru zakuya, Ngodziwa kwambiri.
Ərəbcə təfsirlər:
وَوَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَۚ كُلًّا هَدَيۡنَاۚ وَنُوحًا هَدَيۡنَا مِن قَبۡلُۖ وَمِن ذُرِّيَّتِهِۦ دَاوُۥدَ وَسُلَيۡمَٰنَ وَأَيُّوبَ وَيُوسُفَ وَمُوسَىٰ وَهَٰرُونَۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ
Ndipo tidampatsa (Ibrahim mwana wotchedwa) Ishaq ndi (mdzukulu wotchedwa) Ya’qub. Onse tidawaongola. Nayenso Nuh tidamuongola kale (asadadze Mneneri Ibrahim). Ndipo kuchokera m’mbumba yake (Nuh, tidamuongola) Daud, Sulaiman, Ayubu, Yûsuf, Mûsa, ndi Harun. Ndipo umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino.
Ərəbcə təfsirlər:
وَزَكَرِيَّا وَيَحۡيَىٰ وَعِيسَىٰ وَإِلۡيَاسَۖ كُلّٞ مِّنَ ٱلصَّٰلِحِينَ
Tidamutsogoleranso Zakariya, Yahya, Isa (Yesu) ndi Iliyasa. Onse adali mwa anthu abwino.
Ərəbcə təfsirlər:
وَإِسۡمَٰعِيلَ وَٱلۡيَسَعَ وَيُونُسَ وَلُوطٗاۚ وَكُلّٗا فَضَّلۡنَا عَلَى ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndi Ismail, Eliya, Yunus (Yona) ndi Luti (Loti). Onsewa tidawapatsa ubwino pa zolengedwa zonse.
Ərəbcə təfsirlər:
وَمِنۡ ءَابَآئِهِمۡ وَذُرِّيَّٰتِهِمۡ وَإِخۡوَٰنِهِمۡۖ وَٱجۡتَبَيۡنَٰهُمۡ وَهَدَيۡنَٰهُمۡ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
(Ndiponso tidawatsogolera) ena mwa atate awo, ana awo ndi abale awo. Ndipo tidawasankha ndi kuwaongolera ku njira yolunjika.
Ərəbcə təfsirlər:
ذَٰلِكَ هُدَى ٱللَّهِ يَهۡدِي بِهِۦ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦۚ وَلَوۡ أَشۡرَكُواْ لَحَبِطَ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Ichi ndi chiongoko cha Allah. Ndi icho akuongolera yemwe wamfuna mwa akapolo Ake. Akadakhala kuti (aneneriwo) adamphatikiza (Allah ndi zina) zikadawaonongekera zimene ankachita.
Ərəbcə təfsirlər:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡحُكۡمَ وَٱلنُّبُوَّةَۚ فَإِن يَكۡفُرۡ بِهَا هَٰٓؤُلَآءِ فَقَدۡ وَكَّلۡنَا بِهَا قَوۡمٗا لَّيۡسُواْ بِهَا بِكَٰفِرِينَ
Iwo ndi omwe tidawapatsa mabuku, chiweruzo, ndi uneneri. Choncho ngati awa (osakhulupirira) azikane izi, basi, tazipereka kale kwa anthu omwe sangazikane.
Ərəbcə təfsirlər:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ هَدَى ٱللَّهُۖ فَبِهُدَىٰهُمُ ٱقۡتَدِهۡۗ قُل لَّآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ أَجۡرًاۖ إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرَىٰ لِلۡعَٰلَمِينَ
Iwo ndi omwe Allah adawaongola choncho, tsatira chiongoko chawo. Nena: “Sindikukupemphani malipiro pa izi (zomwe ndikukuphunzitsanizi, koma ndikungotumikira Allah). Ichi sichina koma ndi ulaliki kwa zolengedwa (majini ndi anthu).”
Ərəbcə təfsirlər:
 
Mənaların tərcüməsi Surə: əl-Ənam
Surələrin mündəricatı Səhifənin rəqəmi
 
Qurani Kərimin mənaca tərcüməsi - Şişyo dilinə tərcümə - Xalid İbrahim Bəytələ. - Tərcumənin mündəricatı

Khalid İbrahim Beytala tərəfindən tərcümə.

Bağlamaq