Check out the new design

Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - Die Übersetzung in Chichewa - Khalid Ibrahim Bityala. * - Übersetzungen


Übersetzung der Bedeutungen Surah / Kapitel: Maryam   Vers:
يَٰيَحۡيَىٰ خُذِ ٱلۡكِتَٰبَ بِقُوَّةٖۖ وَءَاتَيۡنَٰهُ ٱلۡحُكۡمَ صَبِيّٗا
“E iwe Yahya! Gwira buku ili mwamphamvu (ndi mwachidwi).” Ndipo tidampatsa nzeru ali mwana.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَحَنَانٗا مِّن لَّدُنَّا وَزَكَوٰةٗۖ وَكَانَ تَقِيّٗا
Ndi chisoni chochokera kwa Ife ndi kumuyeretsa (mwanayo), ndipo adali woopa (Allah).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَبَرَّۢا بِوَٰلِدَيۡهِ وَلَمۡ يَكُن جَبَّارًا عَصِيّٗا
Komanso wochitira zabwino makolo ake ndipo sadali wodzitukumula (kwa anthu) kapena kunyoza (Allah).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَسَلَٰمٌ عَلَيۡهِ يَوۡمَ وُلِدَ وَيَوۡمَ يَمُوتُ وَيَوۡمَ يُبۡعَثُ حَيّٗا
Ndipo mtendere wa Allah udali pa iye kuyambira tsiku lomwe adabadwa ndi tsiku lomwe adamwalira, ndi tsiku limene adzaukitsidwa ku imfa kukhala wamoyo.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَرۡيَمَ إِذِ ٱنتَبَذَتۡ مِنۡ أَهۡلِهَا مَكَانٗا شَرۡقِيّٗا
Ndipo mtchule Mariya m’buku ili pamene adadzipatula ku anthu a kubanja lake (ndikunka) kumalo ambali ya kummawa.[265]
[265] M’sura iyi muli nkhani zododometsa. Yoyamba njakubadwa kwa Yahya (Yohane) yemwe adabadwa kuchokera kwa nkhalamba ziwiri zotheratu; pomwe mwamuna adali ndi zaka 120 ndipo mkazi adali ndi zaka 98. Choncho kubadwa kwa Yahya kudali kododometsa. Koma kubadwa kwa Isa (Yesu) ndikumene kudali kododometsa zedi poti iye anabadwa kwa namwali wosakwatiwa. Tero iye anamubereka popanda mwamuna. Zonsezi Allah adafuna kuwadziwitsa anthu ndi kuwatsimikizira kuti Iye ali ndi mphamvu zolengera munthu popanda mwamuna.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
فَٱتَّخَذَتۡ مِن دُونِهِمۡ حِجَابٗا فَأَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡهَا رُوحَنَا فَتَمَثَّلَ لَهَا بَشَرٗا سَوِيّٗا
Ndipo adadzitsekereza kwa iwo (kuti athe kutumikira Allah mokwanira), choncho tidatuma Mzimu Wathu (Mngelo Gabriel) kwa iye ndipo adadzifanizira kwa iye monga munthu weniweni.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قَالَتۡ إِنِّيٓ أَعُوذُ بِٱلرَّحۡمَٰنِ مِنكَ إِن كُنتَ تَقِيّٗا
(Mariya) adati: “Ndithu ndikudzichinjiriza ndi (Allah) Mwini chifundo chambiri, kwa iwe ngati umaopa (Allah).”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قَالَ إِنَّمَآ أَنَا۠ رَسُولُ رَبِّكِ لِأَهَبَ لَكِ غُلَٰمٗا زَكِيّٗا
(Mngelo) adati: “Ndithu ine ndine Mtumiki wa mbuye wako, (ndadza) kuti ndikupatse mwana woyera.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قَالَتۡ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَٰمٞ وَلَمۡ يَمۡسَسۡنِي بَشَرٞ وَلَمۡ أَكُ بَغِيّٗا
Adati: “Ndingakhale bwanji ndi mwana pomwe sadandikhudze mwamuna (aliyense), ndipo ine sindili (mkazi) wachiwerewere?”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قَالَ كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٞۖ وَلِنَجۡعَلَهُۥٓ ءَايَةٗ لِّلنَّاسِ وَرَحۡمَةٗ مِّنَّاۚ وَكَانَ أَمۡرٗا مَّقۡضِيّٗا
(Mngelo) adati: “Ndimomwemo.” Mbuye Wako akuti: “Zimenezi kwa Ine nzosavuta. Ndipo timchita kukhala chozizwitsa kwa anthu ndi chifundo chochokera kwa Ife. (Nchifukwa chake tachita izi;) ndipo ichi ndi chinthu chimene chidalamulidwa kale. (Chichitika monga momwe Allah adafunira).”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
۞ فَحَمَلَتۡهُ فَٱنتَبَذَتۡ بِهِۦ مَكَانٗا قَصِيّٗا
Choncho adatenga pakati pake, ndipo adachoka ndi pakatipo kunka kumalo akutali.[266]
[266] Izi zidachitika pamene Gabriele adauzira m’thumba la chovala cha Mariya. Ndipo mpweya udafika mpaka m’mimba mwake. Choncho atakhala ndi pakati anadzipatula kwa anthu kunka kutali ali ndi pakati pa mwana wakeyo kuti anthu angamdzudzule pokhala ndi mimba yosadziwika mwamuna wake.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
فَأَجَآءَهَا ٱلۡمَخَاضُ إِلَىٰ جِذۡعِ ٱلنَّخۡلَةِ قَالَتۡ يَٰلَيۡتَنِي مِتُّ قَبۡلَ هَٰذَا وَكُنتُ نَسۡيٗا مَّنسِيّٗا
Ndipo matenda auchembere (atakwana), adampititsa ku thunthu la mtengo wa kanjedza (wouma kuti awutsamire pomubala mwanayo) adati: “Kalanga ine! Ndiponi ndikadafa izi zisanachitike ndikadakhala nditaiwalidwa ndithu.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
فَنَادَىٰهَا مِن تَحۡتِهَآ أَلَّا تَحۡزَنِي قَدۡ جَعَلَ رَبُّكِ تَحۡتَكِ سَرِيّٗا
Kenaka (Mngelo) adamuitana kuchokera chapansi pake (kumuuza kuti): “Usadandaule. Ndithu Mbuye wako wakupangira kamtsinje pansi pako.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَهُزِّيٓ إِلَيۡكِ بِجِذۡعِ ٱلنَّخۡلَةِ تُسَٰقِطۡ عَلَيۡكِ رُطَبٗا جَنِيّٗا
Ndipo ligwedezere kumbali yako thunthu la mtengo wakanjedza (woumawo), zipatso zabwino zakupsa zikugwera.”[267]
[267] Omasulira adati: Adamulamula kuti agwedeze thunthu lamtengo wouma kuti aone chizizwa chachiwiri mtengo wouma pokhala wauwisi ndikubereka zipatso nthawi yomweyo zakupsa. Adamuonetsanso kasupe wamadzi okoma yemwe anafwamphuka uku iye akuona. Ndipo iye adali kudya zipatsozo nkumamwera madziwo. Uku kudali kumulimbikitsa mtima kuti asade nkhawa pokhala ndi mwana wopanda tate wake koma zonsezi wazichita ndi Allah.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
 
Übersetzung der Bedeutungen Surah / Kapitel: Maryam
Suren/ Kapiteln Liste Nummer der Seite
 
Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - Die Übersetzung in Chichewa - Khalid Ibrahim Bityala. - Übersetzungen

Übersetzung von Khalid Ibrahim Bitala.

Schließen