Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - الترجمة الشيشيوا * - Übersetzungen


Übersetzung der Bedeutungen Surah / Kapitel: Az-Zumar   Vers:

Az-Zumar

تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ مِنَ ٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَكِيمِ
Kuvumbulutsidwa kwa Buku ili kwachokera kwa Allah, Mwini mphamvu zoposa; Mwini nzeru zakuya.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
إِنَّآ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ بِٱلۡحَقِّ فَٱعۡبُدِ ٱللَّهَ مُخۡلِصٗا لَّهُ ٱلدِّينَ
Ndithu Ife takuvumbulutsira iwe buku ili mwamtheradi; choncho mpembedze Allah momyeretsera mapemphero Iye yekha.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَلَا لِلَّهِ ٱلدِّينُ ٱلۡخَالِصُۚ وَٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَ مَا نَعۡبُدُهُمۡ إِلَّا لِيُقَرِّبُونَآ إِلَى ٱللَّهِ زُلۡفَىٰٓ إِنَّ ٱللَّهَ يَحۡكُمُ بَيۡنَهُمۡ فِي مَا هُمۡ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَۗ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي مَنۡ هُوَ كَٰذِبٞ كَفَّارٞ
Dziwani kuti Allah Ngolandira mapemphero oyera, (opanda kuphatikizidwa ndi zina). Koma amene adzipangira athandizi kusiya Allah, (akumanena kuti): “Ife sitikuwapembedza awa, koma tikutero ndi cholinga choti atifikitse pafupi ndi Allah.” Ndithu Allah, adzaweruza pakati pawo (pakati pa okhulupirira Allah, ndi okana) pa zimene akusiyana. Ndithu Allah saongola amene ali wabodza; wokanira zedi (Allah).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
لَّوۡ أَرَادَ ٱللَّهُ أَن يَتَّخِذَ وَلَدٗا لَّٱصۡطَفَىٰ مِمَّا يَخۡلُقُ مَا يَشَآءُۚ سُبۡحَٰنَهُۥۖ هُوَ ٱللَّهُ ٱلۡوَٰحِدُ ٱلۡقَهَّارُ
Allah akadafuna kupeza mwana, akadasankha yemwe akum’funa mzomwe adalenga. Wapatukana ndi zimenezo! Iye ndi Allah Mmodzi; Wogonjetsa; (Wochita zimene wafuna).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّۖ يُكَوِّرُ ٱلَّيۡلَ عَلَى ٱلنَّهَارِ وَيُكَوِّرُ ٱلنَّهَارَ عَلَى ٱلَّيۡلِۖ وَسَخَّرَ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَۖ كُلّٞ يَجۡرِي لِأَجَلٖ مُّسَمًّىۗ أَلَا هُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡغَفَّٰرُ
Adalenga thambo ndi nthaka mwamtheradi. Amakulunga usiku mu usana; ndipo amakulunga usana mu usiku. Ndipo dzuwa ndi mwezi wazichita kuti zitumikire monga momwe afunira. Zonsezi zikuyenda kufikira pa nthawi yake imene yaikidwa. Dziwani kuti Iye (Allah) Ngwamphamvu zoposa; Ngokhululuka kwambiri.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
خَلَقَكُم مِّن نَّفۡسٖ وَٰحِدَةٖ ثُمَّ جَعَلَ مِنۡهَا زَوۡجَهَا وَأَنزَلَ لَكُم مِّنَ ٱلۡأَنۡعَٰمِ ثَمَٰنِيَةَ أَزۡوَٰجٖۚ يَخۡلُقُكُمۡ فِي بُطُونِ أُمَّهَٰتِكُمۡ خَلۡقٗا مِّنۢ بَعۡدِ خَلۡقٖ فِي ظُلُمَٰتٖ ثَلَٰثٖۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡ لَهُ ٱلۡمُلۡكُۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ فَأَنَّىٰ تُصۡرَفُونَ
Adakulengani kuchokera mu mzimu umodzi (womwe ndi Adam; tate wa anthu). Ndipo kenako adalenga kuchokera mu mzimu umenewo mnzake, (mkazi wake, Hawa); ndipo adakutsitsirani mitundu isanu ndi itatu ya nyama ziwiriziwiri (zomwe ndi: Ngamira yaimuna ndi yaikazi, ng’ombe yaimuna ndi yaikazi, mbuzi yaimuna ndi yaikazi ndi nkhosa yaimuna ndi yaikazi. Zonse pamodzi, zisanu ndi zitatu, zomwe mumathandizidwa nazo kwambiri). Amakuumbani m’mimba mwa mayi anu mkaumbidwe kosiyanasiyana, mu mdima utatu; (mu mdima wa mimba, chiberekero ndi mdima wa nembanemba). Ameneyo (adakuchitirani zonsezi), ndi Allah, Mleri wanu; ufumu ngwa Iye. Palibe wopembedzedwa mwa choona, koma Iye. Kodi nanga mukutembunuzidwa bwanji (kusiya Allah?)
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
إِن تَكۡفُرُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَنِيٌّ عَنكُمۡۖ وَلَا يَرۡضَىٰ لِعِبَادِهِ ٱلۡكُفۡرَۖ وَإِن تَشۡكُرُواْ يَرۡضَهُ لَكُمۡۗ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٞ وِزۡرَ أُخۡرَىٰۚ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُم مَّرۡجِعُكُمۡ فَيُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَۚ إِنَّهُۥ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ
Ngati mukana ndithu Allah Ngodzikwaniritsa sasaukira kwa inu (chikhulupiliro chanu ndi kuthokoza kwanu); koma sakonda kukanira kwa anthu Ake. Ngati mumthokoza (pa mtendere Wake umene uli pa inu) akuyanja kuthokoza kwanuko. Ndipo mzimu wochimwa sungasenze machimo a mzimu wina. Kenako kobwerera kwanu nkwa Mbuye wanu, ndipo adzakuuzani zimene mudali kuchita. Ndithu Iye Ngodziwa (zinsinsi) za m’mitima.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
۞ وَإِذَا مَسَّ ٱلۡإِنسَٰنَ ضُرّٞ دَعَا رَبَّهُۥ مُنِيبًا إِلَيۡهِ ثُمَّ إِذَا خَوَّلَهُۥ نِعۡمَةٗ مِّنۡهُ نَسِيَ مَا كَانَ يَدۡعُوٓاْ إِلَيۡهِ مِن قَبۡلُ وَجَعَلَ لِلَّهِ أَندَادٗا لِّيُضِلَّ عَن سَبِيلِهِۦۚ قُلۡ تَمَتَّعۡ بِكُفۡرِكَ قَلِيلًا إِنَّكَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلنَّارِ
Ndipo masautso akampeza munthu, amapempha Mbuye wake ndi kutembenukira kwa Iye (pomwe chikhalirecho adali kumnyoza). Kenako (Mbuye wake) akampatsa mtendere wochokera kwa Iye (waukulu), amaiwala (masautso aja) omwe adali kumpempha Allah kuti amchotsere asadampatse mtenderewo, ndipo kenako ndikumpangira Allah milungu inzake kuti asokeretse ku njira Yake. Nena (iwe Mtumiki kwa yemwe ali ndi chikhalidwe chotere): “Sangalala ndi kukanira kwako (mtendere wa Allah) kwa nthawi yochepa. Ndithu iwe ndi mmodzi wa anthu aku Moto.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَمَّنۡ هُوَ قَٰنِتٌ ءَانَآءَ ٱلَّيۡلِ سَاجِدٗا وَقَآئِمٗا يَحۡذَرُ ٱلۡأٓخِرَةَ وَيَرۡجُواْ رَحۡمَةَ رَبِّهِۦۗ قُلۡ هَلۡ يَسۡتَوِي ٱلَّذِينَ يَعۡلَمُونَ وَٱلَّذِينَ لَا يَعۡلَمُونَۗ إِنَّمَا يَتَذَكَّرُ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ
Kodi yemwe akudzichepetsa (kwa Allah ndi kumpembedza) pakati pa usiku uku akugwetsa nkhope pansi ndi kuimilira, kuopa tsiku la chimaliziro ndi kuyembekezera chifundo cha Mbuye wake, (kodi angafanane ndi yemwe amapempha Allah akakhala pa mavuto pokha, akakhala pa mtendere ndikumuiwala?) Nena (kwa iwo, iwe Mtumiki {s.a.w}): “Kodi amene akudziwa ndi amene sakudziwa, ngofanana?” Ndithu ndi eni nzeru amene amalingalira.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قُلۡ يَٰعِبَادِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱتَّقُواْ رَبَّكُمۡۚ لِلَّذِينَ أَحۡسَنُواْ فِي هَٰذِهِ ٱلدُّنۡيَا حَسَنَةٞۗ وَأَرۡضُ ٱللَّهِ وَٰسِعَةٌۗ إِنَّمَا يُوَفَّى ٱلصَّٰبِرُونَ أَجۡرَهُم بِغَيۡرِ حِسَابٖ
Nena (kwa iwo mau Anga akuti): “E inu akapolo Anga amene mwakhulupirira! Muopeni Mbuye wanu. Ndithu amene achita zabwino zotsatira zake nzabwino padziko lapansi, ndipo dziko la Allah ndilophanuka. (Pirirani chifukwa chosiya midzi yanu ndi abale). Ndithu opirira adzalipidwa malipiro awo mokwana mopanda mulingo.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قُلۡ إِنِّيٓ أُمِرۡتُ أَنۡ أَعۡبُدَ ٱللَّهَ مُخۡلِصٗا لَّهُ ٱلدِّينَ
Nena: “Ine ndalamulidwa kuti ndimpembedze Allah momuyeretsera mapemphero Ake (posamphatikiza ndi aliyense pa mapemphero, kapena kupemphera mwa chiphamaso).”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَأُمِرۡتُ لِأَنۡ أَكُونَ أَوَّلَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ
“Ndalamulidwanso kuti ndikhale woyamba mwa ogonjera (malamulo Ake).”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قُلۡ إِنِّيٓ أَخَافُ إِنۡ عَصَيۡتُ رَبِّي عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٖ
Nena: “Ine ndikuopa chilango cha tsiku lalikulu, (loopsa), ngati ndinyoza Mbuye wanga.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قُلِ ٱللَّهَ أَعۡبُدُ مُخۡلِصٗا لَّهُۥ دِينِي
Nena (kwa iwo, iwe Mneneri {s.a.w}): “Ndi Allah Yekha ndikumpembedza pomuyeretsera Iye mapemphero anga.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
فَٱعۡبُدُواْ مَا شِئۡتُم مِّن دُونِهِۦۗ قُلۡ إِنَّ ٱلۡخَٰسِرِينَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ وَأَهۡلِيهِمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۗ أَلَا ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡخُسۡرَانُ ٱلۡمُبِينُ
“Choncho pembedzani zimene mwafuna, kumsiya Iye.” Nena (kwa iwo): “Ndithu otaika ndi kuonongeka kwakukulu, ndi amene adzitaya okha, (adziluzitsa okha), ndi maanja awo, patsiku la Qiyâma. Dziwa, ndithu kumeneko ndiko kuluza koonekera.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
لَهُم مِّن فَوۡقِهِمۡ ظُلَلٞ مِّنَ ٱلنَّارِ وَمِن تَحۡتِهِمۡ ظُلَلٞۚ ذَٰلِكَ يُخَوِّفُ ٱللَّهُ بِهِۦ عِبَادَهُۥۚ يَٰعِبَادِ فَٱتَّقُونِ
Pa iwo padzakhala misanjikosanjiko ya moto ndiponso pansi pawo. Ndi (chilango) chimenechi, Allah akuwaopseza nacho akapolo Ake. “E inu akapolo Anga! Ndiopeni!”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَٱلَّذِينَ ٱجۡتَنَبُواْ ٱلطَّٰغُوتَ أَن يَعۡبُدُوهَا وَأَنَابُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ لَهُمُ ٱلۡبُشۡرَىٰۚ فَبَشِّرۡ عِبَادِ
Ndipo amene apatukana nawo mafano ndi satana posiya kuzipembedza, ndikusiya kuziyandikira, ndipo mmalo mwake nkutembenukira kwa Allah (pa zochita zawo zonse), nkhani yabwino njawo (ponseponse). Auze nkhani yabwino akapolo Anga.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
ٱلَّذِينَ يَسۡتَمِعُونَ ٱلۡقَوۡلَ فَيَتَّبِعُونَ أَحۡسَنَهُۥٓۚ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ هَدَىٰهُمُ ٱللَّهُۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمۡ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ
Amene akumvetsera mawu ndi kutsatira amene ali abwino kwambiri. Iwowo ndi amene Allah wawaongola. Ndipo iwowo ndiwo eni nzeru.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَفَمَنۡ حَقَّ عَلَيۡهِ كَلِمَةُ ٱلۡعَذَابِ أَفَأَنتَ تُنقِذُ مَن فِي ٱلنَّارِ
Kodi yemwe chiweruzo cha chilango chatsimikizika pa iye, (mungamteteze)? Kodi iwe ungampulumutse yemwe ali m’Moto?
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
لَٰكِنِ ٱلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْ رَبَّهُمۡ لَهُمۡ غُرَفٞ مِّن فَوۡقِهَا غُرَفٞ مَّبۡنِيَّةٞ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۖ وَعۡدَ ٱللَّهِ لَا يُخۡلِفُ ٱللَّهُ ٱلۡمِيعَادَ
Koma amene aopa Mbuye wawo, iwo adzakhala nazo Nyumba zikuluzikulu zimene zamangidwa mosanjikizana, mitsinje ikuyenda pansi pake. Ili ndi lonjezo lochokera kwa Allah. Allah saphwanya lonjezo.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَسَلَكَهُۥ يَنَٰبِيعَ فِي ٱلۡأَرۡضِ ثُمَّ يُخۡرِجُ بِهِۦ زَرۡعٗا مُّخۡتَلِفًا أَلۡوَٰنُهُۥ ثُمَّ يَهِيجُ فَتَرَىٰهُ مُصۡفَرّٗا ثُمَّ يَجۡعَلُهُۥ حُطَٰمًاۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَذِكۡرَىٰ لِأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ
Kodi suona kuti Allah amatsitsa madzi kuchokera kumwamba, ndipo amawalowetsa mu akasupe mkati mwa nthaka, kenako amatulutsa ndi madziwo mbewu zosiyana mitundu: (chimanga, mpunga, tirigu, ndi zina zotere). Ndipo kenako zimauma (pambuyo pokhala zobiriwira); umaziona zili zachikasu. Kenako amazichita kukhala zidutswazidutswa? Ndithu muzimenezo muli chikumbutso kwa eni nzeru (zofufuzira zinthu).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَفَمَن شَرَحَ ٱللَّهُ صَدۡرَهُۥ لِلۡإِسۡلَٰمِ فَهُوَ عَلَىٰ نُورٖ مِّن رَّبِّهِۦۚ فَوَيۡلٞ لِّلۡقَٰسِيَةِ قُلُوبُهُم مِّن ذِكۡرِ ٱللَّهِۚ أُوْلَٰٓئِكَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٍ
Kodi amene Allah watsekula chifuwa chake povomereza Chisilamu, kotero kuti iye akuyenda mkuunika kwa Mbuye wake, (angafanane ndi yemwe akunyozera kupenyetsetsa zisonyezo za Allah?) Kuonongeka kwakukulu kuli pa ouma mitima yawo posakumbukira Allah (ndi kulabadira Qur’an). Iwo ali m’kusokera koonekera.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
ٱللَّهُ نَزَّلَ أَحۡسَنَ ٱلۡحَدِيثِ كِتَٰبٗا مُّتَشَٰبِهٗا مَّثَانِيَ تَقۡشَعِرُّ مِنۡهُ جُلُودُ ٱلَّذِينَ يَخۡشَوۡنَ رَبَّهُمۡ ثُمَّ تَلِينُ جُلُودُهُمۡ وَقُلُوبُهُمۡ إِلَىٰ ذِكۡرِ ٱللَّهِۚ ذَٰلِكَ هُدَى ٱللَّهِ يَهۡدِي بِهِۦ مَن يَشَآءُۚ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِنۡ هَادٍ
Allah wavumbulutsa nkhani yabwino zedi yomwe ndi buku logwirizana nkhani zake; (losasemphana). Lobwerezabwereza (malamulo ake). Makungu a omwe amaopa Mbuye wawo amanjenjemera ndi ilo. Kenako makungu awo ndi mitima yawo zimakhazikika pokumbukira Allah. Buku limeneli ndi chiongoko cha Allah; ndi ilo, akumuongola amene wamfuna. Ndipo amene Allah wamulekelera kuti asokere (chifukwa chonyozera kwake choona), sangakhale ndi womuongola (ndi ompulumutsa ku chionongeko).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَفَمَن يَتَّقِي بِوَجۡهِهِۦ سُوٓءَ ٱلۡعَذَابِ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ وَقِيلَ لِلظَّٰلِمِينَ ذُوقُواْ مَا كُنتُمۡ تَكۡسِبُونَ
Kodi yemwe adzakhala akudzitchinjiriza ndi nkhope yake (uku manja atanjatidwa) ku chilango choipa pa tsiku la Qiyâma, (angafanane ndi yemwe adzakhala mchisangalalo mminda ya mtendere?” Ndipo kudzanenedwa kwa oipa: “Lawani zoipa za zochita zanu.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ فَأَتَىٰهُمُ ٱلۡعَذَابُ مِنۡ حَيۡثُ لَا يَشۡعُرُونَ
Amene adalipo patsogolo pawo, adatsutsa. Ndipo chilango chidawadzera kuchokera komwe sadali kuyembekezera.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
فَأَذَاقَهُمُ ٱللَّهُ ٱلۡخِزۡيَ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَكۡبَرُۚ لَوۡ كَانُواْ يَعۡلَمُونَ
Choncho Allah adawalawitsa kunyozeka pa moyo wa pa dziko lapansi; koma ndithu chilango cha tsiku la chimaliziro nchachikulu zedi (kuposa chilango cha m’dziko lapansi) akadakhala akudziwa!
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَلَقَدۡ ضَرَبۡنَا لِلنَّاسِ فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ مِن كُلِّ مَثَلٖ لَّعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ
Ndithu m’buku ili la Qur’an taperekamo mafanizo osiyanasiyana kwa anthu kuti akumbukire.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قُرۡءَانًا عَرَبِيًّا غَيۡرَ ذِي عِوَجٖ لَّعَلَّهُمۡ يَتَّقُونَ
Qur’an ya Chiarabu yopanda zokhota, kuti iwo aope (Allah).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
ضَرَبَ ٱللَّهُ مَثَلٗا رَّجُلٗا فِيهِ شُرَكَآءُ مُتَشَٰكِسُونَ وَرَجُلٗا سَلَمٗا لِّرَجُلٍ هَلۡ يَسۡتَوِيَانِ مَثَلًاۚ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
Allah wapereka fanizo la munthu wotumikira mabwana awiri omwe ngokangana pa za iye, ndi munthu yemwe akutumikira bwana mmodzi. Kodi awiriwa ngofanana? Kuyamikidwa konse nkwa Allah! Koma ambiri a iwo sadziwa.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
إِنَّكَ مَيِّتٞ وَإِنَّهُم مَّيِّتُونَ
Ndithu iwe udzafa; naonso adzafa.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
ثُمَّ إِنَّكُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ عِندَ رَبِّكُمۡ تَخۡتَصِمُونَ
(Ndipo) kenako, inu patsiku la Qiyâma mudzakangana pamaso pa Mbuye wanu.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
۞ فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن كَذَبَ عَلَى ٱللَّهِ وَكَذَّبَ بِٱلصِّدۡقِ إِذۡ جَآءَهُۥٓۚ أَلَيۡسَ فِي جَهَنَّمَ مَثۡوٗى لِّلۡكَٰفِرِينَ
۞ Kodi ndiyani wachinyengo wamkulu woposa yemwe akumnamizira Allah zabodza, ndi kutsutsa choona chikamdzera? Kodi Jahannam simalo a okanira?
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَٱلَّذِي جَآءَ بِٱلصِّدۡقِ وَصَدَّقَ بِهِۦٓ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُتَّقُونَ
Ndipo amene wadza ndi choona, naachikhulupirira, iwowo ndiwo oopa Allah.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
لَهُم مَّا يَشَآءُونَ عِندَ رَبِّهِمۡۚ ذَٰلِكَ جَزَآءُ ٱلۡمُحۡسِنِينَ
Adzapeza zomwe adzakhumba kwa Mbuye wawo. Imeneyo ndiyo mphoto ya ochita zabwino.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
لِيُكَفِّرَ ٱللَّهُ عَنۡهُمۡ أَسۡوَأَ ٱلَّذِي عَمِلُواْ وَيَجۡزِيَهُمۡ أَجۡرَهُم بِأَحۡسَنِ ٱلَّذِي كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Kuti Allah awafafanizire zoipa za zochita zawo, ndi kuti awalipire malipiro awo chifukwa cha zabwino zomwe adali kuchita.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِكَافٍ عَبۡدَهُۥۖ وَيُخَوِّفُونَكَ بِٱلَّذِينَ مِن دُونِهِۦۚ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِنۡ هَادٖ
Kodi Allah sali Wokwanira kwa kapolo Wake? Koma akukuopseza ndi zina zosakhala Iye! Ndipo yemwe Allah wam’lekelera kuti asokere, ndithu alibe womuongola.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَمَن يَهۡدِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِن مُّضِلٍّۗ أَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِعَزِيزٖ ذِي ٱنتِقَامٖ
Ndipo amene Allah wamuongola, palibe amene angathe kumsokeretsa. Kodi Allah sali Mwini mphamvu zoposa; Wokhoza kubwezera chilango?
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۚ قُلۡ أَفَرَءَيۡتُم مَّا تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ إِنۡ أَرَادَنِيَ ٱللَّهُ بِضُرٍّ هَلۡ هُنَّ كَٰشِفَٰتُ ضُرِّهِۦٓ أَوۡ أَرَادَنِي بِرَحۡمَةٍ هَلۡ هُنَّ مُمۡسِكَٰتُ رَحۡمَتِهِۦۚ قُلۡ حَسۡبِيَ ٱللَّهُۖ عَلَيۡهِ يَتَوَكَّلُ ٱلۡمُتَوَكِّلُونَ
Ndipo ukawafunsa (kuti) ndani adalenga thambo ndi nthaka, ndithu anena (kuti ndi) “Allah.” Nena: “Kodi mukuona bwanji, amene mukuwapembedza kusiya Allah angandichotsere masautso ake ngati Allah atafuna kundipatsa masautso? Kapena Allah atafuna kundichitira chifundo, kodi iwo angatsekereze chifundo Chakecho?” Nena: “Allah akundikwanira! Kwa Iye, atsamire otsamira.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قُلۡ يَٰقَوۡمِ ٱعۡمَلُواْ عَلَىٰ مَكَانَتِكُمۡ إِنِّي عَٰمِلٞۖ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ
Nena: “E inu anthu anga! Chitani zochita zanu mmene mungathere. Nanenso ndichita (mmene ndingathere). Koma posachedwa mudziwa.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
مَن يَأۡتِيهِ عَذَابٞ يُخۡزِيهِ وَيَحِلُّ عَلَيۡهِ عَذَابٞ مُّقِيمٌ
Amene chim’dzere chilango chomuyalutsa, ndi kum’fikira iye chilango chamuyaya.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
إِنَّآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ لِلنَّاسِ بِٱلۡحَقِّۖ فَمَنِ ٱهۡتَدَىٰ فَلِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيۡهَاۖ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡهِم بِوَكِيلٍ
Ndithu ife takuvumbulutsira buku ili chifukwa cha anthu (onse) kuti Tiwafotokozere choona. Choncho amene waongoka, zabwino zake nza iye mwini. Koma amene wakhota, ndiye kuti akudzikhotetsa yekha. (Ndipo zoipa za kukhotako zidzakhala pa iye yekha). Ndipo iwe si muyang’anili wawo.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
ٱللَّهُ يَتَوَفَّى ٱلۡأَنفُسَ حِينَ مَوۡتِهَا وَٱلَّتِي لَمۡ تَمُتۡ فِي مَنَامِهَاۖ فَيُمۡسِكُ ٱلَّتِي قَضَىٰ عَلَيۡهَا ٱلۡمَوۡتَ وَيُرۡسِلُ ٱلۡأُخۡرَىٰٓ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمًّىۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَتَفَكَّرُونَ
Allah ndiye amatenga mizimu pa nthawi ya imfa yake ndipo amatenga mizimu yomwe siidafe panthawi yogona tulo. Ndipo amaigwira mizimu imene wailamula kufa, (osaibwezera ku matupi awo). Koma inayo amaitumiza (kumatupi awo, yomwe nthawi yake siidakwane) kuti ikwaniritse nthawi yake imene idaikidwa. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo kwa anthu olingalira.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَمِ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ شُفَعَآءَۚ قُلۡ أَوَلَوۡ كَانُواْ لَا يَمۡلِكُونَ شَيۡـٔٗا وَلَا يَعۡقِلُونَ
Kodi adzipangira awomboli kusiya Allah? Nena: “Ngakhale kuti (awombolio) alibe mphamvu ndi kuzindikira pa chilichonse?”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قُل لِّلَّهِ ٱلشَّفَٰعَةُ جَمِيعٗاۖ لَّهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ ثُمَّ إِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Nena: “Chiombolo chonse chili kwa Allah; ufumu wa kumwamba ndi pansi Ngwake; kenako kwa Iye m’dzabwezedwa.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَإِذَا ذُكِرَ ٱللَّهُ وَحۡدَهُ ٱشۡمَأَزَّتۡ قُلُوبُ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِۖ وَإِذَا ذُكِرَ ٱلَّذِينَ مِن دُونِهِۦٓ إِذَا هُمۡ يَسۡتَبۡشِرُونَ
Ndipo pamene Allah Yekha akutchulidwa, mitima ya amene sakhulupirira tsiku la chimaliziro imanyansidwa; koma akatchulidwa amene sali Iye, iwo amakondwa.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قُلِ ٱللَّهُمَّ فَاطِرَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ عَٰلِمَ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِ أَنتَ تَحۡكُمُ بَيۡنَ عِبَادِكَ فِي مَا كَانُواْ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ
Nena: “E Allah! Mlengi wa thambo ndi nthaka! Wodziwa zobisika ndi zooneka! Inu mudzaweruza pakati pa akapolo Anu pa zimene adali kusemphana.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَلَوۡ أَنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ مَا فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعٗا وَمِثۡلَهُۥ مَعَهُۥ لَٱفۡتَدَوۡاْ بِهِۦ مِن سُوٓءِ ٱلۡعَذَابِ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ وَبَدَا لَهُم مِّنَ ٱللَّهِ مَا لَمۡ يَكُونُواْ يَحۡتَسِبُونَ
Ndipo amene adzichitira zoipa, ngakhale kukadakhala kuti ali nazo zonse za mnthaka pamodzi ndi zina zonga izo, akadadziombola nazo ku chilango choipa cha tsiku la Qiyâma (koma sizikanatheka). Ndipo zidzawaonekera kuchokera kwa Allah, zomwe sadali kuziyembekezera.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَبَدَا لَهُمۡ سَيِّـَٔاتُ مَا كَسَبُواْ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Kukawaonekera kuipa kwa zimene adazichita, ndipo zikawazinga zimene adali kuzichitira chipongwe.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
فَإِذَا مَسَّ ٱلۡإِنسَٰنَ ضُرّٞ دَعَانَا ثُمَّ إِذَا خَوَّلۡنَٰهُ نِعۡمَةٗ مِّنَّا قَالَ إِنَّمَآ أُوتِيتُهُۥ عَلَىٰ عِلۡمِۭۚ بَلۡ هِيَ فِتۡنَةٞ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
Pamene munthu mavuto amkhudza, amatipempha (uku ali wodzichepetsa); koma tikampatsa mtendere wochokera kwa Ife, amanena kuti: “Ndapatsidwa mtendere uwu chifukwa chakudziwa kwanga (njira zoupezera).” (Sichoncho) koma mtendere umenewu ndi mayeso; koma ambiri a iwo sadziwa!
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قَدۡ قَالَهَا ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ فَمَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Ndithu adanenanso zonga zimenezi omwe adalipo patsogolo pawo, koma sizidawathandize zimene adali kuchita.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
فَأَصَابَهُمۡ سَيِّـَٔاتُ مَا كَسَبُواْۚ وَٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡ هَٰٓؤُلَآءِ سَيُصِيبُهُمۡ سَيِّـَٔاتُ مَا كَسَبُواْ وَمَا هُم بِمُعۡجِزِينَ
Choncho, zidawapeza zoipa za zomwe adazichita. Ndipo amene achita chinyengo mwa awa, posachedwa kuwapeza kuipa kwa zomwe achita, ndipo iwo sangamlempheretse (Allah).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَوَلَمۡ يَعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ وَيَقۡدِرُۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ
Kodi iwo sadziwa kuti Allah amamtambasulira zopatsa zake yemwe wamfuna, ndi kumchepetsera (amene wamfuna)? Ndithu m’zimenezi muli malingaliro kwa anthu okhulupirira.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
۞ قُلۡ يَٰعِبَادِيَ ٱلَّذِينَ أَسۡرَفُواْ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡ لَا تَقۡنَطُواْ مِن رَّحۡمَةِ ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ يَغۡفِرُ ٱلذُّنُوبَ جَمِيعًاۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ
Nena (kwa iwo mau anga akuti): “E inu akapolo anga! Amene mwadzichitira chinyengo, musataye mtima ndi chifundo cha Allah. Ndithu Allah amakhululuka machimo onse. Ndithu Iye Ngokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَأَنِيبُوٓاْ إِلَىٰ رَبِّكُمۡ وَأَسۡلِمُواْ لَهُۥ مِن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَكُمُ ٱلۡعَذَابُ ثُمَّ لَا تُنصَرُونَ
Ndipo tembenukirani kwa Mbuye wanu, ndipo m’gonjereni chilango chisadakudzereni. Ndipo zitatero, sim’dzapulumutsidwa.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَٱتَّبِعُوٓاْ أَحۡسَنَ مَآ أُنزِلَ إِلَيۡكُم مِّن رَّبِّكُم مِّن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَكُمُ ٱلۡعَذَابُ بَغۡتَةٗ وَأَنتُمۡ لَا تَشۡعُرُونَ
Ndipo tsatirani zabwino, zimene zavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Mbuye wanu chisadakufikeni chilango mwadzidzidzi pomwe inu simukudziwa!”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَن تَقُولَ نَفۡسٞ يَٰحَسۡرَتَىٰ عَلَىٰ مَا فَرَّطتُ فِي جَنۢبِ ٱللَّهِ وَإِن كُنتُ لَمِنَ ٱلسَّٰخِرِينَ
Kuti mzimu usadzanene: “Kalanga ine! Mzomwe sindidalabadire kumbali ya Allah; ndithu ndidali mmodzi wa ochitira chibwana (zinthu za chipembedzo).”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَوۡ تَقُولَ لَوۡ أَنَّ ٱللَّهَ هَدَىٰنِي لَكُنتُ مِنَ ٱلۡمُتَّقِينَ
Kapena ungadzanene: “Allah akadandiongola, ndithu ndikadakhala mwa oopa (Allah).”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
أَوۡ تَقُولَ حِينَ تَرَى ٱلۡعَذَابَ لَوۡ أَنَّ لِي كَرَّةٗ فَأَكُونَ مِنَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ
Kapena kunena utaona chilango: “Ndikadatha kubwerera (pa dziko lapansi), ndikadakhala mmodzi wa ochita zabwino.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
بَلَىٰ قَدۡ جَآءَتۡكَ ءَايَٰتِي فَكَذَّبۡتَ بِهَا وَٱسۡتَكۡبَرۡتَ وَكُنتَ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ
(Adzauzidwa: “Nchiyani iwe?) Ndithu zidakufika zisonyezo Zanga, ndipo udazitsutsa ndi kudzitukumula; ndipo udali mmodzi wa okanira.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ تَرَى ٱلَّذِينَ كَذَبُواْ عَلَى ٱللَّهِ وُجُوهُهُم مُّسۡوَدَّةٌۚ أَلَيۡسَ فِي جَهَنَّمَ مَثۡوٗى لِّلۡمُتَكَبِّرِينَ
Ndipo tsiku la Qiyâma udzawaona omwe adamnamizira Allah, nkhope zawo zili zakuda. Kodi Jahannam simalo a odzitukumula?
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَيُنَجِّي ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْ بِمَفَازَتِهِمۡ لَا يَمَسُّهُمُ ٱلسُّوٓءُ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ
Ndipo Allah adzawapulumutsa amene adamuopa, chifukwa cha kupambana kwawo. Zoipa sizikawakhudza, ndipo iwo sakadandaula.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
ٱللَّهُ خَٰلِقُ كُلِّ شَيۡءٖۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ وَكِيلٞ
Allah ndiye Mlengi wa chilichonse, ndipo Iye ndi Myang’aniri wa chilichonse.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
لَّهُۥ مَقَالِيدُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ
Makiyi a kumwamba ndi pansi ali kwa Iye. Ndipo amene akanira zisonyezo za Allah, iwo ndiwo oluza, (otaika).
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قُلۡ أَفَغَيۡرَ ٱللَّهِ تَأۡمُرُوٓنِّيٓ أَعۡبُدُ أَيُّهَا ٱلۡجَٰهِلُونَ
Nena: “Kodi mukundilamula kuti ndipembedze yemwe sali Allah, E inu mbuli?”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَلَقَدۡ أُوحِيَ إِلَيۡكَ وَإِلَى ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكَ لَئِنۡ أَشۡرَكۡتَ لَيَحۡبَطَنَّ عَمَلُكَ وَلَتَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ
Ndipo ndithu kwavumbulutsidwa kwa iwe, ndi kwa amene adalipo patsogolo pako (mawu awa:) “Ngati umphatikiza (Allah ndi milungu yabodza), ndithu ntchito zako zionongeka, ndipo ukhala mwa oluza (otaika).”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
بَلِ ٱللَّهَ فَٱعۡبُدۡ وَكُن مِّنَ ٱلشَّٰكِرِينَ
Koma pembedza Allah yekha, ndipo khala mwa othokoza.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَمَا قَدَرُواْ ٱللَّهَ حَقَّ قَدۡرِهِۦ وَٱلۡأَرۡضُ جَمِيعٗا قَبۡضَتُهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وَٱلسَّمَٰوَٰتُ مَطۡوِيَّٰتُۢ بِيَمِينِهِۦۚ سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ
Koma sadamlemekeze Allah, kulemekeza koyenerana Naye, pomwe pa tsiku la Qiyâma nthaka yonse (idzakhala) chofumbata Chake mmanja; ndipo thambo lidzakulungidwa ndi dzanja Lake lamanja. Walemekezeka Allah. Ndipo watukuka ku zimene akum’phatikiza nazozi.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَنُفِخَ فِي ٱلصُّورِ فَصَعِقَ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا مَن شَآءَ ٱللَّهُۖ ثُمَّ نُفِخَ فِيهِ أُخۡرَىٰ فَإِذَا هُمۡ قِيَامٞ يَنظُرُونَ
Ndipo (pamene) lipenga lidzaimbidwa, onse a kumwamba ndi pansi adzakomoka kupatula amene Allah wamfuna. Kenako lidzaimbidwa lachiwiri; pamenepo (onse) adzauka; adzakhala akuyang’ana (modabwa: “Nchiyani chachitika!”)
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَأَشۡرَقَتِ ٱلۡأَرۡضُ بِنُورِ رَبِّهَا وَوُضِعَ ٱلۡكِتَٰبُ وَجِاْيٓءَ بِٱلنَّبِيِّـۧنَ وَٱلشُّهَدَآءِ وَقُضِيَ بَيۡنَهُم بِٱلۡحَقِّ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ
Ndipo nthaka (tsiku limenelo) idzawala ndi kuunika kwa Mbuye wake; ndipo akaundula a zochita, adzaikidwa. Ndipo adzabweretsedwa aneneri ndi mboni (kuti aikire umboni pa anthu). Ndipo padzaweruzidwa pakati pawo mwachoonadi; ndipo iwo sadzaponderezedwa.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَوُفِّيَتۡ كُلُّ نَفۡسٖ مَّا عَمِلَتۡ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِمَا يَفۡعَلُونَ
Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa zimene udachita; ndipo Iye (Allah) Ngodziwa kwambiri zimene akuchita.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَسِيقَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِلَىٰ جَهَنَّمَ زُمَرًاۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءُوهَا فُتِحَتۡ أَبۡوَٰبُهَا وَقَالَ لَهُمۡ خَزَنَتُهَآ أَلَمۡ يَأۡتِكُمۡ رُسُلٞ مِّنكُمۡ يَتۡلُونَ عَلَيۡكُمۡ ءَايَٰتِ رَبِّكُمۡ وَيُنذِرُونَكُمۡ لِقَآءَ يَوۡمِكُمۡ هَٰذَاۚ قَالُواْ بَلَىٰ وَلَٰكِنۡ حَقَّتۡ كَلِمَةُ ٱلۡعَذَابِ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ
Ndipo amene adakanira, adzakusidwa kunka ku Jahannam ali magulumagulu kufikira pomwe adzaifikira, makomo ake adzatsekulidwa, ndipo alonda ake adzawauza: “Kodi sadakudzereni aneneri ochokera mwa inu okulakatulirani zisonyezo za Mbuye wanu, ndi kukuchenjezani za kukumana kwanu ndi tsiku lanuli?” Adzayankha (nati): “Inde, adatidzera; koma lidatsimikizika liwu la chilango pa okanira.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قِيلَ ٱدۡخُلُوٓاْ أَبۡوَٰبَ جَهَنَّمَ خَٰلِدِينَ فِيهَاۖ فَبِئۡسَ مَثۡوَى ٱلۡمُتَكَبِّرِينَ
Kudzanenedwa: “Lowani makomo a ku Jahannam; mukakhalitse mmenemo (nthawi yaitali).” Taonani kuipa malo a odzitukumula!
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَسِيقَ ٱلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْ رَبَّهُمۡ إِلَى ٱلۡجَنَّةِ زُمَرًاۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءُوهَا وَفُتِحَتۡ أَبۡوَٰبُهَا وَقَالَ لَهُمۡ خَزَنَتُهَا سَلَٰمٌ عَلَيۡكُمۡ طِبۡتُمۡ فَٱدۡخُلُوهَا خَٰلِدِينَ
Ndipo amene adamuopa Mbuye wawo, adzakusidwa kunka ku Munda wamtendere ali magulumagulu, mpaka kufikira pomwe adzaufika. (Adzapeza kuti) makomo ake atsekulidwa. Alonda ake adzanena kwa iwo: “Mtendere ukhale pa inu mwachita bwino! Lowani mmenemo, khalani nthawi yaitali.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَقَالُواْ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي صَدَقَنَا وَعۡدَهُۥ وَأَوۡرَثَنَا ٱلۡأَرۡضَ نَتَبَوَّأُ مِنَ ٱلۡجَنَّةِ حَيۡثُ نَشَآءُۖ فَنِعۡمَ أَجۡرُ ٱلۡعَٰمِلِينَ
Ndipo iwo adzanena: “Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Amene watitsimikizira lonjezo Lake, ndipo watipatsa dziko (kuti n’lathulathu). Tikukhala m’Minda yamtendereyi paliponse tafuna.” Taonani kukoma malipiro aochita zabwino!
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَتَرَى ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ حَآفِّينَ مِنۡ حَوۡلِ ٱلۡعَرۡشِ يُسَبِّحُونَ بِحَمۡدِ رَبِّهِمۡۚ وَقُضِيَ بَيۡنَهُم بِٱلۡحَقِّۚ وَقِيلَ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo udzaona angelo atazungulira mphepete mwa Arsh (Mpando wachifumu) uku akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo. Ndipo padzaweruzidwa pakati pawo mwachoonadi, ndipo kudzanenedwa (ndi zolengedwa zonse): “Kuyamikidwa nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa!”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
 
Übersetzung der Bedeutungen Surah / Kapitel: Az-Zumar
Suren/ Kapiteln Liste Nummer der Seite
 
Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - الترجمة الشيشيوا - Übersetzungen

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

Schließen