Check out the new design

Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - Die Übersetzung in Chichewa - Khalid Ibrahim Bityala. * - Übersetzungen


Übersetzung der Bedeutungen Surah / Kapitel: Al-Māʾidah   Vers:
وَقَالَتِ ٱلۡيَهُودُ وَٱلنَّصَٰرَىٰ نَحۡنُ أَبۡنَٰٓؤُاْ ٱللَّهِ وَأَحِبَّٰٓؤُهُۥۚ قُلۡ فَلِمَ يُعَذِّبُكُم بِذُنُوبِكُمۖ بَلۡ أَنتُم بَشَرٞ مِّمَّنۡ خَلَقَۚ يَغۡفِرُ لِمَن يَشَآءُ وَيُعَذِّبُ مَن يَشَآءُۚ وَلِلَّهِ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَاۖ وَإِلَيۡهِ ٱلۡمَصِيرُ
Ndipo Ayuda ndi Akhrisitu akunena: “Ife ndife ana a Mulungu ndiponso okondeka ake.” Nena: (Iwe Mtumiki) “Nchifukwa ninji Allah amakukhaulitsani kamba ka machimo anu? Koma inu ndinu anthu chabe mwa omwe adawalenga. Amamkhululukira amene wamfuna; ndipo amamulanga amene wamfuna. Ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi za pakati pake ngwa Allah. Ndipo kwa Iye nkobwerera.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
يَٰٓأَهۡلَ ٱلۡكِتَٰبِ قَدۡ جَآءَكُمۡ رَسُولُنَا يُبَيِّنُ لَكُمۡ عَلَىٰ فَتۡرَةٖ مِّنَ ٱلرُّسُلِ أَن تَقُولُواْ مَا جَآءَنَا مِنۢ بَشِيرٖ وَلَا نَذِيرٖۖ فَقَدۡ جَآءَكُم بَشِيرٞ وَنَذِيرٞۗ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
E inu anthu a buku! Ndithudi, wakudzerani Mtumiki Wathu yemwe akukufotokozerani inu, pa nthawi yopanda atumiki, kuti musadzanene kuti: “Sadadze kwa ife wonena nkhani zabwino ndiwochenjeza.” Choncho wakudzeranidi wonena nkhani zabwino ndi wochenjeza. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ ٱذۡكُرُواْ نِعۡمَةَ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ إِذۡ جَعَلَ فِيكُمۡ أَنۢبِيَآءَ وَجَعَلَكُم مُّلُوكٗا وَءَاتَىٰكُم مَّا لَمۡ يُؤۡتِ أَحَدٗا مِّنَ ٱلۡعَٰلَمِينَ
(Ndipo kumbukirani) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Inu anthu anga! Kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu, pamene adawachita ena mwa inu kukhala aneneri; ndipo adakuchitani kukhala mafumu (pambuyo poti mudali onyozeka m’dziko la Iguputo m’manja mwa Farawo). Ndipo wakupatsani zomwe sadampatsepo aliyense mwa zolengedwa.” [162]
[162] Mndime iyi akukumbutsa Ayuda chisomo chachikulu chomwe Allah adawadalitsa nacho. Kuyamika zomwe Allah watichitira nkofunika kwabasi. Tisakhale ngati anzathu awa amene Allah adawadalitsa ndimadalitso osiyanasiyana koma osamthokoza, ndiponso osamkonda ndi chikondi chochokera pansi pamtima.
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
يَٰقَوۡمِ ٱدۡخُلُواْ ٱلۡأَرۡضَ ٱلۡمُقَدَّسَةَ ٱلَّتِي كَتَبَ ٱللَّهُ لَكُمۡ وَلَا تَرۡتَدُّواْ عَلَىٰٓ أَدۡبَارِكُمۡ فَتَنقَلِبُواْ خَٰسِرِينَ
“Inu anthu anga. Lowani m’dziko loyeretsedwalo limene Allah adakulemberani, ndipo musabwelere m’mbuyo kuti mungasanduke otaika.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قَالُواْ يَٰمُوسَىٰٓ إِنَّ فِيهَا قَوۡمٗا جَبَّارِينَ وَإِنَّا لَن نَّدۡخُلَهَا حَتَّىٰ يَخۡرُجُواْ مِنۡهَا فَإِن يَخۡرُجُواْ مِنۡهَا فَإِنَّا دَٰخِلُونَ
(Iwo) adati: “Iwe Mûsa, ndithudi mmenemo muli anthu amphamvu. Ndipo ife sitikalowamo kufikira atatulukamo okha. Choncho ngati atatulukamo, pamenepo ndiye tikalowa.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
قَالَ رَجُلَانِ مِنَ ٱلَّذِينَ يَخَافُونَ أَنۡعَمَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمَا ٱدۡخُلُواْ عَلَيۡهِمُ ٱلۡبَابَ فَإِذَا دَخَلۡتُمُوهُ فَإِنَّكُمۡ غَٰلِبُونَۚ وَعَلَى ٱللَّهِ فَتَوَكَّلُوٓاْ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ
Anthu awiri mwa amene ankaopa Allah, omwe awiriwo Allah adawapatsa chisomo, adati (kwa anzawo): “Alowereni pa chipata (cha dzikolo). Ngati mukalowamo ndithudi, inu mukapambana. Ndipo kwa Allah Yekha yadzamirani ngati inu mulidi okhulupirira.”
Arabische Interpretationen von dem heiligen Quran:
 
Übersetzung der Bedeutungen Surah / Kapitel: Al-Māʾidah
Suren/ Kapiteln Liste Nummer der Seite
 
Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - Die Übersetzung in Chichewa - Khalid Ibrahim Bityala. - Übersetzungen

Übersetzung von Khalid Ibrahim Bitala.

Schließen