Check out the new design

Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Eggo e ɗemngal Ciiciiwa - Kaalid Ibrahiima Biitala. * - Tippudi firooji ɗii


Firo maanaaji Simoore: Simoore maa'ida   Aaya:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا قُمۡتُمۡ إِلَى ٱلصَّلَوٰةِ فَٱغۡسِلُواْ وُجُوهَكُمۡ وَأَيۡدِيَكُمۡ إِلَى ٱلۡمَرَافِقِ وَٱمۡسَحُواْ بِرُءُوسِكُمۡ وَأَرۡجُلَكُمۡ إِلَى ٱلۡكَعۡبَيۡنِۚ وَإِن كُنتُمۡ جُنُبٗا فَٱطَّهَّرُواْۚ وَإِن كُنتُم مَّرۡضَىٰٓ أَوۡ عَلَىٰ سَفَرٍ أَوۡ جَآءَ أَحَدٞ مِّنكُم مِّنَ ٱلۡغَآئِطِ أَوۡ لَٰمَسۡتُمُ ٱلنِّسَآءَ فَلَمۡ تَجِدُواْ مَآءٗ فَتَيَمَّمُواْ صَعِيدٗا طَيِّبٗا فَٱمۡسَحُواْ بِوُجُوهِكُمۡ وَأَيۡدِيكُم مِّنۡهُۚ مَا يُرِيدُ ٱللَّهُ لِيَجۡعَلَ عَلَيۡكُم مِّنۡ حَرَجٖ وَلَٰكِن يُرِيدُ لِيُطَهِّرَكُمۡ وَلِيُتِمَّ نِعۡمَتَهُۥ عَلَيۡكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ
“E inu amene mwakhulupirira! Pamene mwaimilira kuti mukaswali, sambitsani nkhope zanu, ndi manja anu mpaka mmagongono; ndipo pakani madzi pa mitu panu ndi kusambitsa mapazi anu mpaka mu akakolo. Ngati muli ndi janaba dziyeretseni (sambani thupi lonse); ndipo ngati muli odwala kapena muli paulendo, kapena mmodzi wanu wachokera kokadzithandiza kapenanso mwakhalira limodzi ndi mkazi, ndiye simudapeze madzi, chitani Tayammamu ndi dothi labwino ndipo pakani ku nkhope zanu ndi mmanja mwanu. Allah sakufuna kukuvutitsani, koma akufuna kukuyeretsani ndi kukwaniritsa chisomo chake pa inu kuti muthokoze.
Faccirooji aarabeeji:
وَٱذۡكُرُواْ نِعۡمَةَ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ وَمِيثَٰقَهُ ٱلَّذِي وَاثَقَكُم بِهِۦٓ إِذۡ قُلۡتُمۡ سَمِعۡنَا وَأَطَعۡنَاۖ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ
Ndipo kumbukirani chisomo cha Allah pa inu ndi pangano lake lomwe mudapangana Naye, pamene mudati: “Tamva, ndipo tamvera.” Muopeni Allah. Ndithudi Allah Ngodziwa za m’mitima.
Faccirooji aarabeeji:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ كُونُواْ قَوَّٰمِينَ لِلَّهِ شُهَدَآءَ بِٱلۡقِسۡطِۖ وَلَا يَجۡرِمَنَّكُمۡ شَنَـَٔانُ قَوۡمٍ عَلَىٰٓ أَلَّا تَعۡدِلُواْۚ ٱعۡدِلُواْ هُوَ أَقۡرَبُ لِلتَّقۡوَىٰۖ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَۚ إِنَّ ٱللَّهَ خَبِيرُۢ بِمَا تَعۡمَلُونَ
E inu amene mwakhulupirira! Khalani olungama kwa Allah, opereka umboni mwachilungamo, ndipo chidani cha anthu pa inu chisakuchititseni kuti musachite chilungamo. Chitani chilungamo; kutero kumakuyandikitsani ku “taquwa” (kuopa Allah). Ndipo opani Allah. Ndithudi, Allah Ngodziwa nkhani zonse za (zinthu) zomwe muchita.
Faccirooji aarabeeji:
وَعَدَ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُم مَّغۡفِرَةٞ وَأَجۡرٌ عَظِيمٞ
Allah walonjeza omwe akhulupirira ndi kuchita zabwino kuti adzapeza chikhululuko ndi malipiro aakulu.
Faccirooji aarabeeji:
 
Firo maanaaji Simoore: Simoore maa'ida
Tippudi cimooje Tonngoode hello ngoo
 
Firo maanaaji al-quraan tedduɗo oo - Eggo e ɗemngal Ciiciiwa - Kaalid Ibrahiima Biitala. - Tippudi firooji ɗii

Eggo mum Khalid Ibrahim Beitala.

Uddude