Check out the new design

Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fassara da harshan Shishiyo - Khalid Ibrahim Bitala * - Teburin Bayani kan wasu Fassarori


Fassarar Ma'anoni Sura: Al'a'raf   Aya:

Al-A’râf

الٓمٓصٓ
Alif-Lâm-Mîm-Sad.
Tafsiran larabci:
كِتَٰبٌ أُنزِلَ إِلَيۡكَ فَلَا يَكُن فِي صَدۡرِكَ حَرَجٞ مِّنۡهُ لِتُنذِرَ بِهِۦ وَذِكۡرَىٰ لِلۡمُؤۡمِنِينَ
(Iyi Qur’an ndi) buku (lopatulika) lomwe lavumbulutsidwa kwa iwe. Choncho chifuwa chako chisabanike ndi ilo (poopa kufikitsa mawu ake kwa anthu kuti angakuyese wabodza;) kuti uwachenjeze nalo (otsutsa) ndi kuti likhale chikumbutso kwa okhulupirira (kuti aonjezere chikhulupiliro chawo).[178]
[178] Apa akumuuza Mtumiki (s.a.w) kuti asaope kulengeza zimene Allah wamuululira. Asatekeseke ndi otsutsa ngakhale atachuluka chotani. Mlaliki aliyense akuuzidwanso chimodzimodzi. Anene choonadi kwa anthu ndipo asaope kudzudzulidwa.
Tafsiran larabci:
ٱتَّبِعُواْ مَآ أُنزِلَ إِلَيۡكُم مِّن رَّبِّكُمۡ وَلَا تَتَّبِعُواْ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءَۗ قَلِيلٗا مَّا تَذَكَّرُونَ
Tsatirani zomwe zavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Mbuye wanu, ndipo musawatsatire omwe sali Allah powayesa atetezi (anu). Ndizochepa zimene mumazikumbukira.
Tafsiran larabci:
وَكَم مِّن قَرۡيَةٍ أَهۡلَكۡنَٰهَا فَجَآءَهَا بَأۡسُنَا بَيَٰتًا أَوۡ هُمۡ قَآئِلُونَ
Ndimidzi yambiri imene tidaiononga ndipo chilango Chathu chidaidzera nthawi ya usiku, kapena usana iwo atagona tulo tamasana (akupumula monga momwe zinawachitikira anthu a Loti ndi anthu a Shuaib).
Tafsiran larabci:
فَمَا كَانَ دَعۡوَىٰهُمۡ إِذۡ جَآءَهُم بَأۡسُنَآ إِلَّآ أَن قَالُوٓاْ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ
Ndipo sikunali kulira kwawo pamene chinawafika chilango chathu koma kunena (ndi kuvomereza): “Ndithudi, ife tinali ochita zoipa.” (Koma kuvomereza kwawoko sikunawapindulire kanthu).
Tafsiran larabci:
فَلَنَسۡـَٔلَنَّ ٱلَّذِينَ أُرۡسِلَ إِلَيۡهِمۡ وَلَنَسۡـَٔلَنَّ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Mtheradi tidzawafunsa (anthu) amene anatumiziridwa (atumiki), naonso atumikiwo tidzawafunsa.
Tafsiran larabci:
فَلَنَقُصَّنَّ عَلَيۡهِم بِعِلۡمٖۖ وَمَا كُنَّا غَآئِبِينَ
Tsono tidzawauza mozindikira bwino-bwino (chilichonse chimene ankachita). Ndipo sitidali kutali (nawo pamene ankachita zochita zawo).
Tafsiran larabci:
وَٱلۡوَزۡنُ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡحَقُّۚ فَمَن ثَقُلَتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ
Ndipo sikero (yoyezera zochita za anthu) tsiku limenelo idzakhala yoona (yopanda chinyengo). Choncho, amene idzalemere miyeso yake (ya zabwino), iwowo ndiwo opambana.
Tafsiran larabci:
وَمَنۡ خَفَّتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُم بِمَا كَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يَظۡلِمُونَ
Ndipo amene idzapepuke miyeso yawo (ya zinthu zawo zabwino), iwo ndi amene ataya pachabe moyo wawo chifukwa cha kuzichitira zosalungama zizindikiro Zathu.
Tafsiran larabci:
وَلَقَدۡ مَكَّنَّٰكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَجَعَلۡنَا لَكُمۡ فِيهَا مَعَٰيِشَۗ قَلِيلٗا مَّا تَشۡكُرُونَ
Ndithudi tinakupatsani mphamvu yokhalira pa dziko, ndipo takupangirani m’menemo zinthu zofunika pa moyo wanu. Koma kuyamika kwanu mpang’ono.
Tafsiran larabci:
وَلَقَدۡ خَلَقۡنَٰكُمۡ ثُمَّ صَوَّرۡنَٰكُمۡ ثُمَّ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ لَمۡ يَكُن مِّنَ ٱلسَّٰجِدِينَ
Ndithudi, tinakulengani, kenako tidakukonzani (pokupatsani ziwalo) ndi kunena kwa angelo kuti: “Mgwadireni Adam.” Ndipo adamgwadira kupatula Iblis, sadali mwa ogwada.
Tafsiran larabci:
 
Fassarar Ma'anoni Sura: Al'a'raf
Teburin Jerin Sunayen Surori Lambar shafi
 
Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fassara da harshan Shishiyo - Khalid Ibrahim Bitala - Teburin Bayani kan wasu Fassarori

Fassararta Khalid Ibrahim Bitala.

Rufewa