Check out the new design

Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fassara da harshan Shishiyo - Khalid Ibrahim Bitala * - Teburin Bayani kan wasu Fassarori


Fassarar Ma'anoni Sura: Alkiyama   Aya:
كَلَّا بَلۡ تُحِبُّونَ ٱلۡعَاجِلَةَ
Iyayi koma mukukonda moyo wa pa dziko.
Tafsiran larabci:
وَتَذَرُونَ ٱلۡأٓخِرَةَ
Ndipo mukusiya moyo wa tsiku lachimaliziro.
Tafsiran larabci:
وُجُوهٞ يَوۡمَئِذٖ نَّاضِرَةٌ
Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zowala,
Tafsiran larabci:
إِلَىٰ رَبِّهَا نَاظِرَةٞ
Zili kumuyang’ana Mbuye wawo.
Tafsiran larabci:
وَوُجُوهٞ يَوۡمَئِذِۭ بَاسِرَةٞ
Ndipo nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zoziya (zokhwinyata).
Tafsiran larabci:
تَظُنُّ أَن يُفۡعَلَ بِهَا فَاقِرَةٞ
Zikuyembekezeka kuti zilandira tsoka lodula msana.
Tafsiran larabci:
كَلَّآ إِذَا بَلَغَتِ ٱلتَّرَاقِيَ
Sichoncho! Pamene mzimu udzafika pa nthitimtima, (pomwe pakumana mafupa am’mapewa).
Tafsiran larabci:
وَقِيلَ مَنۡۜ رَاقٖ
Ndipo ndikunenedwa ndani angamchiritse!
Tafsiran larabci:
وَظَنَّ أَنَّهُ ٱلۡفِرَاقُ
Ndipo (iye mwini wake), nkutsimikiza kuti ndithu uku ndikusiyana (ndi dziko lapansi),
Tafsiran larabci:
وَٱلۡتَفَّتِ ٱلسَّاقُ بِٱلسَّاقِ
Ndipo miyendo idzasanjikizana; (iyi ndi nthawi yochoka mzimu).
Tafsiran larabci:
إِلَىٰ رَبِّكَ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡمَسَاقُ
Tsiku limenelo koperekedwa (anthu onse) nkwa Mbuye wako.
Tafsiran larabci:
فَلَا صَدَّقَ وَلَا صَلَّىٰ
Ndipo sadakhulupirire komanso sadapemphere Swala (zisanu),
Tafsiran larabci:
وَلَٰكِن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ
Koma (m’malo mwake) adatsutsa ndi kunyoza.
Tafsiran larabci:
ثُمَّ ذَهَبَ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ يَتَمَطَّىٰٓ
Kenaka adapita kubanja lake (uku akuyenda) monyada.
Tafsiran larabci:
أَوۡلَىٰ لَكَ فَأَوۡلَىٰ
Kuonongeka nkwako (iwe wotsutsa)! Kuonongeka zedi!
Tafsiran larabci:
ثُمَّ أَوۡلَىٰ لَكَ فَأَوۡلَىٰٓ
Ndiponso kuonongeka nkwako! kuonongeka zedi!
Tafsiran larabci:
أَيَحۡسَبُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَن يُتۡرَكَ سُدًى
Kodi munthu akuganiza kuti angosiidwa chabe? (Sadzaweruzidwa)?
Tafsiran larabci:
أَلَمۡ يَكُ نُطۡفَةٗ مِّن مَّنِيّٖ يُمۡنَىٰ
Kodi sadali dontho la umuna umene udafwamphukira (m’chiberekero)?
Tafsiran larabci:
ثُمَّ كَانَ عَلَقَةٗ فَخَلَقَ فَسَوَّىٰ
Kenako adakhala nthinthi (ntchintchi) ya magazi, ndipo adamlenga ndi kumlinganiza (monga munthu).
Tafsiran larabci:
فَجَعَلَ مِنۡهُ ٱلزَّوۡجَيۡنِ ٱلذَّكَرَ وَٱلۡأُنثَىٰٓ
Ndipo adalenga kuchokera mmenemo mitundu iwiri: mwamuna ndi mkazi.
Tafsiran larabci:
أَلَيۡسَ ذَٰلِكَ بِقَٰدِرٍ عَلَىٰٓ أَن يُحۡـِۧيَ ٱلۡمَوۡتَىٰ
Kodi (Iye amene adayambitsa chilengedwe choyambachi) sangathe kuwapatsa moyo akufa?
Tafsiran larabci:
 
Fassarar Ma'anoni Sura: Alkiyama
Teburin Jerin Sunayen Surori Lambar shafi
 
Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fassara da harshan Shishiyo - Khalid Ibrahim Bitala - Teburin Bayani kan wasu Fassarori

Khalid Ibrahim Bitala ne ya fassarasu

Rufewa