Check out the new design

Kur'an-ı Kerim meal tercümesi - Çevaca Tercüme - Halid İbrahim Pitala * - Mealler fihristi


Anlam tercümesi Sure: Sûratu'l-Bakarah   Ayet:
أَوَلَا يَعۡلَمُونَ أَنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعۡلِنُونَ
“Kodi sadziwa kuti Allah akudziwa zomwe akubisa ndi zomwe akuonetsera poyera? (Kwa Allah palibe chobisika).
Arapça tefsirler:
وَمِنۡهُمۡ أُمِّيُّونَ لَا يَعۡلَمُونَ ٱلۡكِتَٰبَ إِلَّآ أَمَانِيَّ وَإِنۡ هُمۡ إِلَّا يَظُنُّونَ
Ndipo mwa iwo (Ayudawo) zilipo mbuli zosadziwa kuwerenga buku (la Allah), koma ziyembekezero zabodza basi, ndipo iwo alibe china koma kungoganizira.
Arapça tefsirler:
فَوَيۡلٞ لِّلَّذِينَ يَكۡتُبُونَ ٱلۡكِتَٰبَ بِأَيۡدِيهِمۡ ثُمَّ يَقُولُونَ هَٰذَا مِنۡ عِندِ ٱللَّهِ لِيَشۡتَرُواْ بِهِۦ ثَمَنٗا قَلِيلٗاۖ فَوَيۡلٞ لَّهُم مِّمَّا كَتَبَتۡ أَيۡدِيهِمۡ وَوَيۡلٞ لَّهُم مِّمَّا يَكۡسِبُونَ
Chilango cha ukali chili pa amene akulemba buku ndi manja awo, kenako nanena: “Ili lachokera kwa Allah,” (akunena bodzalo) kuti apeze zinthu za mtengo wochepa (za m’dziko lapansi); choncho kuonongeka kuli pa iwo chifukwa cha zomwe manja awo alemba, ndiponso kuonongeka n’kwawo chifukwa cha zomwe akupeza.
Arapça tefsirler:
وَقَالُواْ لَن تَمَسَّنَا ٱلنَّارُ إِلَّآ أَيَّامٗا مَّعۡدُودَةٗۚ قُلۡ أَتَّخَذۡتُمۡ عِندَ ٱللَّهِ عَهۡدٗا فَلَن يُخۡلِفَ ٱللَّهُ عَهۡدَهُۥٓۖ أَمۡ تَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ
Ndipo akunena: “Sudzatikhudza Moto kupatula masiku owerengeka basi.”Auze: “Kodi mudapangana naye Allah, kuti potero sadzaswa lonjezo Lake, kapena mukungomunenera Allah zimene simukuzidziwa?”
Arapça tefsirler:
بَلَىٰۚ مَن كَسَبَ سَيِّئَةٗ وَأَحَٰطَتۡ بِهِۦ خَطِيٓـَٔتُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Sichoncho! Koma amene wachita choipa, nam’zungulira machimo akeo, otero ndi anthu a ku Moto. M’menemo adzakhala nthawi yaitali.
Arapça tefsirler:
وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Ndipo amene akhulupirira nachita zabwino, iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere. M’menemo adzakhala nthawi yaitali.
Arapça tefsirler:
وَإِذۡ أَخَذۡنَا مِيثَٰقَ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ لَا تَعۡبُدُونَ إِلَّا ٱللَّهَ وَبِٱلۡوَٰلِدَيۡنِ إِحۡسَانٗا وَذِي ٱلۡقُرۡبَىٰ وَٱلۡيَتَٰمَىٰ وَٱلۡمَسَٰكِينِ وَقُولُواْ لِلنَّاسِ حُسۡنٗا وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ ثُمَّ تَوَلَّيۡتُمۡ إِلَّا قَلِيلٗا مِّنكُمۡ وَأَنتُم مُّعۡرِضُونَ
Ndipo (akumbutse nkhani iyinso) pamene tidalandira pangano lamphamvu la ana a Israyeli kuti: Musapembedze aliyense koma Allah; ndipo muwachitire zabwino makolo anu ndi achibale anu, ndi amasiye, ndi masikini (osoŵedwa); ndipo nenani kwa anthu mwaubwino; ndipo pempherani Swala moyenera ndi kupereka Zakaat, kenako mudatembenuka monyozera kupatula ochepa mwa inu, ndipo inu ndinu onyozera.
Arapça tefsirler:
 
Anlam tercümesi Sure: Sûratu'l-Bakarah
Surelerin fihristi Sayfa numarası
 
Kur'an-ı Kerim meal tercümesi - Çevaca Tercüme - Halid İbrahim Pitala - Mealler fihristi

Halid İbrahim Pitala Tercümesi.

Kapat