Kur'an-ı Kerim meal tercümesi - الترجمة الشيشيوا * - Mealler fihristi


Anlam tercümesi Ayet: (57) Sure: Sûretu'z-Zuhruf
۞ وَلَمَّا ضُرِبَ ٱبۡنُ مَرۡيَمَ مَثَلًا إِذَا قَوۡمُكَ مِنۡهُ يَصِدُّونَ
Ndipo pamene lidaperekedwa fanizo la mwana wa Mariya, pamenepo anthu anu adali kufuula (monyoza).[344]
[344] Fanizo lomwe likunenedwa apa ndi lomufanizira Isa (Yesu) ndi zomwe zikupembedzedwa kusiya Allah. Akafiri adamfanizira iye pambuyo povumbulutsidwa Ayah yakuti: “Ndithu inu ndi zomwe mukuzipembedza kusiya Allah ndi nkhuni za ku Jahannam.” Choncho adati Isa (Yesu) nayenso akalowa ku Moto chifukwa chakuti Akhrisitu amamupembedza kusiya Allah. Koma Allah adamyeretsa ponena kuti: “Ndithu awo amene ubwino wochokera kwa Ife watsogola kwa iwo, iwowo akatalikitsidwa ndi motowo” Choncho Isa (Yesu) sakalowa ku Moto chifukwa iye sadalamule anthu kuti amupembedze komanso sakudziwa kuti pali aliyense amene akupembedza iye.
Arapça tefsirler:
 
Anlam tercümesi Ayet: (57) Sure: Sûretu'z-Zuhruf
Surelerin fihristi Sayfa numarası
 
Kur'an-ı Kerim meal tercümesi - الترجمة الشيشيوا - Mealler fihristi

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

Kapat