Check out the new design

Kur'an-ı Kerim meal tercümesi - Çevaca Tercüme - Halid İbrahim Pitala * - Mealler fihristi


Anlam tercümesi Sure: Sûretu'n-Nûh   Ayet:
يُرۡسِلِ ٱلسَّمَآءَ عَلَيۡكُم مِّدۡرَارٗا
Akutumizirani mvula yotsika mochuluka,
Arapça tefsirler:
وَيُمۡدِدۡكُم بِأَمۡوَٰلٖ وَبَنِينَ وَيَجۡعَل لَّكُمۡ جَنَّٰتٖ وَيَجۡعَل لَّكُمۡ أَنۡهَٰرٗا
Ndikukupatsani chuma ndi ana, (zomwe ndi zokongoletsa za dziko lapansi), ndi kukupangirani minda (yokongola) ndi kukupangirani mitsinje (yothilira mbewu zanu ndi kumwetsa ziweto zanu).
Arapça tefsirler:
مَّا لَكُمۡ لَا تَرۡجُونَ لِلَّهِ وَقَارٗا
Kodi chifukwa ninji simupereka ulemu kwa Allah (woyenera Umulungu Wake kuti akakuchitireni chifundo ndi kukupulumutsani ku chilango)?
Arapça tefsirler:
وَقَدۡ خَلَقَكُمۡ أَطۡوَارًا
Pomwe Iye adakulengani mnjira zosiyanasiyana; (madzi a umunthu, kenako magazi, kenako magazi ochindikala, kenako mafupa ndipo kenako mnofu),
Arapça tefsirler:
أَلَمۡ تَرَوۡاْ كَيۡفَ خَلَقَ ٱللَّهُ سَبۡعَ سَمَٰوَٰتٖ طِبَاقٗا
Kodi simudaone momwe Allah adalengera thambo zisanu ndi ziwiri mosanjikizana?
Arapça tefsirler:
وَجَعَلَ ٱلۡقَمَرَ فِيهِنَّ نُورٗا وَجَعَلَ ٱلشَّمۡسَ سِرَاجٗا
Ndi kuyika mwezi mthambomo kukhala kuunika, ndiponso kuyika dzuwa kukhala nyali.
Arapça tefsirler:
وَٱللَّهُ أَنۢبَتَكُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ نَبَاتٗا
Ndipo Allah adakulengani kuchokera m’nthaka monga mmera.
Arapça tefsirler:
ثُمَّ يُعِيدُكُمۡ فِيهَا وَيُخۡرِجُكُمۡ إِخۡرَاجٗا
Kenako adzakubwezerani momwemo ndikudzakutulutsaninso (popanda cholepheretsa).
Arapça tefsirler:
وَٱللَّهُ جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ بِسَاطٗا
Ndipo Allah wakupangirani nthaka kukhala ngati choyala,
Arapça tefsirler:
لِّتَسۡلُكُواْ مِنۡهَا سُبُلٗا فِجَاجٗا
Kuti muziyendayenda m’menemo m’njira zazikulu.”
Arapça tefsirler:
قَالَ نُوحٞ رَّبِّ إِنَّهُمۡ عَصَوۡنِي وَٱتَّبَعُواْ مَن لَّمۡ يَزِدۡهُ مَالُهُۥ وَوَلَدُهُۥٓ إِلَّا خَسَارٗا
Adanena Nuh: “Mbuye wanga! Ndithu anthu anga andinyoza (pa zimene ndawalamula kuti akhulupirire Inu ndi kupempha chikhululuko chanu), ndipo (ofooka mwa iwo) amtsatira yemwe chuma chake ndi ana ake sizidzamuonjezera (chilichonse chabwino) koma kutaika (ndi kuonongeka pa tsiku lachimaliziro).
Arapça tefsirler:
وَمَكَرُواْ مَكۡرٗا كُبَّارٗا
Ndipo (eni chuma ndi ana) awatchera (otsatira awo) ndale zazikulu (ndi zopyola muyeso kuti asakhulupirire).”
Arapça tefsirler:
وَقَالُواْ لَا تَذَرُنَّ ءَالِهَتَكُمۡ وَلَا تَذَرُنَّ وَدّٗا وَلَا سُوَاعٗا وَلَا يَغُوثَ وَيَعُوقَ وَنَسۡرٗا
Ndipo adanena (kwa owatsatira awo): “Musasiye kupembedza milungu yanu; musamusiye Wadda, Suwaa’, Yaghutha, Ya’uqa ndi Nasra” (maina a mafano awo).
Arapça tefsirler:
وَقَدۡ أَضَلُّواْ كَثِيرٗاۖ وَلَا تَزِدِ ٱلظَّٰلِمِينَ إِلَّا ضَلَٰلٗا
Ndipo ndithu iwo asokeretsa (anthu) ambiri; ndipo musawaonjezere ochita zoipa (china chake) koma kusokera basi.”
Arapça tefsirler:
مِّمَّا خَطِيٓـَٰٔتِهِمۡ أُغۡرِقُواْ فَأُدۡخِلُواْ نَارٗا فَلَمۡ يَجِدُواْ لَهُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ أَنصَارٗا
Chifukwa cha zochimwa zawo adamizidwa ndi kulowetsedwa ku Moto (waukulu woyaka); sadapeze owapulumutsa ndi kuwateteza m’malo mwa Allah.
Arapça tefsirler:
وَقَالَ نُوحٞ رَّبِّ لَا تَذَرۡ عَلَى ٱلۡأَرۡضِ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ دَيَّارًا
Ndipo adanena Nuh (atataya mtima za anthu ake): “Mbuye wanga! Musasiye aliyense mwa osakhulupirira kukhala pa dziko.”
Arapça tefsirler:
إِنَّكَ إِن تَذَرۡهُمۡ يُضِلُّواْ عِبَادَكَ وَلَا يَلِدُوٓاْ إِلَّا فَاجِرٗا كَفَّارٗا
“Ndithu Inu Mbuye wanga ngati muwasiya (popanda kuwaononga ndi kuwathetsa) asokeretsa akapolo anu (kunjira yolungama). Ndipo sangabereke (ana abwino) koma oipa; osakhulupirira (okhala kutali ndi choonadi, ndiponso onyoza Inu).”
Arapça tefsirler:
رَّبِّ ٱغۡفِرۡ لِي وَلِوَٰلِدَيَّ وَلِمَن دَخَلَ بَيۡتِيَ مُؤۡمِنٗا وَلِلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِۖ وَلَا تَزِدِ ٱلظَّٰلِمِينَ إِلَّا تَبَارَۢا
“Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndi makolo anga, ndi aliyense walowa m’nyumba yanga ali okhulupirira ndi okhulupirira amuna ndi okhulupirira akazi. Ndipo musawaonjezere anthu achinyengo chinachake koma kuwaononga basi.”
Arapça tefsirler:
 
Anlam tercümesi Sure: Sûretu'n-Nûh
Surelerin fihristi Sayfa numarası
 
Kur'an-ı Kerim meal tercümesi - Çevaca Tercüme - Halid İbrahim Pitala - Mealler fihristi

Halid İbrahim Pitala Tercümesi.

Kapat