Uku ndikudzipatula kochokera kwa Allah ndi Mtumiki wake ku (mapangano) amene mudapangana nawo (kenako nkuswa mapangano awowo) a m’gulu la Amushirikina.[204]
[204] (Ndime 1-2) Omasulila Qur’an adati Arabu adali kuswa mapangano amene adamanga pamodzi ndi Mtumiki wa Allah. Potero, Allah adalamula Mtumiki Wake kuti awaponyere mapangano awo. Choncho, Mtumiki adatuma Abubakari (r.a) kukhala mtsogoleri wa anthu kumapemphero a Hajj. Ndipo adamtsatanso Ali (r.a) kumeneko ndi nkhani yokhayokhayo kuti akawawerengere anthu kuti Allah ndi Mtumiki Wake atulukamo m’mapangano okhalirana mwa mtendere ndi Amushirikina sadzaloledwa kuyandikira Nyumba Yopatulika chaka chotsatiracho, ndikutinso sadzaloledwa kuzungulira Nyumba yopatulikayo uku ali maliseche.
Ndipo uku ndi kulengeza kochokera kwa Allah ndi Mtumiki Wake kwa Anthu pa tsiku la Hajj yaikulu kuti ndithu Allah ndi Mtumiki Wake adzichotsa mmapangano a Amushirikina (omwe ali achinyengo). Choncho, ngati mulapa ndibwino kwa inu; ndipo ngati mutembenuka ndi kunyoza, dziwani kuti inu simungamulepheretse Allah. Ndipo auze za chilango chowawa amene sadakhulupirire.
Asinthanitsa Ayah za Allah (ndi zinthu za dziko lapansi) ndi mtengo wochepa, ndipo atsekereza (anthu) kunjira Yake. Ndithu nzoipa kwabasi zomwe iwo akhala akuchita.
Koma ngati alapa nayamba kupemphera Swala ndikupereka chopereka (Zakaat), ndiye kuti ndi abale anu pa chipembedzo. Ndipo tikuzifotokoza Ayah zi (mwabwino) kwa anthu odziwa.
Menyanani nao; Allah awalanga kupyolera m’manja anu, ndipo awasambula ndi kukupulumutsani kwa iwo ndi kuchiritsa kuwawidwa (komwe kudali) m’mitima mwa anthu okhulupirira (chifukwa cha masautso omwe adawapeza kwa iwo).
Kodi mukuganiza kuti mungosiidwa chabe Allah asanawaonetsere poyera amene amenyera chipembedzo mwa inu ndi amene sachita ubwenzi (ndi wina wake) kupatula Allah ndi Mtumiki wake ndi okhulupirira? Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene muchita.
Ndithu oyang’anira Misikiti ya Allah ndi kuiyendera ndi amene akhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro, ndi kumapemphera Swala ndi kupereka chopereka (Zakaat) ndipo saopa aliyense koma Allah yekha. Choncho, iwowo ndi amene akuyembekezeka kukhala mwa oongoka.
Kodi kumwetsa madzi (anthu) ochita Hajj ndi kusunga Msikiti Wopatulika mukukuyesa kuti nkofanana ndi yemwe wakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro, ndi kumenya nkhondo pa njira Ya Allah? Sangakhale ofanana kwa Allah. Ndipo Allah saongola anthu ochita zolakwa.
Amene akhulupirira, ndi kusamuka, ndi kumenya nkhondo pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi matupi awo, ali ndi ulemelero waukulu kwa Allah. Iwowo ndiwo opambana.
E inu amene mwakhulupirira! Musawachite makolo anu ndi abale anu kukhala atetezi anu ngati (iwo) akukonda kusakhulupirira m’malo mokhulupirira. Ndipo mwa inu amene ati awasankhe kukhala atetezi, otero ndiwo adzichitira okha zoipa.
Nena: “Ngati makolo anu, ana anu, abale anu, akazi anu, ndi anansi anu ndi chuma chimene mwachipata, ndi malonda anu amene mukuopa kuti angaonongeke, ndi nyumba zanu zimene mukuzikonda, (ngati zinthuzi zili) zokondeka kwamhiri kwa inu kuposa Allah ndi Mtumiki Wake ndi kuchita Jihâd pa njira Yake, choncho dikirani kufikira Allah adzabwera ndi lamulo Lake (lokukhaulitsani). Ndipo Allah satsogolera anthu otuluka m’chilamulo (Chake).
Kenaka Allah adatsitsa mpumulo Wake kwa Mtumiki Wake ndi kwa okhulupirira. Ndipo adatsitsa asilikali ankhondo (angelo) omwe simudawaone. Ndipo adawakhaulitsa osakhulupirira. Imeneyo ndiyo mphoto ya osakhulupirira.
Ndipo pambuyo pa izi, Allah alandira kulapa kwa amene wamfuna (mwa osakhulupirira powalowetsa m’Chisilamu). Ndipo Allah Ngokhululuka Ngwachisoni chosatha.
Menyanani ndi omwe sakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro, omwenso sakusiya zoletsedwa zomwe Allah ndi Mtumiki Wake waletsa; omwenso satsatira chipembedzo choona mwa amene adapatsidwa mabuku. (Menyanani nawo) kufikira apereke msonkho ndi manja awo uku ali odzichepetsa.
Awachita ophunzira a za chipembedzo chawo ndi ansembe awo kukhala milungu kusiya Allah (powatsata pa zimene akuwalamula popanda umboni wa Allah). (Amsandutsanso) Mesiya (Isa {Yesu}) mwana wa Mariya (kukhala mulungu); chikhalirecho sadalamulidwe china koma kupembedza Mulungu Mmodzi. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye, wapatukana ndi zimene akumphatikiza nazozo.
Akufuna kuzimitsa kuunika kwa Allah (Chisilamu) ndi pakamwa pawo; ndipo Allah sadzalola koma kukwaniritsa kuunika kwake ngakhale kuti osakhulupirira zikuwanyansa.
Iye ndi Yemwe adatuma Mtumiki Wake ndi ulangizi ndiponso chipembedzo choona kuti achiwonetsere pa zipembedzo zonse, ngakhale atanyansidwa nazo Amushirikina.
E inu amene mwakhulupirira! Ndithu ambiri ophunzira a za chipembedzo cha Chiyuda ndi cha Chikhristu, akudya chuma cha anthu mwachinyengo ndi kusekeleza anthu ku njira ya Allah. Ndipo amene akusonkhanitsa golide ndi siliva popanda kuzipereka pa njira ya Allah, auze nkhani ya chilango chowawa.
Pa tsiku lomwe (chuma chawo) chidzatenthedwa ku moto wa Jahannam, ndipo ndi chumacho zidzatenthedwa nkhope zawo, nthiti zawo ndi misana yawo (ali kuwuzidwa kuti): “Izi ndi zija zomwe mudadzisungira nokha. Choncho lawani (chilango) cha zomwe mudali kuzisunga.[207]
[207] Mu Ayah iyi, Allah akuchenjeza amene akusonkhanitsa chumacho nkumangochiunjika m’nkhokwe popanda kutulutsamo chopereka (Zakaat). Akawalanga nacho pa tsiku la chimaliziro ndi chilango cha moto. Tero, tulutsamoni Zakaat m’chuma chanu. Musanyozere lamulo la Allah.
Ndithu chiwerengero cha miyezi kwa Allah (pa chaka), ndi miyezi khumi ndi iwiri m’chilamulo cha Allah kuyambira tsiku lomwe adalenga thambo ndi nthaka. M’menemo muli miyezi inayi yopatulika. Ichi ndicho chipembedzo cha Allah cholunjika, choncho musadzichitire nokha zoipa m’menemo. Ndipo menyanani ndi Amshrikina nonse pamodzi monga momwe akumenyana nanu onse pamodzi. Ndipo dziwani kuti Allah ali pamodzi ndi oopa.[208]
[208] Chiwerengero chamiyezi m’chaka, ndi khumi ndi iwiri monga mwalamulo la Allah. M’miyeziyi muli miyezi inayi yopatulika yomwe ndi Rajabu, Thul Qa’da, Thul Hijja ndi Muharamu. M’miyeziyi nkosaloledwa kuchita nkhondo pokhapokha mutaputidwa ndi adani.
Ndithu kutalikitsa ndi kuchedwetsa (mwezi wopatulika kuti usafike mwamsanga), kumaonjezera kusakhulupirira (mwa Allah), zoterozo akusokerezedwa nazo amene sadakhulupirire. Chaka china amauyesa wosapatulika pomwe chaka china amauyesa wopatulika ndi cholinga chokwaniritsa chiwerengero cholingana ndi miyezi yomwe Allah adaipatula kukhala yopatulika. Choncho, chimene Allah adaletsa, amachiyesa chololedwa. Zakometsedwa kwa iwo zochita zawo zoipa. Ndipo Allah sawatsogolera anthu osakhulupirira.[209]
[209] Kuichedwetsa miyezi yopatulika, kapena ina mwa iyo ndi kuichotsa mu mndondomeko wake umene Allah adaiika monga momwe ankachitira anthu am’nyengo ya umbuli, kumawaonjezera kusakhulupilira anthu osakhulupilira mwa Allah. Arabu m’nyengo ya umbuli amauyesa mwezi wopatulika kukhala wosapatulika akafuna kuti achite nkhondo m’mweziwo. Ndipo mwezi wosapatulika amauyesa wopatulika ncholinga choti akwaniritse chiwerengero cha miyezi yopatulika yomwe Allah adaipatula. Zonsezi zimachitika pofuna kukwaniritsa zilakolako zawo zoipa.
E inu amene mwakhulupirira! Mwatani; mukauzidwa (kuti): “Pitani mukachite Jihâd pa njira ya Allah,” mukudziremetsa pa nthaka (polemedwa ndi kutulukako)? Kodi mwasangalatsidwa ndi moyo wa pa dziko lapansi kuposa moyo wa tsiku lachimaliziro? Koma zosangalatsa za m’moyo wa dziko lapansi poyerekeza ndi (moyo wa) tsiku lachimaliziro, ndi zochepa kwambiri.
Ngati simupita (ku nkhondoko), (Allah) akulangani ndi chilango chowawa, ndipo abweretsa anthu ena m’malo mwa inu; ndipo simungamuvutitse ndi chilichonse (ngati musiya kupita kukamenyera chipembedzo Chake). Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.
Ngati simumthandiza (Mtumuki Muhammad {s.a.w} palibe kanthu), ndithu Allah adamthandiza pamene adamtulutsa aja amene sadakhulupirire. Pamene adali awiriwiri kuphanga, pamene ankanena kwa mnzake: “Usadandaule. Ndithu Allah ali nafe pamodzi.” Ndipo Allah adatsitsa mpumulo Wake pa iye, ndipo adaamthangata ndi asilikali a nkhondo omwe simudawaone. Ndipo mawu a amene sadakhulupirire adawachita kukhala apansi ndipo mawu a Allah ndiwo apamwamba. Ndipo Allah Ngopambana, Ngwanzeru zakuya.
Pitani (mukamenyane) muli opepukidwa ndi olemedwa; ndipo menyerani njira ya Allah nchuma chanu ndi inu nomwe. Zimenezi nzabwino kwa inu ngati muli anthu odziwa.
Sangakupemphe chilolezo (chotsala ku nkhondo) amene akhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro kuti asapite kukamenyera (chipembedzo cha Allah) ndi chuma chawo ndi Matupi awo. Ndipo Allah akuwadziwa amene akumuopa.
Ndithu amakupempha chilolezo aja amene sakhulupirira Allah ndi tsiku la chimaliziro, ndipo mitima yawo yakaikira, ndipo iwo, chifukwa cha kukaika kwawo akungotekeseka.
Akadafunadi kuti atuluke (kupita ku nkhondo) akadakonzekera zokonzekera za ku nkhondo; koma Allah sadafune kuti iwo apiteko; choncho adawatsekereza, ndipo kudanenedwa: “Khalani pamodzi ndi Otsalira.”
Ngati akadatuluka nanu pamodzi, sakadakuonjezerani chilichonse koma chisokonezo ndi kuyenda mwa ukazitape pakati panu ndicholinga chokufunirani chisokonezo, ndipo mwa inu alipo akuwamvelera, ndipo Allah Ngodziwa za oipa.
Palibe chomwe chidaletsa kulandiridwa kwa zopereka zawo koma chifukwa chakuti iwo sadakhulupirire Allah ndi Mtumiki Wake; ndiponso sapita kopemphera koma mwaulesi; ndipo sapereka chopereka koma monyinyirika.
Ndipo chisakudolole chuma chawo kapena ana awo. Ndithu Allah akufuna kuwalanga nazo pa moyo wa pa dziko lapansi, ndi kuti mitima yawo ichoke ali osakhulupirira.
Ndipo ngati iwo akadakondwera ndi chimene Allah ndi Mtumiki Wake wawapatsa, nanena: “Allah watikwanira. Posachedwapa Allah ndi Mtumiki Wake atipatsa zabwino Zake. Ndithu ife tikufunitsitsa kwa Allah.” (Ndiye kuti Allah akadawapatsa zambiri).
Ndithu sadaka (za Zakaati) ndi za mafukara, masikini, ogwira ntchito yosonkhetsa sadakazo, owalimbitsa mitima yawo (pa Chisilamu amene alowa kumene), kuombolera akapolo (kuti akhale afulu), kuthandizira amene ali m’ngongole; kuzipereka pa njira ya Allah; ndi kuwapatsa a paulendo (omwe alibe choyendera). Ili ndi lamulo lochokera kwa Allah, ndipo Allah Ngodziwa kwabasi, Ngwanzeru zakuya.[211]
[211] M’ndime iyi Allah akutifotokozera magulu a anthu amene ngoyenera kuwagawira chuma cha Zakaat. Iwo ndi awa:- 1. Osauka amene sangagwire ntchito nkudzipezera okha chakudya (mafukara). 2. Osauka amene alibe zokwanira pa zofunikira pa moyo wawo (Masikini). 3. Amene akusonkhetsa chuma cha Zakaat cho omwe ntchito yawo ndiyokhayo. 4. Amene angolowa kumene m’Chisilamu omwe akuyembekezedwa kuti akapatsidwa adzalimbikitsidwa mitima yawo pa chipembedzochi. 5. Amene afuna kudziombola ku ukapolo. 6. Amene akulephera kulipira ngongole ya choonadi. 7. Amene akuchita Jihâd panjira ya Allah. 8. Wapaulendo amene alibe choyendera (ndalama zoyendera).
Ndipo alipo ena mwa iwo amene akuzunza Mneneri ponena kuti: “Uyu ndi khutu (lomvetsera nkhani iliyonse popanda kuiganizira).” Nena: “Ndi khutu labwino kwa inu.” (Mwini khutulo) amakhulupirira Allah, amakhulupirira (zonena) za okhulupirira, ndipo (iye) ndichifundo kwa amene akhulupirira mwa inu. Ndipo amene akuvutitsa Mtumiki wa Allah adzakhala ndi chilango chopweteka.
Akulumbira kwa inu potchula dzina la Allah kuti akukondweretseni (chikhalirecho akunyoza Allah ndi Mtumiki Wake), pomwe Allah ndi Mtumiki Wake ndiye wofunika kuti amkondweretse ngati iwo ngokhulupiriradi (mwachoonadi).
Ndipo utawafunsa (chifukwa ninji chipembedzo akuchichitira chipongwe)? Anena: “Ife timangosereula ndi kusewera basi (palibe china).” Nena: “Mumachitira Allah ndi Ayah (ndime) Zake ndi Mtumiki Wake zachipongwe?”
Allah walonjeza achiphamaso aamuna ndi achiphamaso aakazi ndi akafiri moto wa Jahannam, akakhala m’menemo nthawi yaitali. Umenewo ukukwanira kwa iwo (kuwalanga). Ndipo Allah wawatembelera, ndipo iwo adzapeza chilango cha nthawi zonse.
Kodi siidawadzere nkhani ya amene adalipo patsogolo pawo anthu a Nuh, Âdi ndi Samudu; anthu a Ibrahim ndi anthu a ku Madiyan ndi (anthu) a m’midzi imene idatembenuzidwa kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba? Atumiki awo adawadzera ndi zisonyezo zoonekera (koma adakana kuwatsata. Choncho, Allah adawaononga). Allah sadawachitire choipa, koma ankadzichitira okha zoipa.
Okhulupirira aamuna ndi okhulupirira aakazi, ndiabwenzi omvana pakati pawo. Amalamula zabwino ndikuletsa zoipa ndipo amapemphera Swala ndi kupereka chopereka (zakaat), ndipo amamvera Allah ndi Mtumiki Wake. Awo ndi omwe Allah adzawachitira chifundo. Ndithu Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
(Achiphamaso pambuyo pomunenera Allah ndi Mtumiki Wake mawu oipa), akulumbira potchula dzina la Allah (kuti) sadanene (zonyoza), pomwe adanenadi mawu aukafiri, ndipo akana chikhulupiliro pambuyo posonyeza Chisilamu chawo (chabodza); ndipo adatsimikiza (kuchita) zomwe sadathe kuzifika. Komatu sadaone choipa (m’kudza kwa Chisilamu), koma kuti Allah ndi Mtumiki Wake adawalemeretsa ndi zabwino zake. Choncho Ngati alapa, zikhala zabwino kwa iwo. Ndipo ngati anyoza, Allah awalanga ndi chilango chowawa pa moyo wa pa dziko lapansi ndi patsiku lachimaliziro. Ndipo sadzakhala ndi mtetezi ngakhale aliyense wowapulumutsa pa dziko.
(E iwe Mtumiki!) Uwapemphere chikhululuko (achiphamaso) kapena usawapemphere, (zonsezo nchimodzimodzi). Ngakhale utawapemphera chikhululuko chochuluka kwabasi mokwanira makumi asanu ndi awiri (70) Allah sangawakhululukire. Zimenezo nchifukwa chakuti iwo amkana Allah ndi Mtumiki Wake. Ndipo Allah satsogolera anthu ophwanya malamulo (Ake).
[212] Anthu achinyengo (achiphamaso) adakana kupita naye limodzi Mtumiki (s.a.w) ku nkhondo namasangalalira kukhala kwawoko. Ndipo apa Allah akuwauza kuti asangalale ndi kuseka pang’ono. Koma adzalira ndi kukukuta mano nthawi yaitali.
Ndipo chisakudolole chuma chawo kapena ana awo. Ndithu Allah akufuna kuwalanga ndi zimenezo pa dziko lapansi, ndi kuti mizimu yawo ichoke ali osakhulupirira.
Ndipo Sura ikavumbulutsidwa (yonena kuti): “Mkhulupirireni Allah ndi kumenya nkhondo (chifukwa cha chipembedzo Chake) pamodzi ndi Mtumiki Wake,” opeza bwino mwa iwo akukupempha chilolezo (kuti asapite ku nkhondo), ndipo akuti: “Tisiye tikhale pamodzi ndi okhala (otsalira m’mbuyo).”
Koma Mtumiki ndi amene akhulupirira pamodzi ndi iye amenya nkhondo ndi chuma chawo ndi matupi awo. Iwowo ndiwo opeza zabwino, ndiponso iwowo ndiwo opambana.
Ndipo adza eni madandaulo (owona) mwa anthu akumidzi (omwe ndi Asilamu) kuti awapatse chilolezo (chosapita ku nkhondo). Koma adakhala (popanda kupempha chilolezo kwa Mtumiki) amene amunamiza Allah ndi Mtumiki Wake. (Amenewa ndi achiphamaso omwe amadzitcha kuti ndi Asilamu pomwe sadali Asilamu). Mwa iwo amene sadakhulupirire Allah chiwapeza chilango chopweteka.
Palibe tchimo (kusapita kunkhondo) kwa amene ali ofooka (pachilengedwe chawo), ngakhale kwa odwala, ngakhale kwa omwe sapeza chothandiza (pa ulendo ngakhale chosiira akubanja lawo) ngati iwo ali ndi cholinga chabwino pa Allah ndi Mtumiki Wake. Palibe njira (yowadzudzulira) amene akuchita zabwino. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni zedi.
Ndiponso (palibe tchimo) kwa amene akukudzera kuti uwatenge (kupita ku nkhondo) iwe uunena: “Ndilibe choti ndikunyamulireni,” nabwerera maso awo akutuluka misozi chifukwa cha kudandaula posapeza zimene zingawathandize pa ulendowo.
Akudandaulirani madandaulo mukabwerera kwa iwo (ndi kukumana nawo). Nena: “Musapereke madandaulo; sitikukhulupirirani. Allah watifotokozera kale nkhani zanu. Posachedwa Allah ndi Mtumiki Wake aona zochita zanu, kenako muzabwezedwa (pambuyo pa imfa) kwa Wodziwa zamseri ndi zoonekera. Choncho, Iye adzakufotokozerani zimene mudali kuchita.”
Mukabwerera kwa iwo, adzalumbira m’dzina la Allah kwa inu kuti muwasiye (musawachite kanthu). Choncho, apatukireni. Ndithu iwo ndiuve ndipo malo awo ndi ku Jahannam. Iyi ndi mphoto ya zomwe adali kupeza (kuchokera m’zochita zawo zoipa).
Arabu a kumizi ngoyipitsitsa pa kusakhulupirira ndi uchiphamaso ndiponso ngoyenera kusazindikira malire a zomwe Allah wavumbulutsa kwa Mtumiki Wake. Komatu Allah Ngodziwa kwambiri, Ngwanzeru zakuya.
Ndipo alipo ena mwa Arabu a kuchimizi omwe amachichita chimene akupereka pa njira ya Allah ngati dipo (laulere lopanda phindu), ndikumadikira kwa inu kuti miliri ikupezeni. Miliri yoipa ili pa iwo; (iwapeza okha). Ndipo Allah Ngwakumva (nkhani iliyonse), Wodziwa (chilichonse).
Ndipo alipo ena mwa Arabu a kuchimizi omwe akukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro ndipo zomwe akupereka (pa njira ya Allah) amazichita monga chodziyandikitsira nacho kwa Allah, ndi (chowachititsa kuti apeze) mapemphero a Mtumiki. Tamverani! Ndithu zimenezo ndizinthu zowayandikitsa kwa Allah. Allah adzawalowetsa ku Mtendere Wake. Ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Ndipo ena mwa Arabu a kuchimizi omwe akukhala m’mphepete mwanu (m’mphepete mwa mzinda wa Madina) alipo achiphamaso (achinyengo), ndiponso eni mzinda wa Madina aphunzira ukatswiri wachinyengo (kotero kuti) sukuwadziwa, Ife tikuwadziwa. Tiwalanga kawiri (pa dziko lapansi) ndipo kenako adzabwezedwa kuchilango chachikulu (pa tsiku lachimaliziro).
Tenga sadaka (Zakaat) m’chuma chawo kuti uwayeretse nayo (kumachimo ndi umbombo) ndi kuti uwatukulire nayo ulemelero wawo kwa Allah; ndipo apemphere (zabwino ndi chiongoko). Ndithu mapemphero ako kwa iwo ndimpumulo. Ndipo Allah Ngwakumva, Wodziwa (chilichonse).
Kodi sadziwa kuti Allah ndi Yemwe amalandira kulapa kwa akapolo Ake, ndi kulandira sadaka, ndikuti Allah ndi Mwini kulandira kulapa mochuluka ndiponso Wachisoni chosatha?
Ndipo auze: “Gwirani ntchito; Allah ndi Mtumiki Wake ndi okhulupirira aona ntchito yanuyo posachedwa. Ndipo (kenako) mudzabwezedwa kwa Wodziwa zamseri ndi zoonekera poyera. Choncho adzakuuzani zonse (zimene) mudali kuchita.”
Ndipo (alipo achiphamaso ena) amene adamanga msikiti ndi cholinga chodzetsa masautso ndi (kulimbikitsa) kusakhulupirira Allah ndi kuwagawa okhulupirira (mu umodzi wawo) ndi kuupanga kukhala msasa wa omwe adamthira nkhondo Allah ndi Mtumiki Wake kale. Ndithu alumbira (ndikunena): “Sitidali ncholinga china (pomanga msikitiwo) koma ubwino.” Koma Allah akuikira umboni kuti iwo ngabodza.
Kodi amene wakhazikitsa maziko a chomanga chake chifukwa choopa Allah ndi kufunafuna chiyanjo (Chake), sindiye wabwino, kapena Yemwe wakhazikitsa maziko a chomanga chake m’mphepete mwa dzenje (lakuya) lomwe dothi lake likugumukira (m’dzenjemo) ndipo nkugwa pamodzi naye m’moto wa Jahannam, (ameneyu ndiye wabwino)? Ndithudi, Allah saongolera anthu ochita zoipa.
Ndithu Allah wagula kwa okhulupirira moyo wawo ndi chuma chawo (kuti apereke moyo wawo ndi chuma chawo pomenya nkhondo pa njira ya Allah) kuti iwo alandire Munda wamtendere. Akumenya nkhondo pa njira ya Allah, ndipo akupha ndi kuphedwa. Ili ndi lonjezo loona lokakamizika pa Iye lomwe likupezeka m’buku la Taurati, Injili ndi Qur’an. Kodi ndani wokwaniritsa lonjezo lake kuposa Allah? Choncho kondwerani ndi kugulitsa kwanu komwe mwagulitsana Naye. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.
Nkosayenera kwa Mneneri ndi amene akhulupirira kuwapemphera chikhululuko opembedza mafano ngakhale atakhala abale awo, pambuyo poonekera kwa iwo kuti iwowo ndi anthu a ku Moto.
Ndipo sikudali kupempha chikhululuko kwa Ibrahim kuwapemphera bambo wake koma chifukwa cha lonjezo lomwe adamulonjeza. Koma pamene zidaonekera kwa iye poyera kuti iwo (bambo wake) ndi mdani wa Allah, adadzipatula kwa iwo. Ndithudi, Ibrahim adali wochulukitsa kupempha Allah modzichepetsa, woleza mtima.
Ndipo Allah sangasokeretse anthu (ndi kupititsa chilango pa iwo) pambuyo powaongolera ku Chisilamu; koma pokhapokha atawonetsa poyera kwa iwo zimene zingafunike kuzipewa. Ndithu Allah Ngodziwa chilichonse.
Ndithu Allah wafunira zabwino Mtumiki Wake ndi Amuhajirina ndi Answari amene adamtsatira iye (Muhammad {s.a.w}) m’nthawi yamasautso (pokamenyana ndi Aroma pankhondo ya Tabuk), nthawi yomwe mitima ya ena a iwo idatsala pang’ono kupotoka (kutsata machitidwe achikafiri); kenako Allah adawatembenukira ndi chifundo. Ndithu Iye (Allah) kwa iwo Ngodekha, Ngwachisoni chosatha.[213]
[213] Nkhondo ya Tabuk idachitika m’mwezi wa Rajab m’chaka cha chisanu nchinayi chakusamuka. Idali pakati pa Asilamu ndi Aroma. Gulu lankhondo la Chisilamu lomwe lidapita kunkhondo linkatchedwa “Gulu la Masautso” chifukwa kukonzekera kwa nkhondoyi kudachitika m’nyengo ya masautso kwa anthu. Ndipo pamene Mtumiki adafika ku Tabuk, adadza msogoleri wa gulu lankhondo la Aroma wotchedwa Yohane namvana kuti pasakhale nkhondo. M’malo mwake iye adzapereka “Jiziya” (msonkho), motero Mtumiki adabwerera ku Madina. lyi idali nkhondo yake yomaliza.
Nkosayenera kwa anthu a mu mzinda wa Madina ndi amene ali m’mphepete mwawo, mwa Arabu a kuchimizi, kutsalira m’mbuyo mwa Mtumiki wa Allah (poleka kutsagana naye ku nkhondo), ndiponso nkosayenera kwa iwo kudzikonda okha kuposa iye (Mtumiki). Zimenezo nchifukwa chakuti iwo silingaapeze ludzu kapena mavuto kapena njala pa njira ya Allah, ndipo sangaponde malo owakwiitsa osakhulupirira, ndipo sangampatse mdani chompatsa chilichonse chopweteka koma kulembedwa kwa iwo pa zimenezo (kuti achita) ntchito yabwino. Ndithu Allah sawononga malipiro a ochita zabwino.
Nkosafunika kwa okhulupirira kutuluka onse (m’midzi yawo kupita ku Madina ndi kusiya midzi yopanda anthu). Nchifukwa ninji silituluka gulu m’fuko lililonse mwa iwo (ndikupita ku Madina kwa Mtumiki) kukaphunzira bwino za Chipembedzo, ndipo akawachenjeze anthu awo akazabwerera kwa iwo kuti aope.
E inu amene mwakhulupirira! Menyani nkhondo ndi awo osakhulupirira amene ali pafupi nanu, ndipo apeze kuuma mtima mwa inu. Ndipo dziwani kuti ndithu Allah ali pamodzi ndi oopa (Iye).
Ndipo nthawi zonse sura (yatsopano) ikavumbulutsidwa, alipo mwa iwo (achiphamaso) amene akunena: “Ndani mwa inu sura iyi yamuonjezera chikhulupiliro?” Koma amene akhulupirira yawaonjezera chikhulupiliro ndipo iwo akukondwera.
Ndithu wakudzerani Mtumiki wochokera mwa inu. Zimamudandaulitsa iye zomwe zikukuvutitsani; iye ngoikira mtima pa inu pokufunirani zabwino; ndipo pa okhulupirira ngodekha ndiponso ngwachisoni.
Koma ngati (iwo osakhulupirira) apitiriza kunyoza, nena: “Allah wandikwanira (palibe vuto lingapezeke kuchokera kwa inu) palibe woti nkupembedzedwa koma Iye basi. Ndatsamira kwa Iye. Ndipo Iye, ndi Bwana wa Arsh (mpando wachifumu) yaikulu!”
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
Arama sonuçları:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".