Ndipo ungawaganizire kuti ali maso pomwe iwo ali mtulo, uku tikuwatembenuzira mbali yakumanja ndi yakumanzere (kuti nthaka isadye matupi awo), ukunso galu wawo atatambasula miyendo yake (yakutsogolo) pakhomo. Ngati ukadawaona ukadatembenuka kuwathawa; ndipo ndithu ukadadzadzidwa mantha ndi iwo.
“Ndithu iwo akakudziwani (pamene mulipa), akugendani ndi miyala; apo ai akubwezerani ku chipeinbedzo chawo (chopotoka), zikatero ndiye kuti simudzapambananso mpaka kalekale.”
(Ena) akhala akunena (kuti) adali anthu atatu, wachinayi ndi galu wawo; ndipo (ena) akuti adali asanu, wachisanu ndichimodzi ndigalu wawo. (Akunena) mwakungoganizira chabe zomwe sakuzidziwa; ndipo (ena) akuti adali asanu ndi awiri, ndipo wachisanu ndi chitatu ndi galu wawo. Nena: “Mbuye wanga ndiye akudziwa bwinobwino za chiwerengero chawo. Palibe amene akudziwa (za iwo) koma ndi ochepa chabe.” Choncho usatsutsane nawo za iwo, kupatula kutsutsana kwa pa zinthu zodziwika, ndipo usamfunse aliyense mwa iwo za iwo.
Nena: “Allah akudziwa bwinobwino nyengo imene (iwo) adakhala; zobisika za kumwamba ndi za pansi nza Iye (Allah basi); taona Allah kuonetsetsa! Taona Allah kumvetsetsa! (Allah Ngoona chilichonse, ndipo Ngwakumva chilichonse). Ndipo iwo alibe mtetezi popanda Iye (Allah); ndipo Iye sagawira aliyense udindo Wake wakulamula.
Ndipo werenga zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe za m’buku la Mbuye wako, palibe amene angathe kusintha mau Ake, ndipo nawe sungapeze potsamira ndi pothawira (kuti Allah asakupeze.)
Ndipo dzikakamize kukhala pamodzi ndi amene akupempha Mbuye wawo m’mawa ndi madzulo uku akufunafuna nkhope Yake (chiyanjo Chake), ndipo maso ako asachoke pa iwo ndi (kuyang’ana ena) ncholinga chofuna zokongoletsa za moyo wa dziko lapansi; ndipo usamumvere amene mtima wake tauiwalitsa kutikumbukira ndikumangotsatira zilakolako zake, ndipo zinthu zake nkukhala zotaika (zosalongosoka).[259]
[259] Ndime iyi idavumbulutsidwa pamene Uyaina Bun Huswaini ndi mnzake adadza kwa Mtumiki ndi kumpeza atakhala pamodzi ndi omtsatira (Maswahaba) osauka monga: Ammaru, Suhaibu ndi Bilali ndi ena onga iwo. Iwo adati kwa Mtumiki (s.a.w): “Ukadawapirikitsa anthu wambawa, ndiye kuti tikadakhala nawe nkumamvera zimene ukulalikira. Koma ife tikunyansidwa ndi ulaliki wako poona kuti nthawi zonse ukukhala ndi anthu onyozeka amene simabwana.” Choncho Qur’an idatsika kumuuza Mtumiki (s.a.w) kuti: “Usawathamangitse anthu omwe akupempha Allah m’mawa ndi madzulo ngakhale kuti ndionyozeka.”
Ndipo apatse fanizo la anthu awiri mmodzi wa iwo tidampangira minda iwiri ya mphesa ndi kuizunguliza ndi mitengo ya kanjedza; ndipo pakati pa iyo tidaikapo mbewu (zina).
Ndipo iye adali ndi chuma (china) nati kwa mnzakeyo mokambirana naye: “Ine ndili ndi chuma chambiri kuposa iwe, (ndilinso) ndi mphamvu zambiri chifukwa cha onditsatira (omwe ndili nawo).”
Mnzake adanena kwa iye mokambirana naye: “Kodi ukumukana yemwe adakulenga ndi dongo, kenako ndi dontho lamadzi a umuna ndiponso adakupanga kukhala munthu wolingana?”
“Ndipo pamene umalowa m’munda wako ukadanena kuti izi ndi zimene wandifunira Allah, mphamvu sizikadapezeka koma kupyolera mwa Allah (zikadakhala zabwino kwa iwe). Ngati ukundiona ine kuti ndili ndi chuma chochepa ndi ana ochepa kuposa iwe (koma sindisiya kutamanda Allah).”
Chuma ndi ana ndizokometsera za moyo wa dziko lapansi, koma ntchito zabwino zopitirira ndizo zabwino kwa Mbuye wako, monga mphoto ndi chiyembekezo chabwino.
Ndipo (kumbuka) pamene tidawauza angelo: “Mchitireni sijida Adam (mugwadireni momulemekeza).” Onse adachitadi sijida kupatula Iblis. Iye adali mmodzi wa ziwanda, ndipo adatuluka m’chilamulo cha Mbuye wake. Kodi iye ndi mbumba yake mukuwalola kukhala abwenzi (anu) kusiya Ine, pomwe iwo ndiadani anu? Taonani kuipa kusintha kwa anthu oipa!
(Khidhiri) adati: “Awa ndiwo malekano pakati pa ine ndi iwe. Tsopano ndikuuza tanthauzo la zomwe sudathe kupirira nazo.”[261]
[261] Mtumiki Muhammad (s.a.w) adati pankhani iyi ya Musa ndi Khidhiri: “Allah amchitire chifundo Musa. Ndikulakalaka kuti iye akadapilira kukhala limodzi ndi mnzakeyo, akadaona zodabwitsa, ndipo Allah akadatisimbira zambiri za iwo.”
Mpaka pomwe adafika kumlowero kwa dzuwa (ku maiko a kuzambwe), adaliona (ngati) likulowa pa dziwe la matope ambiri. Ndipo pompo adapeza anthu; tidati: “E iwe Thul-Qarnain! Alange, kapena achitire zabwino.”
(Iye) adati: “Ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wanga; koma likadzafika lonjezo la Mbuye wanga (kudza kwa Qiyâma), adzachiswanyaswanya; ndipo lonjezo la Mbuye wanga nloona.”
“Iwo ndi omwe khama lawo lataika m’moyo wa pa dziko lapansi, pomwe iwowo akuganiza kuti akuchita zabwino”.[263]
[263] M’ndime iyi akutiuza kuti amene sadakhulupirire Allah, pa tsiku lachimaliziro ndiye kuti zonse zochita zawo zidzakhala zowonongeka. Ntchito zabwino za munthu kuti zikalandiridwe kwa Allah, poyamba akhulupirire Allah ndiponso akhulupirire kuti tsiku lachimaliziro lilipo. Koma ngati sakhulupilira, ndiye kuti zochita zake sizikayesedwa pasikelo koma akangomponya kung’anjo yamoto. Pankhaniyi Mtumiki (s.a.w) adati: “Tsiku la Qiyâma padzabwera munthu wamtali, wakudyabwino, wakumwa zomwaimwa, koma kwa Allah adzakhala wopepuka wosafanana ngakhale ndikulemera kwa phiko la udzudzu.” Hadisiyi adainena ndi Al -Hafizi Ibn Hajar m’buku la Fatuhul Bari, Volume 8 tsamba la 324.
Nena: “Ngakhale nyanja ikadakhala inki yolembera mawu a Mbuye wanga, nyanjayo ikadatha mawu a Mbuye wanga asadathe, ngakhale tikadabweretsa nyanja ina ndikuionjezera pa iyo (nyanjazo zikadatha, mawu a Allah akalipobe).”
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
ئىزدەش نەتىجىسى:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".