“Adzandilowe chokolo (pa nzeru za utsogoleri ndi uneneri) ndikulowanso ufumu wa banja la Ya’qub; ndipo Mbuye wanga nchiteni kukhala woyanjidwa (ndi Inu)”
Ndipo mtchule Mariya m’buku ili pamene adadzipatula ku anthu a kubanja lake (ndikunka) kumalo ambali ya kummawa.[265]
[265] M’sura iyi muli nkhani zododometsa. Yoyamba njakubadwa kwa Yahya (Yohane) yemwe adabadwa kuchokera kwa nkhalamba ziwiri zotheratu; pomwe mwamuna adali ndi zaka 120 ndipo mkazi adali ndi zaka 98. Choncho kubadwa kwa Yahya kudali kododometsa. Koma kubadwa kwa Isa (Yesu) ndikumene kudali kododometsa zedi poti iye anabadwa kwa namwali wosakwatiwa. Tero iye anamubereka popanda mwamuna. Zonsezi Allah adafuna kuwadziwitsa anthu ndi kuwatsimikizira kuti Iye ali ndi mphamvu zolengera munthu popanda mwamuna.
Ndipo adadzitsekereza kwa iwo (kuti athe kutumikira Allah mokwanira), choncho tidatuma Mzimu Wathu (Mngelo Gabriel) kwa iye ndipo adadzifanizira kwa iye monga munthu weniweni.
(Mngelo) adati: “Ndimomwemo.” Mbuye Wako akuti: “Zimenezi kwa Ine nzosavuta. Ndipo timchita kukhala chozizwitsa kwa anthu ndi chifundo chochokera kwa Ife. (Nchifukwa chake tachita izi;) ndipo ichi ndi chinthu chimene chidalamulidwa kale. (Chichitika monga momwe Allah adafunira).”
[266] Izi zidachitika pamene Gabriele adauzira m’thumba la chovala cha Mariya. Ndipo mpweya udafika mpaka m’mimba mwake. Choncho atakhala ndi pakati anadzipatula kwa anthu kunka kutali ali ndi pakati pa mwana wakeyo kuti anthu angamdzudzule pokhala ndi mimba yosadziwika mwamuna wake.
Choncho udye ndi kumwa ndikutonthoza diso lako, (khala ndi mpumulo wabwino). Ndipo ukaona munthu aliyense (akafunsa za mwanayo), nena: “Ndithu ine ndalonjeza kwa (Allah) Mwini chifundo chambiri kusala kuti lero sindiyankhula ndi munthu aliyense.”
“E iwe mlongo wa Harun! Bambo wako sadali munthu woipa, ngakhalenso mayi wako sadali wachiwerewere.”[268]
[268] Katada adaati: Haaruna adali munthu wolungama kwambiri mu mtundu wa ana alsraeli. Adali wotchuka kwambiri pazakulungama. Choncho ana a Israeli adaili kufanizira Mariya ndi Haaruna chifukwa cha kulungama kwake; sikuti Mariya adali mlongo wake weniweni wa Haaruna yemwe adali m’bale wa Musa. Pakati pa Mariya ndi Haaruna padapita zaka chikwi chimodzi.
“Ndipo mtendere uli pa ine kuyambira tsiku lomwe ndidabadwa ndi tsiku limene ndidzamwalira, ndi tsiku limene ndidzaukitsidwa (kwa akufa tsiku la chiweruziro) ndikukhala ndi moyo.”
Sikoyenera kwa Allah kudzipangira mwana. Iye (Allah) wapatukana ndi zimenezi. Akafuna chinthu, amangonena kwa chinthucho: “Chitika,” ndipo icho chimachitikadi.
(Isa (Yesu) adati:) “Ndipo ndithu Allah ndi Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu. Choncho mpembedzeni; iyi ndinjira yolunjika (yokufikitsani ku mtendere.)[269]
[269] Umu ndimomwe Isa (Yesu) adanenera za ukapolo wake kwa Allah. Iye sadali Mulungu kapena mwana wa Mulungu, kapena mmodzi wa atatu monga momwe Akhrisitu amanenera. Koma iye adali kapolo wa Allah ndiponso Mtumiki Wake. Allah adamulenga mwa mayi popanda bambo kuti akhale chisonyezo chosonyeza mphamvu za Allah zoposa.
Koma magulu (a Akhrisitu ndi Ayuda) adapatukana pakati pawo; (ena adamuyesa Isa (Yesu) kuti ndimwana wa Mulungu, ndipo ena adamuyesa Mulungu weniweni, pomwe Ayuda ankati ndi mwana wobadwa m’njira ya chiwerewere), choncho chilango chaukali chidzatsimikizika pa amene sadakhulupirire pokaonekera tsiku lalikululo (kwa Allah).
Ndipo achenjeze (anthu) za tsiku la madandaulo, pamene chiweruzo chidzagamulidwa, (abwino kulowa ku munda wamtendere, oipa kulowa ku Moto); koma iwo (pano pa dziko lapansi) ali m’kusalabadira ndipo sakhulupirira.[270]
[270] Tsiku la Qiyâma (chimaliziro), anthu oipa adzadandaula kwambiri. Tsiku limenelo kwa iwo lidzakhala tsiku lamadandaulo okhaokha, osatinso chinachake. M’buku la swahihi la Musilim muli hadisi ya Abi Saidi Khuduriyi (r.a). Iye adati: Ndithu Mtumiki (s.a.w) adati: “Pamene anthu olungama adzalowa ku munda wa mtendere ndipo anthu oipa ku Moto, imfa idzadza tsiku la chimalizirolo. Idzaoneka ngati nkhosa yabwino. Ndipo idzaikidwa pakati pa Munda wa mtendere ndi Moto. Tsono kudzanenedwa: “E inu eni munda wa mtendere! Kodi ichi mukuchidziwa?” Onse adzatukula makosi kuyang’ana nkuzati: “Inde iyo ndi imfa.” Kenako kudzanenedwa: “E inu anthu a ku Moto! Kodi ichi mukuchidziwa?” Onse adzatukula makosi awo kuyang’ana nkuzati: “Inde iyo ndi imfa.” Ndipo kudzalamulidwa kuti izingidwe. Kenako kudzanenedwa: “E inu eni munda wa mtendere! Khalani muyaya m’menemo, palibe imfanso. Ndiponso inu eni Moto khalani muyaya mmenemo palibe imfanso.” Kenako Mtumiki (s.a.w) adawerenga Ayah (ndime) yakuti: “Achenjeze za tsiku lamadandaulo aakulu....”
E bambo wanga! Ndithu ine ndikuopa kuti chilango chingakukhudzeni chochokera kwa (Allah) Mwini chifundo chambiri, ndipo potero mdzakhala bwenzi la satana.”
(Bambo wake) adati: “Kodi iwe ukuda milungu yanga, E iwe Ibrahim? Ngati susiya (kunyoza milungu yanga) ndikugenda ndi miyala; choncho ndichokere kwa nthawi yaitali (tisaonanenso).”
Iwowo ndi omwe adawadalitsa Allah, mwa aneneri mu ana a Adam, ndi (m’mbumba ya) amene tidawatenga pamodzi ndi Nuh (m’chombo), ndi m’mbumba ya Ibrahim ndi Israyeli, ndi amene tidawaongola ndi kuwasankha. Ndipo zikawerengedwa kwa iwo Ayah za (Allah) Mwini chifundo chambiri, amagwa ndi kulambira uku akulira.
(Mtumiki adapempha Gabriel kuti akhale akum’bwerera pafupipafupi. Ndipo Gabriel adamuuza kuti): “Ndipo sitimatsika koma mwa lamulo la Mbuye wako. Zapatsogolo pathu ndi zapambuyo pathu ndi zapakati pa zimenezi zonse Nzake (akuzidziwa bwinobwino). Ndipo Mbuye wako sali woiwala.”
“Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pa izo: Choncho mpembedze Iye basi. Ndipo pitiriza ndikupirira popembedza Iye. Kodi ukumudziwa (wina) yemwe ali wofanana Naye (Allah)?”
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
ئىزدەش نەتىجىسى:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".