Check out the new design

قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا * - تەرجىمىلەر مۇندەرىجىسى


مەنالار تەرجىمىسى سۈرە: ئەنئام   ئايەت:
۞ وَإِذۡ قَالَ إِبۡرَٰهِيمُ لِأَبِيهِ ءَازَرَ أَتَتَّخِذُ أَصۡنَامًا ءَالِهَةً إِنِّيٓ أَرَىٰكَ وَقَوۡمَكَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
Ndipo (kumbukirani) pamene Ibrahim adauza bambo ake, Azara: “Kodi mukupanga mafano kukhala milungu? Ndithu ine ndikukuonani inu ndi anthu anu kuti muli m’kusokera koonekera.”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَكَذَٰلِكَ نُرِيٓ إِبۡرَٰهِيمَ مَلَكُوتَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلِيَكُونَ مِنَ ٱلۡمُوقِنِينَ
Ndipo momwemo tidamuonetsa Ibrahim ufumu wa kumwamba ndi pansi (kuti ngwa Allah) kuti akhale m’modzi mwa otsimikiza.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
فَلَمَّا جَنَّ عَلَيۡهِ ٱلَّيۡلُ رَءَا كَوۡكَبٗاۖ قَالَ هَٰذَا رَبِّيۖ فَلَمَّآ أَفَلَ قَالَ لَآ أُحِبُّ ٱلۡأٓفِلِينَ
Ndipo pamene kunam’dera adaona nyenyezi. Adati (mwadaladala kuti abutse nzeru za opembedza mafano): “(Nyenyezi) iyi ndiye mbuye wanga.” Pamene idalowa, adati: “Sindikonda (milungu) yomalowa, (yomasowa, yakutha).”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
فَلَمَّا رَءَا ٱلۡقَمَرَ بَازِغٗا قَالَ هَٰذَا رَبِّيۖ فَلَمَّآ أَفَلَ قَالَ لَئِن لَّمۡ يَهۡدِنِي رَبِّي لَأَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلضَّآلِّينَ
Pamene adaona mwezi ukutuluka, adati: “Uyu ndiye mbuye wanga.” Koma pamene udalowa, adati: “Ngati Mbuye wanga sandiongolera, ndithudi, ndikhala m’gulu la anthu osokera.”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
فَلَمَّا رَءَا ٱلشَّمۡسَ بَازِغَةٗ قَالَ هَٰذَا رَبِّي هَٰذَآ أَكۡبَرُۖ فَلَمَّآ أَفَلَتۡ قَالَ يَٰقَوۡمِ إِنِّي بَرِيٓءٞ مِّمَّا تُشۡرِكُونَ
Pamene adaona dzuwa likutuluka, adati: “Uyu ndiye mbuye wanga; uyu ngwamkulu kwabasi.” Koma pamene lidalowa, adati: “E inu anthu anga! Ine ndili kutali ndi zomwe mukumphatikiza nazo (Allah).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
إِنِّي وَجَّهۡتُ وَجۡهِيَ لِلَّذِي فَطَرَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ حَنِيفٗاۖ وَمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ
Ndithu ine ndalungamitsa nkhope yanga kwa Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, ndapendekera kwa Iye Yekha. Ndipo ine sindili mwa om’phatikiza (Allah ndi mafano).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَحَآجَّهُۥ قَوۡمُهُۥۚ قَالَ أَتُحَٰٓجُّوٓنِّي فِي ٱللَّهِ وَقَدۡ هَدَىٰنِۚ وَلَآ أَخَافُ مَا تُشۡرِكُونَ بِهِۦٓ إِلَّآ أَن يَشَآءَ رَبِّي شَيۡـٔٗاۚ وَسِعَ رَبِّي كُلَّ شَيۡءٍ عِلۡمًاۚ أَفَلَا تَتَذَكَّرُونَ
Ndipo anthu ake adakangana naye (pomuuza kuti: “Bwanji ukusiya chipembedzo chamakolo ako; uona malaulo”). (Iye) adati: “Kodi Mukukangana nane pa za Allah pomwe Iye wanditsogolera? Ndipo Sindingaope zimene mukumphatikiza Naye, kupatula Mbuye wanga akafuna chinthu, (apo chiyenera kuchitika). Mbuye wanga akudziwa chinthu chilichonse bwinobwino. Bwanji simulalikika?”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَكَيۡفَ أَخَافُ مَآ أَشۡرَكۡتُمۡ وَلَا تَخَافُونَ أَنَّكُمۡ أَشۡرَكۡتُم بِٱللَّهِ مَا لَمۡ يُنَزِّلۡ بِهِۦ عَلَيۡكُمۡ سُلۡطَٰنٗاۚ فَأَيُّ ٱلۡفَرِيقَيۡنِ أَحَقُّ بِٱلۡأَمۡنِۖ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ
“Ndipo ndingaope chotani zomwe mwaziphatikiza (ndi Allah) pomwe inu simuopa kuti mukumphatikiza Allah (ndi mafano) omwe Allah sadawatsitsire pa inu umboni (kuti muziwapembedza). Choncho ndi gulu liti m’magulu awa awiri (langa kapena lanu) loyenera koposa kupeza chitetezo? Ngati inu mudziwa (zinthu).”
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
 
مەنالار تەرجىمىسى سۈرە: ئەنئام
سۈرە مۇندەرىجىسى بەت نومۇرى
 
قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا - تەرجىمىلەر مۇندەرىجىسى

خالىد ئىبراھىم بېيتالا تەرجىمىسى.

تاقاش