Check out the new design

የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ * - የትርጉሞች ማዉጫ


የይዘት ትርጉም ምዕራፍ: አዝ ዙኽሩፍ   አንቀጽ:
وَمَا نُرِيهِم مِّنۡ ءَايَةٍ إِلَّا هِيَ أَكۡبَرُ مِنۡ أُخۡتِهَاۖ وَأَخَذۡنَٰهُم بِٱلۡعَذَابِ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ
Ndipo chisonyezo chilichonse chomwe tidawasonyeza chidali chachikulu kuposa chinzake (komabe sadakhulupirire). Ndipo tidawalanga ndi chilango kuti abwelere (kwa Ife).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَقَالُواْ يَٰٓأَيُّهَ ٱلسَّاحِرُ ٱدۡعُ لَنَا رَبَّكَ بِمَا عَهِدَ عِندَكَ إِنَّنَا لَمُهۡتَدُونَ
Ndipo adati (kwa Mûsa): “E iwe wamatsenga! Tipemphere kwa Mbuye wako pa chomwe adakulonjeza; ndithu ife tiongoka, (tikhulupirira).”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَلَمَّا كَشَفۡنَا عَنۡهُمُ ٱلۡعَذَابَ إِذَا هُمۡ يَنكُثُونَ
Choncho, pamene tidawachotsera chilangocho, basi iwo adayamba kuswa pangano.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَنَادَىٰ فِرۡعَوۡنُ فِي قَوۡمِهِۦ قَالَ يَٰقَوۡمِ أَلَيۡسَ لِي مُلۡكُ مِصۡرَ وَهَٰذِهِ ٱلۡأَنۡهَٰرُ تَجۡرِي مِن تَحۡتِيٓۚ أَفَلَا تُبۡصِرُونَ
Ndipo Farawo adaitana anthu ake, adati: “E inu anthu anga! Kodi ulamuliro wa mu Iguputo siwanga pamodzi ndi mitsinje iyi imene ikuyenda pansi panga (pa nyumba zanga?) Kodi simukuona?”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
أَمۡ أَنَا۠ خَيۡرٞ مِّنۡ هَٰذَا ٱلَّذِي هُوَ مَهِينٞ وَلَا يَكَادُ يُبِينُ
“Kodi kapena ine sindine woposa uyu (Mûsa) wonyozeka, ndipo sangathe kuyankhula momveka?”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَلَوۡلَآ أُلۡقِيَ عَلَيۡهِ أَسۡوِرَةٞ مِّن ذَهَبٍ أَوۡ جَآءَ مَعَهُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ مُقۡتَرِنِينَ
“Nanga bwanji sadavekedwe zibangiri zagolide kapena angelo kudza pamodzi ndi iye uku akumtsatira?”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَٱسۡتَخَفَّ قَوۡمَهُۥ فَأَطَاعُوهُۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمٗا فَٰسِقِينَ
Adawapeputsa anthu ake. Ndipo adamvera; iwo adali anthu otuluka mchilamulo (cha Allah).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَلَمَّآ ءَاسَفُونَا ٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡ فَأَغۡرَقۡنَٰهُمۡ أَجۡمَعِينَ
Pamene adatikwiitsa, tidawalanga ndipo tidawamiza onse mmadzi.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَجَعَلۡنَٰهُمۡ سَلَفٗا وَمَثَلٗا لِّلۡأٓخِرِينَ
Tidawachita (Farawo ndi anthu ake) kukhala chitsanzo cha okanira a pambuyo pawo ndikukhala mbiri kwa anthu amene akudza.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
۞ وَلَمَّا ضُرِبَ ٱبۡنُ مَرۡيَمَ مَثَلًا إِذَا قَوۡمُكَ مِنۡهُ يَصِدُّونَ
Ndipo pamene lidaperekedwa fanizo la mwana wa Mariya, pamenepo anthu anu adali kufuula (monyoza).[344]
[344] Fanizo lomwe likunenedwa apa ndi lomufanizira Isa (Yesu) ndi zomwe zikupembedzedwa kusiya Allah. Akafiri adamfanizira iye pambuyo povumbulutsidwa Ayah yakuti: “Ndithu inu ndi zomwe mukuzipembedza kusiya Allah ndi nkhuni za ku Jahannam.” Choncho adati Isa (Yesu) nayenso akalowa ku Moto chifukwa chakuti Akhrisitu amamupembedza kusiya Allah. Koma Allah adamyeretsa ponena kuti: “Ndithu awo amene ubwino wochokera kwa Ife watsogola kwa iwo, iwowo akatalikitsidwa ndi motowo” Choncho Isa (Yesu) sakalowa ku Moto chifukwa iye sadalamule anthu kuti amupembedze komanso sakudziwa kuti pali aliyense amene akupembedza iye.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَقَالُوٓاْ ءَأَٰلِهَتُنَا خَيۡرٌ أَمۡ هُوَۚ مَا ضَرَبُوهُ لَكَ إِلَّا جَدَلَۢاۚ بَلۡ هُمۡ قَوۡمٌ خَصِمُونَ
Ndipo adati: “Kodi milungu yathu ndi yabwino, kapena iye?” Sadamfanizire kwa iwe koma kufuna kutsutsana basi (kopanda kufuna choona). Koma iwo ndi anthu amtsutso.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
إِنۡ هُوَ إِلَّا عَبۡدٌ أَنۡعَمۡنَا عَلَيۡهِ وَجَعَلۡنَٰهُ مَثَلٗا لِّبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ
Iye sadali kanthu koma ndi kapolo amene tidampatsa mtendere; ndipo tidamchita kukhala chitsanzo (chodabwitsa) cha ana a Israyeli.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَوۡ نَشَآءُ لَجَعَلۡنَا مِنكُم مَّلَٰٓئِكَةٗ فِي ٱلۡأَرۡضِ يَخۡلُفُونَ
Ndipo tikadafuna tikadawachita angelo kukhala pa dziko mmalo mwa inu ndi kumasiirana iwo kwa iwo (kuti mudziwe kuti angelo akugonjera malamulo a Allah. Iwo siAllah).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
 
የይዘት ትርጉም ምዕራፍ: አዝ ዙኽሩፍ
የምዕራፎች ማውጫ የገፅ ቁጥር
 
የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ - የትርጉሞች ማዉጫ

በኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ ተተረጎመ

መዝጋት