Check out the new design

የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ * - የትርጉሞች ማዉጫ


የይዘት ትርጉም ምዕራፍ: አል-አንዓም   አንቀጽ:
وَمَا قَدَرُواْ ٱللَّهَ حَقَّ قَدۡرِهِۦٓ إِذۡ قَالُواْ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ عَلَىٰ بَشَرٖ مِّن شَيۡءٖۗ قُلۡ مَنۡ أَنزَلَ ٱلۡكِتَٰبَ ٱلَّذِي جَآءَ بِهِۦ مُوسَىٰ نُورٗا وَهُدٗى لِّلنَّاسِۖ تَجۡعَلُونَهُۥ قَرَاطِيسَ تُبۡدُونَهَا وَتُخۡفُونَ كَثِيرٗاۖ وَعُلِّمۡتُم مَّا لَمۡ تَعۡلَمُوٓاْ أَنتُمۡ وَلَآ ءَابَآؤُكُمۡۖ قُلِ ٱللَّهُۖ ثُمَّ ذَرۡهُمۡ فِي خَوۡضِهِمۡ يَلۡعَبُونَ
Koma (Ayuda) sadamulemekeze Allah monga momwe zikufunikira pomulemekeza pomwe adati: “Allah Sadavumbulutsepo chilichonse kwa munthu aliyense.” (Adanena izi pamene mtumiki adawauza kuti Qur’an ndi buku lomwe Allah wavumbulutsa). Nena: “Kodi ndani adavumbulutsa buku lomwe lidadza ndi Mûsa? Lomwe lidali kuunika ndi chiwongoko kwa anthu, lomwe mwalipanga kukhala magawo-magawo; zimene mwafuna kuonetsa kwa anthu mukuzionetsa. Koma zambiri mukubisa (zomwe sizigwirizana ndi zofuna zanu). Ndipo mwaphunzitsidwa (ndi iyi Qur’an) zomwe simudali kuzidziwa, inu ngakhale makolo anu. Nena: “Allah (ndi Yemwe wavumbulutsa iyi Qur’an ndi mabuku ena.”) Kenako asiye azingosewera m’kubwebweta kwawo (kopanda pake).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَهَٰذَا كِتَٰبٌ أَنزَلۡنَٰهُ مُبَارَكٞ مُّصَدِّقُ ٱلَّذِي بَيۡنَ يَدَيۡهِ وَلِتُنذِرَ أُمَّ ٱلۡقُرَىٰ وَمَنۡ حَوۡلَهَاۚ وَٱلَّذِينَ يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ يُؤۡمِنُونَ بِهِۦۖ وَهُمۡ عَلَىٰ صَلَاتِهِمۡ يُحَافِظُونَ
Ndipo ili ndibuku limene talivumbulutsa lamadalitso ochuluka; lotsimikizira zomwe zidalitsogolera. Ndikuti uchenjeze manthu wa mizinda (Makka) ndi amene ali m’mphepete mwake. Ndipo amene akukhulupirira tsiku lachimaliziro, akulikhulupirira (bukuli). Ndipo iwo Swala zawo akuzisunga bwino.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا أَوۡ قَالَ أُوحِيَ إِلَيَّ وَلَمۡ يُوحَ إِلَيۡهِ شَيۡءٞ وَمَن قَالَ سَأُنزِلُ مِثۡلَ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُۗ وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذِ ٱلظَّٰلِمُونَ فِي غَمَرَٰتِ ٱلۡمَوۡتِ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ بَاسِطُوٓاْ أَيۡدِيهِمۡ أَخۡرِجُوٓاْ أَنفُسَكُمُۖ ٱلۡيَوۡمَ تُجۡزَوۡنَ عَذَابَ ٱلۡهُونِ بِمَا كُنتُمۡ تَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ غَيۡرَ ٱلۡحَقِّ وَكُنتُمۡ عَنۡ ءَايَٰتِهِۦ تَسۡتَكۡبِرُونَ
Kodi ndani woipitsitsa koposa yemwe wampekera bodza Allah kapena wonena: “Kwavumbulutsidwa kwa ine,” pomwe sikunavumbulutsidwe kwa iye chilichonse; ndi yemwe akunena: ‘“Ndivumbulutsa monga chimene Allah wavumbulutsa.” Ukadawaona anthu ochita zoipa akuthatha ndi imfa, nawo angelo atatambasula manja awo (powamenya uku akuwauza): “Tulutsani moyo wanu; lero mulipidwa chilango chonyozetsa chifukwa cha zomwe mudali kunenera Allah popanda choonadi, ndi kudzitukumula kwanu pa zizindikiro zake.” (Ukadaona zoopsa kwabasi).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ جِئۡتُمُونَا فُرَٰدَىٰ كَمَا خَلَقۡنَٰكُمۡ أَوَّلَ مَرَّةٖ وَتَرَكۡتُم مَّا خَوَّلۡنَٰكُمۡ وَرَآءَ ظُهُورِكُمۡۖ وَمَا نَرَىٰ مَعَكُمۡ شُفَعَآءَكُمُ ٱلَّذِينَ زَعَمۡتُمۡ أَنَّهُمۡ فِيكُمۡ شُرَكَٰٓؤُاْۚ لَقَد تَّقَطَّعَ بَيۡنَكُمۡ وَضَلَّ عَنكُم مَّا كُنتُمۡ تَزۡعُمُونَ
Ndipo (tsiku la Qiyâma tidzakuuzani): “Ndithudi, mwatidzera mmodzimmodzi (payekhapayekha popanda chuma ndi ana kuti zikupulumutseni), monga mmene tidakulengerani pachiyambi. Ndipo mwasiya kumbuyo kwanu zonse zomwe tidakupatsani. Ndipo sitikuona pamodzi nanu apulumutsi anu aja, amene munkati ngothandizana (ndi Allah; ndi kuti iwo ndi apulumutsi anu). Ndithudi mgwirizano omwe udali pakati panu waduka. Ndipo zakusokonekerani zimene munkaziganizira (kuti ndi milungu).”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
 
የይዘት ትርጉም ምዕራፍ: አል-አንዓም
የምዕራፎች ማውጫ የገፅ ቁጥር
 
የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ - የትርጉሞች ማዉጫ

ተርጓሙ በኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ።

መዝጋት