ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: لقمان
آية:
 

لقمان

الٓمٓ
“Alif-Lâm-Mîm.
Kuyambira ndime 12 mpaka 20, Allah akufotokoza makhalidwe a anthu ena amene adangolowa m’Chisilamu ndi lirime lokha pomwe mitima yawo siidakhulupirire. Nthawi zambiri ankamchitira Mtumiki (s.a.w) zachinyengo. Mtumiki (s.a.w) akalamula lamulo loti akalimbane ndi adani achipembedzo cha Chisilamu, iwo amagwetsa ulesi anthu kuti asapite ku nkhondoko. Nthawi zambiri samawafunira Asilamu zabwino. Akangouzidwa kuti tiyeni ku nkhondo, amagwidwa ndi mantha.
التفاسير العربية:
تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡحَكِيمِ
“Izi ndi Ayah za buku lodzadza ndi nzeru.
التفاسير العربية:
هُدٗى وَرَحۡمَةٗ لِّلۡمُحۡسِنِينَ
“(Lomwe ndi) chiongoko ndi chifundo kwa ochita zabwino,
التفاسير العربية:
ٱلَّذِينَ يُقِيمُونَ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ يُوقِنُونَ
“Amene akupemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka (Zakaat) omwenso akutsimikiza za tsiku lachimaliziro.
التفاسير العربية:
أُوْلَـٰٓئِكَ عَلَىٰ هُدٗى مِّن رَّبِّهِمۡۖ وَأُوْلَـٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ
“Iwowo ali pa chiongoko chochokera kwa Mbuye wawo; ndipo iwowo ndiwo opambana.
التفاسير العربية:
وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يَشۡتَرِي لَهۡوَ ٱلۡحَدِيثِ لِيُضِلَّ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ بِغَيۡرِ عِلۡمٖ وَيَتَّخِذَهَا هُزُوًاۚ أُوْلَـٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٞ مُّهِينٞ
“Koma alipo ena mwa anthu amene akusankha nkhani ya bodza (ndi kumaifotokoza kwa anthu) ndi cholinga choti awasokeretse ku njira ya Allah popanda kuzindikira. Ndipo akuichitira zachipongwe (njira ya Allah yi). Iwo adzapeza chilango chowasambula.
التفاسير العربية:
وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ءَايَٰتُنَا وَلَّىٰ مُسۡتَكۡبِرٗا كَأَن لَّمۡ يَسۡمَعۡهَا كَأَنَّ فِيٓ أُذُنَيۡهِ وَقۡرٗاۖ فَبَشِّرۡهُ بِعَذَابٍ أَلِيمٍ
“Ndipo pamene Ayah Zathu zilakatulidwa kwa iye, akuzitembenuzira msana modzikuza ngati kuti sanazimve, ngati kutinso m’makutu mwake muli ugonthi. Choncho muuze nkhani ya chilango chopweteka.
التفاسير العربية:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّـٰلِحَٰتِ لَهُمۡ جَنَّـٰتُ ٱلنَّعِيمِ
“Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala ndi Minda yamtendere.
التفاسير العربية:
خَٰلِدِينَ فِيهَاۖ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٗاۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
“Adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Ili nlonjezo la Allah lomwe lili loona. Ndipo Iye Ngwamphamvu, Ngwanzeru zakuya.
التفاسير العربية:
خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ بِغَيۡرِ عَمَدٖ تَرَوۡنَهَاۖ وَأَلۡقَىٰ فِي ٱلۡأَرۡضِ رَوَٰسِيَ أَن تَمِيدَ بِكُمۡ وَبَثَّ فِيهَا مِن كُلِّ دَآبَّةٖۚ وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَنۢبَتۡنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوۡجٖ كَرِيمٍ
“Adalenga thambo popanda mizati yomwe mukuiona. Ndipo adaika mapiri m’nthaka kuti isakugwedezeni. Ndipo (Iye) adafalitsa nyama m’menemo zamitundu yosiyanasiyana. Ndipo tidatsitsa madzi kuchokera ku mitambo, choncho tidameretsa m’menemo (m’nthaka) mmera wokongola wamitundu yosiyanasiyana.
Imamu Ibnu Jarir Taburiyu adalemba m’buku lake kuti Anasi Bun Malik adati:- M’bale wa bambo anga, Anasi bun Nadhari sadakhale nawo pa nkhondo ya Badri, ndipo adati: “Sindidakhale pamodzi ndi Mtumiki pa nkhondo yoyamba. Ngati Allah atandifikitsa pa nkhondo ina Allah adzaona zimene ndidzachita pomenya nkhondo modzipereka.” Pa tsiku la nkhondo ya Uhud, pamene Asilamu adabalalikana kuthawa ndipo iye adati:- “E Allah! Ine ndikudzipatula ku zomwe achita awa, osakhulupilira. Ndiponso ndikudandaula mzimene achita awa, Asilamu amene athawa.” Kenako adayenda ndi lupanga lake nakumana ndi Saad bun Muadhi, nati: “E iwe Saad! Ine ndikumva fungo la ku Munda wa mtendere pafupi ndi phiri ili la Uhud.” Kenako adachita nkhondo kufikira adaphedwa. Ndipo Saad adati: “E iwe Mtumiki wa Allah! Sindinathe kuchita chimene iye adachita.” Anasi bun Malik adati: “Tidampeza ali m’gulu lophedwa uku ali ndi mabala okwanira 80, ena otemedwa ndi malupanga, ndipo ena olasidwa ndi mikondo ndi mipaliro. Sitidamzindikire kufikira pamene adadza mlongo wake naamzindikira kupyolera m’nsonga za zala zake.” Ndipo Anasi adatinso: “Tidali kukambirana kuti ndime iyi ikukamba za iye.”
التفاسير العربية:
هَٰذَا خَلۡقُ ٱللَّهِ فَأَرُونِي مَاذَا خَلَقَ ٱلَّذِينَ مِن دُونِهِۦۚ بَلِ ٱلظَّـٰلِمُونَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
“Izi (zonse) nzolengedwa za Allah. Choncho, tandisonyezani, nchiyani adalenga amene sali Allah. Koma odzichitira okha zoipa ali mkusokera koonekera.
التفاسير العربية:

وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا لُقۡمَٰنَ ٱلۡحِكۡمَةَ أَنِ ٱشۡكُرۡ لِلَّهِۚ وَمَن يَشۡكُرۡ فَإِنَّمَا يَشۡكُرُ لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن كَفَرَ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَنِيٌّ حَمِيدٞ
“Ndipo ndithu tidampatsa Luqmân nzeru (ndipo tidati kwa iye): “Thokoza Allah (pazimene wakupatsa).” Ndipo, amene athokoze, ndithu kuthokozako kumthandiza yekha, ndiponso amene akana (mtendere wa Allah pakusiya kuthokoza), ndithu Allah Ngwachikwanekwane, Ngotamandidwa.
التفاسير العربية:
وَإِذۡ قَالَ لُقۡمَٰنُ لِٱبۡنِهِۦ وَهُوَ يَعِظُهُۥ يَٰبُنَيَّ لَا تُشۡرِكۡ بِٱللَّهِۖ إِنَّ ٱلشِّرۡكَ لَظُلۡمٌ عَظِيمٞ
“Ndipo (akumbutse) pamene Luqmân adauza mwana wake akumulangiza: “E iwe mwana wanga! Usaphatikize Allah ndi mafano. Ndithu kumuphatikiza (Allah), ndi kuipitsa kwakukulu.”
التفاسير العربية:
وَوَصَّيۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ بِوَٰلِدَيۡهِ حَمَلَتۡهُ أُمُّهُۥ وَهۡنًا عَلَىٰ وَهۡنٖ وَفِصَٰلُهُۥ فِي عَامَيۡنِ أَنِ ٱشۡكُرۡ لِي وَلِوَٰلِدَيۡكَ إِلَيَّ ٱلۡمَصِيرُ
“Ndipo tamulangiza munthu kwa makolo ake (kuwachitira zabwino), mayi wake adatenga pathupi pake mofooka pamwamba pakufooka. (Adamuyamwitsa) ndi kumusiyitsa patapita zaka ziwiri, kuti: “Ndithokoze Ine ndi makolo ako, kwa Ine nkobwerera.” [21]
Awa ndi Ayuda amene adasakanikirana ndi osakhulupilira (akafiri) a Chiarabu ochokera mu mtundu wa Banu Quraidhwa omwe adali ndi mapangano ndi Mtumiki (s.a.w) okhalirana mwa mtendere. Koma pamene adaswa mapangano pothandizana ndi adani a Mtumiki kuthira nkhondo Asilamu Mtumiki Muhammad (s.a.w) adawapitira ku malinga awo. Ndipo ena adawapha, pomwe ena adawagwira monga akaidi a pankhondo.
التفاسير العربية:
وَإِن جَٰهَدَاكَ عَلَىٰٓ أَن تُشۡرِكَ بِي مَا لَيۡسَ لَكَ بِهِۦ عِلۡمٞ فَلَا تُطِعۡهُمَاۖ وَصَاحِبۡهُمَا فِي ٱلدُّنۡيَا مَعۡرُوفٗاۖ وَٱتَّبِعۡ سَبِيلَ مَنۡ أَنَابَ إِلَيَّۚ ثُمَّ إِلَيَّ مَرۡجِعُكُمۡ فَأُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
“Ndipo (makolo ako) ngati atakukakamiza kuti undiphatikize Ine ndi zomwe iwe sukuzidziwa, usawamvere; koma khala nawo pa dziko mwaubwino; ndipo tsatira njira ya amene atembenukira kwa Ine. Ndipo kenako kobwerera kwanu nkwa Ine. Choncho ndidzakuuzani zimene mudali kuchita.
التفاسير العربية:
يَٰبُنَيَّ إِنَّهَآ إِن تَكُ مِثۡقَالَ حَبَّةٖ مِّنۡ خَرۡدَلٖ فَتَكُن فِي صَخۡرَةٍ أَوۡ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ أَوۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ يَأۡتِ بِهَا ٱللَّهُۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَطِيفٌ خَبِيرٞ
““E iwe mwana wanga! Ndithu icho (chabwino ndi choipa cha munthu) ngakhale chitakhala cholemera ngati njere ya mpiru ndi kukhala mkati mwa thanthwe kapena m’kati mwa thambo, kapena mkati mwa nthaka, Allah adzachibweretsa (ndi kumulipira amene adachita). Ndithu Allah Ngodziwa zinthu zobisika, (ndiponso) Ngodziwa zinthu zoonekera.”
التفاسير العربية:
يَٰبُنَيَّ أَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ وَأۡمُرۡ بِٱلۡمَعۡرُوفِ وَٱنۡهَ عَنِ ٱلۡمُنكَرِ وَٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَآ أَصَابَكَۖ إِنَّ ذَٰلِكَ مِنۡ عَزۡمِ ٱلۡأُمُورِ
““E iwe mwana wanga! Pemphera Swala moyenera, lamula zabwino, letsa zoipa, ndipo pirira ndi masautso amene akukhudza. Ndithu zimenezo ndizinthu zofunika kuziikirapo mtima (munthu aliyense).”
التفاسير العربية:
وَلَا تُصَعِّرۡ خَدَّكَ لِلنَّاسِ وَلَا تَمۡشِ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَرَحًاۖ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ كُلَّ مُخۡتَالٖ فَخُورٖ
““Ndipo usatembenuze tsaya lako kwa anthu monyogodola, ndipo usayende pa dziko monyada. Ndithu Allah sakonda yense wodzitukumula, wonyada.”
التفاسير العربية:
وَٱقۡصِدۡ فِي مَشۡيِكَ وَٱغۡضُضۡ مِن صَوۡتِكَۚ إِنَّ أَنكَرَ ٱلۡأَصۡوَٰتِ لَصَوۡتُ ٱلۡحَمِيرِ
““Ndipo lingana m’kuyenda kwako (popanda kufulumira kwambiri kapena kuyenda pang’onopang’ono); ndipo tsitsa mawu ako, ndithu mawu oyipitsitsa ndi mawu a bulu.”
التفاسير العربية:

أَلَمۡ تَرَوۡاْ أَنَّ ٱللَّهَ سَخَّرَ لَكُم مَّا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَأَسۡبَغَ عَلَيۡكُمۡ نِعَمَهُۥ ظَٰهِرَةٗ وَبَاطِنَةٗۗ وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يُجَٰدِلُ فِي ٱللَّهِ بِغَيۡرِ عِلۡمٖ وَلَا هُدٗى وَلَا كِتَٰبٖ مُّنِيرٖ
“Kodi simuona kuti Allah adakugonjetserani zakumwamba ndi zapansi ndi kukukwaniritsirani chisomo Chake, choonekera ndi chobisika? Ndipo alipo ena mwa anthu amene akukangana pa za Allah popanda kuzindikira ngakhale chiongoko, ngakhalenso buku lounika.
Mu Ayah imeneyi, akazi a Mtumiki (s.a.w) akuuzidwa kuti iwo akachimwa, Allah adzawalanga chilango chachikulu kuposa momwe akadalangidwira akazi ena omwe sali akazi a Mtumiki (s.a.w). Izi nchifukwa chakuti, iwo ndi atsogoleri; chilichonse chomwe iwo achita, choipa kapena chabwino, chidzatsatidwa ndi ena. Akachita chabwino, Allah adzawapatsa malipiro aakulu. Ndipo akachita choipa, adzawalanga ndi chilango chachikulu. Choncho aliyense amene ndi mtsogoleri, aonetsetse kuti akuchita zolungama zokhazokha.
التفاسير العربية:
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱتَّبِعُواْ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ قَالُواْ بَلۡ نَتَّبِعُ مَا وَجَدۡنَا عَلَيۡهِ ءَابَآءَنَآۚ أَوَلَوۡ كَانَ ٱلشَّيۡطَٰنُ يَدۡعُوهُمۡ إِلَىٰ عَذَابِ ٱلسَّعِيرِ
“Ndipo akauzidwa kuti: “Tsatani zimene Allah watsitsa.” Akunena: “Koma tikutsata zimene tidawapeza nazo makolo athu.” Kodi ngakhale kuti satana akuwaitanira ku chilango cha Moto (woyaka, adzatsatirabe)?
التفاسير العربية:
۞وَمَن يُسۡلِمۡ وَجۡهَهُۥٓ إِلَى ٱللَّهِ وَهُوَ مُحۡسِنٞ فَقَدِ ٱسۡتَمۡسَكَ بِٱلۡعُرۡوَةِ ٱلۡوُثۡقَىٰۗ وَإِلَى ٱللَّهِ عَٰقِبَةُ ٱلۡأُمُورِ
“Ndipo amene akupereka nkhope yake kwa Allah (amene akugonjera Allah kwatunthu) ali ochita zabwino, ndiye kuti wagwira chogwilira cholimba. Ndipo mapeto a zinthu zonse nkwa Allah basi.
التفاسير العربية:
وَمَن كَفَرَ فَلَا يَحۡزُنكَ كُفۡرُهُۥٓۚ إِلَيۡنَا مَرۡجِعُهُمۡ فَنُنَبِّئُهُم بِمَا عَمِلُوٓاْۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ
“Koma amene sadakhulupirire (Allah ndi mtima wake) choncho kusakudandaulitse kusakhulupirira kwake. Kobwerera kwawo nkwa Ife basi. Kumeneko tidzawauza zimene adachita. Ndithu Allah Ngodziwa zonse zam’zifuwa.
التفاسير العربية:
نُمَتِّعُهُمۡ قَلِيلٗا ثُمَّ نَضۡطَرُّهُمۡ إِلَىٰ عَذَابٍ غَلِيظٖ
“Tikuwasangalatsa pang’ono (apo pa dziko lapansi). Kenako tidzawakankhira ku chilango chokhwima.
التفاسير العربية:
وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۚ قُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
“Ndipo ukawafunsa: “Ndani adalenga thambo ndi nthaka?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nena: “Kutamandidwa konse nkwa Allah.” Koma ambiri a iwo sadziwa.
التفاسير العربية:
لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡغَنِيُّ ٱلۡحَمِيدُ
“Zonse zakumwamba ndi za pansi, nza Allah. Ndithu Allah Ngwachikwanekwane, Ngotamandidwa.
التفاسير العربية:
وَلَوۡ أَنَّمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ مِن شَجَرَةٍ أَقۡلَٰمٞ وَٱلۡبَحۡرُ يَمُدُّهُۥ مِنۢ بَعۡدِهِۦ سَبۡعَةُ أَبۡحُرٖ مَّا نَفِدَتۡ كَلِمَٰتُ ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٞ
“Ndipo ndithu ngakhale mitengo yonse ili m’nthaka ikadakhala zolembera, ndipo nyanja (nkukhala inki), ndipo pambuyo pake ndikuionjezeranso (madzi ake) ndi nyanja zisanu ndi ziwiri, mawu a Allah sakadatha. Ndithu Allah Ngwamphamvu, Wanzeru zakuya.
Ndime iyi ikunenetsa kuti sikoyenera kwa Msilamu kutsata maganizo ake pa chinthu chimene Allah ndi Mtumiki walamulapo lamulo, koma afunika kutsatira lamulo la Allah ndi Mtumiki, ndipo asakhale ndi chifuniro pa zinthu zomwe nza chipembedzo koma agonjere zimene Allah walamula ndi Mtumiki Wake. Kunyoza lamulo la Allah ndi Mtumiki kumachititsa kuti munthu atayike.
التفاسير العربية:
مَّا خَلۡقُكُمۡ وَلَا بَعۡثُكُمۡ إِلَّا كَنَفۡسٖ وَٰحِدَةٍۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعُۢ بَصِيرٌ
“Kulengedwa kwanu, ngakhale kuukitsidwa kwanu m’manda sikuli kanthu koma kuli ngati (kulenga kapena kuukitsa kwa) munthu mmodzi. (Palibe chokanika kwa Allah). Ndithu Allah Ngwakumva, Ngopenya chilichonse.
التفاسير العربية:

أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ يُولِجُ ٱلَّيۡلَ فِي ٱلنَّهَارِ وَيُولِجُ ٱلنَّهَارَ فِي ٱلَّيۡلِ وَسَخَّرَ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَۖ كُلّٞ يَجۡرِيٓ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗى وَأَنَّ ٱللَّهَ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرٞ
“Kodi suona (kuona kolingalira) kuti Allah amalowetsa nthawi ya usiku mu usana, ndipo amalowetsa nthawi ya usana mu usiku; ndipo adagonjetsa dzuwa ndi mwezi. Chilichonse chikuyenda mwa nthawi imene idaikidwa? Ndithu Allah akudziwa zonse zimene mukuchita.
التفاسير العربية:
ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡحَقُّ وَأَنَّ مَا يَدۡعُونَ مِن دُونِهِ ٱلۡبَٰطِلُ وَأَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡعَلِيُّ ٱلۡكَبِيرُ
“Izi nchifukwa chakuti Allah, Iye Ngoona; ndipo zomwe akuzipembedza kusiya Iye, nzachabe. Ndipo ndithu Allah ndiye Wotukuka, Wamkulu.
التفاسير العربية:
أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱلۡفُلۡكَ تَجۡرِي فِي ٱلۡبَحۡرِ بِنِعۡمَتِ ٱللَّهِ لِيُرِيَكُم مِّنۡ ءَايَٰتِهِۦٓۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّكُلِّ صَبَّارٖ شَكُورٖ
“Kodi suona kuti zombo zikuyenda pa nyanja mwachisomo cha Allah kuti akusonyezeni zisonyezo Zake (zamtendere Wake)? Ndithu M’zimenezo muli zisonyezo kwa yense wopirira, wothokoza.
التفاسير العربية:
وَإِذَا غَشِيَهُم مَّوۡجٞ كَٱلظُّلَلِ دَعَوُاْ ٱللَّهَ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ فَلَمَّا نَجَّىٰهُمۡ إِلَى ٱلۡبَرِّ فَمِنۡهُم مُّقۡتَصِدٞۚ وَمَا يَجۡحَدُ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَّا كُلُّ خَتَّارٖ كَفُورٖ
“Ndipo mafunde onga mitambo akawavindikira, amampempha Allah modzipereka kwambiri. Koma akawapulumutsira ku ntunda, ena a iwo amachita zolungama (koma ena a iwo amakana mtendere wa Allah). Ndipo sangazikane zisonyezo zathu koma yense wachinyengo wosathokoza.
التفاسير العربية:
يَـٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ٱتَّقُواْ رَبَّكُمۡ وَٱخۡشَوۡاْ يَوۡمٗا لَّا يَجۡزِي وَالِدٌ عَن وَلَدِهِۦ وَلَا مَوۡلُودٌ هُوَ جَازٍ عَن وَالِدِهِۦ شَيۡـًٔاۚ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞۖ فَلَا تَغُرَّنَّكُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا وَلَا يَغُرَّنَّكُم بِٱللَّهِ ٱلۡغَرُورُ
“E inu anthu! Muopeni Mbuye wanu (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa); ndipo liopeni tsiku limene kholo silidzathandiza mwana wake, ngakhalenso mwana sadzathandiza kholo lake chilichonse. Ndithu lonjezo la Allah ndiloona; choncho usakunyengeni moyo wa dziko lapansi, ndiponso asakunyengeni mdyerekezi pa za Allah.
التفاسير العربية:
إِنَّ ٱللَّهَ عِندَهُۥ عِلۡمُ ٱلسَّاعَةِ وَيُنَزِّلُ ٱلۡغَيۡثَ وَيَعۡلَمُ مَا فِي ٱلۡأَرۡحَامِۖ وَمَا تَدۡرِي نَفۡسٞ مَّاذَا تَكۡسِبُ غَدٗاۖ وَمَا تَدۡرِي نَفۡسُۢ بِأَيِّ أَرۡضٖ تَمُوتُۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمٌ خَبِيرُۢ
“Ndithu kudziwa kwa nthawi (yakutha kwa dziko) kuli ndi Allah (Yekha). Iye ndiamene amavumbitsa mvula (nthawi imene wafuna); ndipo akudziwa zimene zili m’ziberekero. Ndipo aliyense sadziwa chomwe apeze mawa; (chabwino kapena choipa); ndiponso sadziwa aliyense kuti ndi dziko liti adzafera. Ndithu Allah Ngodziwa zedi, Ngozindikira kwambiri.
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: لقمان
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق