للإطلاع على الموقع بحلته الجديدة

ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - خالد إبراهيم بتيالا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: الشورى   آية:
وَٱلَّذِينَ يُحَآجُّونَ فِي ٱللَّهِ مِنۢ بَعۡدِ مَا ٱسۡتُجِيبَ لَهُۥ حُجَّتُهُمۡ دَاحِضَةٌ عِندَ رَبِّهِمۡ وَعَلَيۡهِمۡ غَضَبٞ وَلَهُمۡ عَذَابٞ شَدِيدٌ
Ndipo amene akutsutsana ndi Allah pambuyo povomerezedwa (ndi anthu ambiri), mtsutso wawo ndiwachabe kwa Mbuye wawo; mkwiyo waukulu (wa Allah) uli pa iwo. Ndipo iwo adzakhala ndi chilango chokhwima.
التفاسير العربية:
ٱللَّهُ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ ٱلۡكِتَٰبَ بِٱلۡحَقِّ وَٱلۡمِيزَانَۗ وَمَا يُدۡرِيكَ لَعَلَّ ٱلسَّاعَةَ قَرِيبٞ
Allah ndi Amene wavumbulutsa buku (la Qur’an ndi mabuku ena) moona ndi mwachilungamo. Nanga nchiyani chikudziwitse kuti mwina Qiyâma ili pafupi?
التفاسير العربية:
يَسۡتَعۡجِلُ بِهَا ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِهَاۖ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مُشۡفِقُونَ مِنۡهَا وَيَعۡلَمُونَ أَنَّهَا ٱلۡحَقُّۗ أَلَآ إِنَّ ٱلَّذِينَ يُمَارُونَ فِي ٱلسَّاعَةِ لَفِي ضَلَٰلِۭ بَعِيدٍ
Akuifulumizitsa amene sakuikhulupirira; koma amene akhulupirira ali oopa za iyo, ndipo akudziwa kuti imeneyo ndiyoonadi, (za kupezeka kwake palibe chikaiko). Dziwani kuti ndithu amene akutsutsana za nthawi (ya Qiyâma) ali mkusokera konka nako kutali.
التفاسير العربية:
ٱللَّهُ لَطِيفُۢ بِعِبَادِهِۦ يَرۡزُقُ مَن يَشَآءُۖ وَهُوَ ٱلۡقَوِيُّ ٱلۡعَزِيزُ
Allah Ngoleza kwa akapolo (Ake). Amapereka rizq kwa amene wamfuna. Ndipo Iye ndi Wamphamvu zoposa, Wopambana.
التفاسير العربية:
مَن كَانَ يُرِيدُ حَرۡثَ ٱلۡأٓخِرَةِ نَزِدۡ لَهُۥ فِي حَرۡثِهِۦۖ وَمَن كَانَ يُرِيدُ حَرۡثَ ٱلدُّنۡيَا نُؤۡتِهِۦ مِنۡهَا وَمَا لَهُۥ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ مِن نَّصِيبٍ
Amene akufuna (pantchito yake) zokolola za tsiku lachimaliziro, timuonjezera zokolola zakezo; ndipo amene akufuna pa ntchito yake yabwino zokolola za chisangalalo cha m’dziko lapansi timpatsa chimene chidagawidwa kwa iye, ndipo iye sadzakhala ndi gawo (la zabwino) pa tsiku lachimaliziro.
التفاسير العربية:
أَمۡ لَهُمۡ شُرَكَٰٓؤُاْ شَرَعُواْ لَهُم مِّنَ ٱلدِّينِ مَا لَمۡ يَأۡذَنۢ بِهِ ٱللَّهُۚ وَلَوۡلَا كَلِمَةُ ٱلۡفَصۡلِ لَقُضِيَ بَيۡنَهُمۡۗ وَإِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ لَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ
Kodi iwo alinayo milungu imene idawakhazikitsira m’zipembedzo zimene Allah sadaziloleze? Ndipo pakadapanda kutsogola (lonjezo lochedwetsa) liwu la chiweruziro (mpaka pa tsiku la Qiyâma); pakadaweruzidwa pakati pawo (okanira ndi okhulupirira pompano pa dziko lapansi). Ndipo ndithu opondereza chawo nchilango chowawa.
التفاسير العربية:
تَرَى ٱلظَّٰلِمِينَ مُشۡفِقِينَ مِمَّا كَسَبُواْ وَهُوَ وَاقِعُۢ بِهِمۡۗ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فِي رَوۡضَاتِ ٱلۡجَنَّاتِۖ لَهُم مَّا يَشَآءُونَ عِندَ رَبِّهِمۡۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَضۡلُ ٱلۡكَبِيرُ
Udzawaona (tsiku la Qiyâma) amene adadzichitira okha zoipa (popembedza mafano) akuopa chifukwa cha (zoipa) zomwe adachita, ndipo (chilangocho) chidzawapezabe. Koma amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino (udzawaona akusangalala) m’Madimba abwino a ku Minda ya mtendere. Iwo akapeza chilichonse chimene akafune kwa Mbuye wawo. Umenewo ndiwo ulemelero wawukulu.
التفاسير العربية:
 
ترجمة معاني سورة: الشورى
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - خالد إبراهيم بتيالا - فهرس التراجم

ترجمها خالد إبراهيم بيتالا.

إغلاق