ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني آية: (20) سورة: المائدة
وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ ٱذۡكُرُواْ نِعۡمَةَ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ إِذۡ جَعَلَ فِيكُمۡ أَنۢبِيَآءَ وَجَعَلَكُم مُّلُوكٗا وَءَاتَىٰكُم مَّا لَمۡ يُؤۡتِ أَحَدٗا مِّنَ ٱلۡعَٰلَمِينَ
(Ndipo kumbukirani) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Inu anthu anga! Kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu, pamene adawachita ena mwa inu kukhala aneneri; ndipo adakuchitani kukhala mafumu (pambuyo poti mudali onyozeka m’dziko la Iguputo m’manja mwa Farawo). Ndipo wakupatsani zomwe sadampatsepo aliyense mwa zolengedwa.” [162]
[162] Mndime iyi akukumbutsa Ayuda chisomo chachikulu chomwe Allah adawadalitsa nacho. Kuyamika zomwe Allah watichitira nkofunika kwabasi. Tisakhale ngati anzathu awa amene Allah adawadalitsa ndimadalitso osiyanasiyana koma osamthokoza, ndiponso osamkonda ndi chikondi chochokera pansi pamtima.
التفاسير العربية:
 
ترجمة معاني آية: (20) سورة: المائدة
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق