Check out the new design

আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা * - অনুবাদসমূহৰ সূচীপত্ৰ


অৰ্থানুবাদ ছুৰা: আল-আনআম   আয়াত:
وَلَوۡ جَعَلۡنَٰهُ مَلَكٗا لَّجَعَلۡنَٰهُ رَجُلٗا وَلَلَبَسۡنَا عَلَيۡهِم مَّا يَلۡبِسُونَ
Ndipo tikadampanga iyeyo kukhala mngelo, tikadamsandutsa kukhala munthu (chifukwa iwo sangathe kumuona mngelo), ndipo tikadati asakanikirane nawo monga momwe eni amasakanikirana (kotero kuti sakadamdziwa kuti mngelo ndi uyu).
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
وَلَقَدِ ٱسۡتُهۡزِئَ بِرُسُلٖ مِّن قَبۡلِكَ فَحَاقَ بِٱلَّذِينَ سَخِرُواْ مِنۡهُم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Ndithudi, adachitidwa chipongwe atumiki patsogolo pako; koma (mapeto ake) aja mwa iwo omwe adachita chipongwe zidawazinga zomwe adali kuzichitira chipongwe.
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
قُلۡ سِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ ثُمَّ ٱنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُكَذِّبِينَ
Nena: “Yendani pa dziko, kenako tayang’anani momwe adalili mapeto a otsutsa.” [170]
[170] Apa tanthauzo nkuti tayendani padziko mukayang’ane ndi kulingalira zilango zopweteka zimene zidawatsikira anthu akale. Kuyang’ana ndi kulingalira zoterezo kuti zikhale phunziro kwa inu kuti musachitenso zimene zidawagwetsa kuchionongeko.
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
قُل لِّمَن مَّا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ قُل لِّلَّهِۚ كَتَبَ عَلَىٰ نَفۡسِهِ ٱلرَّحۡمَةَۚ لَيَجۡمَعَنَّكُمۡ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَا رَيۡبَ فِيهِۚ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ فَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Nena (mowafunsa): “Nzayani zomwe zili kumwamba ndi pansi?” Nena kwa iwo (ngati sakuyankha): “Nza Allah.” Iye wadzikakamiza kuwachitira chifundo (anthu Ake). (Pachifukwa chimenechi amawapatsa nthawi osawalanga mwachangu). Ndithudi adzakusonkhanitsani tsiku la Qiyâma lopanda chikaiko. Amene adzitaya okha, sakhulupirira (za tsikulo).
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
۞ وَلَهُۥ مَا سَكَنَ فِي ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِۚ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
Nza Iye (Allah) zonse zili mu nthawi ya usiku ndi usana. Iye Ngwakumva, Ngodziwa.
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
قُلۡ أَغَيۡرَ ٱللَّهِ أَتَّخِذُ وَلِيّٗا فَاطِرِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَهُوَ يُطۡعِمُ وَلَا يُطۡعَمُۗ قُلۡ إِنِّيٓ أُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ أَوَّلَ مَنۡ أَسۡلَمَۖ وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ
Nena: “Ndidzipangire mtetezi wanga kusiya Allah, Mlengi wa thambo ndi nthaka? Iye Njemwe amadyetsa ndipo sadyetsedwa.” Nena: “Ndalamulidwa kukhala woyamba mwa olowa m’Chisilamu.” Ndipo (ndauzidwa kuti): “Usakhale mwa ophatikiza (Allah ndi mafano)”
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
قُلۡ إِنِّيٓ أَخَافُ إِنۡ عَصَيۡتُ رَبِّي عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٖ
Nena (kwa iwo): “Ine ndikuopa chilango cha tsiku lalikulu ngati ndinyoza Mbuye wanga.”
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
مَّن يُصۡرَفۡ عَنۡهُ يَوۡمَئِذٖ فَقَدۡ رَحِمَهُۥۚ وَذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡمُبِينُ
Yemwe adzapewetsedwe ku chilangocho tsiku limenelo, ndiye kuti wamchitira chifundo; kumeneko nkupambana kowonekera.
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
وَإِن يَمۡسَسۡكَ ٱللَّهُ بِضُرّٖ فَلَا كَاشِفَ لَهُۥٓ إِلَّا هُوَۖ وَإِن يَمۡسَسۡكَ بِخَيۡرٖ فَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
Ngati Allah atakukhudza ndi mazunzo, palibe aliyense angathe kukuchotsera, koma Iye basi; ndipo ngati atakukhudza ndi zabwino (palibe amene angakutsekereze ku zabwinozo). Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse.[171]
[171] Mu Ayah iyi Allah akuuza Mtumiki Wake ndi omtsatira ake kuti ngati masautso, umphawi ndi matenda zitampeza, palibe amene angamchotsere zimenezi koma Allah basi. Ndiponso ngati zitamkhudza zabwino, monga kukhala ndi moyo wangwiro ndi chuma chambiri, palibe amene angazichotse zimenezi kwa iye ngati Allah safuna. Choncho tiyeni tiike chikhulupiliro chathu chonse mwa Allah.
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
وَهُوَ ٱلۡقَاهِرُ فَوۡقَ عِبَادِهِۦۚ وَهُوَ ٱلۡحَكِيمُ ٱلۡخَبِيرُ
Iye ndi Mgonjetsi pa anthu ake (onse); Iye Ngwanzeru zakuya, Wodziwa nkhani zonse.
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
 
অৰ্থানুবাদ ছুৰা: আল-আনআম
ছুৰাৰ তালিকা পৃষ্ঠা নং
 
আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা - অনুবাদসমূহৰ সূচীপত্ৰ

ইয়াক অনুবাদ কৰিছে খালিদ ইব্ৰাহিম বিতালা।

বন্ধ