Check out the new design

আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা * - অনুবাদসমূহৰ সূচীপত্ৰ


অৰ্থানুবাদ ছুৰা: আল-আ'ৰাফ   আয়াত:
۞ وَإِذۡ نَتَقۡنَا ٱلۡجَبَلَ فَوۡقَهُمۡ كَأَنَّهُۥ ظُلَّةٞ وَظَنُّوٓاْ أَنَّهُۥ وَاقِعُۢ بِهِمۡ خُذُواْ مَآ ءَاتَيۡنَٰكُم بِقُوَّةٖ وَٱذۡكُرُواْ مَا فِيهِ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ
Ndipo(akumbutse) pamene tidalizula phiri ndikulinyamula pamwamba pawo monga denga (kapena mtambo umene wawavindikira) natsimikiza kuti liwagwera, (tidawauza): “Landirani, mwamphamvu malamulo amene takupatsani, ndipo kumbukirani zomwe zili m’menemo (pozitsata ndi kuzichita); kuti inu muope.”
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
وَإِذۡ أَخَذَ رَبُّكَ مِنۢ بَنِيٓ ءَادَمَ مِن ظُهُورِهِمۡ ذُرِّيَّتَهُمۡ وَأَشۡهَدَهُمۡ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡ أَلَسۡتُ بِرَبِّكُمۡۖ قَالُواْ بَلَىٰ شَهِدۡنَآۚ أَن تَقُولُواْ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ إِنَّا كُنَّا عَنۡ هَٰذَا غَٰفِلِينَ
Ndipo (kumbukirani) pamene Mbuye wako adawatulutsa ana a Adam m’misana ya atate awo ndi kuwachititsa umboni okha (powauza kuti): “Kodi Ine sindine Mbuye wanu?” Iwo adati: “Inde tikuikira umboni (kuti Inuyo ndiye Mbuye wathu).” (Allah adawauza kuti): “Kuopera kuti mungadzanene tsiku louka kwa akufa: “Ife sitidali kuzindikira chipanganochi.”
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
أَوۡ تَقُولُوٓاْ إِنَّمَآ أَشۡرَكَ ءَابَآؤُنَا مِن قَبۡلُ وَكُنَّا ذُرِّيَّةٗ مِّنۢ بَعۡدِهِمۡۖ أَفَتُهۡلِكُنَا بِمَا فَعَلَ ٱلۡمُبۡطِلُونَ
Kapena mungadzati: “Makolo athu ndi amene adapembedza mafano kale, ndipo ife tidali ana odza pambuyo pawo (choncho tidawatsatira pazimene ankachita). Kodi nanga mutiononga chifukwa cha zomwe adachita oipa?”
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
وَكَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ وَلَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ
M’menemo ndi momwe tikulongosolera mokwanira zivumbulutso kuti mwina iwo angabwelere (kwa Allah).
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
وَٱتۡلُ عَلَيۡهِمۡ نَبَأَ ٱلَّذِيٓ ءَاتَيۡنَٰهُ ءَايَٰتِنَا فَٱنسَلَخَ مِنۡهَا فَأَتۡبَعَهُ ٱلشَّيۡطَٰنُ فَكَانَ مِنَ ٱلۡغَاوِينَ
Ndipo alakatulire nkhani za yemwe tidampatsa zizindikiro zathu nadzichotsa m’menemo (m’zizindikiromo), ndipo satana anamtsata, choncho adali m’gulu la osokera.
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
وَلَوۡ شِئۡنَا لَرَفَعۡنَٰهُ بِهَا وَلَٰكِنَّهُۥٓ أَخۡلَدَ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ وَٱتَّبَعَ هَوَىٰهُۚ فَمَثَلُهُۥ كَمَثَلِ ٱلۡكَلۡبِ إِن تَحۡمِلۡ عَلَيۡهِ يَلۡهَثۡ أَوۡ تَتۡرُكۡهُ يَلۡهَثۚ ذَّٰلِكَ مَثَلُ ٱلۡقَوۡمِ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَاۚ فَٱقۡصُصِ ٱلۡقَصَصَ لَعَلَّهُمۡ يَتَفَكَّرُونَ
Ndipo tikadafuna tikadamtukula nazo (ulemelero wake). Koma iye adapendekera ku za mdziko natsatira zilakolako zake. Fanizo lake lili ngati galu. Ngati utamkalipira amathawa uku akutulutsa lirime lake kunja. Ngakhale utamsiya amatulutsabe kunja lirime lake. Umo ndi momwe liliri fanizo la anthu otsutsa zizindikiro Zathu. Choncho asimbire nkhani izi kuti angalingalire.
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
سَآءَ مَثَلًا ٱلۡقَوۡمُ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَأَنفُسَهُمۡ كَانُواْ يَظۡلِمُونَ
Taonani kuipa fanizo la anthu omwe atsutsa zizindikiro Zathu ndi kudzichitira okha zoipa.
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
مَن يَهۡدِ ٱللَّهُ فَهُوَ ٱلۡمُهۡتَدِيۖ وَمَن يُضۡلِلۡ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ
Amene Allah wamuongola ndiye woongoka. Ndipo amene wamulekelera kusokera (chifukwa chakusatsatira kwake malangizo a Allah), iwo ndiwo otaika (oonongeka).
আৰবী তাফছীৰসমূহ:
 
অৰ্থানুবাদ ছুৰা: আল-আ'ৰাফ
ছুৰাৰ তালিকা পৃষ্ঠা নং
 
আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা - অনুবাদসমূহৰ সূচীপত্ৰ

ইয়াক অনুবাদ কৰিছে খালিদ ইব্ৰাহিম বিতালা।

বন্ধ